Citani Zinthu Mogwilizana Ndi Pemphelo La Yesu
“Atate, . . . lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni.”—YOH. 17:1.
KODI MUGANIZA BWANJI?
Kodi “kudziŵa” Mulungu kumatanthauza ciani?
M’nthawi ya atumwi, kodi Mulungu anayankha bwanji pemphelo la Yesu la pa Yohane 17?
Kodi tingacite bwanji zinthu mogwilizana ndi pemphelo la Yesu masiku ano?
1, 2. Kodi Yesu anacita ciani pambuyo pocita mwambo wa Pasika ndi atumwi ake m’caka ca 33 C.E?
YESU ndi mabwenzi ake anali atamaliza kucita mwambo wa Pasika pa Nisani 14, mu 33 C.E. Mwambo umenewo unali kuwakumbutsa mmene Mulungu anapulumutsila makolo ao mu ukapolo ku Iguputo. Koma ophunzila ake okhulupilika anali kuyembekezela ‘kulanditsidwa kwamuyaya.’ Tsiku lotsatila, Yesu anaphedwa ndi adani ake. Koma imfa yake inabweletsa madalitso. Nsembe ya moyo wake wangwilo inapangitsa kuti anthu onse apulumuke ku ucimo ndi imfa.—Aheb. 9:12-14.
2 Pofuna kuti tisaiŵale mphatso yacikondi imeneyi, Yesu anayambitsa mwambo watsopano wa pacaka umene unaloŵa m’malo mwa Pasika. Poyambitsa mwambo umenewu, iye ananyema mkate wopanda cotupitsa ndi kupatsa atumwi ake 11 okhulupilika. Ndiyeno, anawauza kuti: “Mkate uwu ukuimila thupi langa limene likupelekedwa cifukwa ca inu. Muzicita zimenezi pondikumbukila.” Anacitanso cimodzi-modzi ndi kapu ya vinyo wofiila ndi kuwauza kuti: “Kapu iyi ikutanthauza pangano latsopano pamaziko a magazi anga, amene adzakhetsedwa cifukwa ca inu.”—Luka 22:19, 20.
3. (a) Ndi kusintha kotani kumene kunacitika pambuyo pa imfa ya Yesu? (b) Ndi mafunso ati amene tiyenela kuganizila okhudza pemphelo la Yesu la pa Yohane 17?
3 Pangano lakale la Cilamulo pakati pa Mulungu ndi mtundu wa Aisiraeli linali pafupi kutha. Pangano limenelo linaloŵedwa m’malo ndi pangano latsopano pakati pa Yehova ndi otsatila a Yesu odzozedwa. Yesu sanafune kuti otsatila ake akhale monga mtundu wa Aisiraeli. Mtundu wa Aisiraeli sunali kulambila Mulungu mogwilizana, ndipo zimenezi zinapangitsa kuti dzina lake loyela linyozeke kwambili. (Yoh. 7:45-49; Mac. 23:6-9) Koma Yesu anafuna kuti otsatila ake azitumikila Mulungu mogwilizana n’colinga cakuti dzina la Mulungu lilemekezeke. Conco, kodi Yesu anacita ciani? Iye anapeleka pemphelo locokela pansi pa mtima limene timaŵelenga m’Baibo. (Yoh. 17:1-26; onani cithunzi-thunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.) Motelo, tingacite bwino kudzifunsa kuti, “Kodi Mulungu anayankha pemphelo la Yesu? Kodi ineyo ndikucita zinthu mogwilizana ndi pemphelo limeneli?”
ZINTHU ZOFUNIKA KWAMBILI KWA YESU
4, 5. (a) Kodi mau amene Yesu anakamba kuciyambi kwa pemphelo lake amatiphunzitsa ciani? (b) Kodi Yehova anayankha bwanji pempho la Yesu lokhudza tsogolo lake?
4 Kuyambila madzulo mpaka usiku kwambili, Yesu anaphunzitsa ophunzila ake zinthu zambili zocititsa cidwi ponena za Mulungu. Kenako, iye anakweza maso ake kumwamba ndi kupemphela kuti: “Atate, nthawi yafika, lemekezani mwana wanu, kuti mwana wanu akulemekezeni. Inu mwamupatsa ulamulilo pa anthu onse, kuti onse amene inu mwamupatsa, awapatse moyo wosatha. . . . Ndakulemekezani padziko lapansi, popeza ndatsiliza kugwila nchito imene munandipatsa. Ndipo tsopano Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemelelo umene ndinali nao pambali panu dziko lisanakhalepo.”—Yoh. 17:1-5.
5 Yesu anayamba pemphelo lake mwa kuchula zinthu zimene iye anaona kuti zinali zofunika kwambili. Cinthu cacikulu cimene iye anaona kuti cinali cofunika ndi kulemekeza Atate wake wakumwamba. Zimenezi ndi zogwilizana ndi cinthu coyamba cimene Yesu anapempha m’pemphelo lake lacitsanzo. Iye anati: “Atate, dzina lanu liyeletsedwe.” (Luka 11:2) Kenako, Yesu anapemphelela zosoŵa za ophunzila ake kuti “awapatse moyo wosatha.” Pambuyo pake, Yesu anapempha zinthu zaumwini. Iye anakamba kuti: “Atate, ndiloleni kuti ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemelelo umene ndinali nao pambali panu dziko lisanakhalepo.” Yehova anadalitsa Mwana wake wokhulupilika ndipo anam’patsa cinthu camtengo wapatali kuposa zimene anapempha. Mulungu anam’patsa “dzina lapamwamba kwambili kuposa” la angelo.—Aheb. 1:4.
‘KUDZIŴA MULUNGU YEKHAYO WOONA’
6. Kodi atumwi anafunika kucita ciani kuti akapeze moyo wosatha? Ndipo tidziŵa bwanji kuti io anapitiliza kucita zimenezo?
6 Yesu anafotokozanso zimene ife anthu ocimwa tiyenela kucita kuti tidzalandile mphatso yamtengo wapatali ya moyo wosatha. (Ŵelengani Yohane 17:3.) Iye anakamba kuti tifunika ‘kuphunzila ndi kudziŵa za” Mulungu ndi Kristu. Njila yoyamba imene tingacitile zimenezi ndi mwa kuphunzila zambili za Yehova ndi Mwana wake. Njila ina yofunika yophunzilila za Mulungu ndi kugwilitsila nchito zimene timaphunzila zokhudza iye. Atumwi anacitadi zinthu zopatsa moyo zimenezi cifukwa cakuti Yesu anapitiliza kunena kuti: “Mau amene munandipatsa ndawapeleka kwa io. Iwo awalandila.” (Yoh. 17:8) Koma kuti io akalandile moyo wosatha, anafunika kupitiliza kusinkha-sinkha Mau a Mulungu ndi kuwagwilitsila nchito pa umoyo wao nthawi zonse. Kodi atumwi okhulupilika anapitiliza kucita zimenezi mpaka pa mapeto a miyoyo yao? Inde anatelo. Tikudziŵa zimenezi cifukwa cakuti maina ao anazokotedwa pa miyala 12 ya maziko a Yerusalemu Watsopano wakumwamba.—Chiv. 21:14.
7. Kodi “kudziŵa” Mulungu kumatanthauza ciani? Ndipo n’cifukwa ciani kuli kofunika?
7 Malinga ndi akatswili a cinenelo ca Cigiriki, mau acigiriki amene anamasulidwa kuti “akamaphunzila ndi kudziŵa,” angamasulidwenso kuti “apitilize kudziŵa” kapena kuti “asaleke kudziŵa.” Conco, ‘kuphunzila ndi kudziŵa’ za Mulungu kumatanthauza kupitiliza kuphunzila zoonjezeleka ponena za iye. Komabe, kudziŵa Mulungu amene ndi wamkulu m’cilengedwe conse kumafuna zambili osati kudziŵa cabe makhalidwe ake ndi colinga cake. Kudziŵa Yehova kumaphatikizapo kukhala pa ubwenzi wolimba ndi iye ndiponso ndi okhulupilila anzathu. Baibo imati: “Munthu wopanda cikondi sadziŵa Mulungu.” (1 Yoh. 4:8) Motelo, munthu amene amadziŵa Mulungu ayenela kumumvela. (Ŵelengani 1 Yohane 2:3-5.) Ndi mwai waukulu kukhala anthu odziŵa Yehova. Koma n’zotheka kutaya mwai umenewu monga mmene anacitila Yudasi Isikariyoti. Conco, tiyenela kuyesetsa kulimbitsa ubwenzi wathu ndi Mulungu. Tikacita zimenezi, tidzalandila mphatso yamtengo wapatali ya moyo wosatha.—Mat. 24:13.
“CIFUKWA CA DZINA LANU”
8, 9. N’ciani cinali colinga cacikulu ca Yesu pa utumiki wake wa padziko lapansi? Nanga anakana kutsatila mwambo uti wacipembedzo?
8 Tikaŵelenga pemphelo la Yesu la pa Yohane 17, timaona kuti iye anali kukonda kwambili atumwi ake ndi ife tonse. (Yoh. 17:20) Komanso, tiyenela kukumbukila kuti colinga cacikulu ca Yesu si cakuti ife tikapulumuke. Pa utumiki wake wonse, iye anaonetsa kuti colinga cake cacikulu ndi kulemekeza Atate wake ndi kuyeletsa dzina lake. Mwacitsanzo, pofotokoza colinga cimene anabwelela padziko, Yesu anaŵelenga mpukutu wa Yesaya m’sunagoge ku Nazareti. Iye anaŵelenga kuti: “Mzimu wa Yehova uli pa ine, cifukwa iye anandidzoza kuti ndilengeze uthenga wabwino kwa osauka.” Sitikaikila kuti Yesu anachula dzina la Mulungu momveka bwino pamene anali kuŵelenga mau amenewa.—Luka 4:16-21.
9 Kale-kale Yesu asanabwele padziko lapansi, atsogoleli a cipembedzo aciyuda analetsa anthu kugwilitsila nchito dzina la Mulungu cifukwa cotsatila miyambo ya Ayuda. Mwacionekele, Yesu anakanilatu kutsatila mwambo wa anthu umenewo. Iye anauza amene anali kumutsutsa kuti: “Ndabwela m’dzina la Atate wanga, ndipo simunandilandile, koma wina akanabwela m’dzina lake, mukanamulandila ameneyo.” (Yoh. 5:43) Masiku angapo Yesu asanafe, anafotokoza colinga cake cacikulu. Popemphela, iye anati: “Atate lemekezani dzina lanu.” (Yoh. 12:28) N’zosadabwitsa kuti m’pemphelo ili limene tikukambilana, iye anafotokoza mobweleza-bweleza mfundo yakuti dzina la Atate wake lilemekezeke.
10, 11. (a) Kodi Yesu anadziŵitsa bwanji dzina la Atate wake? (b) N’cifukwa ciani ophunzila a Yesu amadziŵitsa ena dzina la Yehova?
10 M’pemphelo lake, Yesu anakambanso kuti: “Anthu amene munawatenga m’dziko ndi kundipatsa ine ndawadziŵitsa dzina lanu. Anali anu, koma munawapeleka kwa ine, ndipo io asunga mau anu. Komanso, ine sindikhalanso m’dzikoli pakuti ndikubwela kwa inu, koma io adakali m’dzikoli. Atate Woyela, ayang’anileni cifukwa ca dzina lanu limene mwandipatsa, kuti akhale amodzi mmene ife tilili.”—Yoh. 17:6, 11.
11 Kudziŵitsa ophunzila ake dzina la Atate wake kunatanthauza zambili osati kuchula cabe dzinalo. Yesu anawathandizanso kudziŵa bwino Mulungu, kutanthauza kudziŵa makhalidwe ake apamwamba, ndi mmene amacitila zinthu ndi ife. (Eks. 34:5-7) Ndiponso monga Mfumu yolemekezeka kumwamba, iye akuthandizabe ophunzila ake kudziŵitsa ena dzina la Yehova padziko lonse. Kodi colinga cake n’ciani? Colinga cake ndi kuthandiza anthu ambili kuphunzila za Yehova lisanathe dongosolo loipa lino la zinthu. Panthawi imeneyo, Yehova adzapulumutsa mboni zake zokhulupilika ndipo aliyense adzadziŵa dzina lalikulu la Yehova.—Ezek. 36:23.
“KUTI DZIKO LIKHULUPILILE”
12. Ndi zinthu zitatu ziti zimene tifunika kucita kuti tikwanitse kugwila nchito yathu yopulumutsa moyo?
12 Pamene anali padziko lapansi, Yesu anathandiza ophunzila ake kulimbana ndi zofooka. Zimenezi zinali zofunika kwambili kuti io amalize nchito imene iye anayambitsa. Yesu anapemphela kuti: “Monga mmene munanditumizila ine m’dziko, inenso ndawatumiza m’dziko.” Kuti io akwanitse kugwila nchito yopulumutsa moyo imeneyi, Yesu anatsindika zinthu zitatu zimene anafunikila kucita. Coyamba, iye anapemphelela ophunzila ake kuti asakhale mbali ya dziko la Satana loipali. Caciŵili, iye anawapemphelela kuti ayeletsedwe mwa kutsatila coonadi ca Mau a Mulungu. Cacitatu, anapempha ophunzila ake mobweleza-bweleza kuti akhale ogwilizana monga mmene iye ndi Atate wake alili ogwilizana. Conco, aliyense wa ife afunika kudzifunsa kuti, ‘Kodi zocita zanga zimagwilizana ndi zinthu zitatu zimene Yesu anapempha?’ Yesu anakhulupilila kuti ngati ophunzila ake acita zimenezi, anthu ambili angakhulupilile uthenga wao.—Ŵelengani Yohane 17:15-21.
13. Kodi Mulungu anayankha bwanji pemphelo la Yesu m’nthawi ya atumwi?
13 Timadziŵa kuti Mulungu anayankha pemphelo la Yesu tikaŵelenga buku la m’Baibo la Macitidwe. Ganizilani za Akristu oyambilila. Pakati pao panali Ayuda ndi anthu amitundu ina, olemela ndi osauka ndiponso akapolo ndi anthu amene anali kusunga akapolo. Conco, zinali zosavuta kuti pakhale magaŵano pakati pao. Komabe, onse anali ogwilizana kwambili cakuti anawayelekezela ndi ziwalo zosiyana-siyana za thupi limene mutu wake ndi Yesu. (Aef. 4:15, 16) M’dziko lino la Satana, mgwilizano umenewo unatheka kokha kaamba ka mphamvu ya mzimu woyela wa Mulungu.—1 Akor. 3:5-7.
14. Kodi pemphelo la Yesu layankhidwa bwanji masiku ano?
14 Koma zomvetsa cisoni ndi zakuti mgwilizano umenewo unatha pamene atumwi anafa. Monga mmene ulosi unanenela, mumpingo munayamba mpatuko waukulu umene unapangitsa kuti pakhale magulu osiyana-siyana a Machalichi Acikristu. (Mac. 20:29, 30) Koma mu 1919, Yesu anamasula otsatila ake odzozedwa mu ukapolo wa cipembedzo conama. Ndiyeno, anawasonkhanitsa kuti akhale ogwilizana mwa cikondi cimene “cimagwilizanitsa anthu mwamphamvu.” (Akol. 3:14) Nanga kodi nchito yao yolalikila yakhudza bwanji anthu padzikoli? A “nkhosa zina” opitilila 7 miliyoni ocokela “m’dziko lililonse, fuko lililonse, mtundu uliwonse, ndi cinenelo ciliconse” asonkhanitsidwa kukhala gulu limodzi ndi odzozedwa a Mulungu. (Yoh. 10:16; Chiv. 7:9) Zimenezi zikuyankha pemphelo la Yesu lakuti “dziko lidziŵe kuti inu [Yehova] munandituma ine, ndi kuti munawakonda io mmene munandikondela ine.”—Yoh. 17:23.
MAPETO OCITITSA CIDWI
15. Kodi Yesu anawapemphela ciani ophunzila ake odzozedwa?
15 Pa Nisani 14 m’madzulo, Yesu analemekeza atumwi ake mwa kucita nao pangano kuti adzalamulila pamodzi ndi iye mu Ufumu wake. (Luka 22:28-30; Yoh. 17:22) Yesu anapemphelela otsatila ake onse odzozedwa kuti: “Atate, ine ndikufuna kuti amene mwandipatsawa adzakhale limodzi ndi ine kumene ine ndidzakhale, kuti adzaone ulemelelo wanga umene inu mwandipatsa, cifukwa munandikonda musanayale maziko a dziko.” (Yoh. 17:24) A nkhosa zina sacita nsanje koma amakondwela ndi mphoto imene odzozedwa adzalandila. Izi ndi umboni wakuti Akristu onse oona padziko lapansi ndi ogwilizana masiku ano.
16, 17. (a) Kumapeto kwa pemphelo lake, kodi Yesu anatsimikiza kuti adzapitiliza kucita ciani? (b) Kodi tiyenela kupitiliza kucita ciani?
16 Cifukwa cosonkhezeledwa ndi abusa a zipembedzo zao, anthu ambili m’dzikoli amanyalanyaza umboni wakuti Yehova ali ndi anthu ogwilizana amene amamudziŵa bwino. M’nthawi ya Yesu anthu anacita zofanana ndi zimenezi. Conco, iye anamaliza pemphelo lake ndi mau ocititsa cidwi awa: “Atate wolungama, ndithudi dziko silinakudziŵeni, koma ine ndikukudziŵani ndipo awa adziŵa kuti inu munandituma. Ine ndacititsa kuti io adziŵe dzina lanu ndipo ndidzapitiliza kuwadziŵitsa dzinalo kuti cikondi cimene munandikonda naco cikhale mwa io, inenso ndikhale wogwilizana ndi io.”—Yoh. 17:25, 26.
17 N’zosacita kufunsa kuti Yesu wacita zinthu mogwilizana ndi pemphelo lake. Monga Mutu wa mpingo, iye akutithandiza kudziŵitsa ena dzina la Atate wake ndi colinga cake. Tiyeni tisaleke kugonjela umutu wake mwa kumvela ndi mtima wonse lamulo lake lakuti tizilalikila ndi kupanga ophunzila. (Mat. 28:19, 20; Mac. 10:42) Ndiponso, tiyeni tiyesetse kusunga mgwilizano wathu wamtengo wapatali. Ngati ticita zimenezi, tidzaonetsa kuti timacita zinthu mogwilizana ndi pemphelo la Yesu kuti dzina la Yehova lilemekezeke ndi kuti tidzasangalale kwamuyaya.
[Cithunzi papeji 26]
Akristu a m’nthawi ya atumwi anatsogoleledwa ndi mzimu woyela kuti akhale ogwilizana (Onani ndime 13)
[Cithunzi papeji 28]
Anthu a Yehova padziko lonse ndi ogwilizana (Onani ndime 14)