KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBO
N’ciani cingathandize kuti banja likhale lacimwemwe?
Malangizo a m’Baibo amathandiza kuti banja likhale lacimwemwe cifukwa cakuti ndi ocokela kwa Yehova Mulungu amene anayambitsa banja. Baibo imatiphunzitsa makhalidwe abwino amene amathandiza kuti banja likhale lacimwemwe. Ndiponso imaticenjeza kuti tipewe makhalidwe amene angaononge cikwati. Imatiphunzitsanso kalankhulidwe kabwino kamene kamapangitsa banja kukhala lacimwemwe.—Ŵelengani Akolose 3:8-10, 12-14.
Mwamuna ndi mkazi ayenela kulemekezana. Ngati io acita mbali yao imene Mulungu anawapatsa, angakhale acimwemwe.—Ŵelengani Akolose 3:18, 19.
N’ciani cimapangitsa banja kukhala lolimba?
Mwamuna ndi mkazi angakhale limodzi kwa nthawi yaitali ngati amakondana. Mulungu amatiphunzitsa kuti tizikondana. Iye ndi Mwana wake Yesu, anapeleka citsanzo cabwino kwambili ca mmene tingakhalile ndi cikondi codzimana.—Ŵelengani 1 Yohane 4:7, 8, 19.
Ngati mwamuna ndi mkazi amalemekeza cikwati monga makonzedwe a Mulungu, io amakhala ndi banja lolimba. Mulungu analinganiza kuti cikwati cikhale m’gwilizano wokhalitsa pakati pa mwamuna ndi mkazi ndi colinga cakuti mabanja akhale otetezeka. N’zotheka cikwati kukhalitsa cifukwa cakuti Mulungu analenga mwamuna ndi mkazi m’njila yakuti azigwilizana. Iye anawalenganso m’cifanizilo cake, conco angathe kusonyezana cikondi.—Ŵelengani Genesis 1:27; 2:18, 24.
Kuti mudziŵe zambili onani nkhani 14 m’buku ili, Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova
Mungatenge buku limeneli pa www.jw.org
[Cithunzi papeji 32]
Kodi ndi kalankhulidwe kotani kamene kamapangitsa kuti banja likhale lacimwemwe?