LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • lmd phunzilo 5
  • Kukhala Wosamala

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kukhala Wosamala
  • Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Mmene Paulo Anacitila Zimenezi
  • Tiphunzilaponji kwa Paulo?
  • Tengelani Citsanzo ca Paulo
  • Kudzicepetsa
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kodi Mumawaona Bwanji Anthu a mu Gawo Lanu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Kambilanani pa Zokhudza Munthuyo
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
  • Kukamba Mwacibadwa
    Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
Onaninso Zina
Kondani Anthu Kuti Mupange Ophunzila
lmd phunzilo 5

KUYAMBITSA MAKAMBILANO

Mtumwi Paulo akukambilana ni anthu a ku Atene.

Machitidwe 17:22, 23

PHUNZILO 5

Kukhala Wosamala

Mfundo Yaikulu: “Nthawi zonse mawu anu azikhala acisomo.”—Akol. 4:6.

Mmene Paulo Anacitila Zimenezi

Mtumwi Paulo akukambilana ni anthu a ku Atene.

VIDIYO: Paulo Alalikila Anthu a ku Atene

1. Tambani VIDIYO, kapena ŵelengani Machitidwe 17:22, 23. Kenaka ganizilani pa mafunso otsatilawa:

  1. Kodi Paulo anamva bwanji poona anthu akulambila mafano ku Atene?—Onani Mac. 17:16.

  2. M’malo mowadzudzula, kodi mosamala Paulo analoŵela bwanji ku zikhulupililo zawo kuti awagaŵile uthenga wabwino?

Tiphunzilaponji kwa Paulo?

2. Anthu angatimvetsele tikamasankha bwino zokamba, mozikambila, komanso nthawi yozikambila.

Tengelani Citsanzo ca Paulo

3. Kambani zimene munthuyo angagwilizane nazo. Mwacitsanzo, pokamba na munthu amene si wacipembedzo cacikhristu, mungafunikile kusintha mmene mumachulila za Baibo kapena Yesu.

4. Musafulumile kuwongolela munthu. Muloleni afotokoze za kukhosi kwake momasuka. Akakamba mfundo yosemphana na Baibo, dzigwileni musamukonze. (Yak. 1:19) Mukadekha na kumvetsela, mudzakhala na cithunzi cabwino ca zimene amakhulupilila na zifukwa zake.—Miy. 20:5.

5. Pezani zimene mungagwilizanepo ndipo muyamikileni. Munthuyo angakhale akukhulupilila na mtima wonse kuti ziphunzitso za cipembedzo cake ni zoona. Conco, yambilani pa mfundo imene nonse aŵili mukuivomeleza. Pang’ono-m’pang’ono, muthandizeni kumvetsa bwino zimene Baibo imaphunzitsa.

ONANINSO MALEMBA AWA

Miy. 25:15; 2 Tim. 2:23-26; 1 Pet. 3:15

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani