NYIMBO 56
Khulupilila Coonadi Iwe Mwini
Yopulinta
(Miyambo 3:1, 2)
1. Njila yabwino ni njila ya co’nadi,
Palibe angakusankhile.
Mvela uphungu wocokela kwa M’lungu,
Ndipo um’khulupilile.
(KOLASI)
Panga co’nadi
Cikhale cako-cako.
Ndipo Yehova
‘dzakudalitsa,
Udzapeza cimwemwe.
2. Zonse zabwino zimene umacita
Potumikila M’lungu wathu,
Udzapezadi madalitso ambili,
Inde, moyo wamuyaya.
(KOLASI)
Panga co’nadi
Cikhale cakocako.
Ndipo Yehova
‘dzakudalitsa,
Udzapeza cimwemwe.
3. Kuli Yehova ndise ana ang’ono
Ofunika kulangizidwa.
Ukayenda na Atate wakumwamba
Udzapeza madalitso.
(KOLASI)
Panga co’nadi
Cikhale cakocako.
Ndipo Yehova
‘dzakudalitsa,
Udzapeza cimwemwe.
(Onaninso Sal. 26:3; Miy. 8:35; 15:31; Yoh. 8:31, 32)