LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp16 na. 5 tsa. 16
  • Kodi Baibulo Imakamba Ciani?

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Kodi Baibulo Imakamba Ciani?
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwela Liti?
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Kodi Pali Boma Lodalilika Limene Lingalamulile Dziko Lapansi?—Kodi Baibo Ikambapo Ciyani?
    Nkhani Zina
  • Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
wp16 na. 5 tsa. 16
Kuwala kufika pa dziko lapansi kucokela ku mpando wacifumu kumwamba

Kodi Baibulo Imakamba Ciani?

Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

ANTHU ENA AMAKHULUPILILA kuti Ufumu wa Mulungu ni mtima wa munthu. Ena amaganiza kuti ni mtendele umene anthu adzabweletsa padziko lonse. Inu muganiza bwanji?

ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

“M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. . . . Koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo [a anthu], ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.” (Danieli 2:44) Ufumu wa Mulungu ndi boma leni-leni.

MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

  • Ufumu wa Mulungu uli kumwamba ndipo ukulamulila.—Mateyu 10:7; Luka 10:9.

  • Mulungu amaseŵenzetsa Ufumu umenewo kuti akwanilitse cifunilo cake kumwamba na padziko lapansi.—Mateyu 6:10.

Kodi Ufumu wa Mulungu Udzabwela Liti?

MUNGAYANKHE BWANJI?

  • Palibe amene adziŵa

  • Posacedwa

  • Sudzabwela

ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

“Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Uthenga wabwino ukalalikidwa mokwanila, Ufumu wa Mulungu udzabwela kudzaononga dziko loipali.

MFUNDO ZINA ZIMENE BAIBULO IMAKAMBA

  • Palibe munthu aliyense padziko lapansi amene adziŵa tsiku limene Ufumu wa Mulungu udzabwela.—Mateyu 24:36.

  • Maulosi a m’Baibulo amaonetsa kuti Ufumu wa Mulungu udzabwela posacedwa.—Mateyu 24:3, 7, 12.

Kuti mudziŵe zambili, onani nkhani  8 m’buku ili, Zimene Baibulo Ingatiphunzitse, lofalitsidwa na Mboni za Yehova

Bukuli limapezekanso pa webusaiti ya www.jw.org

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani