LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 35 tsa. 86-tsa. 87 pala. 1
  • Hana Apemphela Kuti Akhale na Mwana

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Hana Apemphela Kuti Akhale na Mwana
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Lolani Kuti Yehova Akutonthozeni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kamnyamata Kotumikila Mulungu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • Mukhuthulileni za Mumtima Mwanu Yehova M’pemphelo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
  • Misozi Yanu Ni Yamtengo Wapatali kwa Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Onaninso Zina
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 35 tsa. 86-tsa. 87 pala. 1
Hana apeleka wacicepele Samueli kwa Eli ku cihema

PHUNZILO 35

Hana Apemphela Kuti Akhale na Mwana

Mwiisiraeli wina, Elikana, anali na akazi aŵili, maina awo anali Hana na Penina. Koma Elikana anali kukonda kwambili Hana. Penina anali kuvutitsa Hana nthawi zonse cifukwa Hana analibe ana, koma Penina anali ndi ana ambili. Caka ciliconse, Elikana anali kupita ku Silo na banja lake kukalambila ku cihema. Tsiku lina ali kumeneko, Elikana anaona kuti mkazi wake wokondedwa, Hana, ni wacisoni kwambili. Anamuuza kuti: ‘Hana, osalila conde. Ine nilipo. Ndipo nimakukonda.’

Tsiku lina Hana anapita kwa yekha kuti akapemphele. Anali kungolila pocondelela Yehova kuti am’thandize. Iye analonjeza kuti: ‘Yehova, mukanipatsa mwana wamwamuna, nidzam’peleka kwa inu ndipo adzakutumikilani kwa moyo wake wonse.’

Eli Mkulu wa Ansembe ayang’ana Hana pamene apemphela uku akulila

Eli Mkulu wa Ansembe anaona Hana akusisima, ndipo anaganiza kuti Hana wakolewa. Koma Hana anamuuza kuti: ‘Iyai mbuyanga, sin’namwe moŵa. Nili na vuto lalikulu, pano nidandaulila Yehova za vutolo.’ Eli anadziŵa kuti walakwa ndiyeno anauza Hana kuti: ‘Mulungu akupatse zimene ufuna.’ Mtima wa Hana unakhala pansi, kenako anapita. Caka cikalibe kutha, Hana anakhala na mwana wamwamuna, anam’patsa dzina lakuti Samueli. Ganizila cabe mmene Hana anakondwelela.

Hana sanaiŵale lonjezo lake kwa Yehova. Samueli atangoleka kuyamwa, anam’peleka ku cihema kuti akatumikile kumeneko. Hana anauza Eli kuti: ‘Uyu ndiye mwana n’nali kupemphelela uja. Masiku onse a moyo wake, nam’peleka kwa Yehova.’ Caka na caka, Elikana pamodzi na Hana anali kupita kukaona Samueli na kum’pelekela covala catsopano copanda manja. Yehova anapatsanso Hana ana ena aamuna atatu, komanso aakazi aŵili.

“Pemphanibe, ndipo adzakupatsani. Pitilizani kufunafuna, ndipo mudzapeza.”—Mateyu 7:7

Mafunso: N’cifukwa ciani Hana anali kuvutika mu mtima? Kodi Yehova anam’dalitsa bwanji Hana?

1 Samueli 1:1–2:11, 18-21

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani