Mau Oyamba
MUGANIZA BWANJI?
Timakumana ndi mavuto ambili paumoyo masiku ano. Muganiza n’kuti kumene tingapeze thandizo na citonthozo?
Baibulo imati: “Tate wacifundo cacikulu ndi Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.” —2 Akorinto 1:3, 4.
Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza mmene Mulungu amatitonthozela.