LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 48 tsa. 116-tsa. 117 pala. 1
  • Mwana wa Mkazi Wamasiye Aukitsidwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mwana wa Mkazi Wamasiye Aukitsidwa
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Nthawi Zina Umaona kuti Uli Wekha Ndipo Ukucita Mantha?
    Phunzitsani Ana Anu
  • Yehova Alimbikitsa Eliya
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Mmene Tingakhalilebe ndi Maganizo Oyenela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 48 tsa. 116-tsa. 117 pala. 1
Eliya afikila mkazi wamasiye amene akutola nkhuni

PHUNZILO 48

Mwana wa Mkazi Wamasiye Aukitsidwa

Mtsuko wa fulawo ndi wa mafuta

Pa nthawi ya cilala, Yehova anauza Eliya kuti: ‘Pita ku Zarefati. Kumeneko mkazi wamasiye adzakupatsa cakudya.’ Atangolowa mu mzinda, Eliya anaona mkazi wamasiye akutola nkhuni. Iye anapempha mzimayiyo madzi akumwa. Pamene mzimayiyo ananyamuka kuti akatenge madzi, Eliya anam’pemphanso kuti: ‘Conde, unibweletselekonso mkate.’ Koma mzimayiyo anati: ‘Nilibe mkate wakuti nikupatseni. Nili na tufulawo tocepa cabe, komanso tumafuta tongokwanila ine na mwana wanga.’ Eliya anamuuza kuti: ‘Yehova walonjeza kuti ngati unipangila mkate, fulawo wako na mafutawo sadzatha mpaka mvula ikabwele.’

Conco, mkazi wamasiyeyo anapita ku nyumba kukakonzela mkate mneneli wa Yehova. Monga mmene Yehova analonjezela, mzimayiyo na mwana wake, cakudya sicinawathele m’nthawi yonse ya cilala. Mtsuko wake wa fulawo komanso wa mafuta sunapunguke.

Koma panacitika cinthu cina coipa kwambili. Mwana wa mzimayiyo anadwala kwambili mpaka anamwalila. Mkaziyo anapempha Eliya kuti am’thandize. Eliya anatenga mwanayo m’manja mwa mayi ake n’kupita naye kucipinda cinali pamwamba. Anam’goneka pa bedi, na kupemphela kuti: ‘Yehova, conde muukitseni mwanayu.’ Zimene Eliya anapempha zinali zocititsa cidwi kwambili. Udziŵa cifukwa cake? Cifukwa mmene tidziŵila, kumbuyo konseko kunalibe munthu amene anaukitsidwapo. Komanso, mkazi wamasiyeyu na mwana wake sanali Aisiraeli n’komwe.

Mwanayo anauka, ndipo anayambanso kupuma! Eliya anauza mkaziyo kuti: ‘Ona! Mwana wako wakhalanso na moyo.’ Mkaziyo anasangalala kwambili, ndipo anauza Eliya kuti: ‘Ndinu munthu wa Mulungu zoona. Nadziŵa, cifukwa mumakamba mawu amene Yehova wakuuzani, ndipo mawuwo amakwanilitsikadi.’

Eliya apeleka mwana amene waukayo kwa mkazi wamasiye

“Onetsetsani makwangwala, iwo safesa mbewu kapena kukolola. Alibe nyumba yosungilamo zinthu kapena nkhokwe, komatu Mulungu amawadyetsa. Kodi inu si ofunika kwambili kuposa mbalame?”—Luka 12:24

Mafunso: Kodi mkazi wamasiye wa ku Zarefati anaonetsa bwanji cidalilo cake mwa Yehova? Tidziŵa bwanji kuti Eliya anali mneneli woona wa Mulungu?

1 Mafumu 17:8-24; Luka 4:25, 26

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani