LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w13 12/1 masa. 8-12
  • “Musafulumile Kugwedezeka Pa Maganizo Anu”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Musafulumile Kugwedezeka Pa Maganizo Anu”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MACENJEZO A PANTHAWI YAKE
  • SANKHANI MABWENZI ANU MWANZELU
  • “GWILANI MWAMPHAMVU MIYAMBO”
  • MMENE MUNGAPEWELE KUGWEDEZEKA
  • Khalanibe Olikonzekela Tsiku la Yehova
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Pitilizani “Kulimbikitsana”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2022
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
w13 12/1 masa. 8-12

“Musafulumile Kugwedezeka Pa Maganizo Anu”

“Abale, . . . tikukupemphani kuti musafulumile kugwedezeka pa maganizo anu.”—2 ATES. 2:1, 2.

MFUNDO ZOFUNIKA KUZIGANIZILA

Ndi macenjezo a panthawi yake ati amene ali m’makalata a Paulo opita kwa Atesalonika?

N’ciani cingatithandize kuti tisanyengedwe?

Kodi kulalikila mwacangu za Ufumu kumatiteteza bwanji?

1, 2. N’cifukwa ciani cinyengo n’cofala kwambili masiku ano? Nanga n’cinyengo cotani cimene cafala masiku ano? (Onani cithunzi-thunzi cimene cili kuciyambi kwa nkhani ino.)

CINYENGO ndi mabodza ndi zofala kwambili m’dzikoli. Zimenezi siziyenela kutidabwitsa. Baibo imanena mosapita m’mbali kuti Satana Mdyelekezi ndi katswili wa cinyengo, ndipo ndi wolamulila wa dzikoli. (1 Tim. 2:14; 1 Yoh. 5:19) Pamene mapeto a dongosolo lino la zinthu loipali ayandikila kwambili, Satana akukwiila-kwiila cifukwa cakuti “wangotsala ndi kanthawi kocepa.” (Chiv. 12:12) Conco, n’zosadabwitsa kuona kuti anthu amene ali kumbali yake aipilatu pankhani ya cinyengo, ndipo amafunitsitsa kwambili kunyenga atumiki a Yehova.

2 Nthawi zina, nkhani zabodza zokhudza atumiki a Yehova ndi zikhulupililo zao zafalitsidwa. Anthu amafalitsa nkhani zabodza mwa kugwilitsila nchito manyuzipepala, mapulogalamu a pa TV ndi Intaneti. Pa cifukwa cimeneci, anthu ena amasokonezeka maganizo kapena kukhumudwa cifukwa cakuti amakhulupilila mabodzawa asanafufuze zoona pa nkhanizo.

3. N’ciani cingatithandize kuti tisanyengedwe?

3 Kuti tisagonjetsedwe ndi njila yacinyengo ya mdani wathu imeneyi, Mulungu watipatsa Mau ake amene ndi “opindulitsa pa.  . . kuwongola zinthu.” (2 Tim. 3:16) Tifunika kutengapo phunzilo pa zimene mtumwi Paulo analemba zokhudza Akristu ena a ku Tesalonika amene anasoceletsedwa ndi mabodza m’nthawi ya atumwi. Iye anawalangiza kuti ‘asafulumile kugwedezeka pa maganizo ao.’ (2 Ates. 2:1, 2) Kodi tingaphunzile ciani pa malangizo acikondi a Paulo amenewa, ndipo tingawagwilitsile nchito bwanji?

MACENJEZO A PANTHAWI YAKE

4. Ponena za kubwela kwa “tsiku la Yehova,” kodi Akristu a ku Tesalonika anathandizidwa bwanji kukhala maso? Nanga ife timalandila bwanji malangizo otithandiza kukhala maso?

4 M’kalata yake yoyamba yopita ku mpingo wa Atesalonika, Paulo anagogomeza za kubwela kwa “tsiku la Yehova.” Iye anali kufuna kuti abale ake adziŵe ndi kukonzekela za tsikulo. N’cifukwa cake anawalimbikitsa ‘kukhalabe maso ndi kukhalabe oganiza bwino’ monga “ana a kuwala.” (Ŵelengani 1 Atesalonika 5:1-6.) Masiku ano, tikuyembekezela kuonongedwa kwa Babulo Wamkulu, amene ndi ufumu wa dziko lonse wa cipembedzo conama. Cimeneci cidzakhala ciyambi ca tsiku lalikulu la Yehova. Ife tili ndi mwai cifukwa cakuti timaphunzila zambili zokhudza kukwanilitsidwa kwa colinga ca Yehova. Komanso pa misonkhano yampingo, timalandila malangizo amene amatithandiza kukhala maso. Kumvela malangizo amenewa kudzatithandiza kulimbikila kucita ‘utumiki wopatulika mwa kugwilitsa ntchito luntha lathu la kuganiza.’—Aroma 12:1.

5, 6. (a) Kodi Paulo anafotokoza ciani m’kalata yake yaciŵili yopita kwa Atesalonika? (b) Kodi Mulungu adzacita ciani posacedwapa kudzela mwa Yesu? Ndipo ife tiyenela kudzifunsa mafunso ati?

5 Paulo anatumiza kalata yaciŵili kwa Akristu a ku Tesalonika mwamsanga pambuyo potumiza kalata yake yoyamba. M’kalata yaciŵili imeneyi, iye anagogomeza za cisautso cimene cidzakhalapo pamene Ambuye Yesu adzapeleka ciweluzo kwa “anthu osadziŵa Mulungu ndi kwa anthu osamvela uthenga wabwino.” (2 Ates. 1:6-8) Caputala caciŵili ca kalatayi cimaonetsa kuti ena mumpingowo anali “kutengeka-tengeka” ponena za tsiku la Yehova ndipo anayamba kuganiza kuti tsikulo latsala pang’ono kufika. (Ŵelengani 2 Atesalonika 2:1, 2.) Akristu oyambilila amenewo anali kudziŵa zocepa cabe zokhudza mmene Yehova anali kukwanilitsila colinga cake. N’cifukwa cake Paulo analemba kuti: “Tikudziŵa mopelewela ndipo tikunenela mopelewelanso. Koma cokwanila cikadzafika, copelewelaci cidzatha.” (1 Akor. 13:9, 10) Koma makalata ouzilidwa okhala ndi macenjezo olembedwa ndi Paulo, mtumwi Petulo ndi abale ena okhulupilika amene anali odzozedwa, akanathandiza abale a m’nthawiyo kukhalabe ndi cikhulupililo colimba.

6 Pofuna kuongolela maganizo ao olakwika, Paulo mouzilidwa anafotokoza kuti mpatuko waukulu ndiponso “munthu wosamvela malamulo” adzafika tsiku la Yehova lisanabwele.a Pambuyo pake, nthawi ikadzakwana, Ambuye Yesu ‘adzaonongelatu’ anthu onse amene akunyengedwa ndi Satana. Mtumwiyo anafotokoza kuti anthu amenewo adzaonongedwa cifukwa cakuti “sanasonyeze kuti akulaka-laka coonadi.” (2 Ates. 2:3, 8-10) Conco, tifunika kudzifunsa kuti: ‘Kodi coonadi ndimacikondadi? Kodi ndimayesetsa kuphunzila mfundo zatsopano za coonadi m’magazini monga ino kapena m’zofalitsa zina zofotokoza Baibo zimene timalandila m’gulu la Mulungu?’

SANKHANI MABWENZI ANU MWANZELU

7, 8. (a) Kodi Akristu oyambilila anali kulimbana ndi mavuto otani? (b) Kodi Akristu oona masiku ano angakumane ndi vuto loopsa liti?

7 Kuonjezela pa mavuto amene Akristu anali kulimbana nao cifukwa ca ampatuko ndi ziphunzitso zao, io anali kudzalimbananso ndi mavuto ena. Paulo analembela Timoteyo kuti: “Kukonda ndalama ndi muzu wa zopweteka za mtundu uliwonse.” Mtumwiyo anaonjezela kuti, “pokulitsa cikondi cimeneci, ena asoceletsedwa n’kusiya cikhulupililo ndipo adzibweletsela zopweteka zambili pathupi lao.” (1 Timoteyo 6:10) “Ntchito za thupi” ndi vuto linanso limene Akristu nthawi zonse anali kulimbana nalo.—Agal. 5:19-21.

8 Koma Paulo anacenjeza mwamphamvu Akristu a ku Tesalonika za kuopsa kwa anthu ampatuko amene anali monga “atumwi onyenga.” Pakati pao panali anthu amene anali kulankhula “zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzila aziwatsatila.” (2 Akor. 11:4, 13; Mac. 20:30) Patapita nthawi, Yesu anayamikila Akristu a mumpingo wa ku Efeso cifukwa cakuti sanali ‘kulekelela anthu oipa.’ Aefeso ‘anayesa’ anthu amenewo ndipo anadziŵa kuti anali atumwi onyenga kapena kuti onama. (Chiv. 2:2) N’zocititsa cidwi kuti m’kalata yake yaciŵili yopita kwa Atesalonika, Paulo anapeleka malangizo akuti: “Tikukulangizani abale m’dzina la Ambuye Yesu Kristu, kuti mupewe m’bale aliyense woyenda mosalongosoka.” Kenako iye anachula mwacindunji Akristu amene sanali ‘kufuna kugwila ntchito.’ (2 Ates. 3:6, 10) Iwo anafunika kupewa munthu waulesi. Ndipo ngati anafunika kupewa munthu waulesi, nanga bwanji ponena zopewa munthu amene anayamba mpatuko? Ndithudi, panthawi imeneyo, kuyanjana ndi anthu ampatuko kunali koopsa kwambili ndipo Akristu anali kufunika kupewa anthu otelo. Nafenso Akristu masiku ano tifunika kupewa anthu ampatuko.—Miy. 13:20.

9. N’cifukwa ciani tifunika kukhala osamala ngati munthu wayamba kukamba zinthu zimene Baibo sinafotokoze kapena akusuliza gulu la Yehova?

9 Popeza kuti cisautso cacikulu cayandikila ndipo mapeto a dongosolo loipali ali pafupi, macenjezo ouzilidwa opita kwa Akristu a m’nthawi ya atumwi ndi ofunikanso kwambili kwa ife. Sitikufuna “kuphonya colinga” ca kukoma mtima kwa Yehova ndi kutaya mwai wodzalandila moyo wosatha, kaya wakumwamba kapena wapadziko lapansi. (2 Akor. 6:1) Tifunika kukhala osamala kwambili ngati munthu amene timasonkhana naye akutinyengelela kukamba maganizo athu pa zinthu zimene Baibo sinafotokoze, kapena akusuliza gulu la Yehova.—2 Ates. 3:13-15.

“GWILANI MWAMPHAMVU MIYAMBO”

10. Kodi Akristu a ku Tesalonika analimbikitsidwa kusunga miyambo iti?

10 Paulo analimbikitsa abale ake a ku Tesalonika kuti ‘akhale olimba’ ndi kumamatila ku zimene anaphunzila. (Ŵelengani 2 Atesalonika 2:15.) Kodi ndi “miyambo” iti imene io anaphunzitsidwa? Mwacionekele, Paulo sanali kunena za miyambo ya cipembedzo conama imene anthu ena anali kuiona kukhala yofunika mofanana ndi miyambo ya m’Malemba. M’malo mwake, anali kutanthauza ziphunzitso zimene iye ndi anthu ena anaphunzila kwa Yesu komanso zimene Mulungu anamuuzila kulemba. Zoculuka mwa ziphunzitso zimenezi tsopano ndi mbali ya Malemba ouzilidwa. Paulo anayamikila abale ake a mumpingo wa ku Korinto cifukwa cakuti anali ‘kumukumbukila m’zinthu zonse, ndipo anali kusunga miyambo monga mmene iye anaipelekela kwa io.’ (1 Akor. 11:2) Zimene anthuwo anaphunzila zinali zodalilika cifukwa cakuti zinacokela kwa Yehova ndi Mwana wake, ndipo anafunika kuzikhulupilila.

11. Kodi cinyengo cingapangitse anthu ena kutani?

11 Pamene Paulo anali kulembela Aheberi, iye anafotokoza zinthu ziŵili zimene zingapangitse Mkristu kutaya cikhulupililo ndi kulephela kucilimika pa cikhulupililo. (Ŵelengani Aheberi 2:1; 3:12.) Iye anakamba za ‘kutengeke pang’ono-pang’ono’ ndi za ‘kucoka’ pa cikhulupililo. Zimakhala zovuta kudziŵa kuti boti limene laima m’mphepete mwa madzi layamba kutengeka pang’ono-pang’ono. Koma m’kupita kwa nthawi, botilo limaoneka kuti lasintha malo. Nthawi zina munthu angakankhile boti lake m’madzi mwadala. Zitsanzo zonse ziŵilizi zikuonetsa mmene anthu ena amasiila kukhulupilila coonadi cifukwa ca cinyengo.

12. Ndi zinthu ziti zimene zingationonge mwakuuzimu masiku ano?

12 Zimenezi ziyenela kuti ndi zimene zinacitikila Akristu ena a ku Tesalonika. Nanga bwanji masiku ano? Zinthu zoonongetsa nthawi n’zambili. Ganizilani za kuculuka kwa nthawi imene munthu amaononga poceza pa Intaneti, kuwelenga ndi kuyankha mauthenga pa kompyuta kapena pa foni, kukonda kwambili zamaseŵela kapena kucita zinthu zina zimene timakonda. Kukonda kwambili zinthu zimenezi kungasokoneze Mkristu ndi kufooketsa cangu cake pa zinthu za kuuzimu. Kodi zotsatilapo zake zingakhale zotani? Mkristuyo angakhale ndi nthawi yocepa yopemphela mocokela pansi pa mtima, kuphunzila Mau a Mulungu, kupezeka pa misonkhano ndi kulalikila uthenga wabwino. Kodi n’ciani cimene tingacite kuti tipewe kugwedezeka mofulumila pa maganizo athu?

MMENE MUNGAPEWELE KUGWEDEZEKA

13. Malinga ndi zimene Baibo inanena, kodi anthu ambili ali ndi maganizo otani? Nanga n’ciani cimene cingathandize kuti cikhulupililo cathu cisafooke?

13 Sitiyenela kuiwala nthawi imene tikukhalamo ndiponso ngozi imene imakhalapo ngati tiyanjana ndi anthu amene amakana kuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza.’ Mtumwi Petulo analemba za nthawi imene tikukhalamo ino kuti: “Kudzakhala onyodola amene azidzatsatila zilakolako zao, amene azidzati: ‘Kukhalapo kwake kolonjezedwa kuja kuli kuti? Taonani, kucokela tsiku limene makolo athu anamwalila, zinthu zonse zikupitililabe cimodzi-modzi ngati mmene zakhalila kuyambila pa ciyambi ca cilengedwe.’” (2 Pet. 3:3, 4) Kuŵelenga ndi kuphunzila Mau a Mulungu tsiku lililonse kudzatithandiza kukumbukila kuti tikukhala ‘m’masiku otsiliza.’ Mpatuko umene unaloseledwa unaonekela kale-kale ndipo ukalipo masiku ano. “Munthu wosamvela malamulo” akalipo ndipo akutsutsa atumiki a Mulungu. Conco, sitifunika kuiwala kuti tsiku la Yehova lili pafupi.—Zef. 1:7.

14. Kodi kukhala otangwanika ndi utumiki wa Mulungu kumatiteteza bwanji?

14 Kulalikila uthenga wabwino nthawi zonse ndi cinthu cina cimene cingatithandize kuti tisagwedezeke pa maganizo athu. Cotelo pamene Kristu Yesu, Mutu wampingo analamula otsatila ake kuti akaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila ake ndi kuwaphunzitsa kusunga zinthu zimene Yesu anawalamulila, iye anali kupeleka malangizo amene anali kudzateteza otsatila ake. (Mat. 28:19, 20) Kuti tionetse kuti tikumvela lamulo limeneli, tiyenela kukhala acangu pa nchito yolalikila. Kodi muganiza kuti abale athu a ku Tesalonika akanakhala okhutila mwa kulalikila ndi kuphunzitsa mwamwambo cabe? Kumbukilani malangizo amene Paulo anawapatsa akuti: “Musazimitse moto wa mzimu. Musanyoze mau aulosi.” (1 Ates. 5:19, 20) N’zosangalatsa kuphunzila ndi kuuzako ena maulosi amenewa.

15. Ndi nkhani zothandiza ziti zimene tingaphunzile pa kulambila kwa pabanja?

15 Tonse timafuna kuthandiza anthu a m’banja lathu kukulitsa maluso ao mu ulaliki. Abale ndi alongo ambili aona kuti njila imodzi yocitila zimenezi ndi kupatula nthawi ina pa kulambila kwao kwa pabanja kuti aphunzile maluso a mmene angacitile ulaliki. Mungakambilane mmene mungacitile maulendo obwelelako kwa anthu amene anaonetsa cidwi. Kodi mudzakambilana nao ciani pa ulendo wotsatila? Kodi ndi nkhani ziti zimene zidzaonjezela cidwi ca anthu amenewo? Kodi nthawi yabwino kwambili yocita maulendo obwelelako ndi iti? Ena amapatula nthawi ina pa kulambila kwao kwa pabanja kukonzekela misonkhano n’colinga cakuti adziŵe zimene zidzaphunzilidwa pa misonkhanoyo. Muyenela kukonzekela mokwanila kuti mukatengemo mbali. Kutengako mbali pa misonkhano kudzalimbitsa cikhulupililo canu, ndipo zimenezi zidzakutetezani kuti musagwedezeke pa maganizo anu. (Sal. 35:18) Kucita kulambila kwa pabanja kudzatiteteza kuti tisamakambe maganizo athu pa zinthu zimene Baibo siinafotokoze kapena kukaikila zimene iyo imanena.

16. N’ciani cimene cimalimbikitsa Akristu odzozedwa kusagwedezeka pa maganizo ao?

16 M’zaka zapitazi, Yehova wathandiza anthu ake kumvetsetsa maulosi a m’Baibo. Zimenezi zimalimbitsa cikhulupililo cathu cakuti tidzalandila mphoto yamtengo wapatali mtsogolo. Akristu odzozedwa ali ndi ciyembekezo codzakhala ndi Kristu kumwamba. Ciyembekezo cimeneci cimawalimbikitsa kusagwedezeka pa maganizo ao. Ponena za io, tinganenenso mau a Paulo kwa Atesalonika akuti: “Tiyeneladi kumayamika Mulungu nthawi zonse cifukwa ca inu abale okondedwa ndi Yehova. Tiyenela kutelo cifukwa Mulungu anakusankhani . . . mwa kukuyeletsani ndi mzimu, ndiponso mwa cikhulupililo canu m’coonadi.”—2 Ates. 2:13.

17. Kodi mau a pa 2 Atesalonika 3:1-5 amakulimbikitsani bwanji?

17 Anthu amene ali ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi afunikanso kucita zimene angathe kuti asagwedezeke mofulumila pa maganizo ao. Ngati muli ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, muyenela kumvela mau olimbikitsa ndi acikondi amene Paulo analembela Akristu anzake odzozedwa ku Tesalonika. (Ŵelengani 2 Atesalonika 3:1-5.) Tonsefe tiyenela kuyamikila kwambili mau acikondi amenewa. Zoonadi, makalata opita kwa Atesalonika amaticenjeza kuti sitiyenela kukamba zinthu zimene Baibo sinafotokoze, kapena kukamba zinthu zina zokaikitsa. Cifukwa cakuti mapeto ayandikila, Akristu masiku ano amayamikila kwambili macenjezo amenewa.

[Mau apansi]

a Malinga ndi lemba la Machitidwe 20:29, 30, Paulo anafotokoza kuti mkati mwa mpingo wacikristu “anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzila aziwatsatila.” Mbili yakale imatsimikizila kuti m’kupita kwa nthawi, panakhala kusiyana pakati pa akulu-akulu a chalichi ndi anthu wamba. Pofika m’zaka za m’ma 200 C.E., “munthu wosamvela malamulo” anaonekela kukhala gulu la atsogoleli a Machalichi Acikristu.—Onani Nsanja ya Olonda ya February 1, 1990, tsamba 10 mpaka 14.

[Cithunzi papeji 9]

Paulo analemba makalata amene anapeleka macenjezo a panthawi yake kwa Akristu (Onani ndime 4 ndi 5)

[Cithunzi papeji 12]

Kukonzekela bwino ndi kutengamo mbali mu ulaliki kungatithandize kuti tisagwedezeke pa maganizo athu (Onani ndime 14 ndi 15)

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani