LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 4/1 masa. 4-6
  • N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • KODI MULUNGU AMAYANKHA MAPEMPHELO ONSE?
  • MMENE MULUNGU AMAYANKHILA MAPEMPHELO
  • KHULUPILILANI KUTI YEHOVA AMATIMVELA
  • Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Kodi Yehova Adzayankha Mapemphelo Anga?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2023
  • Kodi Mulungu Amamva Mapemphelo Athu?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2021
  • Mwayi Wa Pemphelo
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 4/1 masa. 4-6

NKHANI YA PACIKUTON

N’cifukwa Ciani Tiyenela Kupemphela?

Mwina mungadzifunse kuti, ‘Ngati Mulungu amadziŵa zonse, kuphatikizapo maganizo ndi zosoŵa zanga, n’cifukwa ciani ndiyenela kupemphela?’ Funso limenelo n’lomveka. Ngakhale Yesu anakamba kuti Mulungu “amadziŵa zimene mukufuna musanapemphe n’komwe.” (Mateyu 6: 8) Mfumu ya Isiraeli inavomeleza mfundo imeneyi, ndipo inalemba kuti: “Ndisananene kanthu, inu Yehova mumakhala mutadziŵa kale zonse.” (Salimo 139:4) Conco, n’cifukwa ciani tiyenela kupemphela kwa Mulungu? Kuti tipeze yankho, tiyeni tikambilane zimene Baibulo limanena zokhudza mapemphelo a anthu a Mulungu.a

“Yandikilani Mulungu, ndipo iyenso adzakuyandikilani.”—Yakobo 4:8

PEMPHELO LIMATITHANDIZA KUKHALA BWENZI LA MULUNGU

Baibulo limakamba kuti Yehovab Mulungu amadziŵa zonse. Koma limaonetsanso kuti samakhalila kungodziŵa zinthu zokhudza alambili ake. (Salimo 139:6; Aroma 11:33) Mulungu amawadziŵa bwino kwambili anthu kusiyana ndi kompyuta imene imangosunga zinthu zokhudza anthuwo. Ndipo, Mulungu amafunitsitsa kudziŵa zimene tiganiza, cifukwa amafuna kuti tikhale paubwenzi wolimba ndi iye. (Salimo 139:23, 24; Yakobo 4:8) Ndiye cifukwa cake Yesu analimbikitsa otsatila ake kupemphela, ngakhale kuti Atate ake amadziŵa zosoŵa zathu. (Mateyu 6:6-8) Tikamapemphela nthawi zonse kwa Mlengi wathu tidzakhala paubwenzi wolimba ndi iye.

Nthawi zina, tingalephele kuzindikila zinthu zofunika zimene tiyenela kupemphelela. Koma Mulungu angadziŵe zenizeni zimene tifunikila ndipo angatipatse zinthuzo cifukwa amadziŵa zonse. (Aroma 8:26, 27; Aefeso 3:20) Tikadziŵa kuti Mulungu waloŵelelapo kutithandiza, ngakhale m’zinthu zazing’ono, ubwenzi wathu ndi iye ungalimbe.

KODI MULUNGU AMAYANKHA MAPEMPHELO ONSE?

Baibulo limatiuza kuti Mulungu Wamphamvuyonse amayankha mapemphelo a atumiki ake okhulupilika. Koma limapelekanso cifukwa cake samamvetsela mapemphelo ena. Mwacitsanzo, pamene ciwawa cinafala mu Isiraeli, Mulungu anauza mneneli wake Yesaya kuti auze anthu kuti: “Ngakhale mupeleke mapemphelo ambili, ine sindimvetsela. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.” (Yesaya 1:15) Zimenezi zionetsa kuti anthu amene amaphwanya malamulo a Mulungu kapena amene amapemphela ndi zolinga zoipa, mapemphelo ao sangayankhidwe.—Miyambo 28:9; Yakobo 4:3.

Ndiponso, Baibulo limati: “Ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.” (1 Yohane 5:14) Koma, kodi zimenezi zitanthauza kuti Mulungu amayankha mapemphelo onse a olambila ake? Iyai. Ganizilani citsanzo ca Paulo. Iye anapempha Mulungu katatu kuti amucotsele “munga m’thupi.” (2 Akorinto 12:7, 8) Mwina Paulo anali ndi vuto lalikulu la maso. Zioneka kuti anavutika kwambili ndi matendawo. Iye anali ndi mphamvu zocilitsa ndi zoukitsa anthu, koma anali kuvutikabe ndi matenda. (Machitidwe 19:11, 12; 20:9, 10) Ngakhale kuti mapemphelo ake sanayankhidwe mmene anali kufunila, Paulo anayamikila thandizo la Yehova.—2 Akorinto 12:9, 10.

“Ifetu timamudalila kuti ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, amatimvela.”—1 Yohane 5:14

N’zoona kuti mapemphelo a anthu ena a m’Baibulo anayankhidwa mozizwitsa. (2 Mafumu 20:1-7) Koma mapemphelo ambili sanali kuyankhidwa mwa njila imeneyi ngakhale m’nthawi za m’Baibulo. Anthu ena a Mulungu anali kukhumudwa akaona kuti Mulungu sayankha mapemphelo ao. M’pemphelo lake Mfumu Davide anafunsa kuti: “Kodi mudzandiiŵala kufikila liti? Mpaka muyaya?” (Salimo 13:1) Koma pamene Davide anazindikila kuti Yehova anam’teteza nthawi zambili, cidalilo cake mwa Mulungu cinakula. M’pemphelo limenelo Davide anapitiliza kuti: “Koma ine ndakhulupilila kukoma mtima kwanu kosatha.” (Salimo 13:5) Mofanana ndi Davide, masiku ano atumiki a Mulungu ayenela kupitilizabe kupemphela mpaka Mulungu atawapatsa zopempha zao.—Aroma 12:12.

MMENE MULUNGU AMAYANKHILA MAPEMPHELO

Mulungu amatipatsa zimene tifunikiladi.

Nthawi zina, makolo acikondi samapatsa ana ao zinthu zimene apempha panthawi imeneyo. Mofananamo, nthawi zina Mulungu sangatipatse zinthu zimene tifuna panthawi imene tikuzifuna. Koma timakhulupilila kuti Mlengi wathu adzatipatsa zinthu zimene tifunikiladi panthawi yoyenela ndipo m’njila yoyenela, monga mmene tate wacikondi amacitila.—Luka 11:11-13.

Mulungu angayankhe m’njila imene sitingazindikile.

Koma bwanji ngati takhala tikupempha thandizo pa vuto limene lativuta kwa nthawi yaitali? Kodi tingaganize kuti cifukwa cakuti palibe ciliconse cacitika ndiye kuti Yehova sanatiyankhe? Iyai sitingatelo. Koma tingacite bwino kuona ngati Yehova waticilikiza m’njila imene sitinazindikile. Mwacitsanzo, mwina mnzathu anatithandiza panthawi imene tinali kufuna kwambili thandizo. (Miyambo 17:17) Kodi zingakhale kuti ndi Yehova anasonkhezela mnzathuyo? Ndiponso, Yehova amayankha mapemphelo athu kupyolela m’Baibulo. Tikaŵelenga Baibulo tingapeze mfundo zothandiza kuti tilimbane ndi mavuto athu.—2 Timoteyo 3:16, 17.

M’malo mocosapo vuto lathu, nthawi zambili Mulungu amatipatsa mphamvu kuti tipilile vutolo. (2 Akorinto 4:7) Mwacitsanzo, pamene Yesu anapempha kuti Atate ake acotse ciyeso cake, Yehova anatumiza mngelo kukam’limbikitsa kuti dzina la Mulungu lisacitidwe citonzo. (Luka 22:42, 43) Mofananamo, Mulungu angagwilitsile nchito mnzathu kutiuza mau olimbikitsa a panthawi yake. (Miyambo 12:25) Popeza sitingazindikile kuti Mulungu watiyankha mwa njila imeneyo, tiyenela kukhala chelu kuti tidziŵe mmene Mulungu amayankhila mapemphelo athu.

Mulungu amayankha panthawi yake.

Baibulo limanena kuti Mulungu Wamphamvuyonse amathandiza anthu odzicepetsa ‘panthawi yake.’ (1 Petulo 5:6) Conco, ngati zimene timapempha siziyankhidwa mwamsanga, tisaone monga kuti Yehova sasamala za ife. Koma cifukwa cakuti Mlengi wathu amadziŵa zambili, iye amaona ngati zimene tipempha n’zofunikiladi.

“Conco dzicepetseni pansi pa dzanja lamphamvu la Mulungu, kuti adzakukwezeni m’nthawi yake.”—1 Petulo 5:6

Mwacitsanzo: Tinene kuti mwana wanu wamng’ono wakupemphani kuti mum’gulile njinga, kodi mungam’gulile nthawi imeneyo? Ngati muona kuti akali wamng’ono cakuti sangapalase njinga, mungafune kuyembekezela. Koma m’kupita kwa nthawi, mungagule mukaona kuti angathe kupalasa. Mofananamo, Mulungu angatipatse “zokhumba za mtima [wathu]” panthawi yake ngati tipitilizabe kupemphela.—Salimo 37:4.

KHULUPILILANI KUTI YEHOVA AMATIMVELA

Baibulo limalimbikitsa Akristu oona kusapeputsa mphamvu ya pemphelo. Koma ena anakambe kuti: ‘Zimenezo n’zosavuta kunena, koma n’zovuta kucita.’ Ngati takhala ndi vuto linalake kwanthawi yaitali kapena kucitidwa nkhanza, tingaone monga kuti Mulungu sayankha mwamsanga. Ngati zili conco, ndi bwino kukumbukila zimene Yesu anakamba zokhudza kulimbikila kupemphela.

Yesu anakamba fanizo la mkazi wa masiye wosauka amene anali kupita kwa woweluza wosalungama kukapempha thandizo. (Luka 18:1-3) Ngakhale kuti woweluza ameneyu poyamba anali kukana kumthandiza, potsilizila pake anati: “Ndicita zimenezi kuti asapitilize kumangobwela ndi kundisautsa kwambili, cifukwa mkazi ameneyu akundivutitsa mosalekeza.” (Luka 18:4, 5) Ngati woweluza wosalungamayo anathandiza mkazi wamasiye ameneyo cifukwa coopa kuti dzina lake lingacitidwe citonzo, kodi Mulungu wacifundo sangawacitile mwacilungamo anthu “amene amafuulila kwa iye usana ndi usiku?” Monga mmene Yesu anakambila, Mulungu “adzaonetsetsa kuti cilungamo cacitika kwa io mwamsanga.”—Luka 18:6-8.

Ngakhale kuti takhala tikupempha thandizo kwa nthawi yaitali, sitiyenela kuleka kupempha. Kupitilizabe kupempha kumaonetsa kuti timafunitsitsa thandizo la Mulungu paumoyo wathu. Ndipo kumatithandizanso kuona mmene Mulungu amayankhila mapemphelo athu. Kucita zimenezi kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi iye.—Luka 11:9.

a Ngati tifuna kuti Mulungu azimvela mapemphelo athu, tiyenela kucita zimene amafuna ndi mtima wonse. Tikacita zimenezo tidzaona kufunika kwa pemphelo, monga mmene nkhani ino ifotokozela. Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani 17 m’buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni, yofalitsidwa ndi Mboni za Yehova. Mungaonenso Webusaiti yathu ya www.jw.org.

b Baibulo limanena kuti dzina la Mulungu ndi Yehova.

“Pemphanibe, ndipo adzakupatsani.”—Luka 11:9

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani