KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO
N’cifukwa ciani tiyenela kupemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele?
Ufumu wa Mulungu ndi boma la kumwamba. Yesu anauza ophunzila ake kupemphela kuti ufumuwo ubwele, cifukwa udzabwezeletsa cilungamo ndi mtendele padziko lapansi. Kulibe boma la anthu limene lingathetseletu nkhanza, kupanda cilungamo kapena matenda. Koma Ufumu wa Mulungu ndi umene ungakwanitse ndipo udzacitadi zimenezi. Mulungu wasankha Yesu Mwana wake kukhala Mfumu ya Ufumu umenewo. Yehova wasankhanso gulu la otsatila a Yesu kuti akakhale olamulila anzake mu Ufumuwo.—Ŵelengani Luka 11:2; 22:28-30.
Posacedwapa, Ufumu wa Mulungu udzacotsapo anthu onse amene amatsutsa ulamulilo wa Mulungu. Conco, tikamapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele timakhala kuti tikupempha kuti boma la Mulungu liloŵe m’malo mwa maboma a anthu.—Ŵelengani Danieli 7:13, 14; Chivumbulutso 11:15, 18.
N’cifukwa ciani anthu adzapindula ndi Ufumu wa Mulungu?
Yesu ndi Mfumu yoyenelela cifukwa ndi wacifundo. Pokhala Mwana wa Mulungu, iye alinso ndi mphamvu zothandiza anthu amene amafuulila Mulungu pofuna thandizo.—Ŵelengani Salimo 72:8, 12-14.
Ufumu wa Mulungu udzapindulitsa makamaka anthu onse amene amaupemphelela ndi mtima wonse komanso amene amacita zinthu mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu. Kuphunzila zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu ndi kosangalatsa.—Ŵelengani Luka 18:16, 17; Yohane 4:23.