LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 5/1 masa. 8-12
  • Mmene ‘Tingayankhile Munthu Wina Aliyense’

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene ‘Tingayankhile Munthu Wina Aliyense’
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • FUNSANI MAFUNSO KUTI MUDZIŴE MAGANIZO A MWININYUMBA
  • KAMBILANANI ZIMENE MALEMBA AMANENA
  • GWILITSILANI NCHITO MAFANIZO KUTI MUMVEKETSE MFUNDO
  • ONANI ZINTHU MOYENELA
  • Makolo, Thandizani Ana Anu Kukhala na Cikhulupililo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2016
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 5/1 masa. 8-12

Mmene ‘Tingayankhile Munthu Wina Aliyense’

“Nthawi zonse mau anu azikhala acisomo, . . . kuti mudziŵe mmene mungayankhile wina aliyense.”—AKOL. 4:6.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani kufunsa mafunso omvela athu mwauluso n’kofunika?

  • N’ciani cingatithandize kukambitsilana Malemba mwaluso?

  • Ndi motani mmene tingagwilitsile nchito mafanizo mwaluso mu ulaliki?

1, 2. (a) Fotokozani cocitika cimene cionetsa phindu lofunsa mafunso oyenelela. (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) N’cifukwa ciani sitiyenela kucita mantha kukambitsilana ndi anthu nkhani zovuta?

ZAKA zingapo zapita, mlongo wina anali kukambitsilana Baibulo ndi mwamuna wake wosakhulupilila. Kale, mwamuna wake anali kupita ku chalichi mwa apa ndi apo. Pamene anali kukambitsilana, mwamuna wake anakamba kuti amakhulupilila Utatu. Iye atazindikila kuti mwamuna wake sanali kudziŵa zenizeni zokhudza ciphunzitso ca Utatu, mwaluso anamufunsa kuti: “Kodi mumakhulupilila kuti Mulungu ndi Mulungu, Yesu naye ndi Mulungu ndi kuti mzimu woyela naonso ndi Mulungu; ndiponso kuti io si Milungu itatu koma ndi Mulungu mmodzi?” Mwamuna wake anadabwa ndi kukamba kuti: “Iyai, sindimakhulupilila zimenezo!” Ndiyeno io anakambitsilana zoonjezeleka zokhudza Mulungu woona.

2 Cocitika cimeneco cionetsa phindu lofunsa mafunso oyenelela mwaluso. Ndiponso cionetsa mfundo yofunika yakuti: Sitiyenela kucita mantha kukambitsilana ndi anthu nkhani zovuta monga za Utatu, moto wa helo kapena nkhani ya kukhalapo kwa Mlengi. Ngati timadalila Yehova ndi maphunzilo ake, tingapeleke mayankho ogwila mtima. (Akol. 4:6) M’nkhani ino, tikambilana mmene tingakhalile aphunzitsi aluso mwa (1) kufunsa mafunso kuti tidziŵe maganizo a mwininyumba, (2) kukambitsilana zimene Malemba amanena, ndi (3) kugwilitsila nchito mafanizo kuti timveketse mfundo.

FUNSANI MAFUNSO KUTI MUDZIŴE MAGANIZO A MWININYUMBA

3, 4. N’cifukwa ciani kugwilitsila nchito mafunso n’kofunika? Pelekani citsanzo.

3 Mafunso angatithandize kudziŵa zimene munthu amakhulupilila. N’cifukwa ciani mafunso ndi ofunika? Lemba la Miyambo 18:13 limati: “Munthu aliyense woyankhila nkhani asanaimvetsetse n’ngopusa, ndipo amacita manyazi.” Tisanakambitsilane ndi munthu nkhani inayake ya m’Baibulo, tingacite bwino coyamba kudziŵa zimene munthuyo amakhulupilila. Tikacita zimenezo, tidzapewa kuononga nthawi yathu kumuonetsa kuti zimene amakhulupilila n’zolakwika pamene si zimene iye amakhulupilila.—1 Akor. 9:26.

4 Tinene kuti tikukambitsilana ndi munthu nkhani ya helo. Ambili amakhulupilila kuti helo ndi malo ozunzilako anthu oipa. Conco, tingam’funse kuti: “Popeza kuti anthu ali ndi maganizo osiyanasiyana ponena za helo, nanga inu muganiza bwanji?” Tikamva maganizo ake, tingadziŵe mmene tingam’thandizile kuti adziŵe zimene Baibulo limanena pankhani ya helo.

5. Kodi kufunsa mafunso kungatithandize bwanji kudziŵa cifukwa cake womvela wathu amakhulupilila nkhani inayake?

5 Kufunsa mafunso mwaluso kungatithandizenso kudziŵa cifukwa cake womvela wathu amakhulupilila nkhani inayake. Mwacitsanzo, bwanji ngati munthuyo akamba kuti samakhulupilila Mulungu? Mwacionekele tingaganize kuti iye amatengela maganizo a anthu, monga ciphunzitso ca cisanduliko. (Sal. 10:4) Komabe, anthu ena samakhulupilila Mulungu cifukwa ca mavuto aakulu amene io kapena anthu ena amakumana nao. Iwo angalephele kumvetsetsa cifukwa cake Mlengi wacikondi amalola mavuto. Conco, ngati mwininyumba amakaikila zakuti Mulungu aliko, tingam’funse kuti, “Kodi amenewo ndiwo maganizo anu kuyambila kale?” Ngati munthuyo ayankha kuti iyai, tingam’funse cifukwa cake anayamba kukaikila ngati Mulungu aliko. Yankho lake lingatithandize kudziŵa mmene tingam’thandizile.—Ŵelengani Miyambo 20:5.

6. Tikafunsa mwininyumba funso, kodi tiyenela kucita ciani?

6 Tikafunsa funso, tiyenela kumvetsela mosamalitsa yankho la mwininyumba ndi kuona mmene zikum’khudzila. Mwacitsanzo, wina angatiuze kuti zinthu zacisoni zimene zinam’citikila zinacititsa kuti azikaikila ngati Mlengi wacikondi aliko. Tisanapeleke umboni wakuti Mulungu aliko, tingacite bwino kumuonetsa kuti nafenso takhudzidwa ndi kumufotokozela kuti sikulakwa kuganiza cifukwa cake timavutika. (Hab. 1:2, 3) Kudekha ndi kukambitsilana naye mwacikondi zingacititse munthuyo kufuna kuphunzila zambili.a

KAMBILANANI ZIMENE MALEMBA AMANENA

7. Kodi kulalikila mogwila mtima kumadalila pa ciani makamaka?

7 Tsopano tiyeni tione mmene tingakambitsilane ndi mwininyumba zimene Malemba amanena. Baibulo ndico cida cofunika cimene timagwilitsila nchito mu ulaliki. Limatithandiza kukhala ‘okonzeka mokwanila kucita nchito iliyonse yabwino.’ (2 Tim. 3:16, 17) Kulalikila mogwila mtima sikumadalila pa ciŵelengelo ca malemba amene taŵelenga, koma mmene timawafotokozela malembawo. (Ŵelengani Machitidwe 17:2, 3.) Tiyeni tikambilane zitsanzo zitatu za mmene tingacitile zimenezi.

8, 9. (a) Kodi tingakambitsilane bwanji ndi munthu amene amakhulupilila kuti Yesu ndi wolingana ndi Mulungu? (b) Ndi kukambitsilana kwina kuti kumene inu mwapeza kuti n’kothandiza?

8 Citsanzo 1: Tikakumana ndi munthu mu ulaliki amene amakhulupilila kuti Yesu ndi wolingana ndi Mulungu. Ndi malemba ati amene tingagwilitsile nchito pokambitsilana naye nkhaniyi? Mwina tingaŵelenge naye lemba la Yohane 6:38, pamene Yesu anati: “Ndinatsika kucokela kumwamba kudzacita cifunilo ca iye amene anandituma, osati cifunilo canga.” Pambuyo poŵelenga lembali, tingam’funse kuti: “Ngati Yesu ndi Mulungu, ndani anam’tuma kubwela padzikoli? Kodi Ameneyo sangakhale wamkulu kuposa Yesu? Kodi munthu wotuma mnzake samakhala ndi ulamulilo kuposa wotumidwayo?”

9 Tingaŵelengenso Afilipi 2:9, pamene mtumwi Paulo anafotokoza zimene Mulungu anacita pambuyo pakuti Yesu wafa ndi kuukitsidwa. Lembali limati: “Mulungu anamukweza [Yesu] n’kumuika pamalo apamwamba. Ndipo anamukomela mtima n’kumupatsa dzina loposa lina lililonse.” Kuti tim’thandize munthuyo kumvetsetsa nkhaniyi, tingam’funse kuti: “Ngati Yesu asanafe anali wolingana ndi Mulungu ndipo pambuyo pake Mulungu anamukweza ndi kumuika pamalo apamwamba, kodi zimenezo sizikanacititsa Yesu kukhala wamkulu kuposa Mulungu? Koma kodi pali wina angakhale wamkulu kuposa Mulungu?” Ngati munthuyo amalemekeza Mau a Mulungu ndipo amafunitsitsa kuphunzila, kukambilana kwa conco kungam’cititse kufuna kuphunzila zambili.—Mac. 17:11.

10. (a) Tingakambitsilane bwanji ndi munthu amene amakhulupilila moto wa helo? (b) Ndi kukambitsilana kwina kuti kumene inu mwapeza kuti n’kothandiza pankhani ya helo?

10 Citsanzo 2: Ngati munthu wacipembedzo kwambili amavutika kukhulupilila kuti anthu oipa sadzazunzika kwamuyaya m’moto wa helo. Mwina munthuyo amakhulupilila zimenezi cifukwa amafuna kuti anthu oipa akalandile cilango cifukwa ca zoipa zimene anacita. Kodi tingakambitsilane naye bwanji munthu amene amaganiza conco? Coyamba tingavomelezane naye kuti anthu oipa adzalandila cilango. (2 Ates. 1:9) Ndiyeno, tingaŵelenge naye lemba la Genesis 2:16, 17, limene limaonetsa kuti cilango caucimo ndi imfa. Tingam’fotokozele kuti ucimo wa Adamu unacititsa kuti anthu onse azibadwa ocimwa. (Aroma 5:12) Tingam’fotokozelenso kuti Mulungu sanamuuze kuti adzalandila cilango m’moto wa helo. Conco, tingam’funse kuti, “Ngati Adamu ndi Hava anayenela kulandila cilango camuyaya atacimwa, kodi sizikanakhala bwino kuwacenjezelatu?” Tingaŵelengenso Genesis 3:19, limene limanena za cilango cimene io anapatsidwa pambuyo pocimwa, koma silimanena zopita ku moto wa helo. M’malo mwake, Adamu anauzidwa kuti adzabwelela ku nthaka. Ndiyeno tingam’funse kuti, “Kodi cikanakhala cilungamo kuuza Adamu kuti adzabwelela ku nthaka ngati iye anali kudzapitadi ku moto wa helo?” Ngati munthuyo afunitsitsa kuphunzila, funsoli lingamucititse kuganizilapo kwambili pankhaniyi.

11. (a) Tingakambitsilane bwanji ndi munthu amene amakhulupilila kuti anthu onse abwino amapita kumwamba? (b) Ndi kukambitsilana kwina kuti kumene inu mwapeza kuti n’kothandiza pankhani yopita kumwamba?

11 Citsanzo 3: Tikakumana ndi munthu amene amakhulupilila kuti anthu onse abwino amapita kumwamba. Mfundoyi imakhudza mmene mwininyumba amadziŵila Baibulo. Mwacitsanzo, tinene kuti tikuŵelenga naye Chivumbulutso 21:4. (Ŵelengani.) Mwina munthuyo angaganize kuti madalitso amene akuchulidwa palembali akunena za mmene umoyo udzakhalila kumwamba. Kodi tingakambitsilane naye bwanji nkhaniyi? M’malo moŵelenga malemba ambili, tingangosumika maganizo pa mau a Chivumbulutso 21:4. Mau ake amati “imfa sidzakhalaponso.” Conco, tingam’funse kuti, “Kodi munganene kuti cinthu cina sicidzakhalaponso ngati cinthuco sicinakhalepo pa nthawi inayake?” Mwacionekele iye adzayankha kuti iyai. Ndiyeno tingam’fotokozele kuti imfa sinakhalepo kumwamba kucokela paciyambi. Imfa ili cabe pano padziko lapansi. Conco, n’zoonekelatu kuti lemba la Chivumbulutso 21:4 limanena za madalitso amtsogolo pano padziko lapansi.—Sal. 37:29.

GWILITSILANI NCHITO MAFANIZO KUTI MUMVEKETSE MFUNDO

12. N’cifukwa ciani Yesu anali kugwilitsila nchito mafanizo?

12 Yesu anali kugwilitsila nchito mafanizo pamene anali kulalikila. (Ŵelengani Mateyu 13:34, 35.) Mafanizo amenewa anam’thandiza kudziŵa ngati omvela ake anali ofunitsitsa kuphunzila ndi kutumikila Yehova. (Mat. 13:10-15) Yesu anagwilitsilanso nchito mafanizo kuti anthu azikumbukila zimene anali kuwaphunzitsa ndi kuti azisangalala kumvetsela kwa iye. Kodi tingagwilitsile nchito bwanji mafanizo pophunzitsa ena?

13. Kodi tingapeleke fanizo lotani kuti tionetse kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa Yesu?

13 Tiyenela kugwilitsila nchito mafanizo osavuta kumva. Mwacitsanzo, pophunzitsa munthu kuti Mulungu ndi wamkulu kuposa Yesu, tingagwilitsile nchito fanizo ili: Coyamba, tinganene kuti ubale umene ulipo pakati pa Mulungu ndi Yesu tingauyelekezele ndi ubale wa Atate ndi Mwana. (Luka 3:21, 22; Yoh. 14:28) Ndiyeno tingam’funse kuti: “Kodi anthu aŵili a m’banja limodzi angakhale olingana ngati ali paubale wotani?” Mwina munthuyo angayankhe kuti ngati io ndi mapasa. Akanena zimenezo, tingamuuze kuti: “Limenelo ndi fanizo labwino. Conco, ngati inu ndi ine tanena fanizo limeneli mosavuta, n’cifukwa ciani Yesu, Mphunzitsi Wamkulu, sanagwilitsile nchito fanizo lofanana ndi limeneli? M’malo mwake iye anakamba kuti Mulungu ndi Atate wake. Mwakunena zimenezo, Yesu anaonetsa kuti Mulungu ndi wamkulu ndipo ali ndi mphamvu kuposa iye.”

14. Ndi fanizo liti limene lionetsa kuti sikwanzelu kukhulupilila kuti Mulungu anaika Mdyelekezi kuti azizunza anthu m’moto wa helo?

14 Tiyeni tionenso citsanzo cina. Ena amakhulupilila kuti Mulungu anaika Satana kukhala woyang’anila ku helo. Mwina fanizo lingathandize kholo kuona kuti si kwanzelu kukhulupilila zimenezi. Mwina tingafunse kuti: “Tinene kuti mwana wanu wayamba kusamvela ndipo akucita zinthu zoipa kwambili, kodi mungacite ciani?” Mwacionekele, kholo linganena kuti lingacite zimene lingathe kuthandiza mwana wake kusiya khalidwe loipa. (Miy. 22:15) Kholo likanena conco, tingalifunse zimene lingacite ngati mwana wake akanilatu thandizo lililonse. Makolo ambili anganene kuti nthawi imeneyo mwanayo angafunike kupatsidwa cilango. Ndiyeno tingafunse kuti: “Bwanji ngati mwadziŵa kuti mwana wanu amasonkhezeledwa ndi munthu wina woipa kwambili?” Kholo lililonse lingam’kwiile munthu woipayo. Kuti timveketse mfundo ya fanizoli, tingafunse kholo kuti, “Kodi mungapeleke mwana wanu kwa munthu woipayo kuti am’patse cilango?” N’zoziŵikilatu kuti io anganene kuti sangatelo. Conco, Mulungu sangagwilitsile nchito Satana kuzunza anthu amene iye Mdyelekezi amawasonkhezela kucita zoipa.

ONANI ZINTHU MOYENELA

15, 16. (a) N’cifukwa ciani ena sangalandile uthenga wa Ufumu umene timalalikila? (b) Kodi kulalikila mwaluso kumangodalila pa kukhala aphunzitsi abwino? Fotokozani. (Onani bokosi lakuti ““Zimene Zingatithandize Kupeleka Yankho.”)

15 Timadziŵa kuti ena amene timalalikila sadzalandila uthenga wa Ufumu. (Mat. 10:11-14) Zimenezo zidzacitika ngakhale kuti timafunsa mafunso oyenela, timakambitsilana nao bwino, ndi kugwilitsila nchito mafanizo omveka ndi osavuta. Ndi ocepa amene analandila ziphunzitso za Yesu ngakhale kuti iye anali Mphunzitsi wamkulu kuposa onse amene anakhalako padziko lapansi.—Yoh. 6:66; 7:45-48.

16 Kumbali ina, ngakhale kuti timadziona kuti sindife aphunzitsi abwino, tingalalikile mwaluso. (Ŵelengani Machitidwe 4:13.) Mau a Mulungu amatithandiza kukhala ndi cidalilo cakuti ‘onse amene ali ndi maganizo abwino amene angawathandize kupeza moyo wosatha’ adzalandila uthenga wabwino. (Mac. 13:48) Conco, tiyenela kukhala ndi maganizo oyenela ndi kuona moyenela anthu amene timapelekela uthenga wabwino wa ufumu. Ngati tidalila Yehova ndi ziphunzitso zake, tidzakhala aphunzitsi abwino. Ndipo zimenezi zidzapindulitsa ifeyo ndi onse otimvela. (1 Tim. 4:16) Yehova angatithandize kudziŵa mmene tingayankhile “wina aliyense.” M’nkhani yotsatila tidzaphunzila mmene kutsatila Khalidwe Lopambana kungatithandizile mu ulaliki.

a Onani nkhani yakuti, “Kodi N’zotheka Kuyamba Kukhulupilila Mlengi?” mu Nsanja ya Olonda ya October 1, 2009.

Zimene Zingatithandize Kupeleka Yankho

Zitsanzo zambili zimene zachulidwa m’nkhani ino zinatengedwa m’nkhani zakuti, “Kuceza ndi Munthu Wina.” Nkhani zimenezi zimapezeka nthawi ndi nthawi mu Nsanja ya Olonda yogaŵila.b

Mlongo wina anafotokoza mmene nkhani zimenezi zam’thandizila mu ulaliki. Iye analemba kuti: “Nkhani zimenezi zandithandiza kudziŵa mmene ndingakambitsilane bwino ndi munthu, mmene ndingafunsile munthu mafunso om’thandiza kuganiza, ndi mmene ndingamuyankhile mogwilizana ndi yankho limene wapeleka. Ndimaphunzila mwamsanga ndikasonyezedwa mocitila cinacake, conco nkhani zimenezi zandithandiza kwambili.”

Nkhanizi ndi njila imodzi imene Yehova amatithandizila kuti tikwanilitse nchito yaikulu imene watipatsa. (Sal. 32:8) Timayamikila kwambili kuti Yehova amatithandiza kukwanilitsa ulaliki wathu.

b Zina mwa nkhani zimene zafalitsidwa ndi izi: “Kodi Mzimu Woyela N’ciani?” (October 1, 2010); “Kodi Yesu Ndi Mulungu?” (April 1, 2012); “Kodi Anthu Onse Abwino Amapita Kumwamba?” (August 1, 2012); “Kodi Mulungu Amalanga Anthu Kumoto?” (October 1, 2012); “Kodi Mulungu Amamva Cisoni Tikamavutika?” (July 1, 2013) ndi yakuti “N’cifukwa Ciani Mulungu Amalola Kuti Anthufe Tizivutika?” (January 1, 2014).

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani