Kondwelani Ndi Zikumbutso za Yehova
“Ndatenga zikumbutso zanu kukhala cuma canga mpaka kale-kale.”—SAL. 119:111.
KODI MUNGAYANKHE BWANJI?
N’cifukwa ciani tiyenela kukondwela ndi zikumbutso za Yehova?
Kodi tingakulitse bwanji cidalilo cathu pa Yehova?
N’cifukwa ciani tifunika kucita zinthu za Ufumu mwakhama nthawi zonse?
1. (a) Kodi zimene anthu amacita akapatsidwa malangizo zimasiyana-siyana bwanji? (b) Kodi kunyada kungakhudze bwanji mmene munthu amaonela uphungu?
ZIMENE anthu amacita akapatsidwa malangizo zimasiyana-siyana. Ena amatsatila malangizo amene apatsidwa ndi munthu amene ali ndi udindo, koma amakana kutsatila malangizo ocokela kwa anzao kapena kwa munthu wina wamng’ono. Anthu ena amakhumudwa kapena kucita manyazi akapatsidwa uphungu koma ena amalimbikitsidwa ndipo amayesa-yesa kutsatila zimene auzidwa. N’cifukwa ciani anthu amasiyana conco? Cifukwa cimodzi n’cakuti anthu ena ndi onyada. Munthu wonyada akapatsidwa uphungu amaona ngati ndi wopanda phindu ndipo amaukana.—Miy. 16:18.
2. N’cifukwa ciani Akristu oona amayamikila malangizo ocokela m’Mau a Mulungu?
2 Koma Akristu oona amayamikila akapatsidwa uphungu wothandiza maka-maka umene ndi wocokela m’Mau a Mulungu. Zikumbutso za Yehova zimatipatsa nzelu imene imatithandiza kupewa misampha monga kukonda cuma, ciwelewele, kumwa mwaucidakwa kapena kugwilitsila nchito mankhwala oledzeletsa. (Miy. 20:1; 2 Akor. 7:1; 1 Ates. 4:3-5; 1 Tim. 6:6-11) Komanso timasangalala “cifukwa cokhala ndi cimwemwe mumtima” cimene cimabwela cifukwa comvela zikumbutso za Mulungu.—Yes. 65:14.
3. Ndi maganizo a wamasalimo ati amene tiyenela kukhala nao?
3 Kuti tikhalebe pa ubwenzi wamtengo wapatali ndi Atate wathu wakumwamba, tiyenela kupitiliza kutsatila malangizo anzelu a Yehova paumoyo wathu. Tiyenela kukhala ndi maganizo ngati a wamasalimo amene analemba kuti: “Ndatenga zikumbutso zanu kukhala cuma canga mpaka kale-kale, pakuti zimakondweletsa mtima wanga.” (Sal. 119:111) Kodi nafenso timasangalala ndi malamulo a Yehova kapena nthawi zina timawaona kuti ndi olemetsa? Ngakhale kuti nthawi zina tingakhumudwe tikapatsidwa uphungu, sitiyenela kutaya mtima. Tingalimbitse cidalilo cathu mwa Mulungu ndi malangizo ake anzelu. Tiyeni tione njila zitatu za mmene tingacitile zimenezo.
MUZIPEMPHELA KUTI MULIMBITSE CIDALILO CANU MWA YEHOVA
4. Kodi Davide sanaleke kucita ciani paumoyo wake?
4 Ngakhale kuti zinthu paumoyo wa Mfumu Davide zinali kusintha-sintha, iye sanaleke kudalila Mlengi wake ndi mtima wonse. Iye anati: “Ndapeleka moyo wanga kwa inu Yehova. Inu Mulungu wanga, cikhulupililo canga cili mwa inu.” (Sal. 25:1, 2) Kodi n’ciani cinathandiza Davide kukhala ndi cikhulupililo cotelo mwa Atate wake wakumwamba?
5, 6. Kodi Mau a Mulungu amatiuzanji ponena za ubwenzi umene Davide anali nao ndi Yehova?
5 Anthu ambili amapemphela kwa Mulungu kokha pamene akuvutika. Kodi mungamve bwanji ngati bwenzi lanu kapena m’bale wanu amakamba ndi inu kokha ngati afuna ndalama kapena thandizo lina lake? Mosakaikila, m’kupita kwa nthawi mungayambe kumukaikila munthuyo. Koma Davide sanali conco. Ubwenzi wake ndi Yehova unaonetsa kuti anali kukhulupilila Mulungu ndi kumukonda paumoyo wake wonse, kaya pamavuto kapena pamtendele.—Sal. 40:8.
6 Ganizilani mau a Davide awa otamanda ndi kuyamikila Yehova: “Inu Yehova Ambuye wathu, dzina lanu ndi lalikulu padziko lonse lapansi, inuyo ulemelelo wanu ukusimbidwa kumwamba-mwamba!” (Sal. 8:1) Kodi mwaona ubwenzi wolimba umene Davide anali nao ndi Atate wake wakumwamba? Cifukwa coyamikila ulemelelo wa Mulungu, Davide anatamanda Yehova “tsiku lonse.”—Sal. 35:28.
7. Kodi timapindula bwanji ngati tiyandikila Mulungu m’pemphelo?
7 Mofanana ndi Davide, tiyenela kulankhula ndi Yehova nthawi zonse kuti tilimbitse cidalilo cathu mwa iye. Baibo imati: “Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.” (Yak. 4:8) Kuyandikila Mulungu m’pemphelo ndi kofunikanso kuti tilandile mzimu woyela.—Ŵelengani1 Yohane 3:22.
8. N’cifukwa ciani tiyenela kupewa kukamba mau amodzi-modzi popemphela?
8 Kodi mumakonda kukamba mau amodzi-modzi popemphela? Ngati ndi conco, muyenela kuganizila zinthu zimene mufuna kukamba musanayambe kupemphela. Kodi bwenzi lanu lingamve bwanji ngati mumakamba mau amodzi-modzi polankhula nalo? Iye angaleke kukumvetselani. N’zoona kuti Yehova sangalephele kumvetsela pemphelo locokela pansi pa mtima la mtumiki wake wokhulupilika. Koma sitiyenela kukamba zinthu mwamwambo cabe pamene tikupemphela.
9, 10. (a) Kodi tingachule ciani m’mapemphelo athu? (b) N’ciani cingatithandize kupeleka mapemphelo ocokela pansi pa mtima?
9 Kuti tiyandikile Mulungu, mapemphelo athu ayenela kukhala ocokela pansi pa mtima. Ngati tifotokozela Yehova zakukhosi kwathu, timayamba kumuyandikila ndi kumudalila kwambili. Kodi tiyenela kuchula ciani m’mapemphelo athu? Mau a Mulungu amayankha kuti: “Pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” (Afil. 4:6) Tiyenela kupemphelela ciliconse cimene cimakhudza ubwenzi wathu ndi Mulungu kapena umoyo wathu monga atumiki ake.
10 Timaphunzila zambili tikamaganizila mau amene amuna ndi akazi okhulupilika anachula m’mapemphelo ao olembedwa m’Baibo.(1 Sam. 1:10, 11; Mac. 4:24-31) M’buku la Masalimo muli mapemphelo ndi nyimbo zoimbila Yehova zimene zimaonetsa mmene munthu amamvela akamavutika kapena akasangalala. Kupenda mosamalitsa mau a anthu okhulupilika amenewo kungatithandize kuti tizipeleka mapemphelo atanthauzo kwa Yehova.
MUZISINKHA-SINKHA ZIKUMBUTSO ZA MULUNGU
11. N’cifukwa ciani tifunikila kusinkha-sinkha malangizo a Mulungu?
11 Davide anati: “Zikumbutso za Yehova ndi zodalilika, zimapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu.” (Sal. 19:7) Ngakhale kuti sitidziŵa zinthu zambili, tingakhale anzelu ngati timvela malamulo a Mulungu. Kusinkha-sinkha malangizo a m’Malemba kungatithandize kuti tipindule kwambili. Kucita zimenezi kungatithandize kuti tisagonje ngati anzathu atikakamiza kucita zinthu zoipa kusukulu kapena kunchito. Kungatithandizenso kuti tizitsatila mfundo za Mulungu zokhudza kugwilitsila nchito magazi moyenela, kusatenga mbali m’zandale ndi pankhani ya kavalidwe ndi kudzikonza moyenela. Kudziŵa maganizo a Mulungu pa nkhani zimenezi kungatithandize kudziŵa zimene tingacite pa zinthu ngati zimenezo. Kukonzekela zinthu mwa njila imeneyi kungatithandize kuti tipewe mavuto.—Miy. 15:28.
12. Kodi ndi kusinkha-sinkha nkhani ziti kumene kungatithandize kutsatila zikumbutso za Mulungu?
12 Pamene tiyembekezela kukwanilitsidwa kwa malonjezo a Mulungu, kodi umoyo wathu umaonetsa kuti tili maso mwa kuuzimu? Mwacitsanzo, kodi mumakhulupilila kuti Babulo Wamkulu watsala pang’ono kuonongedwa? Kodi mumaona kuti madalitso a mtsogolo monga lonjezo la moyo wosatha m’paladaiso padziko lapansi, ndi eni-eni monga mmene munali kuwaonela mutangophunzila zimenezi? Kodi timaika zofuna zathu patsogolo m’malo mocita khama pa nchito yolalikila? Nanga bwanji ponena za ciyembekezo ca ciukililo, kuyeletsedwa kwa dzina la Yehova ndi kuti iye ndi woyenela kulamulila? Kodi mukali kuona kuti nkhani zimenezi ndi zofunika? Kusinkha-sinkha nkhani zimenezi kungatithandize kutsatila ‘zikumbutso zake kuti zikhale cuma cathu mpaka kale-kale’ monga mmene wamasalimo anacitila.—Sal. 119:111.
13. N’cifukwa ciani Akristu a m’nthawi ya atumwi anavutika kumvetsetsa zinthu zina? Pelekani citsanzo.
13 Zinthu zina zimene Baibo imanena zingakhale zovuta kumvetsa cifukwa cakuti nthawi yakuti Yehova azimveketse bwino sinakwane. Kaŵili-kaŵili Yesu anali kuuza atumwi ake kuti iye anafunikila kuvutika ndi kuphedwa. (Ŵelengani Mateyu 12:40; 16:21) Koma io sanamvetsetse zimene iye anali kunena. Atumwiwo anamvetsetsa zimenezi pambuyo pakuti Yesu waukitsidwa ndi kuonekela kwa ena mwa io, ndi ‘kutsegula maganizo ao kuti amvetse tanthauzo la Malemba.” (Luka 24:44-46; Mac. 1:3) Mofananamo, otsatila a Kristu atalandila mzimu woyela pa Pentekosite mu 33 C.E m’pamene anamvetsetsa mfundo yakuti Ufumu wa Mulungu udzakhazikitsidwa kumwamba.—Mac. 1:6-8.
14. Ndi citsanzo cabwino citi cimene abale ambili anaonetsa kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900, ngakhale kuti anali ndi maganizo olakwika okhudza masiku otsiliza?
14 Mofanana ndi zimenezi, kuciyambi kwa zaka za m’ma 1900, Akristu oona anali ndi maganizo olakwika okhudza “masiku otsiliza.” (2 Tim. 3:1) Mwacitsanzo, m’caka ca 1914, Akristu ena anali kuganiza kuti atsala pang’ono kutengedwa kupita kumwamba. Pamene anaona kuti zimene anali kuyembekezela sizinacitike, io anapendanso Malemba mwakhama ndipo anadziŵa kuti panali nchito yaikulu yolalikila imene inali kufunika kucitika. (Maliko 13:10) Conco, m’caka ca 1922, Mbale J.F. Rutherford, amene anali kutsogolela pa nchito yolalikila, anauza anthu amene anasonkhana pa msonkhano wa maiko ku Cedar Point, Ohio, U.S.A. kuti: “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulila ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza za ufumuwo. Conco lengezani, lengezani, lengezani za Mfumu ndi ufumu wake.” Kuyambila nthawi imeneyo, kulalikila “uthenga wabwino wa ufumu” cakhala cizindikilo cacikulu ca atumiki a Yehova masiku ano.—Mat. 4:23; 24:14.
15. Kodi timapindula bwanji ngati tisinkha-sinkha zimene Mulungu amacitila anthu ake?
15 Ngati tisinkha-sinkha zinthu zabwino zimene Yehova anacitila anthu ake kale ndi zimene akuticitila masiku ano, timamudalila kwambili kuti adzakwanilitsa cifunilo cake mtsogolo. Ndiponso zikumbutso za Mulungu zimatithandiza kuti tizikumbukila nthawi zonse maulosi ake amene adzakwanilitsidwa mtsogolo. Kucita zimenezi kudzatithandiza kuti tizikhulupilila malonjezo ake.
LIMBITSANI CIDALILO CANU PA MULUNGU MWA KUCITA ZINTHU ZA KUUZIMU
16. Ndi madalitso otani amene tingapeze ngati ticita khama mu utumiki wathu?
16 Mulungu wathu, Yehova ndi Mulungu wamphamvu ndipo amagwila nchito nthawi zonse. Wamasalimo anati: “Ndani ali ndi mphamvu ngati inu Ya?” Kenako iye anaonjezela kuti: “Dzanja lanu lamanja ndi lokwezeka.” (Sal. 89:8, 13) Yehova amayamikila ndi kudalitsa atumiki ake amene amacita khama kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Iye amafuna kuti atumiki ake onse kaya ndi amuna kapena akazi, ana kapena okalamba azigwila nchito kuti asadye “cakudya ca ulesi.” (Miy. 31:27) Mofanana ndi Mlengi wathu, tiyenela kutangwanika ndi zinthu zokhudza kulambila. Kutumikila Mulungu ndi mtima wonse kumatipindulitsa ndipo Yehova amadalitsa utumiki wathu.—Ŵelengani Salimo 62:12.
17, 18. N’cifukwa ciani tinganene kuti kucita zinthu mokhulupilika kumalimbitsa cidalilo cathu pa Yehova? Pelekani citsanzo.
17 Kodi timalimbitsa bwanji cidalilo cathu pa Yehova pamene ticita zinthu mokhulupilika? Ganizilani nkhani ya m’Malemba yonena za mmene Aisiraeli analoŵela m’Dziko Lolonjezedwa. Yehova analamula ansembe kuti anyamule likasa la cipangano ndi kupita ku Mtsinje wa Yorodano. Koma anthuwo atayandikila mtsinjewo, anapeza kuti ndi wosefukila. Kodi Aisiraeli anacita ciani? Kodi io anamanga msasa m’mphepete mwa mtsinjewo ndi kuyembekezela kwa milungu kapena kuposelapo kuti madziwo acepe? Ai, io anakhulupilila Yehova ndi kutsatila malangizo ake. Kodi zotsatila zake zinali zotani? Baibo imanena kuti pamene mapazi a ansembe ‘anaponda madzi a m’mphepete mwa mtsinjewo . . . madzi otsika kucokela kumtunda anayamba kuima.’ Imanenanso kuti io “anangoima cilili panthaka youma pakati pa mtsinje wa Yorodano. Anaimabe conco pamene Aisiraeli onse anali kuwoloka panthaka youmayo.” (Yos. 3:12-17) Aisiraeli ayenela kuti analimbikitsidwa pamene anaona kuti madzi othamanga amenewo aima. Kunena zoona, cikhulupililo cao pa Yehova cinalimba cifukwa cakuti anadalila malangizo ake.
18 N’zoona kuti Yehova sacitila anthu ake zinthu zozizwitsa masiku ano, koma iye amawadalitsa ngati acita zinthu mokhulupilika. Mzimu woyela wa Mulungu umawapatsa mphamvu kuti akwanitse kugwila nchito yao yolalikila uthenga wa Ufumu padziko lonse. Ndiponso Mboni yaikulu ya Yehova, Yesu Kristu, ataukitsidwa anatsimikizila otsatila ake kuti adzawathandiza pa nchito yofunika imeneyi. Iye anati: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga . . . ine ndili pamodzi ndi inu masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:19, 20) Abale ndi alongo amene anali ndi manyazi kapena mantha aona kuti mzimu woyela wa Mulungu wawathandiza kulankhula molimba mtima kwa anthu acilendo mu utumiki.—Ŵelengani Salimo 119:46; 2 Akorinto 4:7.
19. Kodi tiyenela kukhala ndi cidalilo cotani ngati timalephela kucita zambili pa utumiki wathu?
19 Abale ndi alongo ena amalephela kucita zambili cifukwa ca matenda kapena ukalamba. Koma amakhala ndi cidalilo cakuti “Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse,” amamvetsa mavuto a Mkristu woona aliyense. (2 Akor. 1:3) Iye amayamikila zilizonse zimene timacita pofuna kupititsa patsogolo zinthu za Ufumu. Aliyense wa ife ayenela kukumbukila kuti tidzapulumuka maka-maka kaamba ka kukhulupilila nsembe ya dipo ya Kristu, ndi kuyesetsa kucita zonse zimene tingakwanitse pa utumiki wathu.—Aheb. 10:39.
20, 21. Ndi njila zina ziti zimene timaonetsela kuti timadalila Yehova?
20 Tiyenela kugwilitsila nchito nthawi yathu, mphamvu zathu ndi cuma cathu mmene tingathele kuti ticilikize kulambila kwathu. Timafunitsitsa ‘kugwila nchito ya mlaliki’. (2 Tim. 4:5) Timasangalala kugwila nchito imeneyi cifukwa cakuti imathandiza ena “kukhala odziŵa coonadi molondola.” (1 Tim. 2:4) Kunena zoona, kulemekeza ndi kutamanda Yehova kumatilemeletsa. (Miy. 10:22) Kumapangitsanso kuti tikhale pa ubwenzi wolimba ndi Mlengi wathu ndipo timamudalila kwambili.—Aroma 8:35-39.
21 Monga mmene taonela, tifunika kucitapo kanthu kuti tikhale ndi cidalilo cakuti Yehova adzatipatsa malangizo anzelu. Conco, yesetsani kudalila Yehova mwa kupemphela. Sinkha-sinkhani mmene Yehova anakwanilitsila cifunilo cake m’mbuyomu ndi mmene adzakwanilitsila colinga cake mtsogolo. Ndipo pitilizani kukulitsa cidalilo canu pa Yehova mwa kucita zinthu zokhudza kulambila. Inde, zikumbutso za Yehova zidzakhalako kosatha ndipo inunso mungathe kukhala ndi moyo wosatha.
[Cithunzi papeji 15]
Kodi mudzaonetsa kuti mumadalila Yehova monga mmene anthu ake anacitila m’nthawi ya Yoswa? (Onani ndime 17 ndi 18)