PHUNZILO 83
Yesu Adyetsa Khamu la Anthu
Tsiku lina, cikondwelelo ca Pasika citayandikila mu 32 C.E. atumwi anabwelako ku maulendo a ulaliki. Anali olema, ndipo Yesu anawatenga kukakwela nawo boti kupita ku Betsaida kuti akapumuleko. Koma boti itayandikila ku mtunda, Yesu anangoona khamu la anthu lija linawalondola. Ngakhale kuti anafuna kupumulako pamodzi na atumwi ake, iye anawalandila bwino anthuwo. Anacilitsa odwala amene anthuwo anabweletsa, na kuyamba kuŵaphunzitsa. Yesu anawaphunzitsa za Ufumu wa Mulungu tsiku lonse. M’madzulo, atumwiwo anauza Yesu kuti: ‘Anthu awa ali na njala. Amasuleni kuti akagule zakudya.’
Koma Yesu anati: ‘Safunika kupita. Apatseni cakudya.’ Atumwiwo anafunsa kuti: ‘Kodi mufuna ife tipite tikaŵagulile cakudya?’ Koma Filipo, mmodzi wa atumwiwo, anati: ‘Olo tikanakhala na ndalama zambili, sembe sitinakwanitse kugula cakudya cokwana khamu lonseli.’
Ndiyeno Yesu anafunsa kuti: ‘Kodi tili na cakudya coculuka bwanji?’ Andireya anayankha kuti: ‘Tili na mitanda ya mkate 5 na tunsomba tuŵili cabe. Situngakwane ngakhale pang’ono.’ Ndiyeno Yesu anati: ‘Nipatseni mkate na tunsombato.’ Anauza anthuwo kuti akhale pansi pa udzu m’magulu a anthu 50 komanso 100. Yesu atatenga mikate na tunsomba tuja, anayang’ana kumwamba, n’kuyamba kupemphela. Atatsiliza, anapatsa atumwi ake cakudyaco kuti agaŵile anthu. Amuna okwana 5,000, komanso akazi ndi ana, onse anadya mpaka kukhuta. Pambuyo pake, atumwiwo anasokhanitsa zotsala kuti pasawonongeke ciliconse. Mabasiketi 12 anadzala! Cinali cozizwitsa cocititsa cidwi kwambili, si telo kodi?
Anthuwo anakondwela ngako, cakuti anafuna kuti Yesu akhale mfumu yawo. Koma iye anadziŵa kuti nthawi ya Yehova siinakwane yakuti akhale mfumu. Conco, anauza anthuwo kuti apite. Anauzanso atumwi ake kuti awolokele ku tsidya la Nyanja ya Galileya. Atumwiwo anakwela boti, koma Yesu anapita kwa yekha m’phili. Cifukwa ciani? Anafuna kupeza mpata wopemphela kwa Atate wake. Taona kuti olo akhale bize bwanji, Yesu nthawi zonse anali kupatula nthawi yopemphela.
“Musamagwile nchito kuti mungopeza cakudya cimene cimawonongeka, koma kuti mupeze cakudya cokhalitsa, copeleka moyo wosatha, cimene Mwana wa munthu adzakupatsani.”—Yohane 6:27