LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • kr nkhani 12 nkhani 118-131
  • Gulu Lotumikila “Mulungu Wamtendele”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Gulu Lotumikila “Mulungu Wamtendele”
  • Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “Ndidzaika Mtendele Kuti Ukhale Ngati Wokuyang’anila”
  • Mmene Kristu Amatsogolela Mpingo
  • “Mukhale Zitsanzo kwa Gulu la Nkhosa”
  • Mmene Akulu Amawetela Nkhosa za Mulungu Masiku Ano
  • Uyang’anilo Wabwino Umalimbikitsa Mgwilizano wa Anthu a Mulungu
  • Oyang’anila Oweta Nkhosa za Mulungu
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Abusa, Tsanzilani Abusa Aakulu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Dongosolo la Mpingo
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Kodi Akulu Amatumikila Mpingo m’Njila Ziti?
    Ndani Amene Akucita Cifunilo Ca Yehova Masiku Ano?
Ufumu wa Mulungu Ukulamulila
kr nkhani 12 nkhani 118-131

NKHANI 12

Gulu Lotumikila “Mulungu Wamtendele”

ZIMENE ZILI M’NKHANI INO

Mmene Yehova wakonzela gulu lake pang’onopang’ono

1, 2. Kodi magazini a Zion’s Watch Tower anasintha bwanji mu January 1895? Nanga abale anamva bwanji ataona kusinthako?

WOPHUNZILA Baibulo wina wacangu wochedwa John A. Bohnet anasangalala ndi zimene anaona pamene analandila magazini ya Zion’s Watch Tower ya January 1895. Magaziniyo inali ndi cikuto catsopano, ndipo pacikutopo panali cithunzi ca nyumba ya nsanja yokhala ndi nyale yowala kwambili usiku. Nyumba ya nsanjayo inali pakati pa nyanja ya mafunde. M’magaziniyo munali cilengezo cokhudza kusintha kwa cithunzi ca pa magazini. Cilengezoco cinali ndi mutu wakuti “Kaonekedwe Katsopano ka Magazini Athu.”

2 M’bale Bohnet anasangalala kwambili, ndipo analembela kalata M’bale Russell kuti: “Ndasangalala kuona mmene magazini a WATCH TOWER akongolela. Akuoneka bwino kwambili.” Wophunzila Baibulo wina wokhulupilika dzina lake John H. Brown analembanso maganizo ake ponena za cithunzi ca pacikutoco. Iye anati: “Cithunzici cikuoneka mwapadela kwambili. Ngakhale kuti nyumba ya nsanjayi ikuombedwa ndi mafunde ndiponso cimphepo ca mkuntho, maziko ake akuoneka kukhala olimba kwambili.” Cimeneci cinali ciyambi cabe ca kusintha kwa cikuto ca magazini. M’mwezi wa November caka cimeneco, abale athu anaonanso kusintha kwina kwakukulu pa cithunzi ca pacikuto ca magazini. Koma zocititsa cidwi ndi kusinthako zinali zakuti cithunzico cinali kuonetsanso cimphepo ca mkuntho panyanja.

3, 4. Ndi vuto liti limene Nsanja ya Mlonda ya November 1895 inafotokoza? Nanga magaziniyo inalengeza kuti padzakhala kusintha kwakukulu kotani?

3 Nkhani imene inatuluka m’magazini ya Watch Tower ya November 15, 1895, inafotokoza mwatsatanetsatane za vuto limene linalipo. Magaziniyo inanena kuti panali mavuto ena amene anali kusokoneza mtendele pakati pa Ophunzila Baibulo. Mavutowo anali monga cimphepo ca mkuntho. Kaŵilikaŵili abale anali kukangana pankhani yokhudza amene ayenela kutsogolela pampingo. Pofuna kuthandiza abale kuthetsa mzimu wogawanitsa anthu umenewu, nkhaniyo inayelekezela gulu la Mulungu ndi combo. Ndipo inanenanso mosapita m’mbali kuti abale amene anali kutsogolela panthawiyo, anali atalephela kukonzekeletsa gulu la Mulungu kaamba ka mavuto. Kodi io anayenela kucita ciani?

4 Nkhani ya m’magaziniyo inafotokoza kuti woyendetsa combo waluso amaonetsetsa kuti wanyamula zovala zothandiza anthu kuti asamile pakacitika ngozi. Amaonetsetsanso kuti ogwila nchito m’combomo, ndi okonzekela ngozi iliyonse imene angakumane nayo panthawi ya cimphepo camkuntho. Mofananamo, abale amene anali kutsogolela gulu anafunika kukonzekeletsa mipingo yonse kaamba ka mavuto amene anali kubwela mtsogolo. Kuti zimenezo zitheke, nkhaniyo inafotokoza za kusintha kwakukulu kumene kunayenela kucitika. Inakamba kuti kuyambila nthawiyo, “akulu anayenela kusankhidwa mumpingo uliwonse kuti ‘aziyang’anila’ nkhosa.”—Mac. 20:28.

5. (a) N’cifukwa ciani makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu anali a panthawi yake? (b) Kodi tikambilana mafunso ati?

5 Makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu anali a panthawi yake cifukwa anathandiza kuti mipingo ikhale yolimba. Makonzedwewa anathandizanso abale kupilila mavuto amene anakumana nao pa Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse. M’zaka zotsatilapo, panakhalanso kusintha kwina m’gulu kumene kunathandiza anthu a Mulungu kutumikila Yehova bwino lomwe. Kodi ndi ulosi wa m’Baibulo uti umene unanenelatu za zocitikazi? Ndi kusintha kotani kumene inu mwaona kukucitika m’gulu? Kodi mwapindula bwanji ndi kusintha kumeneko?

“Ndidzaika Mtendele Kuti Ukhale Ngati Wokuyang’anila”

6, 7. (a) Kodi lemba la Yesaya 60:17 limatanthauza ciani? (b) Kodi mau akuti “wokuyang’anila” ndi “wokupatsa nchito” amasonyeza ciani?

6 Monga mmene tinaphunzilila m’Nkhani 9, Yesaya analosela kuti Yehova adzaculukitsa anthu ake. (Yes. 60:22) Kupyolela mwa Yesaya, Yehova analonjezanso kuti adzacita zinthu zina zambili. Mu ulosi womwewo, Iye anati: “M’malo mwa mkuwa, ndidzabweletsa golide. M’malo mwa citsulo, ndidzabweletsa siliva. M’malo mwa mtengo, ndidzabweletsa mkuwa ndipo m’malo mwa miyala, ndidzabweletsa citsulo. Ndidzaika mtendele kuti ukhale ngati wokuyang’anila, ndi cilungamo kuti cikhale ngati wokupatsa nchito.” (Yes. 60:17) Kodi ulosi umenewu umatanthauzanji? Kodi umatikhudza bwanji masiku ano?

Kusinthako ndi kusintha cinthu cabwino kuti cikhale cabwino kwambili

7 Ulosi wa Yesaya unasonyeza kuti cinthu cina cidzalowedwa m’malo ndi cina. Onani kuti kusinthako ndi kusintha cinthu cabwino kale kuti cikhale cabwino kwambili. Ngati golide aloŵa m’malo mwa mkuwa ndiye kuti zinthu zikuyenda bwino, cimodzimodzinso ndi zinthu zina zomwe zachulidwa mu ulosiwu. Ndi mau ophiphilitsa amenewa, Yehova analosela kuti zinthu pakati pa anthu ake zidzakhala bwino kwambili m’kupita kwa nthawi. Kodi ulosiwu ukunena za kusintha kotani? Pochula “wokuyang’anila” ndi “wokupatsa nchito,” Yehova anasonyeza kuti anthu ake adzayamba kusamalidwa ndi kutsogoleledwa bwino kwambili.

8. (a) Ndani amene akucititsa masinthidwe olembedwa mu ulosi wa Yesaya? (b) Kodi timapindula bwanji cifukwa ca masinthidwewo? (Onani bokosi lakuti “Analandila Uphungu Modzicepetsa.”)

8 Kodi ndani amapangitsa kusinthaku? Mu ulosiwo, Yehova anati: “Ndidzabweletsa golide, . . . ndidzabweletsa siliva, . . . ndidzaika mtendele.” Zoonadi, Yehova ndi amene wacititsa kuti zinthu zisinthe m’gulu lake osati anthu. Ndipo kucokela pamene Yesu anakhala Mfumu, Yehova wakhala akusintha zinthu m’gulu lake kupyolela mwa Mwana wakeyo. Kodi timapindula bwanji ndi kusinthako? Lembalo limasonyeza kuti kusinthako kudzabweletsa “mtendele” ndi “cilungamo.” Tikamagonjela citsogozo ca Mulungu ndi kusintha zinthu zina paumoyo wathu, timakhala ndi mtendele pakati pathu. Ndipo kukonda cilungamo kumatipangitsa kutumikila Yehova amene ndi “Mulungu wamtendele,” mogwilizana ndi mau a mtumwi Paulo.—Afil. 4:9.

9. N’ciani cimathandiza kuti mumpingo mukhale dongosolo ndi mgwilizano? N’cifukwa ciani mwayankha telo?

9 Ponena za Yehova, mtumwi Paulo analemba kuti: “Mulungu si Mulungu wacisokonezo, koma wamtendele.” (1 Akor. 14:33) Pa lembali, Mtumwi Paulo sanasiyanitse khalidwe lacisokonezo ndi khalidwe ladongosolo. M’malo mwake, iye anasiyanitsa khalidwe lacisokonezo ndi khalidwe lamtendele. N’cifukwa ciani anatelo? Cifukwa cakuti ngati zinthu zikuyenda mwadongosolo sizitanthauza kuti nthawi zonse pamakhala mtendele. Mwacitsanzo, gulu la asilikali lingayende mwadongosolo kudela la nkhondo. Koma ngakhale ayende mwadongosolo, zotsatilapo zake zimakhala nkhondo osati mtendele. Motelo, monga Akristu, nthawi zonse tiyenela kukumbukila mfundo yofunika iyi: Gulu lililonse la anthu amene pakati pao palibe mtendele, m’kupita kwa nthawi limasokonezeka kapena kutha kumene. Mosiyana ndi zimenezi, mtendele wa Mulungu umalimbikitsa mzimu wa dongosolo umene umakhalitsa. Conco, ndife osangalala kuti tili m’gulu limene limatsogoleledwa ndi kuyengedwa ndi “Mulungu amene amapatsa mtendele.” (Aroma 15:33) Mtendele umene Mulungu amapeleka umapangitsa kuti m’mipingo yathu padziko lonse lapansi mukhale dongosolo ndi mgwilizano wolimba umene timasangalala nao.—Sal. 29:11.

10. (a) Ndi masinthidwe otani amene anacitika m’gulu lathu m’nthawi ya Ophunzila Baibulo? (Onani bokosi lakuti “Mmene Zinthu Zinasinthila Pankhani ya Kuyang’anila Mpingo.”) (b) Kodi tikambilana mafunso otani tsopano?

10 Bokosi lamutu wakuti, “Mmene Zinthu Zinasinthila Pankhani ya Kuyang’anila Mpingo” likufotokoza za kusintha kumene kunathandiza kuti zinthu ziziyenda mwadongosolo mumpingo m’nthawi ya Ophunzila Baibulo. Koma kodi Yehova posacedwapa wasintha zinthu ziti m’gulu kupyolela mwa Mfumu yathu? Kodi kusintha makonzedwe okhudza anthu amene ayenela kukhala oyang’anila, kwalimbikitsa motani mtendele ndi mgwilizano m’mipingo padziko lonse lapansi? Nanga kusinthako kumakuthandizani bwanji inuyo panokha potumikila “Mulungu wamtendele”?

Mmene Kristu Amatsogolela Mpingo

11. (a) Ndi masinthidwe otani okhudza kamvedwe kathu amene anakhalapo pambuyo pophunzila Malemba? (b) Kodi abale a m’bungwe lolamulila anali otsimikiza mtima kucita ciani?

11 Kuyambila mu 1964 mpaka mu 1971, bungwe lolamulila linali kuyang’anila nchito yophunzila Baibulo mwakuya n’colinga cakuti amvetsetse zinthu zina zambili. Cimodzi mwa zinthu zimene anali kufuna kudziŵa ndi mmene mpingo wacikristu wa m’nthawi ya atumwi unali kuyendela.a Pakafufuku amene anacita, io anadziŵa kuti m’nthawi ya atumwi, mipingo inali kuyang’anilidwa ndi bungwe la akulu osati mkulu kapena woyang’anila mmodzi. (Ŵelengani Afilipi 1:1; 1 Timoteyo 4:14.) Pamene abale anamvetsetsa mfundoyo, bungwe lolamulila linazindikila kuti Mfumu yao, Yesu, inali kuwatsogolela kuti akonze kayendetsedwe ka gulu la Mulungu. Motelo, abale a m’bungwe lolamulila anali ofunitsitsa kutsatila citsogozo ca Mfumuyo. Mwamsanga io anasintha zinthu zina n’colinga cakuti aziika akulu mogwilizana ndi mmene Malemba amanenela. Kodi ndi zinthu zina ziti zimene zinasintha kuciyambi kwa zaka za m’ma 1970?

ANALANDILA UPHUNGU MODZICEPETSA

M’MAGAZINI ya The Watch Tower ya Cifinishi ya April 1, 1916, munali kalata yocokela kwa M’bale Russell. Kalatayo inali kupita kwa m’bale Kaarlo Harteva ndi abale ena a ku Scandinavia. M’kalatayo munali mau akuti: “Inu nonse abale athu okondedwa m’cikhulupililo, tikulimbikitsani kuti mubwelele m’coonadi ndi kucita nchito yofunika kwambili masiku ano.” N’cifukwa ciani M’bale Russell anawacondelela conco?

Kaarlo Harteva

Kaarlo Harteva

M’bale Harteva, amene anabadwa mu 1882, anali mmodzi wa Ophunzila Baibulo oyambilila ku Finland. Iye anabatizidwa mu April 1910, ndipo mu August 1912, M’bale Russell analola m’baleyu kuti azisindikiza magazini ya The Watch Tower mu Cifinishi. Zinthu zonse zinali kuyenda bwino mpaka pamene Nkhondo Yoyamba Yapadziko Lonse inayamba. M’magazini ya The Watch Tower ya December 1, 1914, M’bale Harteva analemba kuti: “Popeza kuti pakhalako vuto la za ndalama, . . . mwina magazini ya The Watch Tower idzayamba kukhala ndi masamba ocepa, ndipo siizituluka kaŵilikaŵili monga momwe yakhala ikutulukila m’buyomu.” Komabe mu 1915, M’bale Harteva ndi abale ena anapanga bungwe lochedwa Ararat ndi colinga cakuti azipeza ndalama. Bungwelo linayamba kufalitsa magazini ochedwa Ararat.

Pamene M’bale Harteva anayamba kuika maganizo ake onse pa bungwe latsopanoli ndi pa magazini atsopano, m’bale wina anayamba kulemba magazini ya The Watch Tower ya Cifinishi. Magazini a Ararat anali kufalitsa nkhani zofotokoza Baibulo, ndiponso nkhani zina zatsopano monga zokhudza kusamwa mankhwala ena aliwonse kupatulapo kugwilitsa nchito zinthu zacilengedwe ngati wina wadwala. Anali kulembanso nkhani zokhudza cilankhulo catsopano ca Esperanto cimene cinali citayamba kumene. Patapita nthawi yocepa, magazini atsopanowa anayamba kupangitsa abale kukaikila ziphunzitso zomveka bwino za coonadi. Zitafika pamenepa, M’bale Russell anadela nkhawa umoyo wakuuzimu wa M’bale Harteva ndi abale enawo, ndipo anawacondelela kuti abwelele m’coonadi.”

Kodi M’bale Harteva anacita bwanji atalandila uphungu umenewo? Iye anafalitsa kalata ya M’bale Russell m’magazini a Ararat limodzi ndi kalata imene iye anayankha M’bale Russell. M’bale Harteva anapepesa pa zimene anacita, ndipo anati: “Ndidzayesetsa kucita zimene ndingathe kuti ngati n’zotheka, ndikonze zimene ndinalakwitsa.” Patangopita nthawi yocepa, m’magazini imene anamalizila kulemba, M’bale Harteva anapepesanso cifukwa ca msokonezo umene iye anabweletsa, ndipo anaonjezela kunena kuti: “Ndidzayesetsa kucita zinthu mosamala kwambili pankhani zokhudza coonadi.” Mosiyana ndi akulu ena odzitukumula a panthawiyo, M’bale Kaarlo Harteva analandila uphungu modzicepetsa.

M’kupita kwa nthawi, M’bale Harteva anaikidwanso kukhala mlembi wa magazini a The Watch Tower a Cifinishi ndiponso monga woyang’anila nthambi. Iye anatumikila pa maudindo amenewa mpaka mu 1950. M’bale Harteva anamaliza moyo wake wa padziko lapansi mu 1957, ndipo anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova ndi kucita zinthu mogwilizana ndi coonadi. Ndithudi, anthu amene amalandila uphungu modzicepetsa kucokela kwa Mfumu yao, Yesu, amayengedwa, ndipo Yehova amawadalitsa.

12. (a) Kodi ndi masinthidwe otani amene anacitika m’bungwe lolamulila? (b) Fotokozani mmene Bungwe Lolamulila lalinganizidwila masiku ano. (Onani bokosi lakuti “Mmene Bungwe Lolamulila Limasamalila Zinthu za Ufumu,” patsamba 130.)

12 Kusintha koyamba kunakhudza bungwe lolamulila lomwelo. Caka ca 1971 cisanafike, madailekitala 7 a Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, amene anali abale odzozedwa, ndi amene anali m’bungwe lolamulila. Komabe, mu 1971, ciŵelengelo ca abale a m’bungwe lolamulila cinakwela kucoka pa mamembala 7 kufika pa mamembala 11. Kuyambila nthawiyo, panakhala kusiyana pakati pa gulu la madailekitala amenewo ndi bungwe lolamulila. Koma mamembalawo anali kuona kuti panalibe kusiyana kulikonse pakati pao, ndipo anayamba kusintha cheyamani caka ciliconse motsatila alifabeti.

13. (a) Kodi ndi makonzedwe otani amene anali kugwila nchito kwa zaka 40? (b) N’ciani cimene Bungwe Lolamulila linacita mu 1972?

13 Kusintha kwina kunakhudza mipingo yonse. Motani? Kuyambila mu 1932 mpaka mu 1972, mpingo unali kuyang’anilidwa ndi m’bale mmodzi. M’baleyo anali kuchedwa wotsogolela utumiki mpaka kudzafika mu 1936. Pambuyo pake dzinalo linasintha, ndipo anayamba kuchedwa mtumiki wa mpingo, kenako anayamba kuchedwa woyang’anila mpingo. Abalewa anali kusamalila nkhosa za Mulungu mwacangu. Woyang’anila mpingo, kaŵilikaŵili anali kupanga zosankha za mpingo popanda kufunsila maganizo a atumiki ena mumpingo. Komabe, mu 1972, Bungwe Lolamulila linasintha zinthu zina. Kodi kusintha kumeneko kunali kotani?

14. (a) Kodi ndi makonzedwe otani amene anayamba kugwila nchito pa October 1, 1972? (b) Kodi mgwilizanitsi wa bungwe la akulu amagwilitsila nchito bwanji uphungu wa pa Afilipi 2:3?

14 Abale ena amene anali kukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba, anayamba kuikidwa kukhala akulu m’mipingo, m’malo mokhala ndi m’bale mmodzi woyang’anila mpingo. Abalewo anayamba kutumikila pamodzi monga bungwe la akulu limene linali kuyang’anila mpingo. Makonzedwe atsopano amenewa anayamba kugwila nchito pa October 1, 1972. Masiku ano, mgwilizanitsi wa bungwe la akulu samadziona ngati wofunika kwambili kuposa akulu ena, koma amadziona “ngati wamng’ono.” (Luka 9:48) Ndi dalitso lalikulu kwambili kukhala ndi abale odzicepetsa amenewo.—Afil. 2:3.

N’zosacita kufunsa kuti Mfumu yathu inacita zinthu mwanzelu potipatsa abusa panthawi yake

15. (a) Kodi makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu akhala opindulitsa bwanji? (b) N’ciani cikusonyeza kuti Mfumu yathu inacita zinthu mwanzelu?

15 Makonzedwe akuti akulu azigwila nchito pamodzi monga bungwe la akulu akhala othandiza kwambili. Taonani mapindu atatu amene akhalapo cifukwa ca makonzedwewa. Coyamba ndiponso cacikulu, makonzedwewa amathandiza akulu onse kukumbukila kuti Yesu ndiye Mutu wa mpingo mosasamala kanthu za maudindo amene akuluwo ali nao pampingo. (Aef. 5:23) Caciŵili, lemba la Miyambo 15:22 limati: “Aphungu akaculuka zimakwanilitsidwa.” Conco, akulu amakumana ndi kukambilana nkhani zokhudza mpingo, ndipo pokambilanapo, amamvetsela maganizo a akulu anzao. Zimenezi zimathandiza kuti io apange zosankha mogwilizana ndi mfundo za m’Baibulo. (Miy. 27:17) Yehova amadalitsa zosankha zaozo moti zimathandiza kuti mpingo upite patsogolo. Cacitatu, kukhala ndi abale ambili otumikila monga akulu, kwathandiza kuti pakhale abale okwanila oti aziyang’anila ndi kuweta nkhosa m’mipingo imene ikuculukilaculukila. (Yes. 60:3-5) Tangoganizilani mmene mipingo yaculukila kucokela pa 27,000 mu 1971 kufika pa mipingo yoposa 113,000 mu 2013. Apa n’zosacita kufunsa kuti Mfumu yathu inacita zinthu mwanzelu potipatsa abusa panthawi yake.—Mika 5:5.

MMENE ZINTHU ZINASINTHILA PANKHANI YA KUYANG’ANILA MPINGO

  • 1881—Kuti Ophunzila Baibulo amene anali kukhala dela limodzi adziŵike, M’bale Russell anauza anthu onse amene anali kusonkhana nthawi zonse kuti adziŵitse ofesi ya Watch Tower za kumene anali kucitila misonkhano yao.

  • 1895—Mipingo yonse inauzidwa kuti izisankha abale oyenelela pakati pao omwe angatumikile monga akulu.

  • 1919—Ofesi ya nthambi inayamba kuika wotsogolela utumiki mumpingo uliwonse. Amene anali kuikidwa pa udindowu anayenela kukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba. Udindo wake unaphatikizapo kulinganiza nchito yolalikila ndi kulimbikitsa abale kutengako mbali m’nchito yolalikila. Akulu ena m’mipingo sanagwilizane ndi makonzedwe okhala ndi wotsogolela utumiki.

  • 1932—Kusankha akulu mwa kucita kuvoteledwa ndi mpingo caka ciliconse kunathetsedwa. M’malo mwake mipingo inayamba kuvotela komiti ya utumiki. Abale otumikila m’komitiyi anayenela kukhala acangu pa nchito yolalikila ndiponso anafunika kukhala mogwilizana ndi tanthauzo la dzina lao latsopano lakuti Mboni za Yehova. M’bale mmodzi pakati pa abale amene anali kuvoteledwa ndi mpingo, anali kuikidwa ndi Sosaiti, kapena kuti ofesi ya nthambi kuti atumikile monga wotsogolela utumiki.

  • 1937—Abale a khamu lalikulu anayamba kutumikila m’makomiti a utumiki pamodzi ndi abale ao odzozedwa.

  • 1938—Mipingo inavomeleza cigamulo cakuti atumiki onse a mipingo aziikidwa pa udindo wao mwa kukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba. Kucita cisankho m’mipingo kunathelatu.

Kuti mudziŵe zambili zokhudza mmene zinthu zinasinthila pa kayendetsedwe ka gulu, onani buku lakuti Jehovah’s Witnesses—Proclaimers of God’s Kingdom, tsamba 204 mpaka 235.

Kusankha akulu mwa kucita kuvoteledwa ndi mpingo m’zaka za m’ma 1920

“Tinali kuvotela akulu mwakunyamula dzanja lamanja. Ndiyeno m’bale anali kuimilila ndi kuŵelenga mavoti.”—Mlongo Rose Swingle, wa ku mzinda wa Chicago ku Illinois, ku dziko la United States.

“Mukhale Zitsanzo kwa Gulu la Nkhosa”

16. (a) Kodi akulu ali ndi udindo wotani? (b) Kodi Ophunzila Baibulo anali kuwaona bwanji malangizo a Yesu akuti ‘weta nkhosa’?

16 Kale m’nthawi ya Ophunzila Baibulo, akulu anali kudziŵa kuti ali ndi udindo wothandiza okhulupilila anzao kupitilizabe kutumikila Mulungu. (Ŵelengani Agalatiya 6:10.) Mu 1908, nkhani inayake ya mu Nsanja ya Mlonda yacingelezi, inafotokoza malangizo a Yesu akuti: “Weta ana a nkhosa anga.” (Yoh. 21:15-17) Nkhaniyo inalangiza akulu kuti: “N’kofunika kuti tiziona nchito imene Ambuye anatipatsa yosamalila nkhosa kukhala yofunika kwambili pa umoyo wathu, ndi kuona kuti ndi mwai wamtengo wapatali kudyetsa ndi kuweta otsatila a Ambuye.” Magazini ina ya The Watch Tower ya mu 1925, inagogomezelanso kufunika kocita ubusa pamene inakumbutsa akulu kuti: “Chalichi ndi ca Mulungu, . . . ndipo onse amene amatumikila abale adzayenela kuyankha mlandu kwa iye.”

17. Kodi oyang’anila akhala akuthandizidwa bwanji kuti akhale abusa abwino?

17 Kodi gulu la Yehova lathandiza bwanji akulu kunola maluso ao monga abusa? Akuluwo akhala akupatsidwa maphunzilo. Mu 1959, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ya akulu inayamba. Nkhani inayake imene inaphunzilidwa panthawi ya sukuluyo inali ndi mutu wakuti, “Kuthandiza Munthu Aliyense Payekha.” Akulu analimbikitsidwa “kupanga ndandanda yoyendela abale ndi alongo kunyumba zao.” Nkhaniyo inasonyeza njila zosiyanasiyana za mmene abusa angapangile maulendo ao kukhala olimbikitsa. Mu 1966, Sukulu ya Utumiki wa Ufumu yatsopano inayamba. Sukuluyo inali ndi nkhani yakuti “Kufunika kwa Nchito ya Ubusa.” Kodi mfundo yaikulu ya nkhaniyo inali yotani? Nkhaniyo inafotokoza kuti abale amene akutsogolela “ayenela kutengako mbali pa nchito yosamalila nkhosa za Mulungu, koma sayenela kunyalanyaza mabanja ao ndiponso ulaliki wakumunda.” M’zaka za posachedwapa, pakhalanso masukulu ena a akulu. Kodi pakhala mapindu otani cifukwa ca maphuzilo amene gulu la Yehova lakhala likupeleka? Masiku ano, mumpingo wacikritsu muli abale ambilimbili oyenelela amene akutumikila monga abusa akuuzimu.

Kalasi ya Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Philippines, mu 1966

Sukulu ya Utumiki wa Ufumu ku Philippines, mu 1966

18. (a) Ndi udindo waukulu uti umene akulu apatsidwa? (b) N’cifukwa ciani Yehova ndi Yesu amakonda kwambili akulu amene amagwila nchito mwakhama?

18 Yehova kupyolela mwa Mfumu yathu, Yesu, ndi amene anapanga makonzedwe akuti pampingo pazikhala akulu kuti azigwila nchito yofunika. Nchito yotani? Nchito yotsogolela nkhosa za Mulungu m’nthawi yovuta kwambili ino. (Aef. 4:11, 12; 2 Tim. 3:1) Yehova ndi Yesu amakonda kwambili akulu amene amagwila nchito yao mwakhama cifukwa cakuti abalewo amamvela lamulo la m’Malemba lakuti: “Wetani gulu la nkhosa za Mulungu lomwe analisiya m’manja mwanu . . . mofunitsitsa . . . , ndi mtima wonse . . . , mukhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.” (1 Pet. 5:2, 3) Tiyeni tsopano tikambilane njila ziŵili zokha za mmene abusa acikristu alili zitsanzo kwa gulu la nkhosa ndi mmene amathandizila kuti mumpingo mukhale mtendele ndi cimwemwe.

“TINACITA CIDWI KWAMBILI”

BANJA lina la amishonale ku Asia linatumizidwa kukatumikila kumpingo umene unali wosoŵa kwa zaka zambili. Amishonalewo atafika pampingowo anaona kuti anthu a mumpingowo anali ndi cikondi, koma sanali kutsatila malangizo a gulu. Pambuyo pakuti amishonalewo akhala paubwenzi ndi ofalitsa a mpingowo, mwamuna wa banjalo anayamba kuthandiza mpingo uja pang’onopang’ono kuti uzicita zinthu mofanana ndi mmene anthu a Yehova amacitila padziko lonse lapansi. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Pambuyo pa zaka ziŵili cabe, ciŵelengelo ca anthu ofika ku misonkhano cinakwela kuwilikiza kaŵili, ofalitsa atsopano anayamba kuloŵa mu ulaliki, ndipo anthu oposa 20 anabatizidwa. Banjalo linati: “Tinacita cidwi kwambili ndi mmene Yehova anatidalitsila. Cifukwa cogwilitsila nchito malangizo a gulu la Mulungu, aliyense mumpingo wakhala wosangalala.”

Mmene Akulu Amawetela Nkhosa za Mulungu Masiku Ano

19. Kodi timamva bwanji akulu akamapita nafe mu ulaliki?

19 Coyamba, akulu amalalikila ndi anthu osiyanasiyana mumpingo. Ponena za Yesu, wolemba Uthenga Wabwino Luka anati: “Yesu anayamba ulendo woyenda mumzinda ndi mzinda komanso mudzi ndi mudzi. Ulendowu unali wokalalikila ndi kulengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu. Ndipo atumwi 12 aja anali naye limodzi.” (Luka 8:1) Monga mmene Yesu anali kulalikila limodzi ndi atumwi ake, akulu acitsanzo cabwino naonso amagwila nchito yolalikila limodzi ndi Akristu anzao. Akuluwo amadziŵa kuti kucita zimenezi kumathandiza kuti mpingo ulimbe. Nanga anthu ena mumpingo amawaona bwanji akulu acitsanzo cabwino amenewo? Mlongo wina dzina lake Jeannine, amene ali ndi zaka za m’ma 80, anati: “Kugwila nchito yolalikila limodzi ndi mkulu kumandipatsa mpata woceza naye ndi kum’dziŵa bwino kwambili.” M’bale wina dzina lake Steven, wa zaka za m’ma 30, anati: “Mkulu akagwila nane nchito yolalikila khomo ndi khomo, ndimaona kuti akufuna kundithandiza. Ndikalandila thandizo lake, ndimasangalala kwambili.”

M’busa apeza nkhosa yosocela usiku, ndipo kuli cimphepo

Monga mmene m’busa amapitila kukafunafuna nkhosa yotayika, naonso akulu amacita khama kuti apeze anthu amene anasiya kuyanjana ndi mpingo

20, 21. Ndi citsanzo cotani cimene akulu angatengele kwa m’busa wa m’fanizo la Yesu? Pelekani citsanzo. (Onani bokosi lakuti “Maulendo Aubusa Aphindu.”)

20 Caciŵili, gulu la Yehova laphunzitsa akulu kuti azithandiza anthu amene anasiya kuyanjana ndi mpingo. (Aheb. 12:12) N’cifukwa ciani akulu ayenela kuthandiza anthu ofooka mwakuuzimu, ndipo ayenela kuwathandiza bwanji? Timapeza yankho la funsoli m’fanizo la Yesu la m’busa ndi nkhosa yotaika. (Ŵelengani Luka 15:4-7.) Pamene m’busa wa m’fanizoli anazindikila kuti nkhosa ina palibe, iye anayamba kuifunafuna monga kuti ndi nkhosa yokhayo imene anali nayo. Kodi akulu acikristu masiku ano angatengele bwanji citsanzo ca m’busa ameneyo? Monga mmene nkhosa yotaika imakhalilabe yofunika kwa m’busa, akulu naonso amaona kuti anthu amene anasiya kuyanjana ndi gulu la Mulungu ndi ofunikabe. Iwo amaona kuti anthu otelo ndi nkhosa zotaika, ndipo ndi ofunikadi kuwathandiza. Ndiponso, monga mmene m’busa amapitila “kukafunafuna [nkhosa] imodzi yotayikayo kufikila ataipeza,” naonso akulu amacita zonse zimene angathe kuti apeze anthu ofooka ndi kuwathandiza.

21 Kodi m’busa wa m’fanizo la Yesu anacita ciani atapeza nkhosa yotaikayo? Iye anainyamula mwacikondi ndi kuiika “paphewa pake,” ndipo anapita nayo kumene kunali nkhosa zina zija. Mofananamo, cikondi cimene mkulu angasonyeze munthu wofooka, cingamulimbikitse kubwelela mumpingo. M’bale wina mu Africa muno dzina lake Victor, anathandizidwapo ndi akulu pamene anasiya kuyanjana ndi mpingo. Iye anati: “Kwa zaka zonse 8 zimene ndinakhala wozilala, akulu sanaleke kundithandiza.” Kodi n’ciani cinam’khudza mtima kwambili mbaleyu? Iye anati: “Tsiku lina, mkulu wina amene ndinaloŵa naye pamodzi Sukulu ya Apainiya, dzina lake John, anandicezela. Iye anandionetsa zithunzi zimene anajambula panthawi imene tinali ku sukulu ya apainiya. Zithunzizo zinandikumbutsa zinthu zambili zabwino cakuti ndinayamba kulakalaka nditakhalanso ndi cimwemwe cimene ndinali naco pamene ndinali kutumikila Yehova.” Victor anayambanso kuyanjana ndi mpingo patangopita nthawi yocepa pambuyo pocezeledwa ndi John. Masiku ano, Victor akutumikilanso monga mpainiya. Ndithudi, akulu amene amadela nkhawa anthu ena amatipangitsa kukhala osangalala.—2 Akor. 1:24.b

Abale aŵili acezela m’bale wacikulile wozilala

MAULENDO AUBUSA APHINDU

POFUNA kuthandiza nkhosa zotaika, akulu a mpingo wina ku United States anayamba kuganizila zimene akanacita kuti athandize anthu amene anasiya kuyanjana ndi mpingo. Iwo anazindikila kuti anthu 30 amene anasiya kutumikila Yehova zaka zambili zapitazo, anali kukhalabe m’gawo la mpingo wao. Ambili a io anali okalamba.

Mkulu wina dzina lake Alfredo anatenga maina a anthu ozilala, ndipo anayamba kuwacezela. M’baleyo anakamba kuti: “M’mawa patsiku Lacisanu lililonse, ndimafika pakhomo la munthu wozilala.” M’bale Alfredo akapeza munthu wozilalayo panyumba pake, amayesa kuceza naye momasuka, ndipo amauza munthu wozilalayo nkhawa imene ali nayo yokhudza iye. Iye amauzanso m’bale kapena mlongo wozilalayo kuti mpingo sunaiwale nchito yabwino imene munthuyo anacita kaamba ka Ufumu wa Yehova. M’bale Alfredo anati: “Tsiku lina nditauza m’bale wacikulile wozilala za kuculuka kwa maola amene iye analalikila, ndiponso magazini amene anagaŵila mwezi womaliza umene iye analoŵa muutumiki mu 1976, misozi inalengeza m’maso mwake.” M’bale Alfredo amaŵelenganso lemba la Luka 15:4-7, 10 kwa anthu ozilala amene iye amacezela, ndiyeno amawafunsa kuti: “N’ciani cimacitika ngati nkhosa yotaika yabwelela mumpingo? Yehova, Yesu, ndi angelo amasangalala, tangoganizilani zimenezo!”

Kwa zaka ziŵili zapitazi, m’bale Alfredo wakhala akucezela anthu ozilala. N’ciani cakhala cotulukapo ca kuleza mtima kwake ndi khama lake? Iye wathandiza abale aŵili kuyamba kuyanjananso ndi mpingo. Abalewo tsopano amapezeka pa misonkhano ya pa Sondo mokhazikika. Akumwetulila, m’bale Alfredo anati: “Pamene abalewa analoŵa pa khomo la Nyumba ya Ufumu, inenso ndinagwetsa misozi.” Ndipo anaonjezela kuti: “Ngakhale kuti abale ozilalawa anayamba kupezeka pa misonkhano, ndimapitabe kukawacezela pa Lacisanu lililonse cifukwa cakuti abalewa amandiuza kuti amasangalala ndi maceza amene timakhala nao mlungu uliwonse. Inenso ndimasangalala kuwacezela.”

Uyang’anilo Wabwino Umalimbikitsa Mgwilizano wa Anthu a Mulungu

22. Kodi cilungamo ndi mtendele zimalimbikitsa bwanji mgwilizano mumpingo wacikristu? (Muonenso bokosi lakuti “Tinacita Cidwi Kwambili.”)

22 Monga mmene taonela poyamba, Yehova ananenelatu kuti cilungamo ndi mtendele zidzaculuka pakati pa anthu a Mulungu. (Yes. 60:17) Makhalidwe aŵili amenewa amapangitsa kuti mpingo ukhale wogwilizana. Motani? Pa nkhani yokhudza cilungamo, “Yehova Mulungu wathu ndi Yehova mmodzi.” (Deut. 6:4) Mipingo yonse padziko lapansi imatsatila mfundo za Mulungu za cilungamo zofanana. Mfundo zake pa cabwino ndi coipa n’zofanana, ndipo sizimasiyana “m’mipingo yonse ya oyelawo.” (1 Akor. 14:33) Motelo, tikamatsatila mfundo za Mulungu, mipingo imapita patsogolo. Ndipo ponena za mtendele, Mfumu yathu imafuna kuti tizisangalala ndi mtendele mumpingo, komanso kuti tikhale “anthu amene amabweletsa mtendele.” (Mat. 5:9) Conco, timatsatila “zinthu zobweletsa mtendele.” Izi zikutanthauza kuti timayamba ndife kuthetsa kusiyana maganizo kumene kungakhalepo pakati pathu nthawi zina. (Aroma 14:19) Mwakutelo, timathandiza kuti mumpingo mukhale mtendele ndi mgwilizano.—Yes. 60:18.

23. N’ciani cimene tikusangalala naco masiku ano monga atumiki a Yehova?

23 Mu November 1895, pamene magazini ya Watch Tower inalengeza kuti pampingo pazikhala akulu, abale audindo naonso anasonyeza mtima wofuna kucilikiza makonzedwe amenewo. Kodi anasonyeza bwanji zimenezo? Iwo anapemphela kuti makonzedwe atsopanowo athandize anthu a Mulungu kuti “agwilizane mofulumila pa cikhulupililo.” Tikakumbukila mmene zinthu zinali kuyendela m’nthawi za kumbuyo, timayamikila mmene Yehova kupyolela mwa Mfumu yathu wakhala akusinthila zinthu. Kusintha kumeneko kwapangitsa kuti tikhale ogwilizana pa kulambila kwathu. (Sal. 99:4) Masiku ano, anthu onse a Yehova padziko lapansi, amasangalala pamene akuyenda “mumzimu umodzi,” kutsatila “m’mapazi amodzimodzi,” ndi kutumikila “Mulungu wamtendele” “mogwilizana.”—2 Akor. 12:18; ŵelengani Zefaniya 3:9.

a Zimene anapeza atacita kafukufuku ameneyo zinafalitsidwa m’buku la Aid to Bible Understanding.

b Onani nkhani yakuti “Akulu Achikhristu ndi Antchito Anzathu Otipatsa Chimwemwe,” imene ili mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2013, tsamba 27-31.

Kodi Mumaona Kuti Ufumu wa Mulungu ndi Weniweni?

  • Ndi masinthidwe otani amene Ufumu wacititsa m’gulu?

  • Kodi kusintha kwa uyang’anilo mumpingo kwakuthandizani bwanji kutumikila “Mulungu wamtendele”?

  • N’ciani cimene mkulu anakuuzani kapena kukucitilani cimene caonjezela cimwemwe canu?

  • N’ciani cimene inuyo mungacite kuti mumpingo mukhale mtendele ndi mgwilizano?

Msonkhano wa Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova

Kuyambila kumanzele kupita kulamanja: M’bale Gerrit Lösch, M’bale Geoffrey Jackson, M’bale Samuel Herd, M’bale Guy Pierce, M’bale Mark Sanderson, M’bale David Splane, M’bale Anthony Morris III, M’bale Stephen Lett

MMENE BUNGWE LOLAMULILA LIMASAMALILA ZINTHU ZA UFUMU

BUNGWE Lolamulila la Mboni za Yehova ndi lopangidwa ndi abale amene ndi atumiki odzozedwa a Yehova Mulungu. Monga gulu, io amapanga “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Iwo ali ndi udindo wopeleka cakudya cakuuzimu ndi kupeleka malangizo oyendetsela nchito yolalikila Ufumu kuti nchitoyo izigwilika bwinobwino padziko lonse.—Mat. 24:14, 45-47.

Bungwe Lolamulila limakhala ndi msonkhano mlungu uliwonse, makamaka pa Lacitatu. Zimenezi zimathandiza abalewa kuti azigwila nchito mogwilizana. (Sal. 133:1) Abale a m’Bungwe Lolamulila amatumikilanso m’makomiti osiyanasiyana. Posamalila zinthu za Ufumu, komiti iliyonse ili ndi nchito imene imayang’anila, ndipo zimenezi zafotokozedwa mwacidule m’munsimu.

  • Abale akugwilizana zocita pankhani yosamalila abale pa dziko lonse pansi

    Komiti ya Ogwilizanitsa

    Abale amene amagwila nchito mu komiti imeneyi amayang’anila nkhani zokhudza malamulo ndi kugwilitsila nchito mabungwe ofalitsa nkhani ngati pakufunika kutelo kuti anthu amvetsetse bwino zikhulupililo zathu. Amathandizanso pakacitika tsoka, Akristu m’dela lina akayamba kuzunzidwa, kapena pakacitika zinthu zina zadzidzidzi zimene zikukhudza Mboni za Yehova kulikonse padziko lapansi.

  • A m’banja la beteli akugwila nchito zosiyanasiyana

    Komiti Yoona za Atumiki a pa Beteli

    Komiti imeneyi ili ndi udindo wosamalila za moyo wakuuzimu ndi wakuthupi wa atumiki a pa Beteli pa dziko lonse lapansi. Imayang’anilanso nchito yoitana anthu atsopano kuti akatumikile pa Beteli, ndipo imayankhanso mafunso okhudza utumiki wao.

  • M’bale wa m’banja la beteli akugwila nchito yosindikiza ndi kutumiza mabuku ofotokoza za m’Baibulo

    Komiti Yoona za Nchito Yofalitsa Mabuku

    Abale a m’komitiyi amayang’anila nchito yosindikiza, kufalitsa ndi kutumiza mabuku ofotokoza za m’Baibulo. Iwo amayang’anilanso nyumba zosindikizila mabuku ndi zinthu zina zimene zimagwilitsidwa nchito ndi mabungwe a Mboni za Yehova. Amayang’anilanso nchito ya zomangamanga padziko lonse kuphatikizapo nchito yomanga Nyumba za Ufumu. Abalewa amaonetsetsa kuti zopeleka zothandiza pa nchito ya Ufumu zikugwilitsilidwa nchito bwino.

  • M’bale akukonzekela ndipo pa desiki lake pali mabuku osiyanasiyana

    Komiti ya Utumiki

    Abale a m’komitiyi amayang’anila mbali zonse zokhudza nchito yolalikila ndi zinthu zina zokhudza mipingo, ofalitsa, apainiya, akulu, ndi oyang’anila oyendela ndiponso amishonale. Amayang’anilanso zinthu zina zambili monga nchito zokhudza Makomiti Olankhulana ndi Acipatala.

  • M’bale akamba nkhani pa pulatifomu

    Komiti Yoona za Ntchito Yophunzitsa

    Komiti imeneyi imayang’anila nchito yokonza nkhani za pa misonkhano ikuluikulu ndi misonkhano ya mpingo. Imayang’anilanso Sukulu ya Gileadi, Sukulu ya Alengezi a Ufumu, Sukulu ya Apainiya, ndi masukulu ena. Kuonjezela pamenepo, komiti imeneyi imayang’anilanso nchito yokonza nkhani za m’kabuku ka Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhiristu komanso nchito yokonza ma CD ndi mavidiyo.

  • Zofalitsa zosiyanasiyana kuphatikizapo webusaiti ya jw.org

    Komiti Yoona za Nchito Yolemba Mabuku

    Abale amene amagwila nchito mu komiti imeneyi amayang’anila nchito yokonza cakudya cakuuzimu kupyolela m’mabuku, ndi pa makompyuta. Cakudyaci cimapelekedwa kwa Mboni za Yehova ndiponso anthu ena onse. Komiti imeneyi imayang’anilanso nkhani zimene zimaikidwa pa Webu saiti yathu ndiponso nchito yomasulila imene ikucitika padziko lonse lapansi. Komiti imeneyi imayankhanso mafunso a m’Baibulo ndi mafunso ena okhudza mfundo zina zolembedwa m’mabuku athu.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani