LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 23 tsa. 60-tsa. 61 pala. 4
  • Lonjezo kwa Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Lonjezo kwa Yehova
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Yehova Apeleka Malamulo Ake
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Sanasunge Lonjezo Lawo
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Citsamba Coyaka Moto
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 23 tsa. 60-tsa. 61 pala. 4
Aisiraeli aimilila munsi mwa Phili la Sinai

PHUNZILO 23

Lonjezo kwa Yehova

Patapita miyezi pafupi-fupi iŵili pambuyo potuluka mu Iguputo, Aisiraeli anafika pa Phili la Sinai na kumanga msasa. Yehova anauza Mose kuti akwele m’phili. Mmenemo iye anamuuza kuti: ‘N’napulumutsa Aisiraeli. Ngati adzamvela mawu anga na kusunga malamulo anga, adzakhala anthu anga apadela.’ Mose anaseluka m’phili, na kukauza Aisiraeli zimene Yehova anakamba. Kodi iwo anati ciani? Iwo anayankha kuti: ‘Zonse zimene Yehova wakamba tidzacita zimenezo.’

Mose anakwelanso m’phili muja. Mmenemo, Yehova anamuuza kuti: ‘Pakapita masiku atatu, nidzakamba na iwe. Ukauze anthu kuti asayese kukwela m’Phili la Sinai.’ Mose anaseluka na kukauza Aisiraeli kuti akonzekele kukamvetsela kwa Yehova.

Aisiraeli aona mphenzi na mtambo wakuda pa Phili la Sinai

Patapita masiku atatu, Aisiraeli anaona mphenzi na mtambo wakuda bii pa phili. Anamvelanso kugunda kwamphamvu kwa mabingu na kulila kwa lipenga. Pamenepo Yehova anatsikila pa philipo m’moto. Aisiraeli anali nje-nje-nje cifukwa ca mantha. Phili lonse linagwedezeka mwamphamvu, ndipo linaphimbika mu ciutsi. Kulila kwa lipenga kunakwelela-kwelela. Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ine ndine Yehova. Musalambile milungu ina iliyonse.’

Mose anabwelelanso m’phili, ndipo Yehova anam’patsa malamulo a mmene anthuwo ayenela kulambilila Mulungu, na mmene ayenela kukhalila. Mose analemba malamulowo na kuyaŵelenga kwa Aisiraeli. Iwo analonjeza kuti: ‘Zonse zimene Yehova wakamba tidzacita zimenezo.’ Inde, iwo anapanga lonjezo kwa Mulungu. Koma kodi anasunga lonjezo lawo?

“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”—Mateyu 22:37

Mafunso: Cinacitika n’ciani pa Phili la Sinai? Nanga Aisiraeli analonjeza kucita ciani?

Ekisodo 19:1–20:21; 24:1-8; Deuteronomo 7:6-9; Nehemiya 9:13, 14

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani