LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 11/1 masa. 27-31
  • Abusa, Tsanzilani Abusa Aakulu

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Abusa, Tsanzilani Abusa Aakulu
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “ADZAWANYAMULILA PACIFUWA PAKE”
  • “NDAKUPATSANI CITSANZO”
  • ‘GWILANI MWAMPHAMVU MAU OKHULUPILIKA’
  • ‘ZITSANZO KU GULU’
  • “THANDIZANI OFOOKA”
  • Muzimvela Abusa A Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 11/1 masa. 27-31

Abusa, Tsanzilani Abusa Aakulu

“Kristu anavutika cifukwa ca inu, ndipo anakusiilani citsanzo kuti mutsatile mapazi ake mosamala kwambili.”—1 PET. 2:21.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Monga abusa, kodi akulu angatsanzile bwanji Yehova?

Kodi akulu angatengele bwanji citsanzo ca Yesu Kristu?

N’cifukwa ciani akulu amacita maulendo aubusa?

1, 2. (a) Kodi cimacitika n’ciani ngati nkhosa zimasamalidwa bwino? (b) N’cifukwa ciani anthu ambili m’nthawi ya Yesu anali ngati nkhosa zopanda m’busa?

NKHOSA zimakula bwino ngati m’busa amazisamalila bwino. Buku lina la malangizo a kasamalidwe ka nkhosa linati: “Ngati munthu amatengela nkhosa zake ku ubusa popanda kuzisamalila mokwanila kapena kuzisonyeza cidwi, nkhosazo zimayamba kudwala-dwala ndipo m’kupita kwa nthawi zimasoŵa malonda cifukwa cakuti zimakhala zosaoneka bwino. Koma ngati nkhosa zimasamalidwa mokwanila, izo zimakula bwino.

2 Mmene abusa amasamalila nkhosa za Mulungu iliyonse payokha-payokha, zimakhudza mpingo wonse. Mungakumbukile kuti Yesu anamvela cisoni cikhamu ca anthu cifukwa cakuti io “anali onyuka-nyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) N’cifukwa ciani anthuwo anali mumkhalidwe wotelo? Cifukwa cakuti anthu amene anali ndi udindo wophunzitsa anthu Malamulo a Mulungu anali ankhanza, opondeleza ndi acinyengo. M’malo mothandiza nkhosa zao ndi kuzisamalila, atsogoleli a cipembedzo aciyuda anali kusenzetsa nkhosazo “akatundu olemela” pamapewa.—Mat. 23:4.

3. N’ciani cimene akulu mumpingo ayenela kukumbukila pamene akusamalila udindo wao monga abusa akuuzimu?

3 Abusa acikristu a masiku ano amene ndi akulu oikidwa, ali ndi udindo waukulu. Nkhosa zimene io amasamalila ndi za Yehova ndi Yesu amene anadzidziŵikitsa kuti ndi “m’busa wabwino.” (Yoh. 10:11) Nkhosa zimenezo ‘zinagulidwa pa mtengo wokwela’ umene Yesu analipila ndi ‘magazi ake amtengo wapatali.’ (1 Akor. 6:20; 1 Pet. 1:18, 19) Iye amakonda kwambili nkhosa zimenezi ndipo anapeleka moyo wake mofunitsitsa kaamba ka izo. Nthawi zonse akulu ayenela kukumbukila kuti io ndi abusa aang’ono amene amafunikila kugonjela utsogoleli wa Mwana wokondedwa wa Mulungu, Yesu Kristu, amene ndi “m’busa wamkulu wa nkhosa.”—Aheb. 13:20.

4. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

4 Kodi abusa acikristu ayenela kusamalila bwanji nkhosa? Anthu onse mumpingo amalimbikitsidwa kuti ayenela ‘kumvela amene akutsogolela’ pakati pao. Koma akulu acikristu amalangizidwa kuti ayenela kupewa ‘kucita ufumu pa anthu amene ali colowa cocokela kwa Mulungu.’ (Aheb. 13:17;ŵelengani 1 Petulo 5:2, 3) Koma kodi akulu angatsogolele bwanji popanda kucita ufumu pa nkhosa? M’mau ena tifunse kuti, Kodi akulu ayenela kucita ciani kuti asamalile nkhosa popanda kugwilitsila nchito molakwika udindo umene Mulungu anawapatsa?

“ADZAWANYAMULILA PACIFUWA PAKE”

5. Kodi tikuphunzila ciani pa lemba la Yesaya 40:11?

5 Ponena za Yehova, mneneli Yesaya anati: “Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa. Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulila pacifuwa pake. Nkhosa zoyamwitsa adzayenda nazo mosamala.” (Yes. 40:11) Mau amenewa akusonyeza mmene Yehova amasamalila anthu ofooka ndiponso amene amafunikila citetezo mumpingo. Monga mmene m’busa wabwino amadziŵila bwino zosoŵa za nkhosa zonse zimene amasamalila ndipo amakhala okonzeka kuzithandiza, Yehova nayenso amadziŵa bwino zosoŵa za anthu onse mumpingo ndipo amawathandiza. M’busa amanyamula mwana wa nkhosa wobadwa kumene pa covala cake pakakhala pofunika kutelo. Nayenso Yehova amene ndi “Tate wacifundo cacikulu,” adzatithandiza pamavuto. Iye adzatitonthoza pamene takumana ndi ciyeso coopsa kapena pamene tikufunikila thandizo lina lapadela.—2 Akor. 1:3, 4.

6. Monga m’busa, kodi mkulu angatsatile bwanji citsanzo ca Yehova?

6 Limeneli ndi phunzilo labwino kwambili limene abusa mumpingo angaphunzile kwa Atate wathu wakumwamba. Monga mmene Yehova amacitila, abusa aang’ono amafunika kuganizila zosoŵa za nkhosa. Mkulu akadziŵa mavuto amene nkhosa zikukumana nao komanso zosoŵa zofunika cisamalilo ca mwamsanga, iye angapeleke cilimbikitso ndi thandizo loyenelela. (Miy. 27:23) Mkulu afunika kulankhulana momasuka ndi okhulupilila anzake. Ngakhale kuti mkulu saloŵelela m’nkhani za ena, iye amacita cidwi ndi zimene amaona ndi kumva mumpingo ndipo amakhala wokonzeka ‘kuthandiza ofooka.’—Mac. 20:35; 1 Ates. 4:11.

7. (a) Kodi abusa a m’nthawi ya Ezekieli ndi Yeremiya anali kusamalila nkhosa za Mulungu? Fotokozani. (b) Kodi akulu akuphunzilapo ciani pa mau amene Yehova ananena podzudzula abusa osakhulupilika?

7 Ganizilani abusa amene Mulungu anadzudzula m’nthawi ya Ezekieli ndi Yeremiya. Yehova anakana abusa amenewo cifukwa cakuti io sanali kusamalila nkhosa zake. Yehova anati: “Nkhosa zanga . . . zinakhala cakudya ca zilombo zonse zakuchile. Nkhosa zanga zinalibe m’busa, ndipo abusa anga sanazifune-fune koma anali kumangodzidyetsa okha, osadyetsa nkhosa zanga.” Anthu anavutika cifukwa cakuti atsogoleli ao anali odzikonda ndi adyela. (Ezek. 34:7-10; Yer. 23:1) Mau odzudzula amene Mulungu anauza abusa amenewo ndi oyenelela atsogoleli a Machalichi Acikristu masiku ano. Koma mau amenewo amagogomezanso mfundo yakuti akulu acikristu ayenela kusamalila mwacikondi nkhosa za Yehova.

“NDAKUPATSANI CITSANZO”

8. Kodi Yesu anapeleka citsanzo cabwino citi pa nkhani yothandiza ena?

8 Cifukwa ca kupanda ungwilo, nkhosa zina za Mulungu zimacedwa kumvetsetsa zimene Yehova amafuna. Nthawi zina nkhosazo zimalephela kutsatila malangizo a m’Malemba, ndiponso zimacita zinthu moonetsa kuti si Akristu okhwima mwa kuuzimu. Kodi akulu ayenela kucita bwanji zinthu zikakhala conco? Iwo ayenela kutsanzila Yesu amene anali woleza mtima ndi ophunzila ake. Mwacitsanzo, pamene ophunzilawo anali kukangana kwambili pa nkhani yakuti ndani adzakhala wamkulu mu Ufumu wa Mulungu, Yesu sanali kuwakalipila. M’malo mowapsela mtima, Yesu anapitiliza kuwaphunzitsa ndi kuwalangiza mwacikondi kuti ayenela kukhala odzicepetsa. (Luka 9:46-48; 22:24-27) Mwa kusambitsa mapazi ao, Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca kudzicepetsa ndipo limeneli ndi khalidwe limene oyang’anila acikristu ayenela kukhala nalo.—Ŵelengani Yohane 13:12-15; 1 Pet. 2:21.

9. Kodi Yesu analimbikitsa ophunzila ake kukhala ndi maganizo otani?

9 Mtumwi Yakobo ndi mtumwi Yohane anali ndi maganizo akuti m’busa amafunikila kulamulila ena. Iwo anapempha Yesu kuti adzawapatse udindo wapamwamba mu Ufumu wa Mulungu. Koma Yesu anawapatsa malangizo akuti: “Inu mukudziŵa kuti olamulila a anthu a mitundu ina amapondeleza anthu ao ndipo akulu-akulu amasonyeza mphamvu zao pa io. Sizili conco pakati panu, koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenela kukhala mtumiki wanu.” (Mat. 20:25, 26) Atumwiwo anafunika kupewa cizolowezi cofuna ‘kupondeleza’ anzao.

10. Kodi Yesu amafuna kuti akulu azisamalila bwanji nkhosa? Nanga Paulo anapeleka citsanzo cotani pa nkhani imeneyi?

10 Yesu amafuna kuti akulu acikristu azisamalila nkhosa monga mmene iye anali kucitila. Iwo afunika kukhala ololela kutumikila ena osati kucita ufumu pa nkhosa. Mtumwi Paulo anali wodzicepetsa. Ndiye cifukwa cake anauza akulu a mumpingo wa ku Efeso kuti: “Inu mukudziŵa bwino mmene ndinali kukhalila nanu nthawi zonse kucokela tsiku loyamba limene ndinaponda m’cigawo ca Asia. Ndinali kutumikila Ambuye monga kapolo, modzicepetsa kwambili.” Mtumwi ameneyu anafuna kuti akuluwo azithandiza ena mwakhama ndi modzicepetsa. Iye anati: “M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwila nchito molimbika comweci, muthandize ofookawo.” (Mac. 20:18, 19, 35) Paulo anauza Akristu a ku Korinto kuti iye sanali wolamulila cikhulupililo cao. Koma anali wanchito mnzao wodzicepetsa kuti io akhale ndi cimwemwe. (2 Akor. 1:24) Paulo anapeleka citsanzo cabwino ca kudzicepetsa ndi kugwila nchito mwakhama kwa akulu masiku ano.

‘GWILANI MWAMPHAMVU MAU OKHULUPILIKA’

11, 12. Kodi mkulu angathandize bwanji Mkristu kuti apange cosankha cabwino?

11 Mkulu wa mumpingo amafunikila ‘kugwila mwamphamvu mau okhulupilika pamene akuphunzitsa mwaluso.” (Tito 1:9) Koma iye amacita zimenezo “ndi mzimu wofatsa.” (Agal. 6:1) M’malo mokakamiza ena mumpingo kuti azicita zinthu mmene iye afunila, m’busa wacikristu wabwino amayesetsa kulangiza ena mowafika pamtima. Mkulu angafotokoze mfundo za m’Malemba zimene Mkristu afunikila kulingalila asanapange cosankha cacikulu, ndi kukambilana naye mfundo zina zokhudza nkhaniyo zopezeka m’mabuku athu. Iye angalimbikitse Mkristuyo kuganizila mmene zosankha zake zingakhudzile ubwenzi wake ndi Yehova. Mkuluyo angagogomeze mfundo yakuti Mkristuyo afunika kupempha citsogozo ca Mulungu asanapange cosankha. (Miy. 3:5, 6) Pambuyo pokambilana zimenezi ndi Mkristuyo, mkulu ayenela kumulola kupanga yekha cosankha.—Aroma 14:1-4.

12 Uphungu umene akulu acikristu amapeleka nthawi zonse umafunika kuzikidwa pa Malemba. Conco, n’zofunika kwambili kuti io azigwilitsila nchito Baibo mwaluso ndi kutsatila zimene imanena. Kucita zimenezi kudzathandiza akulu kuti asamagwilitsile nchito mphamvu zao molakwika. Akulu sayenela kuiwala kuti io ndi abusa aang’ono, ndi kuti munthu aliyense mumpingo adzayankha yekha mlandu kwa Yehova ndi Yesu pa zosankha zimene amapanga.—Agal. 6:5, 7, 8.

‘ZITSANZO KU GULU’

13, 14. Kodi mkulu afunika kupeleka citsanzo cabwino kwa nkhosa m’njila ziti?

13 Pambuyo pakuti mtumwi Petulo wacenjeza akulu mumpingo kuti ‘asamacite ufumu pa anthu amene ali coloŵa cocokela kwa Mulungu,’ iye anawalangiza kuti ‘akhale zitsanzo ku gulu la nkhosa.’ (1 Pet. 5:3) Kodi mkulu angakhale bwanji citsanzo ku gulu la nkhosa? Ganizilani ziyeneletso ziŵili zimene m’bale afunika kukwanilitsa ngati “akuyesetsa kuti akhale woyang’anila.” Iye afunika kukhala “woganiza bwino” ndi “woyang’anila bwino banja lake.” Ngati mkulu ali ndi banja afunika kuliyang’anila bwino cifukwa cakuti “ngati munthu sadziŵa kuyang’anila banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalile bwanji?” (1 Tim. 3:1, 2, 4, 5) Kuti m’bale ayenelele kukhala woyang’anila afunika kukhala woganiza bwino. Izi zikutanthauza kuti iye ayenela kumvetsetsa mfundo za m’Baibo ndi kudziŵa mmene angazigwilitsile nchito pa umoyo wake. Iye ayenela kukhala wodekha. Abale ndi alongo mumpingo amadalila akulu amene ali ndi makhalidwe amenewa.

14 Njila ina imene oyang’anila amapelekela citsanzo cabwino kwa Akristu anzao ndi mwa kutsogolela pa nchito yolalikila. Pa nkhani imeneyi, Yesu anapeleka citsanzo cabwino kwa oyang’anila. Pamene iye anali padziko lapansi, nchito yake yaikulu inali yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. Iye anaphunzitsa ophunzila ake mmene angagwilile nchito imeneyi. (Maliko 1:38; Luka 8:1) Masiku ano, abale ndi alongo amalimbikitsidwa akamalalikila limodzi ndi akulu ndi kuona cangu cao pa nchito yopulumutsa moyo imeneyi. Ndipo amaphunzila maluso a ulaliki kwa akulu. Ngati oyang’anila amayesetsa kuthela nthawi ndi mphamvu yao pa nchito yolalikila uthenga wabwino ngakhale kuti amakhala ndi zocita zambili, abale ndi alongo amatengela citsanzo cao. Komanso akulu amapeleka citsanzo cabwino kwa abale ndi alongo mwa kukonzekela misonkhano ndi kutengamo mbali, ndiponso kugwila nchito zina monga kuyeletsa ndi kusamalila Nyumba ya Ufumu.—Aef. 5:15, 16; welengani Aheberi 13:7.

“THANDIZANI OFOOKA”

15. Kodi akulu amacita maulendo aubusa pa zifukwa zina ziti?

15 Nkhosa ikavulala kapena kudwala, m’busa wabwino amacitapo kanthu mwamsanga. Mofanana ndi zimenezi, akulu afunika kuthandiza mwamsanga aliyense mumpingo amene akuvutika kapena amene akufunikila thandizo la kuuzimu. Ngakhale kuti Akristu acikulile ndiponso odwala amafunikila thandizo lakuthupi mogwilizana ndi zosoŵa zao, io amafunikila kwambili thandizo la kuuzimu ndi cilimbikitso. (1 Ates. 5:14) Acinyamata mumpingo amakumana ndi ziyeso zosiyana-siyana monga kulimbana ndi “zilako-lako zaunyamata.” (2 Tim. 2:22) Ndiye cifukwa cake kuweta nkhosa kumaphatikizapo kuyendela abale ndi alongo a mumpingo nthawi ndi nthawi ndi colinga cofuna kudziŵa mavuto amene akukumana nao ndi kuwalimbikitsa ndi Malemba. Ngati akulu acitapo kanthu madzi akali m’nkhongono, mavuto angathetsedwe zinthu zisanaipe kwambili.

16. Kodi akulu angathandize bwanji Mkristu amene akufunikila thandizo la kuuzimu?

16 Nanga bwanji ngati Mkristu ali ndi vuto lalikulu limene lingaononge ubwenzi wake ndi Yehova? Wolemba Baibo Yakobo analemba kuti: “Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo io amupemphelele ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphelo lacikhulupililo lidzacilitsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anacita macimo, adzakhululukidwa.” (Yak. 5:14, 15) Ngati Mkristu wodwala mwa kuuzimu ‘sanaitane akulu a mpingo,’ akuluwo afunika kum’thandiza mwamsanga akadziŵa za vuto lake. Akulu ayenela kupemphela ndi abale ndi alongo ao ndiponso kuwapemphelela ndi kuwacilikiza akakumana ndi mavuto. Akamacita zimenezo, akuluwo amatsitsimula ndi kulimbikitsa anthu amene ndi udindo wao kuwasamalila.—Ŵelengani Yesaya 32:1, 2.

17. Kodi cimacitika n’ciani ngati akulu amatsanzila “m’busa wamkulu”?

17 Pa ciliconse cimene abusa acikristu amacita m’gulu la Yehova, io amayesetsa kutsanzila “m’busa wamkulu,” Yesu Kristu. Mwa thandizo la akulu, anthu onse mumpingo amapindula kwambili ndipo amapita patsogolo. Tikaganizila zinthu zonse zimene akulu amaticitila, timayamikila ndi kutamanda kwambili Mbusa wathu wamkulu koposa onse, Yehova.

[Cithunzi papeji 30]

Akulu amathandiza mabanja ao kukonzekela ulaliki (Onani ndime 13)

[Zithunzi papeji 31]

Oyang’anila amapeleka citsanzo cabwino pa nchito yolalikila (Onani ndime 14)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani