“Uzikonda Yehova Mulungu Wako”
“Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.”—MAT. 22:37.
1. N’cifukwa ciani cikondi pakati pa Mulungu ndi Mwana wake cinakula kwambili?
YESU KRISTU, Mwana wa Yehova, anati: “Ndimakonda Atate.” (Yoh. 14:31) Yesu ananenanso kuti: “Atatewo amakonda Mwana wake.” (Yoh. 5:20) Zimenezi n’zomveka cifukwa cakuti kwa zaka zambili Yesu asanabwele padziko lapansi, anali “mmisili waluso” wa Mulungu. (Miy. 8:30) Pamene Yehova ndi Yesu anali kugwila nchito limodzi, Yesu anaphunzila zambili ponena za makhalidwe a Atate wake. Zimenezi zinacititsa kuti Yesu akhale ndi zifukwa zambili zokondela Atate wake. Mwacionekele, mgwilizano umenewo unacititsa kuti azikondana kwambili.
2. (a) Kodi cikondi n’ciani? (b) Tidzakambilana mafunso ati?
2 Cikondi ndico kukhudzika mtima ndi munthu amene mumakondwela naye. Wamasalimo Davide anaimba kuti: “Ndidzakukondani inu Yehova, mphamvu yanga.” (Sal. 18:1) Tiyenela kukonda Mulungu cifukwa cakuti nayenso amatikonda. Ngati timamvela Yehova, iye adzaonetsa kuti amatikonda. (Ŵelengani Deuteronomo 7:12, 13.) Koma kodi n’zothekadi kukonda Mulungu ngakhale kuti sitimuona? Kodi kukonda Yehova kumatanthauzanji? N’cifukwa ciani tiyenela kukonda Mulungu? Nanga tingaonetse bwanji kuti timam’konda?
N’ZOTHEKA KUM’KONDA MULUNGU
3, 4. N’cifukwa ciani n’zotheka kukonda Yehova?
3 “Mulungu ndiye Mzimu,” conco sitingamuone. (Yoh. 4:24) Komabe, n’zotheka kukonda Yehova, ndipo Malemba amatiuza kuti tizim’konda. Mwacitsanzo, Mose anauza Aisiraeli kuti: “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi mphamvu zako zonse.”—Deut. 6:5.
4 N’cifukwa ciani n’zotheka kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse? N’cifukwa cakuti anatilenga kuti tizicita zinthu zakuuzimu ndi kuonetsa cikondi. Ngati tikhutilitsa zosoŵa zathu zakuuzimu, cikondi cathu pa Yehova cimakula ndipo timakhala ndi cimwemwe. Yesu anati: “Odala ndi anthu amene amazindikila zosoŵa zao zauzimu, cifukwa ufumu wakumwamba ndi wao.” (Mat. 5:3) Ponena za cibadwa ca anthu cofuna kulambila, buku lina lochedwa Man Does Not Stand Alone, lombedwa ndi A.C. Morrison linati: “Tiyenela kucita mantha, kudabwa ndiponso kupeleka ulemu poona kuti anthu kulikonse amafunafuna wina wake wapamwamba kwambili ndi kum’khulupilila.”
5. Timadziŵa bwanji kuti kufunafuna Mulungu si kopanda phindu?
5 Kodi kufunafuna Mulungu n’kopanda phindu? Iyai. Mulungu amafuna kuti tim’peze. Mtumwi Paulo anamveketsa bwino mfundoyi pamene analalikila gulu la anthu amene anasonkhana ku Areopagi. Zimenezi zinacitika pafupi ndi kacisi wa mulungu wamkazi wochedwa Athena mumzinda wa Atene wakale. Ganizilani kuti munalipo pamene Paulo anakamba zokhudza ‘Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemo,’ amenenso “sakhala mu akacisi opangidwa ndi manja.” Paulo anakambanso kuti Mulungu, “kucokela mwa munthu mmodzi anapanga mtundu wonse wa anthu, kuti akhale padziko lonse lapansi. Iye anakhazikitsa nthawi zoikidwilatu komanso anaika malile acikhalile a malo oti anthu azikhala. Anacita zimenezi kuti anthuwo afunefune Mulungu, amufufuzefufuze ndi kumupezadi, ngakhale kuti kwenikweni, iye sali kutali ndi aliyense wa ife.” (Mac. 17:24-27) Ndithudi, anthu angam’pezedi Mulungu. Mboni za Yehova zoposa 7,500,000 ‘zam’pezadi’ ndipo zimam’konda kwambili.
ZIMENE KUKONDA MULUNGU KUMATANTHAUZA
6. Kodi Yesu anati “lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba” ndi liti?
6 Tiyenela kukonda Yehova kucokela pansi pamtima. Yesu anamveketsa bwino mfundoyi pamene Mfarisi wina anam’funsa kuti: “Mphunzitsi, kodi lamulo lalikulu kwambili m’Cilamulo ndi liti?” Yesu anamuyankha kuti: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, ndi maganizo ako onse.’ Limeneli ndilo lamulo lalikulu kwambili komanso loyamba.”—Mat. 22:34-38.
7. Kumatanthauza ciani kukonda Mulungu ndi (a) ‘mtima wathu wonse’? (b) ‘moyo wathu wonse’? (c) ‘maganizo athu onse’?
7 Kodi Yesu anatanthauzanji pokamba kuti tizikonda Mulungu ndi ‘mtima wathu wonse’? Iye anatanthauza kuti tiyenela kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse wophiphilitsa. Zimenezi zimakhudza malingalilo athu, zokhumba zathu, ndi zinthu zimene timakonda kwambili. Tiyenelanso kum’konda ndi ‘moyo wathu wonse,’ kutanthauza kuti mbali zonse za umoyo wathu ziyenela kuonetsa kuti timam’konda. Ndiponso, tiyenela kukonda Mulungu ndi ‘maganizo athu onse,’ kutanthauza nzelu zathu zonse. Conco, n’kofunika kuti tizikonda Yehova ndi mtima wathu wonse.
8. Kukonda Mulungu mokwanila kudzatithandiza kucita ciani?
8 Kukonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, ndi maganizo athu onse kudzatithandiza kuphunzila Mau ake mwakhama. Kudzatithandizanso kum’tumikila ndi mtima wonse ndi kulalikila uthenga wabwino wa Ufumu mwacangu. (Mat. 24:14; Aroma 12:1, 2) Cikondi ceniceni pa Yehova cidzatithandiza kumuyandikila kwambili. (Yak. 4:8) Sitingathe kulemba mndandanda wa zifukwa zonse zimene timakondela Mulungu. Koma tiyeni tikambilaneko zina mwa zifukwa zimenezo.
CIMENE TIYENELA KUKONDELA MULUNGU
9. N’cifukwa ciani timakonda Yehova Mlengi wathu?
9 Yehova ndi Mlengi wathu, ndipo amatisamalila. Paulo anati: “Cifukwa ca iye tili ndi moyo, timayenda ndipo tilipo.” (Mac. 17:28) Yehova anatipatsa dziko lapansi lokongola kwambili monga malo athu okhala. (Sal. 115:16) Iye amatipatsanso cakudya ndi zinthu zina kuti tikhalebe ndi moyo. Paulo anauza anthu a ku Lusitara amene anali kupembedza mafano kuti: “Mulungu wamoyo . . . sanangokhala wopanda umboni wakuti anacita zabwino. Anakupatsani mvula kucokela kumwamba ndi nyengo zimene zokolola zanu zimakhala zambili. Anadzaza mitima yanu ndi cakudya komanso cimwemwe.” (Mac. 14:15-17) Kodi cimeneci si cifukwa comveka cokondela Mlengi Wamkulu amene amatisamalila mwacikondi?—Mlal. 12:1.
10. Tiyenela kumva bwanji poona kuti Mulungu anakonza njila yotimasula ku ucimo ndi imfa?
10 Mulungu adzacotsa ucimo ndi imfa zimene tinatengela kwa Adamu. (Aroma 5:12) Baibulo limati: “Mulungu akuonetsa cikondi cake kwa ife, moti pamene tinali ocimwa, Kristu anatifela.” (Aroma 5:8) Ngati tilapa mocokela pansi pamtima ndi kukhulupilila nsembe ya dipo, Mulungu adzatikhululukila macimo athu. Timayamikila Yehova kwambili pa cikondi cimene anaonetsa potumiza Mwana wake kudzatifela.—Yoh. 3:16.
11, 12. Kodi Yehova wapeleka ziyembekezo ziŵili ziti?
11 Yehova watipatsa ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha. (Aroma 15:13) Ciyembekezo cimene Mulungu watipatsa cimatithandiza kupilila mayeso. Akristu odzozedwa amene adzaonetsa ‘kukhulupilika kwao mpaka imfa adzapatsidwa mphoto ya moyo kumwamba’. (Chiv. 2:10) Ndipo Akristu ena okhulupilika akuyembekezela kudzakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso padziko lapansi. (Luka 23:43) Kodi timamva bwanji kukhala ndi ciyembekezo cimeneci? Timakhala acimwemwe, ndi amtendele, ndiponso timakonda Mulungu amene amatipatsa “mphatso iliyonse yabwino ndi yangwilo.”—Yak. 1:17.
12 Yehova watipatsa ciyembekezo ca ciukililo. (Mac. 24:15) Timamva cisoni kwambili munthu amene timakonda akamwalila. Koma podziŵa kuti adzauka, ‘siticita cisoni mofanana ndi onse opanda ciyembekezo.’ (1 Ates. 4:13) Cifukwa Yehova Mulungu ndi wacikondi, amalakalaka kuukitsa akufa, makamaka anthu okhulupilika ndi olungama monga Yobu. (Yobu 14:15) Ganizilani cimwemwe cimene tidzakhala naco polandila anthu oukitsidwa padziko lapansi. Ndithudi, Atate wathu wakumwamba timamukonda ndi mtima wonse, potipatsa ciyembekezo cimeneci.
13. N’ciani cimaonetsa kuti Mulungu amatisamaliladi?
13 Yehova amatisamaliladi. (Ŵelengani Salimo 34:6, 18, 19; 1 Petulo 5:6, 7.) Timakhala otetezeka monga ‘nkhosa zimene akuweta’ cifukwa timadziŵa kuti nthawi zonse Mulungu amathandiza anthu amene amam’khulupilila. (Sal. 79:13) Ganizilani zinthu zambili zimene Mulungu adzaticitila mtsogolo kupyolela mu Ufumu wa Mesiya. Pokhala Mfumu ya Ufumu wa Mulungu, Yesu Kristu adzacotsa ciwawa, kupondelezana, ndi kuipa padziko lapansi. Ndiyeno, Mulungu adzapatsa anthu onse omvela mtendele ndi zinthu zambili kuti adzasangalale ndi umoyo. (Sal. 72:7, 12-14, 16) Pamene tiganizila kwambili malonjezo amenewa, timakonda Mulungu ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse, mphamvu zathu zonse, ndi maganizo athu onse.—Luka 10:27.
14. Ndi mwai waukulu uti umene Mulungu watipatsa?
14 Yehova watipatsa mwai waukulu wokhala Mboni zake. (Yes. 43:10-12) Timam’konda Mulungu cifukwa watipatsa mwai wocilikiza ulamulilo wake, ndi kupatsa anthu okhala m’dziko la mavutoli ciyembekezo ceniceni. Ndipo timalalikila uthenga wabwino ndi cikhulupililo ndi cidalilo cifukwa uthenga wathu umacokela m’Mau a Mulungu, Baibulo. Malonjezo a m’Mau a Mulungu adzakwanilitsidwa ndithu. (Ŵelengani Yoswa 21:45; 23:14.) Pali zifukwa zambili zokondela Yehova. Koma tingaonetse bwanji kuti timam’konda?
MMENE TINGAONETSELE KUTI TIMAM’KONDA MULUNGU
15. Kodi kuphunzila ndi kugwilitsila nchito Mau a Mulungu kumatithandiza bwanji?
15 Tiziphunzila ndi kugwilitsila nchito Mau a Mulungu nthawi zonse. Ngati ticita zimenezi, tidzaonetsa kuti timakonda Yehova, ndi kuti timafuna kuti mau ake ‘aziunikila mapazi athu.’ (Sal. 119:105) Pamene tivutika, tingatonthozedwe ndi malonjezo monga akuti: “Inu Mulungu, simudzanyoza mtima wosweka ndi wophwanyika” ndi akuti “Kukoma mtima kwanu kosatha, inu Yehova, kunandicilikiza.” (Sal. 51:17; 94:18, 19) Yehova ndi Yesu amamvelela cisoni anthu onse ovutika. (Yes. 49:13; Mat. 15:32) Ngati tiphunzila Baibulo, tidzazindikila kuti Yehova amatikonda, ndipo nafenso tidzam’konda kwambili.
16. Kodi kupemphela nthawi zonse kungatithandize bwanji kukulitsa cikondi cathu pa Mulungu?
16 Tizipemphela kwa Mulungu nthawi zonse. Kupemphela kumatiyandikilitsa kwa Mulungu, “Wakumva pemphelo.” (Sal. 65:2) Ndipo tikaona kuti Mulungu amayankha mapemphelo athu, cikondi cathu pa iye cimakula. Mwacitsanzo, mwina pa zocitika zina munadzionela nokha kuti Mulungu salola kuti tiyesedwe ndi zimene sitingapilile. (1 Akor. 10:13) Ngati tili ndi nkhawa ndipo tikucondelela Yehova, tingakhale ndi “mtendele wa Mulungu.” (Afil. 4:6, 7) Mofanana ndi Nehemiya, nthawi zina tingapemphele ca mumtima, ndipo pambuyo pake tingazindikile kuti Yehova watiyankha. (Neh. 2:1-6) Ngati tipitilizabe kupemphela ndi kuzindikila kuti Yehova amayankha mapemphelo athu, cikondi cathu pa iye cimakula. Ndipo cikhulupililo cathu cikayesedwa, tidzakhala otsimikiza mtima kuti Yehova adzatithandiza kupilila.—Aroma 12:12.
17. Ngati timakonda Mulungu, kodi misonkhano tidzaiona motani?
17 Nthawi zonse tizipezeka pamisonkhano ya mpingo, ya dela ndi ya cigawo. (Aheb. 10:24, 25) Aisiraeli anali kusonkhana kuti amvetsele ndi kuphunzila za Yehova kotelo kuti azimuopa ndi kutsatila Cilamulo cake. (Deut. 31:12) Ngati timam’kondadi Mulungu, kucita cifunilo cake sikudzakhala kolemetsa. (Ŵelengani 1 Yohane 5:3.) Conco, tiyeni tiziyesetsa kupezeka pamisonkhano yonse. Tisalole ciliconse kusokoneza cikondi cathu pa Yehova cimene tinaonetsa poyamba.—Chiv. 2:4.
18. Kodi kukonda Mulungu kumatilimbikitsa kucita ciani?
18 Tizilalikila mwacangu “coonadi ca uthenga wabwino” kwa ena. (Agal. 2:5) Kukonda Mulungu kumatilimbikitsa kuuzako ena za Ufumu wa Mwana wake, amene ‘adzakwela pahachi yake cifukwa ca coonadi” pa Aramagedo. (Sal. 45:4; Chiv. 16:14, 16) Timakondwela kwambili pamene tithandiza anthu kudziŵa za cikondi ca Mulungu, ndi madalitso amene watilonjeza m’dziko latsopano.—Mat. 28:19, 20.
19. N’cifukwa ciani tiyenela kuyamikila akulu mumpingo?
19 Tizionetsa kuti timayamikila akulu mumpingo. (Mac. 20:28) Nthawi zonse Yehova amatifunila zabwino. Conco, iye watipatsa akulu mumpingo. Akulu ali “ngati malo obisalilapo mphepo ndi malo ousapo mvula yamkuntho, ngati mitsinje yamadzi m’dziko lopanda madzi, ndiponso ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu m’dziko louma.” (Yes. 32:1, 2) Ganizilani mmene timakhalila otetezeka ku cimphepo camphamvu, ku mvula yamkuntho kapena mmene timamvelela tikakhala pamthunzi kukatentha kwambili. Mofananamo, akulu amatithandiza ndi kutilimbikitsa kuti tipitilizebe kutumikila Yehova ngakhale kuti timakumana ndi mavuto. N’cifukwa ciani timamvela akulu? Cifukwa cakuti timayamikila “mphatso za amuna” zimenezi, ndipo timakonda Yehova ndi Kristu, Mutu wa mpingo.—Aef. 4:8; 5:23; Aheb. 13:17.
PITILIZANI KUKULITSA CIKONDI CANU PA MULUNGU
20. Ngati timakonda Mulungu, kodi tiyenela kucita zotani?
20 Yehova watipatsa ‘lamulo langwilo,’ limene limatiuza zonse zimene tiyenela kucita. (Ŵelengani Yakobo 1:22-25.) Kuti tikhale paubale wolimba ndi Yehova, tiyenela kucita zambili kuposa kungomumvela cabe. (Sal. 19:7-11) Tiyenela kutsatila zimene timaphunzila. Mwacitsanzo, cifukwa cokonda Mulungu, tiyenela kuuzako ena za iye ndi kuyankhapo pamisonkhano.
21. Kodi mapemphelo athu ocokela pansi pamtima tingawayelekezele ndi ciani?
21 Nthawi zonse timapemphela kwa Yehova cifukwa cakuti timam’konda. Mu Isiraeli, ansembe anali kufukiza nsembe kwa Yehova tsiku ndi tsiku. Mfumu Davide anayelekezela mapemphelo ake ngati zofukiza pamene anaimba kuti: “Pemphelo langa likhale lokonzedwa ngati zofukiza pamaso panu [Yehova], mapembedzelo anga akhale ngati nsembe yambeu yamadzulo.” (Sal. 141:2; Eks. 30:7, 8) Yehova anayankha mapemphelo a Davide. Ngati timapemphela modzicepetsa, moona mtima, ndi moyamikila, mapemphelo athu nafenso adzakhala ngati zofukiza, ndipo Yehova adzakondwela nao.—Chiv. 5:8.
22. Tidzaphunzila ciani m’nkhani yotsatila?
22 Yesu anakamba kuti tizikonda Mulungu ndi munthu mnzathu. (Mat. 22:37-39) Kukonda Yehova ndi mfundo zake, kudzatithandiza kukonda munthu mnzathu. M’nkhani yotsatila tidzaphunzila mmene tingacitile zimenezi.