Muzionetsa Khalidwe Lopambana mu Ulaliki
“Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.”—MAT. 7:12.
1. Pelekani citsanzo coonetsa mmene zocita zathu mu ulaliki zingakhudzile ena. (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)
ZAKA zingapo zapita, mwamuna wina ndi mkazi wake kudziko la Fiji anali ndi nchito yapadela yoitanila anthu ku Cikumbutso ca imfa ya Kristu. Pamene anali kukambitsilana ndi mkazi wina pabwalo la nyumba yake, mvula inayamba kugwa. Conco, mwamunayo ndi mkazi wake anagwilitsila nchito ambulela imodzi, ndi kupatsa mwininyumba ambulela inayo. Mwininyumbayo anasangalala kwambili ndipo anaganiza zopita ku Cikumbutso. Iye anakamba kuti sakumbukila zonse zimene m’bale ndi mlongoyo ananena, koma anali kukumbukila kwambili kukoma mtima kumene io anaonetsa kwa iye. M’bale ndi mlongoyo anaonetsa Khalidwe Lopambana.
2. Kodi Khalidwe Lopambana n’ciani? Ndipo tingalionetse motani?
2 Kodi Khalidwe Lopambana n’ciani? Ndi malangizo amene Yesu anapeleka pamene anati: “Zinthu zonse zimene mukufuna kuti anthu akucitileni, inunso muwacitile zomwezo.” (Mat. 7:12) Kodi tingatsatile bwanji malangizo amenewa? Coyamba, tiyenela kudzifunsa kuti, ‘Ngati ine ndinali munthu winayu, kodi ndingafune kuti iye andicitile ciani? Caciŵili, tiyenela kucitila munthu wina zimene tingafune kuti iye aticitile.—1 Akor. 10:24.
3, 4. (a) Fotokozani cifukwa cake sitiyenela kuonetsa Khalidwe Lopambana kwa Akristu anzathu okha. (b) Kodi tikambilana ciani m’nkhani ino?
3 Nthawi zambili timaonetsa Khalidwe Lopambana kwa Akristu anzathu. Koma Yesu sanakambe kuti tiyenela kuonetsa khalidwe limeneli kokha kwa abale ndi alongo athu m’cikhulupililo. Pamene anali kukamba za Khalidwe limeneli, iye anali kufotokoza za mmene tiyenela kucitila ndi anthu onse ngakhale adani athu. (Ŵelengani Luka 6:27, 28, 31, 35.) Ngati tiyenela kuonetsa Khalidwe Lopambana kwa adani athu, bwanji ponena za anthu amene timalalikila, anthu amene ali ndi ‘maganizo abwino amene angawathandize kukapeza moyo wosatha.’—Mac. 13:48.
4 Tsopano tikambilana mafunso anai amene tiyenela kukumbukila tikakhala mu ulaliki. Mafunsowa ndi akuti: Kodi ndikukambilana ndi munthu wotani? Ndi kuti kumene ndimakambilana ndi anthu? Ndi nthawi iti yabwino yokambilana ndi anthu? Kodi anthu ndiyenela kukambitsilana nao motani? Monga mmene tidzaphunzilila, mafunso awa angatithandize kudziŵa zimene anthu amafuna kuti tiwacitile ndi mmene tingakambitsilane nao bwino.—1 Akor. 9:19-23.
KODI NDIKUKAMBILANA NDI MUNTHU WOTANI?
5. Ndi mafunso ati amene tingadzifunse?
5 Tikakhala mu ulaliki timakambitsilana ndi anthu osiyanasiyana. Mmene munthu aliyense anakulila zimasiyana ndi ena, ndipo aliyense amakhala ndi mavuto akeake. (2 Mbiri 6:29) Pamene tikambitsilana ndi munthu, tiyenela kudzifunsa kuti: ‘Ngati ine ndinali munthu winayo, kodi ndingafune kuti andicitile zinthu zotani? Kodi ndingafune kuti ena azindiona mosiyana ndi mmene ndilili? Kapena ndingafune kuti andidziŵe bwino?’ Mafunso a conco angatithandize kucitila mwininyumba aliyense zimene afuna.
6, 7. Kodi tiyenela kukumbukila ciani tikapeza munthu waukali mu ulaliki?
6 Mwacitsanzo, pokhala Akristu timayesetsa kutsatila malangizo a m’Baibulo akuti ‘nthawi zonse mau athu azikhala acisomo.’ (Akol. 4:6) Komabe, cifukwa copanda ungwilo, nthawi zina tingakambe zinthu zimene tingacite nazo manyazi pambuyo pake. (Yak. 3:2) Zimenezo zikacitika tingayamikile ngati ena atimvetsetsa ndipo aona kuti si mmene tilili. Sitingafune kuti ena atiganizile kukhala anthu amwano kapena osaganizila ena. Kukumbukila zimenezi kudzatithandiza kuwamvetsetsa anthu amene angatilankhule mau oipa.
7 Tikapeza munthu waukali mu ulaliki, tizikumbukila kuti mwina pali cam’khumudwitsa. Kodi n’cifukwa cakuti wapanikizika ndi sukulu, kapena akulimbana ndi matenda aakulu? Zacitikapo kuti eninyumba amene poyamba anali aukali asintha khalidwe lao cifukwa anthu a Yehova anawayankha mofatsa ndi mwaulemu.—Miy. 15:1; 1 Pet. 3:15.
8. N’cifukwa ciani tiyenela kulalikila uthenga wa Ufumu kwa “anthu osiyanasiyana”?
8 Timalalikila kwa anthu osiyanasiyana. Ndipo nkhani zokhudza zocita za anthu zoposa 60 za mutu wakuti “Baibulo Limasintha Anthu,” zafalitsidwa mu Nsanja ya Olonda kwa zaka zingapo tsopano. Ena mwa anthu amenewa kale anali mbala, zidakwa, zigaŵenga, ndipo ena anali kugwilitsila nchito mankhwala osokoneza bongo. Ndiponso ena anali m’zipani zandale, anali abusa acipembezo, ndipo ena anali ofunitsitsa nchito zapamwamba kwambili. Ena anali ndi khalidwe laciwelewele. Komabe, anthu onsewa anamva uthenga wabwino, anayamba kuphunzila Baibulo, anasintha umoyo wao ndipo ali m’coonadi tsopano. Conco, sitiyenela kuganiza kuti anthu ena sangamvetsele uthenga wa Ufumu. (Ŵelengani 1 Akorinto 6:9-11.) M’malo mwake, tizikumbukila kuti “anthu osiyanasiyana” angalandile uthenga wabwino.—1 Akor. 9:22.
NDI KUTI KUMENE NDIMAKAMBILANA NDI ANTHU?
9. N’cifukwa ciani tiyenela kulemekeza nyumba za ena polalikila?
9 Nthawi zambili timakambilana ndi anthu panyumba zao. (Mat. 10:11-13) Timayamikila ngati ena alemekeza nyumba ndi katundu wathu. Timaona nyumba yathu kukhala yofunika kwambili, ndipo timafuna kuti ena aziilemekeza. Ifenso tifunika kulemekeza nyumba za ena. Conco, polalikila ku kunyumba ndi nyumba, tifunikila kulemekeza nyumba za anthu.—Mac. 5:42.
10. Kodi tingapewe bwanji kukumudwitsa ena mu ulaliki?
10 Tikukhala m’dziko lodzaza ndi upandu, ndipo eninyumba amacita mantha kucezeledwa ndi anthu acilendo. (2 Tim. 3:1-5) Conco, tiyenela kupewa kuwacititsa mantha. Mwacitsanzo, tinene kuti tikugogoda pacitseko ca nyumba ya munthu. Ngati palibe amene atsegula citseko, kodi tingayambe kuyang’ana pa windo kapena kuyamba kuzungulila nyumba kuti tione ngati pali munthu? Kodi kudela lanu eninyumba angakhumudwe mutacita zimenezi? Kodi anansi ao angakuoneni bwanji? N’zoona kuti timafunikila kulalikila anthu onse. (Mac. 10:42) Timafunitsitsa kulengeza uthenga wabwino ndipo kucita zimenezi n’kofunika. (Aroma 1:14, 15) Komabe, n’kwanzelu kupewa kucita ciliconse cimene cingakhumudwitse anthu m’gawo lathu. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Sitikucita ciliconse cokhumudwitsa, kuti utumiki wathu usapezedwe cifukwa.” (2 Akor. 6:3) Ngati timalemekeza nyumba ndi katundu wa anthu a m’gawo lathu, io angalandile coonadi.—Ŵelengani 1 Petulo 2:12.
NDI NTHAWI ITI YABWINO YOKAMBILANA NDI ANTHU?
11. N’cifukwa ciani timayamikila ngati ena alemekeza nthawi yathu?
11 Ambili a ife timakhala ndi zocita zambili. Kuti tikwanilitse udindo wathu, timakhala ndi ndandanda yocita zinthu. (Aef. 5:16; Afil. 1:10) Ndipo sitimakondwela ngati ndandanda yathu yasokonezeka. Conco, timayamikila ngati ena amalemekeza nthawi yathu mwa kukamba nafe mwacidule. Kodi kutsatila Khalidwe Lopambana kungatithandize bwanji kulemekeza nthawi ya anthu amene timakambilana nao?
12. Kodi tingadziŵe bwanji nthawi yabwino yokambitsilana ndi anthu m’gawo lathu?
12 Timafunika kudziŵa nthawi yabwino yofikila anthu. Kodi ndi nthawi iti imene anthu amapezeka panyumba m’gawo lathu? Ndi nthawi iti pamene amakhala okonzeka kumvetsela? Tingacite bwino kusintha ndandanda yathu kuti tizifikila anthu panthawi yoyenela. M’maiko ena, nchito yolalikila kunyumba ndi nyumba imagwilika bwino m’masana kapena m’mazulo. Ngati n’cimodzimodzi ndi kwanuko, kodi simungaciteko ulaliki wa kunyumba ndi nyumba panthawi zimenezi? (Ŵelengani 1 Akorinto 10:24.) Tili ndi cidalilo cakuti Yehova adzadalitsa kuyesayesa kwanu kuti muzilalikila anthu a m’gawo lanu panthawi yoyenela.
13. Tingaonetse bwanji kuti timalemekeza mwininyumba?
13 Kodi tingaonetse bwanji ulemu kwa mwininyumba? Tikapeza munthu wacidwi tiyenela kumulalikila uthenga wathu, koma sitiyenela kukhalitsa. Mwininyumba angakhale ndi zocita zina zimene iye amaona kuti n’zofunika. Ngati watiuza kuti ndi wotangwanika, tingam’pemphe kuti tilankhule naye mwacidule, ndipo tiyenela kucita zimenezo. (Mat. 5:37) Kumapeto a makambilano athu, tingam’funse nthawi yabwino imene tingabweleleko. Ofalitsa ena aona njila iyi kukhala yothandiza. Iwo amati: “Ndingakonde kuti ndikabwelenso, kodi ndingakulembeleni uthenga pafoni kapena kukutumilani foni ndisanabwele?” Ngati timacezela anthu panthawi yoyenela kwa io, tidzatsatila citsanzo ca Paulo amene sanali ‘kungofuna zopindulitsa iye yekha ayi, koma zopindulitsa anthu ambili, kuti apulumutsidwe.’—1 Akor. 10:33.
KODI NDIYENELA KUKAMBILANA NAO MOTANI ANTHU?
14-16. (a) N’cifukwa ciani n’kofunika kuuza mwininyumba colinga cimene tabwelela? Pelekani citsanzo. (b) Nanga ndi njila iti imene woyang’anila woyendela wina anapeza kukhala yothandiza?
14 Tinene kuti munthu wina wakutumilani foni, koma simunam’zindikile. Iye ndi wacilendo ndipo akukufunsani kuti adziŵe zakudya zimene mukonda. Mungadabwe ndipo mungafune kudziŵa cifukwa cake munthuyo akufunsa zimenezo. Posafuna kuti munthuyo aganize kuti ndinu wamwano, mungakambe naye pang’ono ndi kuthetsa makambilanowo. Koma, bwanji ngati munthuyo wadzidziŵikitsa ndipo wakuuzani kuti amagwila nchito yofufuza zakudya zopatsa thanzi ndi kuti ali ndi mfundo zina zothandiza? Mwacionekele, mungafune kumvetsela zoonjezeleka. Tonsefe timafuna kuti munthu amene wafika panyumba pathu adzidziŵikitse coyamba ndi kutiuza zimene wabwelela. Kodi tingacite motani zimenezi pamene tili mu ulaliki?
15 M’magawo ambili, zimakhala bwino kuuza eninyumba cifukwa cimene tapitila panyumba pao. N’zoona kuti tili ndi uthenga wabwino umene anthu ayenela kumva. Koma bwanji ngati popanda kudzidziŵikitsa ndi kuuza eninyumba cimene tabwelela, tingofikila kuwafunsa kuti: “Ngati munali ndi mphamvu yothetsa mavuto, kodi mukanathetsa vuto liti?” N’zoona kuti colinga ca funsoli n’cakuti tidziŵe maganizo a mwininyumbayo kuti tiyambitse makambilano a m’Baibulo. Koma mwininyumba angadzifunse kuti: ‘Nanga ndani ameneyu, ndipo n’cifukwa ciani akundifunsa funso ili? Kodi akufuna ciani? Conco, tiyenela kucititsa eninyumba kukhala omasuka. (Afil. 2:3, 4) Nanga tingacite bwanji zimenezi?
16 Woyang’anila woyendela wina anapeza njila iyi kukhala yothandiza. Akapeleka moni ndi kudzidziŵikitsa, iye amapatsa mwininyumba kapepala kauthenga kakuti, Kodi Mufuna Kudziŵa Mayankho Azoona pa Mafunso Aya? Ndiyeno amanena kuti: “Lelo tikupatsa kapepala aka kwa aliyense m’gawo muno. Kali ndi mafunso okwana 6 amene anthu amafunsa. Kanu ndi aka.” M’baleyu anakamba kuti anthu amamasuka akadziŵa cifuno cowacezela. Tikacita zimenezo zimakhala zosavuta kukambilana momasuka. Woyang’anila woyendela ameneyo anakamba kuti pambuyo pake amafunsa munthuyo kuti: “Kodi munawaganizilapo mafunso awa?” Ngati mwininyumba wasankha funso, m’baleyo amatsegula kapepalako ndi kukambitsilana zimene Baibulo limanena pankhaniyo. Ngati mwininyumba sanasankhe, m’baleyo amasankha funso ndi kukambilana naye popanda kumucititsa manyazi. Koma pali njila zambili zoyambila makambilano. M’madela ena, eninyumba amafuna kuti mukambitsilane zambili musanachule cifuno canu cowacezela. N’kofunika kusinthasintha makambilano athu kuti zikhale zosavuta kwa anthu kumvetsela uthenga wathu.
PITILIZANIBE KUONETSA KHALIDWE LOPAMBANA MU ULALIKI
17. Kodi tingaonetse bwanji Khalidwe Lopambana polalikila?
17 Kodi tingaonetse bwanji Khalidwe Lopambana polalikila? Tingaonetse khalidweli mwa kukomela mtima munthu aliyense, kulemekeza eninyumba ndi katundu wao, kufikila anthu panthawi imene amapezeka panyumba ndi panthawi imene amakhala omasuka, ndiponso mwa kupeleka uthenga wathu m’njila imene ingacititse eninyumba kukhala ofunitsitsa kumvetsela.
18. Kodi kucitila anthu amene timalalikila zinthu zimene tingafune kuti io aticitile kuli ndi ubwino wotani?
18 Pali ubwino waukulu ngati ticitila anthu amene timalalikila zinthu zimene tingafuna kuti io aticitile. Ngati ndife okoma mtima ndi oganizila ena, tidzaonetsa kuwala kwathu, tidzaonetsa kuti timatsatila mfundo za m’Baibulo, ndi kuti timalemekeza atate wathu wakumwamba. (Mat. 5:16) Tiyeni tithandize anthu ambili kulandila coonadi mwa kukambilana nao bwino. (1 Tim. 4:16) Kaya anthu amve uthenga wathu kapena akane, tidzadziŵa kuti tacita zimene tingathe kuti tikwanilitse ulaliki wathu. (2 Tim. 4:5) Tiyeni titsanzile mtumwi Paulo amene analemba kuti: “Ndikucita zinthu zonse cifukwa ca uthenga wabwino, kuti ndiugaŵilenso kwa ena.” (1 Akor. 9:23) Cotelo, nthawi zonse tizionetsa Khalidwe Lopambana mu ulaliki.