LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lfb phunzilo 84 tsa. 196-tsa. 197 pala. 4
  • Yesu Anayenda pa Madzi

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yesu Anayenda pa Madzi
  • Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Nkhani Zofanana
  • Boti Iwonongeka Pacisumbu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
  • “Limbani m’Cikhulupililo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Yesu Adyetsa Khamu la Anthu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
lfb phunzilo 84 tsa. 196-tsa. 197 pala. 4
Yesu ayenda pa madzi, ndipo auza Petulo kuti abwele kwa iye

PHUNZILO 84

Yesu Anayenda pa Madzi

Yesu anali kukwanitsa kucilitsa odwala, kuukitsa akufa, ngakhalenso kulamulila mphepo na mvula. Atatsiliza kupemphela pa phili, Yesu anayang’ana ku Nyanja ya Galileya, ndipo anaona cimphepo pa nyanjapo. Atumwi ake anali m’boti, ndipo anali kulimbana na cimphepoco. Kenako Yesu anaseluka m’phili muja na kuyamba kuyenda pa madzi kupita ku botiyo. Atumwi ataona munthu akuyenda pa madzi, anacita mantha kwambili. Koma Yesu anawauza kuti: ‘Ndine. Musacite mantha.’

Yesu ayenda pa madzi, ndipo auza Petulo kuti abwele kwa iye

Ndiyeno Petulo anati: ‘Ambuye, ngati ndimwedi, niuzeni nibwele kwa imwe.’ Yesu anauza Petulo kuti: ‘Bwela.’ Conco cimphepo cili mkati, Petulo anaseluka m’boti na kuyamba kuyenda pa madzi kupita kwa Yesu. Koma atafika pafupi na Yesu, anayang’ana cimphepo, ndipo anacita mantha. Anaona kuti wayamba kumila. Pamenepo Petulo anafuula kuti: ‘Ambuye, nipulumutseni!’ Yesu anam’gwila dzanja na kum’funsa kuti: ‘N’cifukwa ciani wayamba kukaikila? Cikhulupililo cako cili kuti?’

Pamene Yesu na Petulo anakwela m’botimo, cimphepo cija cinaleka. Kodi uganiza kuti atumwi anamvela bwanji? Iwo anauza Yesu kuti: “Ndinudi Mwana wa Mulungu.”

Aka sikanali koyamba Yesu kulamulila mphepo. Tsiku linanso, Yesu na ophunzila ake akupita kutsidya lina m’boti, Yesu anagona kumbuyo m’boti. Iye ali m’tulo, kunabwela cimphepo camphamvu. Mafunde amphamvu anali kuwomba botiyo cakuti munaloŵa madzi ambili. Anafuulila Yesu, amvekele: ‘Mphunzitsi, tithandizeni! Tikufa!’ Yesu anagalamuka, na kuuza nyanja kuti: “Leka! Khala bata!” Pamenepo cimphepo cinaleka, ndipo nyanja inakhala bata. Lomba Yesu anafunsa atumwi ake kuti: ‘Kodi cikhulupililo canu cili kuti?’ Iwo anayamba kuuzana kuti: “Ngakhale mphepo ndi nyanja zimumvela.” Atumwiwo anaphunzila kuti ngati akhulupilila Yesu na mtima wonse, sanafunike kuwopa ciliconse.

“Ngati ndikanakhala wopanda cikhulupililo poona ubwino wa Yehova m’dziko la anthu amoyo, ndikanataya ciyembekezo.”—Salimo 27:13

Mafunso: Kodi n’cifukwa ciani Petulo anayamba kumila? Nanga atumwi anaphunzila ciani kwa Yesu?

Mateyu 8:23-27; 14:23-34; Maliko 4:35-41; 6:45-52; Luka 8:22-25; Yohane 6:16-21

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani