LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 9/1 masa. 7-11
  • Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalilika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalilika
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MVELANI MULUNGU KUTI MUKHALE NDI MOYO
  • ZIKUMBUTSO ZA MULUNGU ZINATHANDIZA AKHRISTU OYAMBILILA KUKHALABE OKHULUPILIKA
  • PITILIZANI KUDALILA YEHOVA
  • Kondwelani Ndi Zikumbutso za Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Zikumbutso za Msonkhano Wacigawo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 9/1 masa. 7-11

Zikumbutso za Yehova Ndi Zodalilika

“Zikumbutso za Yehova ndi zodalilika, zimapatsa nzelu munthu wosadziŵa zinthu.”—SAL. 19:7.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Ndi zikumbutso zotani zimene Yehova amapeleka kupyolela m’Malemba?

Kodi zikumbutso za Yehova zingawathandize bwanji Akristu masiku ano?

Kodi tiyenela kudalila zikumbutso za Yehova pa zifukwa ziti?

1. Ndi nkhani ziti zimene anthu a Mulungu amaphunzila kaŵili-kaŵili? Nanga timapindula bwanji tikamaphunzila nkhani zimenezi?

POKONZEKELA phunzilo la Nsanja ya Mlonda, kodi munadzifunsako kuti, ‘Kodi nkhani iyi sitinaiphunzileko m’mbuyomu?’ Ngati mwakhala mumpingo wacikristu kwa nthawi yaitali, mosakaikila mwaona kuti nkhani zina zimaphunzilidwa mobweleza-bweleza. Zina mwa nkhani zimenezi ndi zokhudza Ufumu wa Mulungu, dipo, nchito yopanga ophunzila, ndiponso zokhudza makhalidwe ena monga cikondi ndi cikhulupililo. Kaŵili-kaŵili, izi zakhala mbali ya cakudya cathu ca kuuzimu. Tikamaphunzila nkhani zimenezi mobweleza-bweleza, cikhulupililo cathu cimalimba ndipo ‘timacita zimene mau amanena, osati kumva cabe.’—Yak. 1:22.

2. (a) Kodi kaŵili-kaŵili zikumbutso za Mulungu zimatanthauza ciani? (b) Kodi zikumbutso za Mulungu zimasiyana bwanji ndi malamulo a anthu?

2 Liu la Ciheberi limene linatembenuzidwa kuti “zikumbutso,” kaŵili-kaŵili limatanthauza malamulo kapena malangizo amene Mulungu amapatsa anthu ake. Mosiyana ndi malamulo a anthu amene kaŵili-kaŵili amafunika kusinthidwa, malamulo ndi malangizo a Yehova ndi odalilika nthawi zonse. Ngakhale kuti malamulo ndi malangizo ena a Mulungu amagwila nchito pa nthawi kapena pa zocitika zinazake, iwo samatha nchito. Wamasalimo anati: “Zikumbutso zanu zidzakhalabe zolungama mpaka kale-kale.”—Sal. 119:144.

3, 4. (a) Kodi zikumbutso za Yehova zingaphatikizepo ciani? (b) Kodi Aisiraeli akanapindula bwanji akanamvela zikumbutso za Mulungu?

3 Mwina inuyo mwaona kuti nthawi zina zikumbutso za Yehova zimaphatikizapo macenjezo. Nthawi zambili Mulungu anali kucenjeza mtundu wa Aisiraeli kupyolela mwa aneneli ake. Mwacitsanzo, Aisiraeli atatsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawacenjeza kuti: “Samalani kuti mitima yanu isakopeke ndipo musapatuke ndi kupembedza milungu ina n’kumaiwelamila. Mukatelo mkwiyo wa Yehova udzakuyakilani.” (Deut. 11:16, 17) Baibo imatiuza kuti Mulungu anapatsa anthu ake zikumbutso zambili zothandiza.

4 Nthawi zambili, Yehova anauza Aisiraeli kuti azimuopa, azimumvela ndi kuti ayeletse dzina lake. (Deut. 4:29-31; 5:28, 29) Iwo akanamvela zikumbutso zimenezi, akanalandila madalitso ambili.—Lev. 26:3-6; Deut. 28:1-4.

5. N’cifukwa ciani Yehova anamenyela nkhondo Mfumu Hezekiya?

5 Pa nthawi yonse imene Aisiraeli sanamvele Mulungu, iye anasungabe malonjezo ake. Mwacitsanzo, pamene Senakeribu Mfumu ya Asuri, inaukila mzinda wa Yuda ndi kuopseza kuti idzacotsa Mfumu Hezekiya pa ulamulilo, Yehova anacitapo kanthu mwa kutumiza mngelo. Usiku umodzi cabe, mngelo wa Mulungu anapha “mwamuna aliyense wamphamvu ndi wolimba mtima,” amene anali m’gulu la asilikali a Asuri. Conco Senakeribu anabwelela kwao ali ndi manyazi. (2 Mbiri 32:21; 2 Maf. 19:35) Kodi n’cifukwa ciani Mulungu anamenyela nkhondo Mfumu Hezekiya? Cifukwa cakuti “anapitiliza kumamatila Yehova. Sanasiye kum’tsatila, koma anapitiliza kusunga malamulo” ake.—2 Maf. 18:1, 5, 6.

6. Kodi Mfumu Yosiya inaonetsa bwanji kuti inadalila Yehova?

6 Munthu wina amene anamvela malamulo a Yehova ndi Mfumu Yosiya. Iye akali mwana wamng’ono wa zaka 8 zokha, “anacita zoyenela pamaso pa Yehova . . . Sanapatukile mbali ya kudzanja lamanja kapena lamanzele.” (2 Mbiri 34:1, 2) Yosiya anaonetsa kuti anadalila Yehova pamene anayeletsa dziko la Isiraeli mwa kucotsa mafano ndi kubwezeletsa kulambila koona. Mwa kucita zimenezi, Yosiya analandila madalitso pamodzi ndi mtundu wonse wa Isiraeli.—Ŵelengani 2 Mbiri 34:31-33.

7. Kodi Aisiraeli anali kukumana ndi zotsatilapo zotani ngati sanamvele zikumbutso za Yehova?

7 Koma n’zomvetsa cisoni kuti nthawi zina anthu a Mulungu sanali kudalila zikumbutso za Yehova. Kwa zaka zambili, iwo anali kucita zinthu ndi mtima wogaŵanika. Kaŵili-kaŵili cikhulupililo cao cikafooka anali ‘kutengeka kupita uku ndi uku ndi mphepo iliyonse ya ciphunzitso’ monga mmene mtumwi Paulo anakambila. (Ephesians 4:13, 14) Monga mmene Mulungu anakambila, nthawi zonse iwo akanyalanyaza zikumbutso zake, anali kukumana ndi mavuto aakulu.—Lev. 26:23-25; Yer. 5:23-25.

8. Kodi tingaphunzile ciani pa citsanzo ca Aisiraeli?

8 Kodi tingapindule bwanji ndi citsanzo ca Aisiraeli? Mofanana ndi Aisiraeli, atumiki a Mulungu masiku ano amalandila uphungu ndi malangizo. (2 Pet. 1:12) Mau ouzilidwa a Mulungu amakhala zikumbutso kwa ife nthawi zonse pamene timawaŵelenga. Popeza kuti tili ndi ufulu wodzisankhila zocita, tingasankhe kumvela malangizo a Yehova kapena kucita zimene tiona kuti n’zabwino. (Miy. 14:12) Tiyeni tikambilane zifukwa zimene zingatipangitse kudalila zikumbutso za Yehova ndi mmene tingapindulile ngati tizigwilitsila nchito.

MVELANI MULUNGU KUTI MUKHALE NDI MOYO

9. Pamene Aisiraeli anali m’cipululu, kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti anali kuwasamalila?

9 Pamene Aisiraeli anayamba ulendo wa ‘m’cipululu cocititsa mantha’ umene unawatengela zaka 40, Yehova sanawauze zonse zokhudza mmene anali kudzawatsogolela, kuwateteza, ndi kuwasamalila. Komabe Mulungu nthawi zambili anaonetsa kuti ndi wodalilika mwakuti Aisiraeli anali ndi zifukwa zokwanila zomukhulupilila ndi kudalila malangizo ake. Mwa kugwilitsila nchito mtambo masana ndi moto usiku, Yehova anakumbutsa Aisiraeli kuti iye anali nao limodzi paulendo wao wodutsa m’dela loopsa limenelo. (Deut. 1:19; Eks. 40:36-38) Iye anali kuwasamalila mwakuthupi. “Zovala zao sizinathe ndipo mapazi ao sanatupe.” Inde “io sanasoŵe kanthu.”—Neh. 9:19-21.

10. Kodi Yehova amatsogolela bwanji anthu ake masiku ano?

10 Atumiki a Mulungu atsala pang’ono kuloŵa m’dziko latsopano lolungama. Kodi timakhulupilila kuti Yehova adzatipatsa zinthu zimene timafunikila kuti tikapulumuke pa “cisautso cacikulu” cimene cikubwela? (Mat. 24:21, 22; Sal. 119:40, 41) N’zoona kuti Yehova satitsogolela ndi mtambo kapena moto kuti tikaloŵe m’dziko latsopano. Koma amagwilitsila nchito gulu lake kuti atithandize kukhala maso. Mwacitsanzo, iye wakhala akutilimbikitsa kuti tiziŵelenga Baibo, tizicita Kulambila kwa Pabanja, ndi kupezeka pa misonkhano ndi muulaliki nthawi zonse kuti tikhale olimba kuuzimu. Kodi tasintha zinthu zina paumoyo wathu kuti titsatile malangizo amenewa? Kucita zimenezi n’kofunika kuti tikhale ndi cikhulupililo cimene cidzatithandiza kuloŵa m’dziko latsopano.

11. Kodi Mulungu amaonetsa kuti amatikonda m’njila ziti?

11 Kuonjezela pa kutithandiza kuti tikhale maso mwa kuuzimu, malangizo amene Mulungu amatipatsa amatithandiza paumoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Mwacitsanzo, malangizo amenewa amatithandiza kuona zinthu zakuthupi moyenela ndi kukhala ndi diso la kumodzi kuti tisakhale ndi nkhawa kwambili. Timapindulanso ndi malangizo okhudza kavalidwe ndi kudzikonza, kusankha zosangulutsa, ndi kusamala ndi maphunzilo apamwamba. Ganizilaninso za malangizo okhudza mmene tingapewele ngozi panyumba, pamseu, pa Nyumba ya Ufumu ndi mmene tingakonzekelele zinthu zakugwa mwadzidzidzi. Malangizo amenewa amaonetsa kuti Mulungu amafuna kuti tikhale ndi umoyo wabwino.

ZIKUMBUTSO ZA MULUNGU ZINATHANDIZA AKHRISTU OYAMBILILA KUKHALABE OKHULUPILIKA

12. (a) N’ciani cimene Yesu anali kuuza ophunzila ake mobweleza-bweleza? (b)  Ndi citsanzo citi ca kudzicepetsa cimene Petulo sanaiwale? Nanga citsanzo cimeneci ciyenela kutikhudza bwanji?

12 M’nthawi ya atumwi, anthu a Mulungu anali kulandila zikumbutso mobweleza-bweleza. Nthawi zambili, Yesu anauza ophunzila ake kuti akhale odzicepetsa. Iye sanangoŵauza tanthauzo la kudzicepetsa koma anaŵaonetsanso mmene akanakhalila odzicepetsa. Tsiku lomaliza la moyo wake padziko, Yesu anasonkhanitsa atumwi kuti acite Pasika. Pamene atumwi ake anali kudya, Yesu anaimilila ndi kusambitsa mapazi ao. Kawili-kawili nchito imeneyi anali kucita ndi akapolo. (Yoh. 13:1-17) Limeneli linali phunzilo losaiwalika kwa ophunzila ake. Zaka 30 izi zitacitika, mtumwi Petulo amene analipo pacakudya analangiza okhulupilila anzake kuti akhale odzicepetsa. (1 Pet. 5:5) Citsanzo ca Yesu ciyenela kutilimbikitsa kuti tizikhala odzicepetsa pocita zinthu ndi ena.—Afil. 2:5-8.

13. Ndi khalidwe lofunika liti limene Yesu analimbikitsa ophunzila ake kukhala nalo?

13 Nthawi zambili, Yesu anali kuuzanso ophunzila ake kuti anafunikila kukhala ndi cikhulupililo colimba. Pambuyo pakuti ophunzila ake alephela kutulutsa ciŵanda mwa mnyamata wina, iwo anafunsa Yesu kuti: “N’cifukwa ciani ife tinalephela kutulutsa ciŵanda cija?” Yesu anawayankha kuti: “Cifukwa ca kucepa kwa cikhulupililo canu. Pakuti ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi cikhulupililo cofanana ndi kanjele ka mpilu, . . . palibe cimene cidzakhala cosatheka kwa inu.” (Mat. 17:14-20) Mu utumiki wake wonse, Yesu anali kuuza ophunzila ake kuti cikhulupililo ndi cofunika. (Ŵelengani Mateyu 21:18-22.) Kodi timatengela mwai malangizo amene timalandila ndi mayanjano olimbikitsa amene timakhala nao pa misonkhano yacigawo, yadela, ndi yampingo kuti tilimbitse cikhulupililo cathu? Misonkhano imeneyi siimakhala cabe yosangalatsa, koma imatipatsanso mwai kuti tionetse kuti timadalila Yehova.

14. N’cifukwa ciani tifunika kukulitsa cikondi cacikristu masiku ano?

14 Malemba Acigiriki Acikristu ali ndi zikumbutso zambili zotilimbikitsa kuti tizikondana. Yesu anakamba kuti lamulo laciŵili lalikulu ndi lakuti “uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha.” (Mat. 22:39) Yakobo m’bale wa Yesu anakambanso kuti cikondi ndi “lamulo lacifumu.” (Yak. 2:8) Mtumwi Yohane analemba kuti: “Okondedwa, sindikukulembelani lamulo latsopano, koma lamulo lakale limene mwakhala nalo kuyambila pa ciyambi.” (1 Yoh. 2:7, 8) Kodi Yohane anatanthauza ciani pamene anakamba kuti “lamulo lakale”? Anali kutanthauza za lamulo la kukonda anzathu. Lamulo limeneli linali “lakale” m’lingalilo lakuti Yesu analipeleka “kuyambila pa ciyambi,” kutanthauza zaka makumi angapo m’mbuyomo. Koma linalinso “latsopano” cifukwa cakuti ophunzilawo anafunika kuonetsa cikondi codzimana pa nthawi zovuta. Pokhala ophunzila a Kristu, kodi sitimayamikila macenjezo amene amatiteteza kuti tisakhale ndi mzimu wodzikonda wofala m’dzikoli, umene ungacititse kuti cikondi cathu pa abale cicepe?

15. Ndi nchito yaikulu iti imene Yesu anacita padziko lapansi?

15 Yesu anaonetsa kuti anali kukonda anthu. Anaonetsa zimenezi pamene anacilitsa odwala, olemala, ndi kuukitsa akufa. Koma nchito yake yaikulu siinali kucilitsa anthu. Nchito yake yolalikila ndi kuphunzitsa inathandiza anthu kwambili kuposa nchito yocilitsa. Motani? Tidziŵa kuti anthu amene Yesu anacilitsa ndi kuukitsa m’nthawi ya atumwi anakalamba ndi kufa, koma aja amene analabadila uthenga umene analalikila ali ndi ciyembekezo ca moyo wosatha.—Yoh. 11:25, 26.

16. Kodi nchito yolalikila Ufumu ndi kupanga ophunzila yafika pati?

16 Nchito yolalikila imene Yesu anayamba m’nthawi ya atumwi ikucitika pa mlingo waukulu kwambili masiku ano. Yesu analamula ophunzila ake kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.” (Mat. 28:19) Ndithudi iwo anacita nchito imeneyi mokwanila ndipo ifenso tikucita cimodzi-modzi. Mboni za Yehova zoposa 7 miliyoni zimalalikila mwacangu za Ufumu wa Mulungu m’maiko oposa 230, ndipo amaphunzila Baibo ndi anthu mamiliyoni ambili. Nchito yolalikila imeneyi ikusonyeza kuti tili m’masiku otsiliza.

PITILIZANI KUDALILA YEHOVA

17. Ndi malangizo ati amene Paulo ndi Petulo anapeleka?

17 Kunena zoona, zikumbutso zinathandiza Akristu oyambilila kukhala ndi cikhulupililo colimba. Ganizilani mmene Timoteyo analimbikitsidwila pamene mtumwi Paulo amene anali kundende ku Roma anamuuza kuti: “Gwilitsitsabe citsanzo ca mau olondola amene unawamva kwa ine.” (2 Tim. 1:13) Pambuyo pakuti Mtumwi Petulo walimbikitsa Akristu kukulitsa makhalidwe monga kupilila, kukonda abale ndi kudziletsa anati: “Nthawi zonse ndizikukumbutsani zinthu zimenezi, ngakhale kuti mukuzidziŵa kale ndipo ndinu olimba m’coonadi.”—2 Pet. 1:5-8, 12.

18. Kodi Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kuziona bwanji zikumbutso za Mulungu?

18 Makalata amene Paulo ndi Petulo analemba ali ndi “mau amene aneneli oyela ananena kale.” (2 Pet. 3:2) Kodi abale athu a m’nthawi ya atumwi anakhumudwa ndi malangizo amenewa? Ayi, cifukwa anaona kuti Mulungu anawapatsa malangizo amenewa cifukwa cowakonda. Malangizo amenewa anawathandiza ‘kupitiliza kulandila kukoma mtima kwakukulu ndi kumudziŵa Ambuye ndi Mpulumutsi wathu Yesu Kristu.’—2 Pet. 3:18.

19, 20. N’cifukwa ciani tiyenela kudalila zikumbutso za Yehova? Ndipo tingapindule bwanji tikacita zimenezi?

19 Masiku ano, tili ndi zifukwa zambili zodalila zikumbutso za Yehova zopezeka m’Mau ake amene samatha mphamvu. (Ŵelengani Yoswa 23:14.) Tikamaŵelenga Baibo timamva mmene Mulungu wacitila ndi anthu opanda ungwilo kwa zaka masauzande ambili. Nkhani za m’Baibo zinalembedwa kuti zitithandize. (Aroma 15:4; 1 Akor. 10:11) Taona kukwanilitsidwa kwa maulosi a m’Baibo. Maulosi angayelekezedwe ndi zikumbutso zimene zinanenedwa kale zinthu zisanacitike. Mwacitsanzo, anthu mamiliyoni ambili abwela m’gulu la Yehova ndipo akumulambila m’njila yovomelezeka mogwilizana ndi mmene ulosi unanenela kuti zimenezi zidzacitika “m’masiku otsiliza.” (Yes. 2:2, 3) Zinthu zoipa zimene zikucitika masiku ano zikukwanilitsa ulosi wa m’Baibo. Ndipo monga mmene tanenela, kupita patsogolo kwa nchito ya padziko lonse yolalikila kukukwanilitsa mau a Yesu.—Mat. 24:14.

20 M’Baibo muli mbili yoonetsa mmene Mlengi wathu anacitila zinthu ndi anthu. Kodi timapindula ndi mbili imeneyi? Tiyenela kukhulupilila zikumbutso za Mulungu. Izi ndi zimene Rosellen anacita. Iye anati: “Pamene ndinayamba kukhulupilila kwambili Yehova, ndinayamba kuona kuti iye anali kundisamalila ndi kundilimbikitsa.” Nafenso tiyenela kusunga zikumbutso za Yehova kuti tipindule.

[Cithunzi papeji 8]

Zikumbutso za Yehova zinalimbikitsa Yosiya kuteteza kulambila koona (Onani ndime 6)

[Cithunzi papeji 10]

Kutsatila zikumbutso za Yehova kumatithandiza kuti tizisunga Nyumba ya Ufumu mumkhalidwe wabwino ndi mwaukhondo (Onani ndime 11)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani