PHUNZILO 46
Mulungu Woona Adziŵika pa Phili la Karimeli
Ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 unali na mafumu ambili oipa. Koma mmodzi wa oipitsitsa kwambili anali Ahabu. Iye anakwatilanso mkazi woipa kwambili wolambila Baala. Dzina lake anali Yezebeli. Cifukwa ca Ahabu na Yezebeli, kulambila Baala kunali paliponse. Ndipo aŵiliwa anapha aneneli a Yehova. Kodi Yehova anacitapo ciani? Anatuma mneneli Eliya kuti akapeleke uthenga kwa Ahabu.
Eliya anauza Mfumu Ahabu kuti cifukwa ca kuipa kwake, mu Isiraeli simudzagwa mvula. Kwa zaka zitatu na kuposapo, mbewu sizinamele, cakuti kunali njala yaikulu. M’kupita kwa nthawi, Yehova anatumizanso Eliya kwa Ahabu. Mfumu inauza Eliya kuti: ‘Wobweletsa mavuto iwe! Zonse izi n’cifukwa ca iwe.’ Eliya anayankha kuti: ‘Sindine nabweletsa cilala. Ndimwe munabweletsa cilala cifukwa ca kulambila kwanu Baala. Tidzafuna tione kuti Mulungu woona ndani. Sonkhanitsani Aisiraeli onse, na aneneli a Baala pa Phili la Karimeli.’
Anthu atasonkhana pa phililo, Eliya anati: ‘Sankhani amene mudzam’tumikila. Ngati Yehova ndiye Mulungu woona, m’tsatileni. Ngati Baala ndiye woona, m’tsatileni. Aneneli 450 a Baala akonze nsembe yawo, ndiyeno apemphele kwa mulungu wawo. Inenso nikonza nsembe ndipo nidzapemphela kwa Yehova. Mulungu amene ayankhe potumiza moto ndiye Mulungu woona.’ Anthu onse anagwilizana nazo.
Aneneli a Baala anakonza nsembe yawo. Ndipo tsiku lonse anafuula kwa mulungu wawo, amvekele: ‘Mbuyathu Baala, tiyankheni conde!’ Pamene Baala sanali kuyankha, Eliya anali kumuseka, amvekele: ‘Kuwani mofikapo. Mwina mulungu wanu wagona, wina amuutseko.’ Mpaka m’madzulo, aneneli a Baala anali kufuulabe. Koma kunalibe yankho iliyonse.
Tsopano Eliya anaika nsembe yake paguwa, ndipo anathila madzi paguwa ponsepo. Kenako anapemphela kuti: ‘Mbuyanga Yehova, conde pangitsani kuti anthu awa adziŵe kuti inu ndinu Mulungu woona.’ Pamenepo, Yehova anatumiza moto kucokela kumwamba na kunyeketsa nsembeyo. Anthu poona izi anafuula kuti: ‘Yehova ndiye Mulungu woona!’ Eliya anati: ‘Musalole kuti aneneli a Baala athaŵe!’ Pa tsiku limenelo, aneneli 450 a Baala anaphedwa.
Eliya ataona kamtambo kakang’ono pamwamba pa nyanja, anauza Ahabu kuti: ‘Kubwela mvula yamkuntho. Mangani mahosi ku galeta mupite ku nyumba.’ Kumwamba kunacita mdima wa mitambo, ndipo kunja kunawomba cimphepo. Kenako cimvula cinayamba kugwa. Ndiye kunali kutha kwa cilala. Ahabu anathamangitsa kwambili galeta lake. Koma mwa thandizo la Yehova, Eliya anathamanga wapansi mpaka kupitilila galetayo! Koma kodi mavuto a Eliya anatha? Tidzaona m’nkhani yotsatila.
“Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, Ndinu Wam’mwamba-mwamba pa dziko lonse lapansi.”—Salimo 83:18, nwt-E