LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 4
  • Kudzicepetsa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kudzicepetsa
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli
  • Tiphunzilaponji kwa Paulo?
  • Tengelani Citsanzo ca Paulo
  • Yehova Amaona Atumiki Ake Odzicepetsa Kukhala Amtengo Wapatali
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Kulitsani Makhalidwe Aumulungu—Kudzicepetsa
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • “Musamadziganizile Kuposa Mmene Muyenela Kudziganizila”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kukhala Wosamala
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 4

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Mtumwi Paulo atam’manga unyolo womulumikiza kwa msilikali. Akulankhula mwaulemu kwa Mfumu Agiripa, Bwanamkubwa Fesito, komanso Berenike.

Machitidwe 26:2, 3

PHUNZILO 4

Kudzicepetsa

Mfundo Yaikulu: ‘Modzicepetsa muziona ena kukhala okuposani.’—Afil. 2:3.

Mmene Paulo Anaonetsela Khalidwe Limeneli

Mtumwi Paulo atam’manga unyolo womulumikiza kwa msilikali. Akulankhula mwaulemu kwa Mfumu Agiripa, Bwanamkubwa Fesito, komanso Berenike.

VIDIYO: Paulo Alalikila Mfumu Agiripa

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 26:2, 3. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Kodi Paulo anaonetsa bwanji kudzicepetsa pokamba na Mfumu Agiripa?

  2. Kodi Paulo anaika motani patsogolo Yehova na Malemba m’malo mwa iyemwini?—Onani Mac. 26:22.

Tiphunzilaponji kwa Paulo?

2. Anthu amakopeka na uthenga wathu tikamakamba nawo modzicepetsa komanso mwaulemu.

Tengelani Citsanzo ca Paulo

3. Osalankhula modzionetsela. Pewani kulankhula monga mudziŵa zonse ndipo munthuyo palibe cimene adziŵa. Kambani naye mwaulemu.

4. Onetsani bwino lomwe kuti coonadi cimene muphunzitsa n’cocokela m’Baibo. Mfundo za m’Mawu a Mulungu zimatha kuwasintha mtima anthu. Pophunzitsa anthu Mawu a Mulungu timakhala tikumanga cikhulupililo cawo pa maziko olimba.

5. Khalanibe ofatsa. Osacita nthota pofuna kumveketsa mfundo yanu. Sitifuna kukangana ni anthu. Onetsani kudzicepetsa poika mtima wanu m’malo, komanso kucokapo mwamsanga ngati paoneka kuti pangabuke mkangano. (Miy. 17:14; Tito 3:2) Ngati tiyankha mofatsa, tingasiye khomo lili citsegukile kaamba ka makambilano abwino m’tsogolo.

ONANINSO MALEMBA AWA

Aroma. 12:16-18; 1 Akor. 8:1; 2 Akor. 3:5

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani