LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w14 7/15 masa. 28-32
  • “Mudzakhala Mboni Zanga”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Mudzakhala Mboni Zanga”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “ZINTHU ZAZIKULU ZA MULUNGU”
  • ‘DIPO LOOMBOLA ANTHU AMBILI’
  • ‘LIMBANI MTIMA KUTI MULANKHULE UTHENGA WABWINO’
  • Citani Zinthu Mogwilizana Ndi Pemphelo La Yesu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2013
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
w14 7/15 masa. 28-32

“Mudzakhala Mboni Zanga”

“[Yesu] anawauza kuti: ‘. . . Mudzakhala mboni zanga . . . Mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.’”—MAC. 1:7, 8.

KODI MUNGAYANKHE KUTI CIANI?

  • Kodi Yesu anacita ciani mogwilizana ndi tanthauzo la dzina lake?

  • N’cifukwa ninji Yesu anati: “Mudzakhala mboni zanga”?

  • N’cifukwa ciani tili ndi cidalilo cakuti tidzapambana panchito yathu yocitila umboni?

1, 2. (a) Kodi mboni ya Yehova yopambana onse ndani? (b) Kodi dzina lakuti Yesu litanthauzanji? Nanga iye anacita ciani mogwilizana ndi dzina lake?

“CIMENE ndinabadwila ndiponso cimene ndinabwelela m’dziko ndico kudzacitila umboni coonadi.” (Ŵelengani Yohane 18:33-37.) Yesu Kristu anakamba mau amenewa kwa bwanamkubwa waciroma wa Yudeya pamene anali kumzenga mlandu. Yesu anali atangoŵauza kumene kuti iye ndi mfumu. Patapita zaka, mtumwi Paulo anafotokoza mmene Yesu anapelekela citsanzo ca kulimba mtima pamene “anapeleka umboni wabwino kwambili pamaso pa Pontiyo Pilato.” (1 Tim. 6:13) Kukamba zoona, nthawi zina pamafunika kulimba mtima kuti tikhale “mboni yokhulupilika ndi yoona” m’dziko lodzala cidani la Satana.—Chiv. 3:14.

2 Popeza kuti Yesu anali Myuda, iye anabadwa ali kale mboni ya Yehova. (Yes. 43:10) Ndithudi, Yesu anafika pokhala mboni yopambana wina aliyense pakuimila dzina la Mulungu. Iye anakhala ndi moyo mogwilizana ndi dzina limene Mulungu anam’patsa, lakuti Yesu. Mngelo anauza Yosefe, tate wake wa Yesu kuti, Mariya wakhala ndi pathupi mwa mphamvu ya mzimu woyela. Ndiyeno anaonjezela kuti: “Iye adzabeleka mwana wamwamuna, ndipo dzina lake udzamuche Yesu, cifukwa adzapulumutsa anthu ake ku macimo ao.” (Mat. 1:20,21) Akatswili a Baibulo ambili amavomeleza kuti dzina lakuti Yesu linacokela ku dzina laciheberi lakuti Yesuwa, limene mbali yake ina inatengedwa ku dzina la Mulungu. Motelo, dzinali lakuti Yesuwa limatanthauza kuti “Yehova Ndiye Cipulumutso.” Mogwilizana ndi tanthauzo la dzina lake, Yesu anathandiza “nkhosa zosocela za nyumba ya Isiraeli” kulapa macimo ao kuti Yehova awalandilenso. (Mat. 10:6; 15:24; Luka 19:10) Pacifukwa cimeneci, Yesu analalikila mwacangu za Ufumu wa Mulungu. Wolemba Uthenga Wabwino, Maliko, anati: “Yesu anapita ku Galileya kukalalikila uthenga wabwino wa Mulungu kuti: ‘Nthawi yoikidwilatu yakwanilitsidwa! Ufumu wa Mulungu wayandikila! Lapani anthu inu! Khulupililani uthenga wabwino!’” (Maliko 1:14, 15) Mopanda mantha, Yesu anadzudzula atsogoleli acipembedzo aciyuda. Ici n’cifukwa cinanso cimene anamuphela.—Maliko 11:17, 18; 15:1-15.

“ZINTHU ZAZIKULU ZA MULUNGU”

3. Cinacitika n’ciani Yesu atakhala m’manda masiku atatu?

3 Anthu anadabwa kwambili kuona Yesu ataukitsidwa pambuyo pokhala m’manda masiku atatu. Yehova sanaukitse Yesu monga munthu, koma monga mngelo wosakhodza kufa. (1 Pet. 3:18) Kuti anthu atsimikize kuti Yesu waukadi, anavala thupi laumunthu ndi kuonekela kwa anthu. Tsiku limene Yesu anaukitsidwa, anaonekela kwa ophunzila ake osiyanasiyana nthawi zosacepela zisanu.—Mat. 28:8-10; Luka 24:13-16;30-36; Yoh. 20:11-18.

4. Kodi Yesu anacita msonkhano wanji ndi ophunzila ake patsiku limene anaukitsidwa? Ndipo anawathandiza kumvetsetsa udindo wao uti?

4 Nthawi yacisanu Yesu anaonekela kwa atumwi ake ndi ena amene anali nao pamodzi. Pa cocitika cosaiŵalika cimeneco, Yesu anacita nao phunzilo la Mau a Mulungu, titelo kukamba kwake. Iye “anatsegulilatu maganizo ao kuti amvetse tanthauzo la malemba.” Conco, io anazindikila kuti kuphedwa kwa Yesu ndi adani ake ndi kuukitsidwa kwake, zinali zoloseledwa kale m’Malemba. Yesu atatsiliza msonkhano wake ndi ndi ophunzila ake patsiku limene anaukitsidwa, anawathandiza kumvetsetsa udindo wao. Iye anawafotokozela kuti “pa maziko a dzina lake, m’mitundu yonse mudzalalikidwa za kulapa kuti macimo akhululukidwe.” Ndiyeno anati: “Kuyambila ku Yerusalemu Inu mudzakhala mboni za zimenezi.”—Luka 24:44-48.

5, 6. (a) N’cifukwa ciani Yesu anakamba kuti: “Mudzakhala mboni zanga”? (b) N’colinga ca Yehova catsopano citi cimene ophunzila a Yesu anadziŵitsa anthu?

5 Komabe, pamene Yesu anaonekela kwa atumwi ake kotsilizila patapita masiku 40, io anamvetsetsa tanthauzo la zimene Yesu anakamba m’mbuyomo. Iye anati: “Mudzakhala mboni zanga mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekedzelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) N’cifukwa ninji Yesu anakamba kuti “Mudzakhala mboni zanga,” osati mboni za Yehova? Cifukwa anali kukamba ndi Aisiraeli amene anali kale mboni za Yehova. Conco, m’malo mowauza kuti adzakhala mboni za Yehova, iye anawauza kuti adzakhala mboni zake.

6 Tsopano ophunzila a Yesu anafunikila kudziŵitsa anthu colinga ca Yehova catsopano. Colingaco cinali cofunika kwambili kuposa kumasulidwa kwa Aisiraeli ku ukapolo ku Iguputo, ndiponso pambuyo pake ku Babulo. Imfa ya Yesu Kristu ndi kuukitsidwa kwake zinatimasula ku ukapolo woipitsitsa kupambana wina uliwonse, ukapolo ku ucimo ndi imfa. Pa Pentekosite mu 33 C.E., ophunzila a Yesu odzozedwa atsopano anadziŵitsa anthu “zinthu zazikulu za Mulungu,” ndipo ambili amene anamvetsela anacitapo kanthu. Conco, Yesu ali ku dzanja lamanja la Atate wake kumwamba, anayamba kuona kuti m’dzina lake anthu ambili anayamba kulapa ndi kukhulupilila kuti iye ndiye njila ya Yehova yopulumutsila anthu.—Mac. 2:5, 11, 37-41.

‘DIPO LOOMBOLA ANTHU AMBILI’

7. Zimene zinacitika pa Pentekosite mu 33 C.E., zinatsimikizila ciani?

7 Zimene zinacitika pa Pentekosite mu 33 C.E., zinatsimikizila kuti Yehova analandila mokondwela nsembe yangwilo, ya mtengo wapatali ya Yesu yophimba macimo. (Aheb. 9:11, 12, 24) Malinga n’zimene Yesu anakamba, iye “sanabwele kudzatumikilidwa koma kudzatumikila ndi kudzapeleka moyo wake dipo kuombola anthu ambili.” (Mat. 20:28) “Anthu ambili” amene anali kudzapindula ndi dipo la Yesu sanali cabe Ayuda amene analapa. Cifunilo ca Mulungu n’cakuti “anthu kaya akhale a mtundu wotani apulumuke,” cifukwa dipo ‘likucotsa ucimo wa dziko.’—1 Tim. 2:4-6; Yoh. 1:29.

8. Kodi ophunzila a Yesu analalikila uthenga wabwino kufika pamlingo wotani? Ndipo anakwanitsa bwanji kucita zimenezi?

8 Kodi ophunzila a Yesu anakwanitsa kucitila umboni za iye molimba mtima? Inde anatelo, koma osati mwa mphamvu zao. Mzimu woyela wa Yehova wamphamvuwo unawalimbikitsa ndi kuwathandiza kupitiliza kucitila umboni. (Ŵelengani Machitidwe 5:30-32.) Patapita zaka 27 kucokela pa Pentekosite mu 33 C.E., zinaonekelatu kuti “coonadi ca uthenga wabwino” cinalalikidwa kwa Ayuda, ndi anthu a mitundu ina “m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo.”—Akol. 1:5, 23.

9. Malinga n’zimene Yesu anakambilatu, cinacitika n’ciani mumpingo wacikristu woyamba?

9 Koma n’zacisoni kuti mumpingo wacikristu woyamba pang’onopang’ono munaloŵa mpatuko. (Mac. 20:29, 30; 2 Pet. 2:2, 3; Yuda 3, 4) Malinga n’zimene Yesu anakamba, mpatuko umenewu wocititsidwa ndi “woipayo,” Satana, unali kudzakula ndi kudzalepheletsa anthu kudziŵa cipembedzo coona kufikila “mapeto a nthawi ino.” (Mat. 13:37-43) Ndiyeno, Yehova anali kudzaika Yesu kukhala Mfumu yolamulila anthu padziko lapansi. Zimenezi zinacitika mu October 1914, ndipo cinali ciyambi ca “masiku otsiliza” a dongosolo loipa la Satana.—2 Tim. 3:1.

10. (a) Kodi Akristu odzozedwa amakono ananenelatu za caka citi capadela? (b) Nanga cinacitika m’caka cimeneco n’ciani? Ndipo pakhala umboni wotani wotsimikizila zimenezo?

10 Akristu odzozedwa amakono anakambilatu pasadakhale kuti 1914 cidzakhala caka capadela. Anakamba zimenezi malinga ndi ulosi wa Danieli wonena za mtengo waukulu umene unadulidwa ndi kuphukanso patapita “nthawi zokwanila 7.” (Dan. 4:16) Yesu anakamba za nthawi imodzimodziyi kuti “nthawi zoikidwilatu za anthu a mitundu,” mu ulosi wake wonena za kukhalapo kwake ndi “mapeto a nthawi ino.” Kucokela mu 1914, anthu onse akudzionela okha “cizindikilo ca kukhalapo kwa [Kristu] “monga wolamulila wa dziko lapansi. (Mat. 24:3, 7, 14; Luka 21:24) Conco, kucokela nthawiyo, “zinthu zazikulu za Mulungu” ziphatikizapo Yehova kuika Yesu monga Mfumu yolamulila anthu padziko.

11, 12. (a) Kodi Mfumu yatsopano inayamba kucita ciani pambuyo pankhondo m’caka ca 1919? (b) Kuyambila ca m’ma 1935, ndi nchito ina iti imene yakhala ikucitika? (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)

11 Yesu Kristu atakhala Mfumu yatsopano, anayamba kulanditsa otsatila ake odzozedwa kucoka mu ukapolo ku “Babulo Wamkulu.” (Chiv. 18:2, 4) Mu 1919 pambuyo pankhondo, panayambika nchito yapadziko lonse yolengeza za njila ya Mulungu yopulumutsila anthu ndi za Ufumu umene unakhazikitsidwawo. Akristu odzozedwa anatengela mwai nthawi imeneyi kucitila umboni. Zotulukapo n’zakuti ciŵelengelo ca Akristu odzozedwa odzalamulila ndi Kristu cinaonjezeka.

12 Ca m’ma 1935, zinaonekelatu kuti Kristu anayamba kusonkhanitsa anthu a “nkhosa zina” ocokela m’mitundu yosiyanasiyana. Anthu amenewa anali kudzapanga “khamu lalikulu.” Motsogoleledwa ndi Akristu odzozedwa, a nkhosa zina naonso amatsatila citsanzo ca Yesu ca kulimba mtima, ndipo amalengeza poyela kuti cipulumutso cao cidzacokela kwa Mulungu ndi Kristu. Cifukwa copitilizabe kucitila umboni ndi kukhulupilila nsembe ya Kristu, a khamu lalikulu adzapulumuka “cisautso cacikulu” cimene cidzaononga dziko la Satana.—Yoh. 10:16; Chiv. 7:9, 10, 14.

‘LIMBANI MTIMA KUTI MULANKHULE UTHENGA WABWINO’

13. Monga Mboni za Yehova, tifunikila kucitanji kuti tipambane?

13 Tiyeni tipitilize kuyamikila mwai umene tili nao wocitila umboni “zinthu zazikulu” zimene Yehova Mulungu wacita ndi malonjezo ake amtsogolo. N’zoona kuti si nthawi zonse pamene kucitila umboni kumakhala kopepuka. Abale athu ambili amalalikila m’magawo amene ali ndi anthu oculuka opanda cidwi, onyoza, kapena ozunza. Tiyenela kutengela zimene mtumwi Paulo ndi anzake anacita. Paulo anati: “Tinalimba mtima mothandizidwa ndi Mulungu wathu ndipo tinalankhula kwa inu uthenga wabwino wa Mulungu movutikila kwambili.” (1 Ates. 2:2) Conco, tisaleke kucitila umboni. M’malo mwake, tiyesetse kukhalabe okhulupilika mogwilizana ndi kudzipeleka kwathu pamene dongosolo la Satana lionongedwa. (Yes. 6:11) Koma sitingakwanitse kucita zimenezi mwa mphamvu zathu. Ndiye cifukwa cake, potengela citsanzo ca Akristu oyambilila, tizipemphela kwa Yehova kuti atipatse mzimu wake umene umapeleka “mphamvu yoposa yacibadwa.”—Ŵelengani 2 Akorinto 4:1, 7; Luka 11:13.

14, 15. (a) Kodi anthu anali kuwaona bwanji Akristu m’nthawi ya atumwi? Nanga mtumwi Petulo anati ciani ponena za io? (b) Tiyenela kumva bwanji ena akamatizunza pokhala Mboni za Yehova?

14 Lelolino, anthu ambili amanena kuti ndi Akristu, “koma amamukana [Mulungu] ndi zocita zao cifukwa ndi onyansa ndi osamvela, ndipo ndi osayenelela nchito iliyonse yabwino.” (Tito 1:16) Tizikumbukila kuti m’nthawi ya atumwi, Akristu oona anali kudedwa ndi anthu ambili. N’cifukwa cake mtumwi Petulo analemba kuti: “Ngati anthu akukunyozani cifukwa ca dzina la Kristu, ndinu odala cifukwa . . . mzimu wa Mulungu, wakhazikika pa inu.”—1 Pet. 4:14.

15 Kodi mau ouzilidwa amenewa akunenanso Mboni za Yehova za lelolino? Inde, cifukwa timacitila umboni za Ufumu wa Yesu. Conco, kudedwa cifukwa cocitila umboni za dzina la Yehova n’cimodzimodzi ndi ‘kunyozedwa cifukwa ca dzina la [Yesu] Kristu,’ amene anati: “Ndabwela m’dzina la Atate wanga, ndipo simunandilandile.” (Yoh. 5:43) Conco, mukadzakumana ndi otsutsa mu ulaliki, mudzakhale olimba mtima. Zimenezo ndi umboni wakuti Mulungu amakondwela nanu, ndi kuti mzimu wake ndi ‘wokhazikika pa inu.’

16, 17. (a) Kodi Mboni za Yehova zimakondwela kuona ciani m’maiko ambili? (b) Kodi inu muyenela kutsimikiza mtima kucita ciani?

16 Tizikumbukilanso kuti m’maiko ambili anthu oculukilaculukila akulandila coonadi. Ngakhale m’magawo amene amalalikidwa kwambili timapezabe anthu amene amafuna kumvetsela uthenga wokondweletsa wa cipulumutso. Tiyeni ticite khama kumabwelelako kwa anthu acidwi, ndipo ngati n’kotheka, tiziphunzila nao Baibulo ndi kuwathandiza kuti akadzipeleke ndi kubatizika. N’zotheka kuti inunso mumamva mmene Sarie, mlongo wa ku South Africa, amamvelela. Iye wakhala akucitila umboni mokangalika kwa zaka zopitilila 60. Iye anati: “Ndimayamikila kwambili kuti dipo la Yesu landithandiza kukhala paubale wolimba ndi Yehova, Mfumu ya cilengedwe conse. Ndine wokondwa kuti ndimathandiza ena kudziŵa dzina lake laulemelelo.” Mlongo ameneyu pamodzi ndi mwamuna wake Martinus, athandiza anthu ambili, kuphatikizapo ana ao atatu, kuyamba kulambila Yehova. Sarie ananenanso kuti: “Palibe nchito ina imene imandikondweletsa kuposa yolalikila. Ndipo mwa mzimu wake woyela, Yehova amatipatsa mphamvu yotithandiza kupitiliza kugwila nchito yopulumutsa moyo imeneyi.”

17 Kaya ndife Akristu obatizika kapena tikufuna kubatizika, tiyenela kuyamikila mwai umene tili nao wogwilizana ndi gulu la padziko lonse la Mboni za Yehova. Conco, tipitilize kucitila umboni mwakhama ndi kukhalabe oyela m’dziko lodetsedwa la Satana. Ngati ticita zimenezi, tidzapeleka ulemelelo kwa Atate wathu wakumwamba, amene timaimila dzina lake.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani