LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 52 tsa. 126-tsa. 127 pala. 1
  • Asilikali a Yehova Amoto

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Asilikali a Yehova Amoto
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Ife Tili ndi Ambili Kuposa Amene Ali ndi Iwo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2022
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 52 tsa. 126-tsa. 127 pala. 1
Elisa na mtumiki wake azungulidwa na gulu la asilikali a Siriya

PHUNZILO 52

Asilikali a Yehova Amoto

Beni-hadadi Mfumu ya Siriya, anali kuukila Isiraeli kaŵili-kaŵili. Koma mneneli Elisa anali kucenjeza mfumu ya Isiraeli nthawi zonse kuti ithaŵe. Conco Beni-hadadi anaganiza zogwila Elisa. Atafufuza anadziŵa kuti Elisa anali mu mzinda wa Dotana. Ndiye anatuma asilikali ake kuti akam’gwile.

Asilikali acisiriya aja anafika ku Dotana usiku. M’mawa mwake, mtumiki wa Elisa atacoka panja, anangoona kuti mzindawo wazingidwa na asilikali ambili-mbili. Anacita mantha na kufuula kuti: ‘A Elisa, tidzacita bwanji?’ Elisa anamuuza kuti: ‘Ife tili na ambili kumbali yathu kuposa amene ali kumbali yawo.’ Pamenepo, Yehova anatsegula maso a mtumiki wa Elisa, ndipo anaona kuti mapili ozungulila mzindawo, anali odzala na mahosi na magaleta ankhondo oyaka moto.

Elisa na mtumiki wake ayang’ana angelo ankhondo atawazungulila

Pamene asilikali acisiriya anayesa kugwila Elisa, iye anapemphela kwa Yehova kuti am’thandize. Mwadzidzidzi, ngakhale kuti asilikaliwo anali kuona, anasokonezeka cakuti sanadziŵenso kumene anali. Ndiyeno Elisa anaŵauza kuti: ‘Mwataika, mwabwela ku mzinda wolakwika. Tiyeni nikupelekeni kwa munthu amene mufuna.’ Conco iwo anatsatila Elisa mpaka ku Samariya kwa mfumu ya Isiraeli.

Apa lomba asilikali acisiriya anazindikila kumene anali, koma mocedwa, anali kale m’manja mwa mfumu ya Isiraeli. Ndiye mfumuyo inafunsa Elisa kuti: ‘Kodi niŵaphe?’ Kodi Elisa anapezelapo mwayi wokhaulitsa asilikaliwo, amene anafuna kumucita zoipa? Iyai. Elisa anati: ‘Iyai musaŵaphe. Apatseni cakudya, akadya muŵalole apite kwawo.’ Conco, mfumuyo inawakonzela phwando lalikulu. Pambuyo pake inaŵalola kupita kwawo.

Asilikali acisiriya akudya cakudya ku Samariya

“Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.”—1 Yohane 5:14

Mafunso: Kodi Yehova anamuteteza bwanji Elisa na mtumiki wake? Kodi uona kuti na iwe Yehova angakuteteze?

2 Mafumu 6:8-24

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani