LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • od masa. 206-212
  • Makambilano othela na ofunsila ubatizo

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Makambilano othela na ofunsila ubatizo
  • Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Nkhani Zofanana
  • Zakumapeto
    Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
  • Ubatizo ni Khomo la ku Madalitso Oculuka!
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
  • Bokosi La Mafunso
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Kodi Ubatizo Ndi Wofunika Bwanji Paubwenzi Wanu ndi Mulungu?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Onaninso Zina
Gulu Lokhazikitsidwa Kucita Cifunilo ca Yehova
od masa. 206-212

MAFUNSO KWA OFUNSILA UBATIZO

Makambilano othela na ofunsila ubatizo

Kaŵili-kaŵili, ubatizo umacitikila ku misonkhano yadela komanso yacigawo ya Mboni za Yehova. Nkhani ya ubatizo ikatha, mkambi amapempha opita ku ubatizo kuti aimilile na kuyankha mokweza mafunso aŵili awa:

1. Kodi munalapa macimo anu, munadzipatulila kwa Yehova, komanso munalandila njila yake ya cipulumutso mwa Yesu Khristu?

2. Kodi mukumvetsa kuti mukabatizika lelo, ndiye kuti mwakhala Mboni ya Yehova yeni-yeni, ndiponso mwaloŵa m’gulu lake la Yehova?

Mmene opita ku ubatizo ayankhila motsimikiza mafunso amenewa, ndiye kuti ‘alengeza poyela’ kuti amakhulupilila dipo, komanso anadzipatulila kothelatu kwa Yehova. (Aroma 10:9, 10) Ofunsila ubatizo ayenela kuganizila mwapemphelo mafunso otsatilawa, kotelo kuti akawayankhe mocokela pansi pa mtima.

Kodi munadzipatulila kwa Yehova mwa pemphelo, na kumulonjeza kuti mudzalambila iye yekha basi, ndipo cinthu cacikulu kopambana mu umoyo wanu cidzakhala kucita cifunilo cake? Kodi pali pano ndimwe wotsimikiza na mtima wonse kuti ndimwe wokonzeka kukabatizika pa msonkhano umene ukubwela?

Kodi mavalidwe oyenelela ku ubatizo ni abwanji? (1 Tim. 2:9, 10; Yoh. 15:19; Afil. 1:10)

Tiyenela kuvala ‘mwaulemu ndi mwanzelu’ ‘molemekeza Mulungu.’ Conco, opita ku ubatizo sayenela kuvala kovala konyayila koonetsa thupi, kapena covala colembedwa mawu olengeza zina zake kapena ojambulidwa zithunzi.Ayenela kuvala mwaudongo, mwaukhondo, komanso moyenelela cocitikaco.

Kodi munthu ayenela kuonetsa khalidwe lotani pamene akubatizika? (Luka 3:21, 22)

Ubatizo wa Yesu unapeleka citsanzo ca ubatizo wa Akhristu lelolino. Iye anazindikila kuti ubatizo ni sitepu yaikulu kwambili, ndipo anaonetsa izi mwa khalidwe lake pobatizika. Mwa ici, malo a ubatizo si ocitilako nthabwala zosayenela, maseŵela, kunyaya, kapena khalidwe lililonse limene lingacotsele ulemu cocitikaco. Komanso Mkhristu watsopanoyo sayenela kusangalala mocita kunyanya ngati kuti wapata cikho. Ngakhale kuti ubatizo ni cocitika cosangalatsa, cisangalaloco ticionetse mwaulemu wake.

Kodi kupezeka ku misonkhano nthawi zonse, komanso kuyanjana na mpingo, kudzakuthandizani bwanji kutumikilabe monga wodzipatulila kwa Yehova?

Mukabatizika, n’cifukwa ciani mudzafunika kukhala na pulogilamu yabwino ya phunzilo laumwini, na kumapita mu ulaliki nthawi zonse?

MALANGIZO KWA AKULU A MPINGO

Wofalitsa wosabatizika akakudziŵitsani kuti afuna kubatizika, mulimbikitseni kukaŵelenganso “Mafunso kwa Ofunsila Ubatizo,” pa masamba 185-​207 m’buku lino. Muuzeni kuti akaŵelengenso “Mawu kwa Wofalitsa Wosabatizika,” kuyambila pa tsamba 182, ofotokoza zimene ayenela kucita pokonzekela makambilano ake na akulu. Monga tachulila pamenepo, wofunsila ubatizoyo angaseŵenzetse manotsi ake, ndipo buku lake lingakhale lotsegula pa makambilano amenewo. Komabe, n’kosafunikila kuti wina wake apitemo naye m’mafunso amenewo asanakumane na akulu.

Aliyense wofuna kubatizika ayenela kudziŵitsa mgwilizanitsi wa bungwe la akulu. Pambuyo pakuti wofunsila ubatizo watsiliza kuŵelenga “Mafunso kwa Ofunsila Ubatizo,” mgwilizanitsi wa bungwe la akulu ayenela kufunsa ngati munthuyo anadzipatulila m’pemphelo kwa Yehova kuti afuna kucita cifunilo cake. Ngati munthuyo anadzipatulila, mgwilizanitsi wa bungwe la akulu apange makonzedwe akuti akulu aŵili akakambilane na munthuyo “Mafunso a Ofunsila Ubatizo.” Mkulu aliyense agaŵilidwe imodzi ya magawo aŵiliwo. Makambilano amenewa safunika kuyembekezela kuti mpaka cilengezo ca msonkhano wadela kapena wacigawo cikapelekedwe iyayi.

Makambilano a gawo lililonse angatenge pafupi-fupi ola limodzi. Koma palibe coletsa kutenga nthawi yoposelapo ngati n’kofunikila. Makambilano alionse aziyamba na pemphelo, n’kuthanso na pemphelo. Pokambilana mafunsowo, pakati pa mkulu na wofunsila ubatizo, pasakhale wofulumizitsa mnzake. Akulu aŵili akagaŵilidwa asainimenti imeneyi, conde asaigonekeze, aisamalile mmangu-mmangu.

Ni bwino kwambili kufunsa mafunso amenewa kwa munthu aliyense payekha, osati gulu la ofunsila ubatizo. Pamene munthu ayankha funso lililonse, akulu amakhala na cithunzi cabwino ca cidziŵitso cake, kuona ngati munthuyo ali wokonzeka kubatizika kapena ayi. Komanso, wofunsila ubatizo amakhala womasuka bwino kufotokoza maganizo ake. Koma mwamuna na mkazi wake akhoza kufunsidwa capamodzi.

Ngati wofunsila ubatizo ni mlongo, ayenela kukhala pamalo oonekela bwino kwa anthu ena, koma pakuti ena sangamve kukambilana kwawo. Ngati pangafunikile kutengako munthu wina, azikhala mkulu kapena mtumiki wothandiza, malinga na mbali imene akambilane, monga tafotokozela m’ndime yotsatilayi.

M’mipingo imene akulu ni ocepa kwambili, atumiki othaniza okhoza bwino, amene aonetsa kukhala oganiza bwino komanso ozindikila, angakambilane na wofunsila ubatizo “Gawo 1 yakuti: Zimene Ife Akhristu Timakhulupilila.” Akulu okha ni amene ayenela kusamalila “Gawo 2 yakuti: Umoyo Wacikhristu.” Ngati mpingo ulibe abale oyenelela okwanila, mungafunsile kwa woyang’anila dela kuti aone mpingo wapafupi umene ungathandize.

Ngati wofunsila ubatizo ni mwana, kholo kapena makolo ake amene ni Mboni ayenela kukhalapo pa makambilanowo. Ngati sangakhalepo, pakhale akulu aŵili (kapena mkulu na mtumiki wothandiza, malinga na mbali imene akuipendayo) pa magawo onse aŵili.

Akuluwo ayenela kutsimikiza kuti munthu wofuna kubatizikayo amamvetsa ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo pa mlingo wabwino, osati kucita kudziŵa zonse. Komanso, ayenela kuona ngati munthuyo amaciyamikiladi coonadi, ndipo amaoneka kuti amalemekeza gulu la Yehova. Ngati sanafike pomvetsetsa bwino ziphunzitso zoyambilila za m’Baibo, akulu akonze zakuti athandizidwe kuti akayenelele ubatizo panthawi ina. Ena angafunikile kuwapatsa nthawi kuti afikedi pokonda ulaliki, kapena kugonjela ku makonzedwe a gulu. Mkulu aliyense ayenela kuiseŵenzetsa bwino nthawi ya ola imeneyo, kapena kuposelapo, kuti akhale na cithunzi cabwino kuona ngati munthuyo alidi wokonzeka kubatizika. Ngakhale kuti mungatengeko nthawi pa mafunso ena kuposa ena, mafunso onse ayenela kufunsidwa.

Pambuyo pakuti mafunso a gawo laciŵili apendedwa, akuluwo akumane na kuona ngati angamuyeneleze munthuyo kubatizika kapena ayi. Akuluwo ayenela kuganizilanso mmene munthuyo anakulila, kukhoza kwake kucita zinthu, komanso mikhalidwe ina pa umoyo. Cacikulu kwa ife ni kuona ngati mtima wa munthu unatembenukiladi kwa Yehova, ndiponso akumvetsa mfundo zikulu-zikulu za coonadi ca m’Baibo. Na thandizo lanu lacikondi, okabatizikawo adzakhala okonzeka mokwanila kukagwila nchito yofunika kwambili yolengeza uthenga wabwino.

Pambuyo pake, mmodzi wa akuluwo kapena onse aŵili, akumane na munthuyo na kumudziŵitsa ngati apeza kuti ni woyenelela kubatizika kapena ayi. Ngati ni woyenelela, akuluwo akambilane naye “Makambilano Othela na Ofunsila Ubatizo,” opezeka pa masamba 206-207. Ngati munthuyo sanatsilize kuphunzila buku la Zimene Ingatiphunzitse komanso lakuti Tikhalebe mu Cikondi ca Mulungu, akuluwo am’limbikitse kukatsilizabe pambuyo pa ubatizo. Mudziŵitseni wopita ku ubatizoyo kuti tsiku lake la ubatizo lidzalembedwa ku khadi yake Yolembapo Nchito za Wofalitsa. Muchulileni kuti cifukwa cimene akulu akutengela cidziŵitso caumwini cokhudza iye n’cakuti gulu lizitha kusamalila nchito za Mboni za Yehova padziko lonse, kuti nayenso azitengako mbali m’nchito zauzimu na kulandilanso cilimbikitso. Akulu ayenelanso kudziŵitsa ofalitsa atsopano kuti cidziŵitso caumwini ciliconse cimasamalidwa m’cigwilizano na mfundo yakuti Global Data Protection Policy of Jehovah’s Witnesses, yopezeka pa jw.org. Makambilano amenewa azikhala a mphindi 10 basi, ngakhale zocepelapo.

Pakapita caka cimodzi kucokela pamene wofalitsa anabatizika, akulu aŵili akumane naye kuti am’patse cilimbikitso na malingalilo othandiza. Mmodzi wa akuluwo akhale woyang’anila kagulu wa munthuyo. Ngati watsopanoyo ni mwana wam’ng’ono, kholo kapena makolo ake amene ni Mboni akhalepo. Mzimu wake pa kukumanaku uzikhala waubwenzi komanso wolimbikitsa kwambili. Akuluwo akambilane naye za kupita kwake patsogolo mwauzimu, na kum’patsa malingalilo a mmene angapitilizile na pulogilamu yabwino ya phunzilo laumwini, kuŵelenga Baibo tsiku na tsiku, kulambila kwa pabanja kwa mlungu na mlungu, kupezeka ku misonkhano mokhazikika na kutengapo mbali, komanso kulalikila mlungu na mlungu. (Aef. 5:15, 16) Ngati sanatsilize kuphunzila buku la Zimene Ingatiphunzitse komanso Tikhalebe mu Cikondi ca Mulungu, akulu apange makonzedwe akuti wina wake atsilize nawo. Akuluwo azikhala oyamikila mosaumila. Kaŵili-kaŵili, uphungu wacikondi pa mfundo imodzi kapena ziŵili, na kupelekapo malingalilo othandiza kungakhale kofunikila.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani