NKHANI 17
Yandikilani kwa Mulungu Kupitila M’pemphelo
N’cifukwa ciani tiyenela kupemphela kwa Mulungu?
Kodi tiyenela kucita ciani kuti Mulungu azimvela mapemphelo athu?
Kodi Mulungu amawayankha bwanji mapemphelo athu?
“Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi” ali wofunitsitsa kumvela mapemphelo athu
1, 2. N’cifukwa ciani tiyenela kuona pemphelo kukhala mwai waukulu? Ndipo n’cifukwa ciani tiyenela kudziŵa zimene Baibo imakamba pa nkhani ya pemphelo?
DZIKO LAPANSI ndi kanthu kakang’ono kwambili poliyelekezela ndi cilengedwe conse. Ndipo kwa Yehova, “Wopanga kumwamba ndi dziko lapansi,” mitundu ya anthu ili ngati kadontho kamadzi kocokela mu mgomo. (Salimo 115:15; Yesaya 40:15) Ngakhale ni conco, Baibo imakamba kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’coonadi. Adzakwanilitsa zokhumba za anthu amene amamuopa, ndipo adzamva kufuula kwao kopempha thandizo.” (Salimo 145:18, 19) Ganizani cabe zimenezi! Mlengi wa cilengedwe conse ali pafupi ndi ife, ndipo adzachela khutu kwa ife ngati ‘tiitana kwa iye m’coonadi.’ Kunena zoona, tili ndi mwai wosaneneka wokamba ndi Mulungu m’pemphelo.
2 Koma ngati tifuna kuti Yehova azimvela mapemphelo athu, tiyenela kupemphela kwa iye m’njila imene amavomeleza. Koma zimenezi sizingatheke ngati sitimvetsetsa zimene Baibo imakamba pa nkhani ya pemphelo. Conco, tifunikila kudziŵa zimene Malemba amakamba pa nkhani ya pemphelo. Zimenezi n’zofunika kwambili cifukwa pemphelo limatithandiza kuyandikila kwa Yehova.
N’CIFUKWA CIANI TIYENELA KUPEMPHELA KWA YEHOVA?
3. Kodi n’cifukwa cacikulu citi cimene tiyenela kupemphelela kwa Yehova?
3 Cifukwa cacikulu cimene tiyenela kupemphelela kwa Yehova n’cakuti, iye mwini wake, ndiye amatipempha kuti tizipemphela kwa iye. Mau ake amatilimbikitsa kuti: “Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo, pamodzi ndi ciyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” (Afilipi 4:6, 7) Kunena zoona, kungakhale kusaganiza bwino ngati tinyalanyaza mwai wa pemphelo umene Wolamulila Wamkulu wa cilengedwe conse wapeleka kwa ife mwacikondi.
4. Kodi kupemphela kwa Yehova nthawi zonse kumalimbikitsa bwanji ubwenzi wanu ndi iye?
4 Cifukwa cina copemphelela n’cakuti kupemphela kwa Yehova nthawi zonse kumalimbitsa ubwenzi wathu ndi iye. Mabwenzi eni-eni sakambitsana cabe pamene wina afuna cinthu kwa mnzake. Amakhala ndi cidwi cofuna kudziŵa za umoyo wa wina ndi mnzake. Ubwenzi wao umalimbilako nthawi zonse pamene auzana maganizo ao ndi nkhawa zao. N’cimodzi-modzi ndi ubwenzi wathu ndi Yehova Mulungu. M’buku lino, mwaphunzila zambili zimene Baibo imaphunzitsa za Yehova, makhalidwe ake, ndi zolinga zake. Tsopano mwadziŵa kuti iye aliko zoona, ndipo mukhoza kukhala naye paubwenzi. Pemphelo limakupatsani mpata wouzako Atate wanu wakumwamba maganizo anu ndi nkhani za kukhosi kwanu. Ndipo pocita zimenezo, mumayandikila kwambili kwa Yehova.—Yakobo 4:8.
KODI TIFUNIKILA KUCITA ZINTHU ZITI KUTI YEHOVA AZIMVELA MAPEMPHELO ATHU?
5. Kodi n’ciani cimaonetsa kuti si mapemphelo onse amene Yehova amamvela?
5 Kodi Yehova amamvela mapemphelo onse? Ganizilani zimene iye anauza Aisiraeli opanduka m’masiku a mneneli Yesaya: “Ngakhale mupeleke mapemphelo ambili, ine sindimvetsela. Manja anu adzaza magazi amene mwakhetsa.” (Yesaya 1:15) Conco, pali zocita zina zimene zingapangitse Mulungu kusamvela mapemphelo athu. Kuti Mulungu azimvela mapemphelo athu, pali zinthu zina zimene tifunikila kucita.
6. Kodi cofunika coyambilila n’ciani kuti Mulungu azimvela mapemphelo athu? Ndipo tingacionetse bwanji?
6 Cinthu cofunika kwambili n’cakuti tikhale ndi cikhulupililo. (Maliko 11:24) Mtumwi Paulo analemba kuti: “Popanda cikhulupililo n’zosatheka kukondweletsa Mulungu. Pakuti aliyense wofika kwa Mulungu ayenela kukhulupilila kuti iye alikodi, ndi kuti amapeleka mphoto kwa anthu omufuna-funa ndi mtima wonse.” (Aheberi 11:6) Kukhala ndi cikhulupililo ceni-ceni sikutanthauza kudziŵa cabe kuti Mulungu aliko ndi kuti amamvela mapemphelo ndi kuwayankha. Cikhulupililo cimaonekela m’zocita zathu. Conco, zimene timacita tsiku ndi tsiku ziyenela kuonetsa kuti tili ndi cikhulupililo.—Yakobo 2:26.
7. (a) N’cifukwa ciani tiyenela kuonetsa ulemu pokamba ndi Yehova m’pemphelo? (b) Nanga tingaonetse bwanji kuti ndife odzicepetsa ndi oona mtima popemphela kwa Mulungu?
7 Yehova amafunanso kuti pom’fikila m’pemphelo tizikamba naye modzicepetsa ndi moona mtima. Kodi si zomveka kuti tiyenela kukhala odzicepetsa pokamba ndi Yehova? Pamene anthu akhala ndi mwai wokamba ndi mfumu kapena pulezidenti, amakamba naye mwaulemu cifukwa ca udindo wapamwamba umene ali nao. Nanga kuli bwanji kwa ife pamene tipemphela kwa Yehova! (Salimo 138:6) Ndi iko komwe, iye ali “Mulungu Wamphamvuyonse.” (Genesis 17:1) Tikamapemphela kwa Mulungu, tiyenela kukamba naye moonetsa kuti ndife otsika kwambili kwa iye. Kudzicepetsa kwa mtundu umenewu kudzatithandiza kumapemphela mocokela pansi pamtima, ndi kupewa mapemphelo a mwambo cabe, oloŵeza pamtima.—Mateyu 6:7, 8.
8. Kodi kucita zinthu mogwilizana ndi mapemphelo athu kumatanthauza ciani?
8 Cinthu cina cofunika kuti Mulungu azimvela mapemphelo athu ndico kucita mogwilizana ndi mapemphelo athu. N’zimene Yehova amayembekezela kwa ife. Mwacitsanzo, tikapemphela kuti, “Mutipatse ife lelo cakudya cathu ca lelo,” tiyenela kugwila nchito iliyonse imene ilipo kuti tipeze cakudya. (Mateyu 6:11; 2 Atesalonika 3:10) Tikapemphela kuti Mulungu atithandize kugonjetsa cofooka cina cake, tiyenela kuyesa-yesa kupewa anthu, zinthu, malo kapena mikhalidwe imene ingatibweletse mayeselo pa cofookaco. (Akolose 3:5) Kuonjezela pa zinthu zofunika zimenezi, palinso mafunso okhudza pemphelo amene tiyenela kudziŵa mayankho ake.
MAYANKHO PA MAFUNSO ENA OKHUDZA PEMPHELO
9. Kodi tiyenela kupemphela kwa ndani? Ndipo kupitila mwa ndani?
9 Kodi tiyenela kupemphela kwa ndani? Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kwa “Atate wathu wakumwamba.” (Mateyu 6:9) Conco, mapemphelo athu onse ayenela kupita kwa Yehova Mulungu cabe. Koma Yehova amafunanso kuti tizipemphela kwa iye kupitila m’dzina la Yesu Kristu. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti, monga tinaphunzilila m’Nkhani 5, Yesu ndi amene anatumizidwa padziko lapansi kuti adzatifele monga dipo lotiombola ku ucimo ndi imfa. (Yohane 3:16; Aroma 5:12) Ndi amenenso anaikidwa kukhala Mkulu wa Ansembe ndi Woweluza. (Yohane 5:22; Aheberi 6:20) Mwa ici, Malemba amatiuza kuti tiyenela kupeleka mapemphelo athu kupyolela mwa Yesu yekha. Iye mwini wake anakamba kuti: “Ine ndine njila, coonadi ndi moyo. Palibe amene amafika kwa Atate osadzela mwa ine.” (Yohane 14:6) Inde, kuti Yehova amve mapemphelo athu, tiyenela kupemphela kwa iye yekha, kupitila mwa Mwana wake.
10. N’cifukwa ciani palibe kakhalidwe kapadela kofunikila popemphela?
10 Kodi pali kakhalidwe kapadela kofunikila popemphela? Iyai. Popemphela, sikuti pali mtundu winawake wa kakhalidwe, kaimililidwe, kagwadidwe kapena kaikidwe ka manja kamene Yehova amafuna iyai. Baibo imaonetsa kuti tingapemphele m’kakhalidwe kosiyana-siyana. Tingapemphele cokhala pansi, coŵelama, cogwada, kapena coimilila. (1 Mbiri 17:16; Nehemiya 8:6; Danieli 6:10; Maliko 11:25) Cofunika kweni-kweni popemphela, si kaimidwe kapena kakhalidwe kuti ena aone iyai, koma zimene zili mu mtima mwathu. Ndipo pamene tikumana ndi vuto lililonse paumoyo wathu wa tsiku ndi tsiku, tikhoza kupemphela ngakhale ca mumtima kuli konse kumene tingakhale. Yehova amamvela mapemphelo amenewo ngakhale pamene ena amene alipo sanadziŵe kuti tapemphela.—Nehemiya 2:1-6.
11. Kodi ndi nkhani zaumwini ziti zimene tingapemphelele?
11 Kodi ndi nkhani zanji zimene tingapemphelele? Baibo imafotokoza kuti: “Ciliconse cimene tingamupemphe mogwilizana ndi cifunilo cake, [Yehova] amatimvela” (1 Yohane 5:14) Conco, tingapemphelele cinthu ciliconse malinga n’cogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu. Koma kodi kupemphelela nkhawa za umoyo wathu nako n’kogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu? N’zosacita kufunsa! Kupemphela kwa Yehova kungakhale monga kukamba ndi mnzathu wa pamtima. Pokamba ndi Mulungu m’pemphelo, tikhoza ‘kum’khuthulila za kumtima kwathu.’ (Salimo 62:8) Tiyenelanso kupempha mzimu woyela, cifukwa umatithandiza kucita zinthu zoyenela. (Luka 11:13) Komanso, tifunika kumapempha Mulungu kuti azitithandiza kupanga zosankha zanzelu, ndi kuti azitipatsa mphamvu zakuti tipilile mavuto. (Yakobo 1:5) Tikacita chimo, tiyenela kupempha cikhululukilo kupitila mu nsembe ya Kristu. (Aefeso 1:3, 7) Komabe, si bwino kuti nthawi zonse tizingopemphelela nkhani zathu cabe. Nthawi zina tizipemphelelako anthu ena—acibanja athu ndi amene timalambila nao.—Machitidwe 12:5; Akolose 4:12.
12. Kodi tingaonetse bwanji kuti m’mapemphelo athu timaika patsogolo nkhani zokhudza Atate wathu wakumwamba?
12 Koma nkhani zokhudza Yehova Mulungu n’zimene tiyenela kuika patsogolo m’mapemphelo athu. Tiyenela kum’tamanda ndi mtima wonse ndi kumuyamikila pa zabwino zonse zimene amaticitila. (1 Mbiri 29:10-13) Yesu anapeleka pemphelo la citsanzo pa Mateyu 6:9-13. M’pemphelo limenelo, coyamba Yesu amatiphunzitsa kupemphela kuti dzina la Mulungu liyeletsedwe, kutanthauza kuti, tiyenela kuliona kukhala lopatulika, kapena kuti loyela. Cotsatila, anachula zakuti Ufumu wa Mulungu ubwele ndi kuti cifunilo cake cicitike padziko lapansi mofanana ndi kumwamba. Pambuyo pochula nkhani zofunika zokhudza Yehova zimenezi, m’pamene Yesu anachula zinthu zaumwini zimene tingapemphelele. Ngati ifenso tiika za Mulungu patsogolo m’mapemphelo athu, tidzaonetsa kuti sitimaganizila za ubwino wathu cabe.
13. Kodi Malemba amaonetsa ciani ponena za utali wa mapemphelo amene Mulungu amamvela?
13 Kodi mapemphelo athu ayenela kukhala aatali bwanji? Baibo siichula utali umene mapemphelo aumwini kapena apagulu ayenela kutenga. Pemphelo lingakhale lalifupi cabe lopemphelela cakudya, kapena lingakhale lalitali la pawekha pamene tingauze Yehova zonse za kukhosi kwathu. (1 Samueli 1:12, 15) Komabe, Yesu anadzudzula anthu amene anali kudziona kukhala olungama, amenenso anali kupeleka mapemphelo aatali odzionetsela pamaso pa anthu. (Luka 20:46, 47) Mapemphelo a conco sakondweletsa Yehova iyai. Cofunika n’cakuti tizipemphela mocokela pansi pa mtima. Conco, mapemphelo amene Mulungu amamvela angakhale aatali kapena aafupi, malinga ndi zimene mupempha ndi mikhalidwe imene ilipo.
Mulungu angamvele pemphelo lanu pa nthawi iliyonse
14. Kodi Baibo imatanthauza ciani pamene imatiuza kuti ‘pemphelani kosalekeza’? Ndipo n’cifukwa ciani zimenezi n’zolimbikitsa?
14 Kodi tiyenela kupemphela kangati patsiku? Baibo imatilimbikitsa kuti “pemphelani kosalekeza,” “limbikilani kupemphela,” ndi kuti ‘pemphelani nthawi zonse, osaleka.’ (Mateyu 26:41; Aroma 12:12; Luke 18:1) Mau amenewa satanthauza kuti tizingocomela kupemphela kwa Yehova tsiku lonse iyai. M’malo mwake, Baibo imatilimbikitsa kupemphela nthawi ndi nthawi, kuyamikila Yehova pa zabwino zimene amaticitila. Ndiponso tiyenela kumam’pempha kuti azititsogolela, kutilimbikitsa ndi kutipatsa mphamvu. N’zolimbikitsa kuti Yehova sanatiikile utali wa pemphelo, kapena nthawi zimene tiyenela kupemphela kwa iye patsiku. Ngati timayamikiladi mwai wa pemphelo, tidzapeza mipata yambili yopemphela kwa Atate wathu wakumwamba.
15. N’cifukwa ciani tiyenela kukamba kuti ‘Ameni’ kumapeto kwa mapemphelo aumwini ndi apagulu?
15 N’cifukwa ciani tiyenela kukamba kuti ‘Ameni’ kumapeto kwa pemphelo? Mau akuti ‘ameni’ amatanthauza kuvomeleza kuti “ndithudi,” kapena kuti “zikhale mmenemo.” Zitsanzo za m’Baibo zimaonetsa kuti n’koyenela kukamba kuti ‘Ameni’ kumapeto kwa pemphelo laumwini kapena la pagulu. (1 Mbiri 16:36; Salimo 41:13) Mwa kukamba kuti ‘Ameni’ kumapeto kwa pemphelo laumwini, timaonetsa kuti zimene takamba zacokeladi pansi pamtima. Pamene tikamba kuti ‘Ameni’ kumapeto kwa pemphelo la pagulu, kaya ca mumtima kapena motulutsa mau, timaonetsa kuti tagwilizana ndi zimene zakambidwa.—1 Akorinto 14:16.
MMENE MULUNGU AMAYANKHILA MAPEMPHELO ATHU
16. Kodi tili ndi cidalilo canji ponena za mapemphelo?
16 Kodi n’zoona kuti Yehova amayankha mapemphelo? Inde, amayankha. Ndipo sitikaikila ngakhale pang’ono kuti “Wakumva pemphelo” amayankha mapemphelo ocokela pansi pamtima, opelekedwa ndi anthu mamiliyoni ambili. (Salimo 65:2) Koma Yehova amayankha mapemphelo athu m’njila zosiyana-siyana.
17. Poyankha mapemphelo a anthu, kodi Mulungu amaseŵenzetsa bwanji angelo ndi atumiki ake a padziko?
17 Poyankha mapemphelo a anthu, Yehova amagwilitsila nchito angelo ndi atumiki ake a padziko lapansi. (Aheberi 1:13, 14) Pakhala zocitika zambili za anthu amene anapemphela kwa Mulungu kuti awathandize kumvetsa Baibo, ndipo posapita nthawi mmodzi wa atumiki a Yehova anawafikila. Zocitika zimenezi zimapeleka umboni wakuti angelo amatitsogolela pamene tili m’nchito yolalikila za Ufumu. (Chivumbulutso 14:6) Kuti Yehova ayankhe mapemphelo amene anthu amapeleka panthawi imene afunikadi thandizo, angagwilitsile nchito Mkristu wina kuti akawathandize.—Miyambo 12:25; Yakobo 2:16.
Kuti Yehova ayankhe mapemphelo athu, angagwilitsile nchito Mkristu mnzathu kutithandiza pa zimene tapempha
18. Kodi Yehova amagwilitsila nchito bwanji mzimu wake woyela ndi Mau ake, kuyankha mapemphelo a atumiki ake?
18 Yehova Mulungu amagwilitsilanso nchito mzimu wake woyela ndi Mau ake, Baibo, kuti ayankhe mapemphelo a atumiki ake. Mwacitsanzo, pamene tipempha thandizo lakuti tipilile mayeselo, iye angayankhe mapemphelo athu mwa kutitsogolela ndi kutipatsa mphamvu kupitila mwa mzimu wake woyela. (2 Akorinto 4:7) Ngati mapemphelo athu ndi opempha citsogozo, nthawi zambili Yehova amatiyankha kupitila m’Baibo, mmene muli malangizo ake otithandiza kupanga zosankha zanzelu. Tingapeze malemba othandiza pamene ticita phunzilo laumwini la Baibo, ndi pamene tiŵelenga mabuku acikristu monga lino. Komanso, pamene tili pamsonkhano wa mpingo tingamve mfundo za m’Malemba zofunika kuziganizilapo. Ndiponso nthawi zina, mkulu pampingo amene amatiganizila angatiuze mfundo zimenezo.—Agalatiya 6:1.
19. Kodi tiyenela kukumbukila ciani pamene mapemphelo athu aoneka monga sayankhidwa?
19 Ngati Yehova aoneka monga wacedwa kuyankha mapemphelo athu, sizitanthauza kuti walephela kutiyankha iyai. Tiyenela kukumbukila kuti Iye amayankha mapemphelo mogwilizana ndi cifunilo cake, ndiponso panthawi yake. Amadziŵa bwino zimene timafunikila ndi mmene tingazipezele kuposa ife eni. Kaŵili-kaŵili amatilola kuti ‘tipitilize kupempha, kufuna-funa ndi kugogoda.’ (Luka 11:5-10) Kulimbikila kwa conco kumaonetsa Mulungu kuti ndife ofunitsitsa kupemphela, ndipo timakhulupilila ndi mtima wonse kuti adzatiyankha. Ndiponso, Yehova angayankhe mapemphelo athu mwa njila imene sitingaizindikile kweni-kweni. Mwacitsanzo, angayankhe pemphelo lathu lokhudza mayeselo ena ake, osati mwa kuwacotsa, koma mwa kutipatsa mphamvu yakuti tiwapilile.—Afilipi 4:13.
20. N’cifukwa ciani tiyenela kuugwilitsila nchito mokwana mwai wapadela wa pemphelo?
20 Tiyenela kukhala oyamikila kwambili kuti Mlengi wa cilengedwe conse ali pafupi ndi anthu onse amene amapemphela kwa iye m’njila yoyenela. (Salimo 145:18) Tiyeni tiugwilitsile nchito mokwana mwai wapadela umenewu wokamba ndi Mulungu m’pemphelo. Tikacita zimenezi, cidzakhala cotheka kuti timuyandikile kwambili Yehova, amene ndi Wakumva pemphelo.