LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 47 tsa. 114-tsa. 115 pala. 3
  • Yehova Alimbikitsa Eliya

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Alimbikitsa Eliya
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Nthawi Zina Umaona kuti Uli Wekha Ndipo Ukucita Mantha?
    Phunzitsani Ana Anu
  • Mulungu Woona Adziŵika pa Phili la Karimeli
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Dalilani Yehova Pamene Muli na Nkhawa
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 47 tsa. 114-tsa. 115 pala. 3
Eliya waimilila panja pa phanga pa Phili la Horebe ndipo akumvetsela kwa mngelo wa Mulungu

PHUNZILO 47

Yehova Alimbikitsa Eliya

Yezebeli atamva zimene zinacitika kwa aneneli a Baala, anakwiya kwambili. Ndipo anatumiza uthenga kwa Eliya. Uthengawo unati: ‘Mailo, iwenso udzafa monga aneneli a Baala.’ Eliya anayopa kwambili, ndipo anathaŵila ku cipululu. Atafika kumeneko anapemphela kuti: ‘Yehova, nalema nazo. Lekani nife cabe.’ Atalema, Eliya anagona tulo tofa nato pansi pa mtengo.

Pambuyo pake, mngelo anamuutsa mwakacetecete, amvekele: ‘Uka udye.’ Eliya anaona kapu ya madzi na buledi yozungulila pa miyala yotentha. Anadya na kumwa madzi, kenako anagonanso. Mngelo uja anamuutsanso kuti: ‘Uka udye. Ufunikila mphamvu pakuti ulendowu ni wautali.’ Conco, Eliya anadyanso. Kucoka apo, anayenda ulendo wa masiku 40, usana na usiku mpaka kukafika ku Phili la Horebe. Kumeneko, Eliya analoŵa m’phanga, kapena kuti m’mphako, kuti agone. Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Ucita ciani kuno Eliya?’ Eliya anayankha kuti: ‘Aisiraeli anaphwanya lonjezo lawo kwa imwe. Anagwetsa maguwa anu ansembe, ndipo anapha aneneli anu. Lomba afuna kuphanso ine.’

Yehova anamuuza kuti: ‘Pita ukaimilile pa phili.’ Pamenepo, cimphepo camphamvu cinawomba kudutsa pa phangapo. Ndiyeno panacitika civomezi, kenako kunabuka moto. Pamapeto pake, Eliya anamvela mawu ofeŵa apansi-pansi. Anaphimba nkhope yake na covala, na kuimilila panja pa phangapo. Ndiyeno Yehova anamufunsanso cifukwa cake anathaŵa. Eliya anati: ‘Ndatsala ndekha amene ndikutumikila inu.’ Koma Yehova anamuuza kuti: ‘Suli wekha. Mu Isiraeli muli anthu 7,000 amene akali kunilambila. Pita ukadzoze Elisa kuti akhale mneneli m’malo mwa iwe.’ Pamenepo, Eliya anapita kukacita zimene Yehova anamuuza. Kodi uganiza kuti na iwe Yehova adzakuthandiza ngati ucita zimene afuna kuti ucite? Inde, adzakuthandizadi. Tidzaonanso cina cimene cinacitika pa nthawi ya cilala cimeneci.

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu.”—Afilipi 4:6

Mafunso: N’cifukwa ciani Eliya anathaŵa? Ndipo Yehova anamuuza ciani?

1 Mafumu 19:1-18; Aroma 11:2-4

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani