Kodi Mudzapeleka Nsembe Kaamba Ka Ufumu?
“Mulungu amakonda munthu wopeleka mokondwela.”—2 AKOR. 9:7.
MALEMBA OFUNIKA KUWASINKHA-SINKHA
Kodi malemba otsatilawa angakuthandizeni bwanji kupenda bwino nsembe zimene mumapeleka kaamba ka Ufumu?
1 Mbiri 29:9
2 Akorinto 8:12
1. Kodi anthu ambili amadzimana ciani? Ndipo n’cifukwa ciani amacita zimenezi?
ANTHU amadzimana zinthu zina mwa kufuna kwao kuti acite zinthu zofunika kwambili. Makolo amagwilitsila nchito nthawi yao, ndalama zao, ndi mphamvu zao kuthandiza ana ao. Acinyamata amene amafuna kuimila dziko lao ku masewela a Olimpiki, amataila nthawi yambili kulimbitsa thupi lao pamene anzao ena akungosangalala ndi moyo. Yesu nayenso anadzimana zinthu zina kuti acite zinthu zofunika kwambili. Iye sanafune-fune moyo wawofu-wofu ndipo analibe ana. Koma anaika maganizo ake pakupititsa patsogolo nchito ya Ufumu. (Mat. 4:17; Luka 9:58) Otsatila ake naonso anadzimana zinthu zambili kuti acilikize Ufumu wa Mulungu. Iwo anacita zimenezi cifukwa cakuti anali kuona kuti Ufumuwo ndi cinthu cofunika kwambili. (Mat. 4:18-22; 19:27) Ndiye cifukwa cake tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Kodi cinthu cofunika kwambili kwa ine n’ciani?’
2. (a) Kodi ndi zinthu zofunika kwambili ziti zimene Akristu onse oona amacita modzimana? (b) Kodi anthu ena amadzipeleka kucita ciani?
2 Kucita zinthu modzimana n’kofunika kwambili kwa Akristu oona, ndipo kungathandize Mkristu kukhala paubwenzi wabwino ndi Yehova. Mwacitsanzo, timagwilitsila nchito nthawi yathu ndi mphamvu zathu popemphela, kuŵelenga Baibo, kucita kulambila kwa pabanja, kupita ku misonkhano ndi mu utumiki wakumunda.a (Yos. 1:8; Mat. 28:19, 20; Aheb. 10:24, 25) Cifukwa ca khama lathu ndi dalitso la Yehova, nchito yolalikila ikupita patsogolo kwambili ndipo anthu ambili akukhamukila ku “phili la nyumba ya Yehova.” (Yes. 2:2) Kuti acilikize nchito za Ufumu, anthu ambili adzipeleka kutumikila pa Beteli, kuthandiza panchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi Malo a Misonkhano, kukonza misokhano ikulu-ikulu kapena kupeleka thandizo kukacitika ngozi zacilengedwe. Sikuti munthu adzapeza moyo wosatha cifukwa cogwila nchito zimenezi, koma n’zowonjezela cabe ndipo n’zofunika pocilikiza nchito ya Ufumu.
3. (a) Kodi timapindula bwanji tikapeleka nsembe kaamba ka Ufumu? (b) Kodi aliyense wa ife ayenela kuganizila mafunso ati?
3 Tifunika kucilikiza Ufumu masiku ano kuposa ndi kale lonse. N’zosangalatsa kuona kuti anthu ambili amapeleka nsembe kwa Yehova modzifunila. (Ŵelengani Salimo 54:6.) Kuolowa manja kwa conco kumabweletsa cimwemwe pamene tikuyembekezela Ufumu wa Mulungu. (Deut. 16:15; Mac. 20:35) Komabe, aliyense wa ife ayenela kudzipenda bwino-bwino ndi kuganizila mafunso awa: ‘Kodi ndi zinthu zina ziti zimene ndingacite kuti ndicilikize kwambili Ufumu? Kodi ndimagwilitsila nchito bwanji nthawi yanga, ndalama zanga ndi maluso anga? Kodi sindiyenela kuiwala ciani ndikafuna kupeleka nsembe?’ Tiyeni tikambilane zitsanzo zimene tiyenela kutengela pamene tikupeleka nsembe zaufulu. Nsembe zimenezi zingatipatse cimwemwe coculuka.
NSEMBE ZA M’NTHAWI YA AISIRAELI
4. Kodi Aisiraeli anapindula bwanji cifukwa copeleka nsembe?
4 Aisiraeli anali kufunika kupeleka nsembe kuti akhululukidwe macimo ao. Nsembe zinali zofunika kuti munthu ayanjidwe ndi Yehova. Nsembe zina anali kuzipeleka cifukwa colamulidwa koma zina anali kuzipeleka mwa kufuna kwao. (Lev. 23:37, 38) Nsembe zopseleza anali kuzipeleka modzifunila kapena monga mphatso kwa Yehova. Citsanzo capadela ca mmene nsembe zinali kupelekedwela timaciona pa zimene zinacitika potsegulila kacisi m’nthawi ya Solomo.—2 Mbiri 7:4-6.
5. Kodi Yehova anapanga makonzedwe otani kamba ka osauka?
5 Yehova anali kudziŵa kuti anthu onse sakanapeleka nsembe zofanana. Conco analola aliyense kupeleka zimene akanakwanitsa. Malinga ndi cilamulo ca Yehova, magazi a nyama anayenela kukhetsedwa, ndipo zimenezo zinali “mthunzi cabe wa zinthu zabwino zimene zikubwela” kudzela mwa Mwana wake, Yesu. (Aheb. 10:1-4) Komabe, Yehova sanakhwimitse lamulo limeneli. Mwacitsanzo, Yehova anali kulola kuti anthu azipeleka njiwa ngati sakanakwanitsa kupeleka nsembe ya nkhosa kapena ng’ombe. Motelo, anthu osauka naonso anali kupeleka nsembe kwa Yehova mwacimwemwe. (Lev. 1:3, 10, 14; 5:7) Ngakhale kuti nyama zimene anali kupeleka nsembe zinali zosiyana-siyana, anthu amene anali kupeleka nsembe zaufulu anafunika kucita zinthu ziŵili.
6. Kodi munthu amene anali kupeleka nsembe anafunika kucita ciani? N’cifukwa ciani kutsatila malangizo amenewa kunali kofunika kwambili?
6 Coyamba, munthu anayenela kupeleka nsembe yabwino koposa. Yehova anauza Aisiraeli kuti anayenela kupeleka nsembe zopanda cilema kuti iye ‘awayanje.’ (Lev. 22:18-20) Ngati nyama inali ndi cilema, Yehova sanali kuiona kukhala nsembe yovomelezeka. Caciŵili, munthu amene anali kupeleka nsembe anafunika kukhala woyela ndi wosadetsedwa. Munthu wodetsedwa anafunika kupeleka nsembe yaucimo kapena yopalamula asanapeleke nsembe yaufulu n’colinga cakuti akhalenso paubwenzi wabwino ndi Yehova. (Lev. 5:5, 6, 15) Nkhani imeneyi inali yoopsa kwambili. Yehova analamula kuti ngati munthu wodetsedwa wadya nyama ya nsembe yaciyanjano, imene inaphatikizapo nsembe zaufulu, munthuyo anafunika kuphedwa ndithu. (Lev. 7:20, 21) Koma ngati munthu amene wapeleka nsembe anali paubwenzi wabwino ndi Yehova ndipo nsembe yake inali yopanda cilema, wopeleka nsembeyo anali kusangalala kwambili.—Ŵelengani 1 Mbiri 29:9.
KUPELEKA NSEMBE MASIKU ANO
7, 8. (a) Kodi anthu ambili amasangalala bwanji cifukwa codzimana zinthu zina kaamba ka Ufumu? Kodi tili ndi zinthu ziti zimene tingagwilitsile nchito potumikila Yehova?
7 Masiku ano, palinso anthu ambili amene amatumikila Yehova modzipeleka ndipo iye amasangalala ndi zimene anthuwo amacita. Kutumikila abale athu kumabweletsa madalitso ambili. M’bale wina amene amagwila nao nchito yomanga Nyumba za Ufumu ndi kuthandiza kumene kwagwa matsoka acilengedwe ananena kuti cimwemwe cimene amakhala naco cifukwa cotumikila mwa njila imeneyi n’cosaneneka. Iye anati: “Ndikaona abale ndi alongo akusangala ndi kuyamikila Nyumba ya Ufumu yatsopano kapena thandizo limene alandila kukagwa matsoka acilengedwe, ndimaona kuti nchito imene tinagwila ndiponso nkhama lathu sizinapite pacabe.”
8 Gulu la Yehova la makono limayesetsa kupeza njila zocilikizila nchito ya Yehova. Mu 1904, m’bale C. T. Russell analemba kuti: “Aliyense ayenela kudziona monga woikidwa ndi Ambuye kukhala mdindo wa nthaŵi yake, mphamvu, ndalama, ndi zina zotelo, ndipo aliyense ayenela kuyesetsa kugwilitsila nchito maluso ameneŵa mmene angathele, ku ulemelelo wa Ambuye.” Ngakhale kuti timakhala ndi madalitso ambili cifukwa cotumikila Yehova, timayenela kudzimana zinthu zina kuti tikwanitse kucita zimenezi. (2 Samueli 24:21-24) Tiyeni tizigwilitsila nchito zinthu zimene tili nazo potumikila Yehova.
9. Kodi Yesu anakamba mfundo yotani pa Luka 10:2-4 imene tingatsatile pankhani yogwilitsila nchito bwino nthawi?
9 Nthawi yathu. Kuti mabuku athu atembenuzidwe ndi kusindikizidwa pamafunika khama ndi nthawi yoculuka. Pamafunikanso nthawi yoculuka pokonza misonkhano ikulu-ikulu ndi malo olambilila, ndiponso pothandiza kukagwa tsoka lacilengedwe. Palinso nchito zina zambili zofuna nthawi ndi khama. Patsiku timakhala ndi maola owelengeka cabe. Yesu anafotokoza mfundo imene ingatithandize kugwilitsila nchito bwino nthawi. Pamene anatuma ophunzila ake kukalalikila, iye anawauza kuti: “Musamacedwe mukamapeleka moni panjila.” (Luka 10:2-4) N’cifukwa ciani Yesu anapeleka malangizo amenewa? Katswili wina wa maphunzilo a zaumulungu anati: “Moni wa anthu a ku Isiraeli ndi mayiko ozungulila, sunali wongogwilana manja n’kuwelama pang’ono ngati mmene ena amacitila, koma anali kukumbatilana ndi kuwelama mobweleza-bweleza, ndipo nthawi zina anali kugona pansi cafufumimba. Zonsezi zinafunika nthawi yambili.” Yesu sanali kusonkhezela otsatila ake kukhala odzikonda. Koma anali kuwathandiza kukumbukila kuti anali ndi nthawi yocepa ndi kuti anafunika kuigwilitsila nchito mwanzelu mwa kucita zinthu zofunika kwambili. (Aef. 5:16) Ifenso tiyenela kutsatila mfundo imeneyi kuti tikhale ndi nthawi yokwanila yogwila nchito zocilikiza Ufumu.
10, 11. (a) Kodi zopeleka zathu za nchito ya padziko lonse zimagwila nchito zina ziti? (b) Kodi pa 1 Akorinto 16:1, 2 pali mfundo iti imene ingatithandize?
10 Ndalama zathu. Pamafunika ndalama zambili zothandiza pa nchito za Ufumu. Caka ciliconse ndalama mamiliyoni ambili zimagwilitsilidwa nchito posamalila oyang’anila oyendela, apainiya apadela ndi amishonale. Kucokela m’caka ca 1999, Nyumba za Ufumu zoposa 24,500 zamangidwa m’maiko osauka. Koma pakufunikabe Nyumba za Ufumu zina zokwanila 6,400. Mwezi uliwonse, magazini a Nsanja ya Mlonda ndi a Galamukani! okwana 100 miliyoni amasindikizidwa. Nchito zonsezi zimacilikizidwa ndi zopeleka zanu.
11 Mtumwi Paulo anafotokoza mfundo imene tiyenela kutsatila tikafuna kupeleka zopeleka. (Ŵelengani 1 Akorinto 16:1, 2.) Mouzilidwa, iye analimbikitsa abale ake a ku Korinto kuti asamayembekezele kutha kwa mlungu kuti akonze zopeleka koma kuti tsiku lililonse loyamba la mlungu, aziika kenakake pambali kunyumba kwao malinga ndi mmene zinthu zikuyendela pa moyo wao. Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, abale ndi alongo masiku ano amakonzekela pasadakhale kuti akapeleke zopeleka moolowa manja mogwilizana ndi ndalama zimene amapeza. (Luka 21:1-4; Mac. 4:32-35) Yehova amayamikila kwambili anthu amene amasonyeza mzimu umenewu.
12, 13. N’ciani cingalepheletse ena kugwilitsila nchito mphamvu ndi luso lao kutumikila Mulungu mokwanila? Nanga Yehova angawathandize bwanji?
12 Mphamvu ndi luso lathu. Yehova amatithandiza tikamayesetsa kugwilitsila nchito mphamvu ndi maluso athu kucilikiza Ufumu. Iye watilonjeza kuti adzatithandiza tikatopa. (Yes. 40:29-31) Kodi timaona kuti tilibe luso lokwanila lothandiza pa nchito ya Ufumu? Kapena kodi timaganiza kuti ena ndi amene angacite bwino kwambili kuposa ife? Kumbukilani kuti Yehova angaonjezele luso limene munthu angakhale nalo mwacibwadwa, monga mmene anacitila ndi Bezaleli ndi Oholiabu.—Eks. 31:1-6; onani cithunzi-thunzi cili ku ciyambi kwa nkhani ino.
13 Yehova amatilimbikitsa kuti tisalole ciliconse kutilepheletsa kucita zimene tingathe pom’tumikila. (Miy. 3:27) Panthawi yomanga kacisi, Yehova anauza Ayuda ku Yerusalemu kuti aganizile mofatsa zimene anali kucita pa nchito yomangayo. (Hag. 1:2-5) Iwo anali ataleka kugwila nchitoyo ndipo anayamba kugwila nchito zina. Ifenso tifunika kupenda bwino zocita zathu kuti tione ngati timaikadi zofuna za Yehova patsogolo. Tiyeni ‘tiganizile mofatsa zimene tikucita’ kuti ticite zambili pa nchito ya Ufumu masiku otsiliza ano.
KUPELEKA NSEMBE ZIMENE TINGATHE
14, 15. (a) Kodi tikuphunzila ciani pa citsanzo ca abale athu osauka? (b) Kodi tifunika kukhala ndi colinga cotani?
14 Anthu ambili amakhala ku madela kumene umoyo ndi wovuta ndipo mavuto monga umphawi ali paliponse. Gulu lathu limayesetsa kuthandiza pa zosowa za abale athu okhala m’madela otelo. (2 Akor. 8:14) Koma naonso abale a m’madela osauka amaona kuti ndi mwai kupeleka zopeleka. Anthu osauka akamapeleka zopeleka zao mokondwela, Yehova amayamikila.—2 Akor. 9:7.
15 M’dziko lina losauka mu Africa muno, abale amapatula kacigawo kakang’ono ka munda wao n’colinga cakuti akagulitsa mbeu zimenezo akapeleke zopeleka zocilikiza nchito ya Ufumu. M’dzikolo, gulu linapanga makonzedwe omanga Nyumba ya Ufumu m’dela lina limene kunalibe malo osonkhanila. Abale ndi alongo anali kufuna kuthandiza pa nchitoyi. Koma imeneyi inali nthawi imene io anali kubzala mbeu zao. Ngakhale zinali conco, anadzipeleka kugwila nchitoyo. Iwo anali kugwila nchito yomanga Nyumba ya Ufumu kukaca m’mawa mpaka m’madzulo kenako anali kukabzala mbeu zao. Kodi si mzimu wodzipeleka umenewu? Zimenezi zikutikumbutsa abale a m’nthawi ya atumwi a ku Makedoniya. Iwo anali “pa umphawi wadzaoneni,” koma anapempha kuti apatsidwe mwai wopeleka nao zopeleka zacifundo. (2 Akor. 8:1-4) Tiyeni nafenso tizipeleka ‘molingana ndi madalitso amene Yehova watipatsa.’—Ŵelengani Deuteronomo 16:17.
16. Kodi tingacite ciani kuti nsembe zathu zikhale zovomelezeka kwa Yehova?
16 Koma tifunika kucita zinthu mosamala. Monga mmene zinalili m’nthawi ya Aisiraeli, tifunika kuonetsetsa kuti nsembe zathu zaufulu n’zovomelezeka kwa Mulungu. Kodi n’ciani cingacititse kuti nsembe zathu zikhale zosavomelezeka? Tikamapeleka nsembe, tifunika kusamala kuti tisanyalanyaze udindo wathu waukulu wotumikila Yehova ndi kusamalila mabanja athu. Nthawi ndi ndalama zimene timapeleka pothandize ena siziyenela kuticititsa kunyalanyaza moyo wauzimu kapena wakuthupi wa banja lathu. Ngati ticita zimenezo ndiye kuti tikupeleka zimene sitingakwanitse. (Ŵelengani 2 Akorinto 8:12.) Komanso tifunika kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu kuopela kuti tingakhale wosayenela m’njila inayake. (1 Akor. 9:26, 27) Koma musakaikile kuti ngati tipitilizabe kutsatila mfundo za m’Baibo, nsembe zathu zidzatibweletsela cisangalalo coculuka ndipo Yehova ‘adzakondwela’ nazo.
NSEMBE ZATHU N’ZOFUNIKA KWAMBILI
17, 18. Kodi anthu amene amadzimana cifukwa ca Ufumu timawaona bwanji? Nanga tonsefe tiyenela kuganizila za ciani?
17 Abale ndi alongo athu ambili ‘akudzipeleka ngati nsembe yacakumwa’ mwa nchito zao zocilikiza nchito za Ufumu zimene n’zofunika. (Afil. 2:17) Timayamikila kwambili anthu onse amene ali ndi mzimu umenewu. Akazi ndi ana a abale amene amatsogolela pa nchito za Ufumu tiyenelanso kuwayamikila kwambili cifukwa ca mzimu wao wopatsa ndi wodzimana.
18 Pali nchito yaikulu imene iyenela kucitika kuti ticilikize zinthu za Ufumu. Tiyeni tonse tiganizilepo mwapemphelo mmene tingaonjezele nchito yathu muutumiki. Dziŵani kuti mphoto yanu idzakhala yaikulu tsopano ndi “m’nthawi imene ikubwelayo.”—Maliko 10:28-30.
[Mau apansi]
a Onani nkhani yakuti “Tizipeleka Nsembe Kwa Yehova ndi Moyo Wathu Wonse” mu Nsanja ya Olonda ya January 15, 2012, tsamba 21 mpaka 25.
[Cithunzi papeji 14, 15]
Nsembe zambili zinali zaufulu mofanana ndi zimene timapeleka masiku ano (Onani ndime 7 mpaka 13)
[Cithunzi papeji 14]
Ofalitsa Ufumu pa Nyumba ya Ufumu ku Kenya mu Africa
[Cithunzi papeji 14, 15]
Wanchito wodzipeleka wa m’Komiti Yomanga Yacigawo ku Tuxedo, New York, U.S.A.
[Cithunzi papeji 15]
Atumiki a pa Beteli ku Australia