LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 11/1 masa. 22-26
  • Muzimvela Abusa A Yehova

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Muzimvela Abusa A Yehova
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • M’BUSA WABWINO WATIPATSA ABUSA AANG’ONO
  • M’BUSA WABWINO AMADYETSA NDI KUTETEZA NKHOSA ZAKE
  • KODI ZOPHOPHONYA ZA ABUSA AANG’ONO TIYENELA KUZIONA BWANJI?
  • “GULU LIMODZI NDI M’BUSA MMODZI”
  • Abusa, Tsanzilani Abusa Aakulu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • “Inetu Ndidzafunafuna Nkhosa Zanga”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 11/1 masa. 22-26

Muzimvela Abusa A Yehova

“Muzimvela amene akutsogolela pakati panu ndipo muziwagonjela. Iwo amayang’anila miyoyo yanu.”—AHEB. 13:17.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

Kodi akulu mumpingo amaweta bwanji nkhosa za Mulungu?

N’cifukwa ciani nkhosa ziyenela kumvela abusa aang’ono?

N’cifukwa ciani zophophonya za abusa aang’ono si cifukwa conyalanyazila malangizo ao a m’Malemba?

1, 2. N’cifukwa ciani n’zocititsa cidwi kuti Yehova amadziyelekezela ndi m’busa?

YEHOVA amadziyelekezela yekha ndi m’busa. (Ezek. 34:11-14) Zimenezi ndi zocititsa cidwi cifukwa zimatithandiza kudziŵa mmene Yehova alili. M’busa wabwino amasamala nkhosa zake mwacikondi kuti zikule bwino. Amazitengela kumene kuli msipu wambili ndi madzi ambili, (Sal. 23:1, 2) amaziyang’anila usana ndi usiku, (Luka 2:8) amaziteteza ku zilombo zolusa, (1 Sam. 17:34, 35) amanyamula ana a nkhosa pacifuwa cake, (Yes. 40:11) ndipo amafuna-funa zosocela ndi kusamalila zimene zavulazidwa.—Ezek. 34:16.

2 Popeza kuti anthu a Yehova a m’nthawi zakale anali kukhala ku malo kumene anthu anali kukonda kusunga ziŵeto ndipo anali kukonda ulimi, io anali kumvetsa kufunika koona Yehova Mulungu monga m’busa wacikondi. Iwo anali kudziŵa kuti nkhosa zimafunikila kusamalidwa mwacikondi kuti zikule bwino. Mofananamo, anthu amafunikila cisamalilo ndi malangizo ocokela kwa Yehova. (Maliko 6:34) Popanda cisamalilo ndi citsogozo ca Yehova, anthu amavutika. Amakhala osatetezeka ndiponso amakhalidwe oipa. Iwo amakhala monga “nkhosa zopanda m’busa” zimene zabalalika. (1 Maf. 22:17) Komabe, Yehova mwacikondi amasamalila zosoŵa za anthu ake.

3. Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?

3 Ngakhale masiku ano, kuona Yehova monga m’busa n’kofunika kwambili. Iye amasamalabe anthu ake amene ali monga nkhosa. M’nkhani ino tikambilana mmene iye amatsogolela anthu ake ndi kuwasamalila. Tikambilananso zimene tiyenela kucita kuti tipindule ndi citsogozo ndiponso cisamalilo ca Yehova.

M’BUSA WABWINO WATIPATSA ABUSA AANG’ONO

4. Kodi Yesu ali ndi mbali yanji pankhani yosamalila nkhosa za Yehova?

4 Yehova waika Yesu kukhala Mutu wa mpingo wacikristu. (Aef. 1:22, 23) Mofanana ndi Atate wake, Yesu ndi “m’busa wabwino.” Yesu amakonda ndi kusamalila nkhosa ndipo ‘anataya moyo wake cifukwa ca nkhosazo.’ (Yoh. 10:11, 15) Nsembe ya dipo la Kristu ndi dalitso lalikulu kwa anthu onse. (Mat. 20:28) Cifunilo ca Yehova n’cakuti “aliyense wokhulupilila iye [Yesu] asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yoh. 3:16.

5, 6. (a) Kodi Yesu waika ndani kuti asamalile nkhosa zake? Nanga nkhosa ziyenela kucita ciani kuti zipindule ndi makonzedwe amenewa? (b) Kodi cifukwa cacikulu cimene tiyenela kumvela akulu mumpingo n’citi?

5 Kodi nkhosa zimasonyeza bwanji kuti zimaona Yesu Kristu kukhala M’busa wao Wabwino? Yesu anati: “Nkhosa zanga zimamva mau anga. Ine ndimazidziŵa, ndipo izo zimanditsatila.” (Yoh. 10:27) Kumvela mau a M’busa Wabwino kumatanthauza kutsatila citsogozo cake m’zinthu zonse. Zimenezo zimaphatikizapo kugwilizana ndi abusa aang’ono akuuzimu amene iye wawaika. Yesu anaonetsa kuti atumwi ake ndi ophunzila ake anayenela kupitiliza nchito imene iye anayamba. Iwo anafunikila ‘kuphunzitsa’ ndi ‘kudyetsa ana a nkhosa a Yesu.’ (Mat. 28:20; ŵelengani Yohane 21:15-17.) Pamene uthenga wabwino unafalikila, ciŵelengelo ca ophunzila cinaonjezeka ndipo Yesu anakonza zakuti Akristu okhwima mwakuuzimu awete anthu m’mipingo.—Aef. 4:11, 12.

6 Pamene mtumwi Paulo anali kukamba ndi oyang’anila a mumpingo wa m’nthawi ya atumwi ku Efeso, iye ananena kuti mzimu woyela ndi umene unawaika kuti akhale oyang’anila ‘kuti awete mpingo wa Mulungu.’ (Mac. 20:28) Oyang’anila acikristu masiku ano naonso amaikidwa pa udindo ndi mzimu m’njila yakuti amafunikila kukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba amene ndi ouzilidwa ndi mzimu woyela wa Mulungu. Conco, ngati timvela oyang’anila acikristu, timaonetsa kuti timalemekeza Yehova ndi Yesu amene ndi abusa aakulu kwambili. (Luka 10:16) Ndipo cimeneci ndi cifukwa cacikulu cimene tiyenela kukhalila ogonjela kwa akulu. Koma pali zifukwa zina zimene tiyenela kutsatilila malangizo a akulu.

7. Kodi akulu amakuthandizani bwanji kuti mukhalebe pa ubwenzi wabwino ndi Yehova?

7 Popeleka malangizo kwa Akristu anzao, akulu amapeleka cilimbikitso ndi malangizo ocokela m’Malemba kapena ozikidwa pa mfundo za m’Baibo. Pamene apeleka malangizo amenewa, colinga cao si kulamulila zocita za abale ao. (2 Akor. 1:24) Koma colinga cao ndi kupeleka malangizo a m’Malemba othandiza Akristu anzao kupanga zosankha zabwino ndiponso kuthandiza kuti zinthu zizicitika mwadongosolo ndi mwamtendele mumpingo. (1 Akor. 14:33, 40) Akulu “amayang’anila miyoyo” m’njila yakuti io amayesetsa kuthandiza munthu aliyense mumpingo kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. N’cifukwa cake amapeleka thandizo mwamsanga akazindikila kuti m’bale kapena mlongo afuna kuloŵela “njila yolakwika” kapena wayamba kale kutelo. (Agal. 6:1, 2; Yuda 22) Kodi izi si zifukwa zabwino zokhalila ‘omvela kwa amene akutsogolela’?—Ŵelengani Aheberi 13:17.

8. Kodi akulu amateteza bwanji nkhosa za Mulungu?

8 Mtumwi Paulo amenenso anali m’busa wakuuzimu, analembela abale a ku Kolose kuti: “Samalani: mwina wina angakugwileni ngati nyama, mwa nzelu za anthu ndi cinyengo copanda pake, malinga ndi miyambo ya anthu, malinganso ndi mfundo zimene zili maziko a moyo wa m’dzikoli, osati malinga ndi Kristu.” (Akol. 2:8) Cenjezo limeneli limatithandiza kudziŵa cifukwa cina cimene tiyenela kumvela malangizo a m’Malemba a akulu. Iwo amateteza nkhosa mwa kuzichinjiliza kwa anthu amene angafune kuononga cikhulupililo ca nkhosazo. Mtumwi Petulo anacenjeza kuti “aneneli onyenga” ndi “aphunzitsi onyenga” adzayesa ‘kukopa anthu apenda-penda’ kuti acite zoipa. (2 Pet. 2:1, 14) Akulu a masiku ano ayenela kupeleka macenjezo ofanana ndi amenewa pakakhala pofunika kutelo. Pokhala kuti ndi Akristu okhwima mwakuuzimu, io amadziŵa zambili. Ndipo asanaikidwe kukhala akulu, amakhala kuti aonetsa kale kuti amamvetsetsa bwino Malemba ndiponso kuti akhoza kuphunzitsa molondola. (1 Tim. 3:2; Tito 1:9) Akulu amakwanitsa kupeleka malangizo othandiza kwa nkhosa cifukwa cakuti ndi okhwima mwakuuzimu, amaona zinthu moyenela ndipo amagwilitsila nchito nzelu zocokela m’Baibo.

M’BUSA WABWINO AMADYETSA NDI KUTETEZA NKHOSA ZAKE

9. Kodi Yesu amatsogolela ndi kudyetsa bwanji mpingo wacikristu masiku ano?

9 Kudzela mwa gulu lake, Yehova amapeleka cakudya ca kuuzimu ca mwana alilenji ku gulu lonse la abale padziko lapansi. Timalandila malangizo ambili a m’Malemba m’zofalitsa zathu. Nthawi zinanso, gulu limapeleka malangizo kwa akulu mumpingo mwacindunji, kupyolela m’makalata kapena kudzela m’malangizo amene oyang’anila oyendela amapeleka. Mwa njila zimenezi, nkhosa zimalandila malangizo omveka bwino.

10. Kodi abusa acikristu ali ndi udindo wotani munthu wina akasiya gulu la Yehova?

10 Oyang’anila ali ndi udindo woteteza, kuweta ndi kusamalila mwakuuzimu anthu onse mumpingo, maka-maka amene ndi ovulala kapena amene akudwala mwakuuzimu. (Ŵelengani Yakobo 5:14, 15.) Ena mwa anthu amenewa, angakhale kuti ndi nkhosa zosocela ndipo analeka kucita nchito zacikristu. Zikakhala conco, mkulu wacikondi amacita zonse zimene angathe kuti apeze nkhosa yosocela ndi kuilimbikitsa kubwelela ku khola kapena kuti ku mpingo. Yesu anakamba kuti: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mat. 18:12-14.

KODI ZOPHOPHONYA ZA ABUSA AANG’ONO TIYENELA KUZIONA BWANJI?

11. N’cifukwa ciani zingakhale zovuta kwa anthu ena kutsatila malangizo a akulu?

11 Yehova ndi Yesu ndi Abusa angwilo. Koma abusa aang’ono amene apatsidwa udindo wosamalila mipingo ndi opanda ungwilo. Zimenezi zingapangitse kuti zikhale zovuta kwa ena kutsatila malangizo a akulu. Anthu otelo angakhale ndi maganizo akuti: ‘Akulu amenewa ndi opanda ungwilo monga ife. N’cifukwa ciani tiyenela kumvela malangizo ao?’ N’zoona kuti akulu ndi opanda ungwilo. Komabe, tiyenela kuona zophophonya zao ndi zifooko zao moyenelela.

12, 13. (a) M’nthawi zakale, kodi anthu ena a maudindo anacita zolakwa zotani? (b) N’cifukwa ciani Mulungu anafuna kuti zophophonya za anthu amene anali kutsogolela zilembedwe m’Baibo?

12 Malemba sabisa zophophonya za anthu amene Yehova anawagwilitsila nchito kutsogolela anthu ake m’nthawi zakale. Mwacitsanzo, Davide anadzozedwa kukhala mfumu ndi mtsogoleli wa Aisiraeli. Komabe iye anacita cigololo ndiponso anapha munthu. (2 Sam. 12:7-9) Ganizilaninso za mtumwi Petulo. Ngakhale kuti anali ndi udindo waukulu mumpingo wacikristu m’nthawi ya atumwi, iye anacita zolakwa zazikulu. (Mat. 16:18, 19; Yoh. 13:38; 18:27; Agal. 2:11-14) Kocokela pamene Adamu ndi Hava anacimwa, palibe munthu wina wangwilo amene anakhalapo padziko lapansi kupatulapo Yesu.

13 N’cifukwa ciani Yehova anaonetsetsa kuti zophophonya za anthu amene anawagwilitsila nchito zalembedwa m’Baibo? Cifukwa cimodzi ndi cakuti Mulungu anafuna kuonetsa kuti angagwilitsile nchito anthu opanda ungwilo kutsogolela anthu ake. Ndipo n’zimene iye wakhala akucita. Motelo, ngakhale kuti anthu amene amatitsogolela masiku ano ali ndi zophophonya, sitiyenela kung’ung’udza za io kapena kunyalanyaza utsogoleli wao. Yehova amafuna kuti tizilemekeza ndi kumvela abale amenewa.—Ŵelengani Ekisodo 16:2, 8.

14, 15. Kodi tikuphunzilapo ciani tikaganizila njila imene Yehova anagwilitsila nchito polankhula ndi anthu ake m’nthawi zakale?

14 Kumvela anthu amene akutitsogolela masiku ano n’kofunika kwambili. Ganizilani njila imene Yehova anali kulankhulila ndi anthu ake akale m’nthawi zovuta. Pamene Aisiraeli anatuluka mu Aiguputo, io anali kulandila malangizo a Mulungu kudzela mwa Mose ndi Aroni. Kuti asaphedwe ndi mlili wa nambala 10, Aisiraeli anafunikila kumvela malangizo akuti adye cakudya capadela ndi kuwaza magazi ena a nkhosa pamafelemu aŵili a m’mbali mwa khomo ndi pafelemu la pamwamba pa citseko. Kodi Mulungu analankhula mwacindunji ndi Aisiraeli? Iyai. Iwo anali kumvela akulu amene analandila malangizo kucokela kwa Mose. (Eks. 12:1-7, 21-23, 29) Mwa njila imeneyo, Yehova anagwilitsila nchito Mose ndi akulu kutsogolela anthu ake. Masiku ano Yehova amagwilitsilanso nchito akulu mumpingo kucita zofanana ndi zimenezi.

15 Mosakaikila, inunso mukudziŵa zocitika zina zambili zolembedwa m’Baibo zimene zimaonetsa kuti Yehova anali kupeleka malangizo opulumutsa moyo kwa anthu ake kudzela mwa anthu kapena angelo omuimila. Pa zocitika zonsezo, Yehova anapatsa anthu ena udindo wom’lankhulila ndi kuuza anthu ake zofunika kucita panthawi ya mavuto. Yehova angacitenso zofanana ndi zimenezi pa Aramagedo. N’cifukwa cake akulu onse amene apatsidwa udindo woimila Yehova kapena gulu lake masiku ano, ayenela kukhala osamala kwambili kuti asagwilitsile nchito udindo wao molakwika.

“GULU LIMODZI NDI M’BUSA MMODZI”

16. Kodi tiyenela kumvela “mau” ati?

16 Anthu a Yehova ali ‘m’gulu limodzi’ ndipo ali ndi “mbusa mmodzi,” Yesu Kristu. (Yoh. 10:16) Yesu anaonetsa kuti adzakhala ndi ophunzila ake “masiku onse mpaka m’nyengo ya mapeto a nthawi ino.” (Mat. 28:20) Monga Mfumu yakumwamba, Yesu ali ndi ulamulilo waukulu pa zinthu zonse zimene zidzacitika dziko la Satana lisanaonongedwe. Kuti tikhalebe otetezeka ndi ogwilizana m’gulu la Mulungu, tiyenela kumvela ‘mau kumbuyo kwathu’ amene akutiuza kumene tiyenela kupita. “Mau” amenewa amaphatikizapo zimene mzimu woyela wa Mulungu umatiuza kudzela m’Baibo ndi zimene Yehova ndi Yesu amatiuza kupyolela mwa anthu amene iye waika monga abusa aang’ono.—Ŵelengani Yesaya 30:21; Chivumbulutso 3:22.

17, 18. (a) Kodi anthu a Mulungu ali pangozi yotani? Nanga tiyenela kukhala otsimikiza ponena za ciani? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

17 Baibo imakamba kuti Satana akuyenda-yenda uku ndi uku ngati “mkango wobangula, wofunitsitsa kuti umeze winawake.” (1 Pet. 5:8) Monga mmene cilombo colusa cimacitila, Satana amaŵendelela nkhosa kuti ambwandile yosocela kapena yopanda chelu. Ndiye cifukwa cake tiyenela kugwilizana kwambili ndi gulu la Mulungu ndiponso kumvela ‘m’busa ndi woyang’anila miyoyo yathu.’ (1 Pet. 2:25) Ponena za anthu amene adzapulumuka cisautso cacikulu, lemba la Chivumbulutso 7:17 limati: “Mwanawankhosa, . . . adzawaweta ndi kuwatsogolela ku akasupe a madzi a moyo. Ndipo Mulungu adzapukuta misozi yonse m’maso mwao.” Limeneli ndi lonjezo losangalatsa kwambili.

18 Popeza kuti takambilana udindo wofunika wa akulu acikristu monga abusa aang’ono a kuuzimu, mkulu aliyense ayenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi ndi motani mmene ndingasamalile bwino nkhosa za Yesu?’ Tidzakambilana yankho la funso limeneli m’nkhani yotsatila.

[Cithunzi papeji 24]

Monga mmene m’busa amatetezela nkhosa, akulu amateteza nkhosa za Mulungu (Onani ndime 8)

[Cithunzi papeji 26]

Akulu amathandiza mabanja a kholo limodzi kupewa mayanjano oipa (Onani ndime 17 ndi 18)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani