Bokosi La Mafunso
◼ Kuti wofalitsa wosabatizika ayenelele ubatizo, kodi ayenela kuti wakhala akupezeka pa misonkhano yonse ya mpingo komanso kucilikiza ulaliki motani?
Ubatizo ndi cosankha cofunika kwambili cimene munthu angapange. Conco, kuti munthu ayenelele ubatizo ayenela kumvetsetsa bwino zimene Mulungu amafuna kwa iye. Kuonjezela apo, khalidwe lake liyenela kuonetsa kuti anayamba kale kusonyeza mtima wofuna kucita zimene Mulungu amafuna.
Akristu amalamulidwa kuti asaleke kusonkhana pamodzi, conco wofalitsa wosabatizika ayenela kuonetsa kuti akucita khama kupezeka pa misonkhano ya mpingo. (Aheb. 10:24, 25) Ayenelanso kuyankhapo pamisonkhano. Komanso angalembetse m’Sukulu ya Ulaliki, ngakhale kuti kulembetsa m’Sukulu si ciyeneletso.
Kuonjezela pamenepa, popeza kuti Akristu analamulidwa kulalikila uthenga wabwino ndi kupanga ophunzila, wofalitsa wosabatizika ayenela nthawi zonse kucilikiza ulaliki akalibe kubatizika. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Kodi ayenela kulalikila kwa miyezi ingati asanabatizike? Ayenela kupatsidwa nthawi yokwanila bwino yoonetsa kuti ndi wotsimikiza kutengamo mbali mokhazikika komanso mwacangu m’nchito yolalikila mwezi uliwonse. (Sal. 78:37) Komabe, sipayenela kupita nthawi yaitali kwambili kucokela pamene anayamba kulalikila mpaka pamene angayenelele kubatizika, mwina miyezi yocepa. Kodi ayenela kucitila lipoti maola angati a ulaliki? Palibe malamulo oikika pamenepa. Akulu ayenela kuona mikhalidwe ya wofalitsa aliyense komanso ayenela kucita zinthu mololela ndi mosamala.—Luka 21:1-4.
Akulu (kapena atumiki othandiza m’mipingo imene ili ndi akulu ocepa) amene akukumana ndi oyembekeza ubatizo ayenela kukumbukila kuti munthu aliyense ndi wosiyana, ndipo ayenela kucita mosamala pamene agamula zakuti munthu ayenelele kupita kuubatizo kapena ai. Akulu ayenela kuona kuti munthuyo akufunitsitsa kukhala m’modzi wa Mboni za Yehova ndi kuti akuyamikila mwai wopezeka m’gulu la Yehova komanso kutengako mbali m’nchito yolalikila. Akulu amadziŵa kuti munthuyo akalibe kukhwima mwa kuuzimu kapena kukhala ndi luso la alaliki obatizika akale. Ngati akulu aona kuti munthuyo sanayenelele ubatizo, ayenela mokoma mtima kumuuza zifukwa za m’Malemba zimene zacititsa kuti agamule conco, komanso kumuthandiza mwa kuuzimu.