LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 June masa. 4-8
  • Yehova Amatitonthoza m’Masautso Athu Onse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amatitonthoza m’Masautso Athu Onse
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “NSAUTSO M’THUPI”
  • KULANDILA CITONTHOZO TIKAKHALA PA MAVUTO
  • CITONTHOZO M’BANJA
  • Kulimbikitsa Amene Anacitilidwapo Zolaula
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Mmene Mulungu Amatitonthozela
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • Mau Oyamba
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 June masa. 4-8
Hana apemphela

Yehova Amatitonthoza m’Masautso Athu Onse

“Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, . . . amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 AKOR. 1:3, 4.

NYIMBO: 38, 56

MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani tingayembekezele kuti munthu akaloŵa m’banja adzakumana ndi mavuto?

  • Kodi pemphelo linawatonthoza bwanji anthu ena ochulidwa m’Baibo?

  • Inu pamwekha, mungacite ciani kuti mutonthoze ena?

1, 2. Kodi Yehova amatitonthoza bwanji tikakumana ndi mavuto? Nanga Mau ake amatitsimikizila ciani?

M’BALE wina wacinyamata wosakwatila, amene tam’patsa dzina lakuti Eduardo, anafotokozela Stephen, mkulu wacikulile wokwatila, zinthu zimene zimamudetsa nkhawa. Eduardo anali kuganizila mau amene timaŵelenga pa 1 Akorinto 7:28. Mauwo amati, “Oloŵa m’banja adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” Iye anafunsa m’bale Stephen kuti: “Kodi ‘nsautso’ imeneyi n’ciani? Nanga nidzathana nayo bwanji nikadzakwatila?” M’bale Stephen asanayankhe funso limenelo, anapempha Eduardo kuti aganizilenso mau ena amene mtumwi Paulo analemba akuti, Yehova ni “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse, amenenso amatitonthoza m’masautso athu onse.”—2 Akor. 1:3, 4.

2 Kunena zoona, Yehova ni Tate wacikondi, ndipo amatitonthoza tikakumana ndi mavuto. Mwina imwe mukumbukila nthawi ina pamene Mulungu anakuthandizani ndi kukutsogolelani kupitila m’Mau ake. Tingakhale otsimikiza kuti iye amatifunila zabwino, monga mmene anacitila na atumiki ake akale.—Ŵelengani Yeremiya 29:11, 12.

3. Kodi tidzakambilana mafunso ati?

3 Nthawi zambili, tikadziŵa cimene cipangitsa mavuto amene tikumana nawo, cimakhala copepukako kuwapilila. Ni mmenenso zilili na mavuto a m’banja. Conco tingafunse kuti, N’zinthu ziti zimene zingabweletse “nsautso m’thupi,” imene Paulo anakamba? Nanga n’zitsanzo ziti zakale na zamakono zimene zingatilimbikitse? Kudziŵa mayankho a mafunso amenewa kudzatithandiza kupilila.

“NSAUTSO M’THUPI”

4, 5. N’zinthu ziti zimene zimayambitsa “nsautso m’thupi”?

4 Mulungu atalenga anthu aŵili oyambilila, anakamba kuti: “Mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake, n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo iwo adzakhala thupi limodzi.” (Gen. 2:24) Yehova anakamba mau amenewa pomanga cikwati coyambilila. Komabe, popeza ndise opanda ungwilo, anthu akakwatilana n’kukhala na banja lawo, pamakhala mavuto ena amene angasokoneze mgwilizano wawo ndi acibululu awo. (Aroma 3:23) Mwacitsanzo, mkazi asanakwatiwe amafunika kugonjela ulamulilo wa makolo, koma akakwatiwa amafunika kugonjela ulamulilo wa mwamuna wake. Mulungu anaika mwamuna kukhala mutu wa mkazi wake. (1 Akor. 11:3) Koma amuna ndi akazi ena akaloŵa m’banja, zimawavuta kutsatila dongosolo limeneli. Malinga n’zimene Mau a Mulungu amakamba, mkazi wokwatiwa afunika kuvomeleza kuti mwamuna wake ndiye azimutsogolela osati makolo ake. Komanso, anthu amene aloŵa kumene m’banja, nthawi zina angakangane ndi azipongozi awo, ndipo zimenezi zingakhalenso nsautso kwa iwo.

5 Nkhawa m’banja imawonjezekanso pamene mkazi wakhala na pakati. N’zoona kuti mwamuna na mkazi amakhala na cimwemwe podziŵa kuti adzakhala na mwana. Koma amadelanso nkhawa za thanzi la mayi na mwana wodzabadwayo. Cinanso, pamafunika ndalama zoculukilapo zosamalila mayi woyembekezela na mwana amene adzabadwa. Ndipo mwanayo akabadwa, iwo amafunikanso kusintha zinthu zina n’zina paumoyo wawo. Mwacitsanzo, mayi akhoza kumathela nthawi yaitali akusamalila mwana wake. Pa cifukwa cimeneci, amuna ambili amaona monga kuti akunyalanyazidwa na mkazi wawo, popeza kuti mkaziyo amatangwanika ndi kusalamalila mwana. Komanso, mwamuna akakhala tate, maudindo ake amawonjezeka cifukwa amafunika kusamalila onse aŵili, mayi ndi mwana.

6-8. Kodi vuto la kusabala lingacititse bwanji munthu kukhala na nkhawa?

6 Palinso vuto lina limene anthu ena a pabanja amakumana nalo. Amafunitsitsa kukhala na mwana, koma alibe mphatso yobala. Ngati mkazi satenga pakati, angayambe kukhala na nkhawa kwambili. N’zoona kuti kukhala pabanja ndi kubala ana kumakhala na mavuto ake. Komabe, ngati munthu amafunitsitsa kubala koma sizitheka, imakhalanso “nsautso m’thupi.” (Miy. 13:12) M’nthawi zakale, kukhala wosabala cinali cinthu cocititsa manyazi. Ndiye cifukwa cake Rakele, mkazi wa Yakobo, anadandaula ataona kuti mkulu wake akubala ana koma iye ayi. (Gen. 30:1, 2) Amishonale amene amatumikila ku mayiko kumene anthu amakhala na ana oculuka, nthawi zambili amafunsidwa cifukwa cake sakhala ndi ana. Ngakhale kuti amayesetsa kuwayankha momveka bwino ndi mosamala, ena mwa anthuwo amawauza kuti, “Pepani, koma nidziŵako munthu wina amene angakufunileni mankhwala.”

7 Komanso, ganizilani za mlongo wina wa ku England, amene anali kufunitsitsa kukhala na mwana koma sizinatheke. Iye anafika pa msinkhu wakuti sangabeleke. Atadziŵa kuti sadzabala m’dongosolo lino la zinthu, zinamupweteka kwambili mumtima. Conco, iye na mwamuna wake anaganiza zotenga mwana wa anthu ena kuti azimulela monga wawo. Olo kuti anacita zimenezi, iye anati: “N’napitilizabe kudzimvela cisoni. N’nali kuona kuti kutenga mwana wa munthu wina n’kosiyana ndi kukhala ni wanga-wanga.”

8 Baibo imakamba kuti mkazi wacikhristu ‘amatetezeka mwa kubeleka ana.’ (1 Tim. 2:15) Koma izi sizitanthauza kuti kubala ana n’kumene kungapangitse munthu kudzakhala na moyo wosatha. Koma zitanthauza kuti mkazi akakhala ndi ana amakhala wotangwanika kusamalila anawo ndi kugwila nchito zina za pakhomo, ndipo izi zingam’thandize kupewa mijedo na kuloŵelela m’nkhani za eni. (1 Tim. 5:13) Ngakhale n’telo, iye angakumanebe ndi mavuto ena a m’banja.

Mlongo amene ali na cisoni atonthozedwa ndi kulimbikitsidwa na mlongo wina. Alimbikitsidwanso mwa kupezeka pa misonkhano, ndi kupita muulaliki

Kodi mungapilile bwanji ngati munthu amene munali kukonda wamwalila? (Onani palagilafu 9, 12)

9. N’cifukwa ciani tingakambe kuti kufeledwa mnzako wa m’cikwati n’kosiyana na ziyeso zina?

9 Pa mavuto amene anthu a m’banja amakumana nawo, pali vuto lina limene saliyembekezela. Vuto limeneli ni imfa ya mnzawo wa m’cikwati. Ili ni vuto limene nthawi zambili mwamuna kapena mkazi saganizilako kuti angakumane nalo m’dongosolo lino. Komabe, Akhristu amakhulupilila kwambili lonjezo la Yesu lakuti akufa adzauka. (Yoh. 5:28, 29) Kodi lonjezo limeneli limathandiza bwanji mwamuna kapena mkazi amene wafeledwa? Ndi lotonthoza kwambili. Iyi ni njila ina imene Atate wathu wacikondi, kupitila m’Mau ake, amathandizila ndi kutonthoza anthu amene akumana ndi mavuto aconco. Lomba, tiyeni tikambilane mmene atumiki ena a Mulungu anatonthozedwela na Yehova, ndi mmene anapindulila na citonthozo cake.

KULANDILA CITONTHOZO TIKAKHALA PA MAVUTO

10. Kodi Hana anapeza kuti thandizo pamene anali na nkhawa? (Onani pikica kuciyambi.)

10 Hana, mkazi wokondedwa wa Elikana, anakumana ndi vuto lalikulu. Iye sanali kubala, koma mkazi mnzake, Penina, anali kubala. (Ŵelengani 1 Samueli 1:4-7.) Hana anali kutonzedwa na Penina “caka ndi caka.” Izi zinali kumupweteka kwambili mumtima. Komabe, iye anapeza citonthozo mwa kuuza Yehova vuto lake m’pemphelo. Hana ‘anapemphela kwa Yehova kwa nthawi yaitali.’ Kodi anali kuyembekezela kuti Yehova adzam’patsa zimene anapempha? Mosakayikila. Ndipo atapemphela, “sanakhalenso ndi nkhawa.” (1 Sam. 1:12, 17, 18) Hana anali kukhulupilila kuti Yehova adzathetsa vuto lake la kusabala kapena adzamuthandiza mwa njila ina.

11. Kodi pemphelo limatitonthoza bwanji?

11 Popeza ndise opanda ungwilo ndipo tikukhala m’dziko lolamulidwa na Satana, tidzapitilizabe kukumana ndi mavuto. (1 Yoh. 5:19) Komabe, n’zokondweletsa kudziŵa kuti Yehova ni “Mulungu amene amatitonthoza m’njila iliyonse.” Njila imodzi imene Mulungu amatithandizila kulimbana ndi mavuto, ni kupitila m’pemphelo. Hana anakhutulila Yehova za mumtima mwake. Nafenso tikakumana na mavuto, tifunika kumuuza Yehova mmene timvelela. Koma tifunika kucita zambili kuposa pamenepa. Tifunika kum’pepha mopembedzela komanso mocokela pansi pa mtima.—Afil. 4:6, 7.

12. N’ciani cinathandiza Anna mkazi wamasiye kukhala wacimwemwe?

12 Ngati tili na cisoni cacikulu cifukwa cakuti tilibe mwana, kapena cifukwa wokondedwa wathu anamwalila, n’zotheka kupeza citonthozo. M’nthawi ya Yesu, mneneli wamkazi Anna atakhala m’cikwati zaka 7 cabe, mwamuna wake anamwalila. Ndipo Baibo sionetsa kuti iye anali ndi ana. Koma kodi n’ciani cimene Anna anali kucita ngakhale pamene anali na zaka 84? Lemba la Luka 2:37 limakamba kuti: “Sanali kusoŵa pakacisi. Anali kucita utumiki wopatulika usana ndi usiku, anali kusala kudya ndi kupeleka mapembedzelo.” Ndithudi, Anna anatonthozedwa ndiponso anapeza cimwemwe cifukwa colambila Yehova.

13. Fotokozani citsanzo coonetsa mmene mabwenzi eni-eni amatonthozela ngati acibale athu alephela kucita zimenezo.

13 Pamene tiyanjana ndi abale na alongo athu, timapeza mabwenzi eni-eni komanso apamtima. (Miy. 18:24) Mwacitsanzo, pamene Paula anali na zaka 5, amayi ake anasiya coonadi. Iye akumbukila kuti panthawiyo anamvela cisoni kwambili. Ndipo kulimbana ndi ciyeso cimeneci kunali kovuta. Koma analimbikitsidwa kwambili ndi mlongo Ann, mpainiya mumpingo mwawo. Mlongoyu anayesetsa kum’thandiza mwauzimu. Paula anati: “Ngakhale kuti Ann sanali m’bululu wanga, cikondi cimene ananionetsa cinanithandiza kwambili. Cinanithandiza kuti nipitilize kutumikila Yehova.” Mpaka pano, Paula akutumikilabe Mulungu mokhulupilika. Amayi ake anabwelela mumpingo, ndipo iye ni wokondwela ngako kuti akutumikilanso nawo pamodzi. Nayenso Ann ni wokondwa ngako, cifukwa wakhala monga amayi ake auzimu a Paula.

14. Kodi anthu amene amatonthoza ena amapeza madalitso anji?

14 Ngati ticitila zabwino anthu ena, timacepetsako nkhawa zathu. Alongo, okwatiwa ndi osakwatiwa omwe, amakhala na cimwemwe coculuka ngati auzako ena uthenga wabwino monga anchito anzake a Mulungu. Colinga cawo ni kulemekeza Mulungu mwa kucita cifunilo cake. Ena amafika poona nchito yolalikila monga mankhwala. Kunena zoona, ngati tonse ticitila anzathu zabwino, kaya akhale a mumpingo kapena a m’gawo lathu, timathandiza kuti mumpingo mukhale mgwilizano. (Afil. 2:4) Mtumwi Paulo anali citsanzo cabwino pankhani imeneyi. Iye anali monga “mayi woyamwitsa” kwa Akhristu a mumpingo wa ku Tesalonika. Analinso ngati tate wawo kuuzimu.—Ŵelengani 1 Atesalonika 2:7, 11, 12.

CITONTHOZO M’BANJA

15. N’ndani maka-maka amene ali na udindo wophunzitsa ana coonadi?

15 Cinthu cimodzi cofunika cimene tingacite ndi kulimbikitsa ndi kuthandiza makolo na ana awo. Nthawi zina, anthu atsopano m’coonadi, amapempha ofalitsa ena okhwima mwauzimu kuti awathandize kuphunzitsa ana awo coonadi, mwina ngakhale kuwaphunzitsa Baibo. Malinga n’zimene Malemba amakamba, makolo ndi amene ali na udindo wophunzitsa ndi kulangiza ana awo. (Miy. 23:22; Aef. 6:1-4) Komabe, nthawi zina makolo atsopano m’coonadi angafunike thandizo la ena ndipo amaliyamikila kwambili. Olo n’conco, iwo safunika kusiyila ena udindo wawo wophunzitsa ana. Nthawi zonse afunika kumakambilana ndi ana awo.

16. Pothandiza ana, kodi Mkhristu afunika kukumbukila ciani?

16 Ngati makolo apempha Mkhristu wina kuti aziphunzitsa ana awo coonadi, Mkhristuyo afunika kucita zinthu mosamala kuti asakhale ngati akulanda udindo wa makolo. Nthawi zina, Mkhristu angapemphedwe kuti aziphunzitsa Baibo ana amene makolo awo sali m’coonadi. Komabe, Mkhristuyo afunika kukumbukila kuti ngakhale wapemphedwa kuthandiza ana mwauzimu, iye sindiye kholo la anawo. Ndipo ngati acititsa phunzilo laconco, angacite bwino kumaphunzilila panyumba pa anawo pamodzi na makolo awo, kapena ali na Mkhristu wina wokhwima mwauzimu, kapenanso atakhala pa malo oonekela bwino. Akatelo, anthu sangakayikile zimene akucita. Ndipo m’kupita kwa nthawi, mwina makolowo adzakwanilitsa udindo umene Mulungu anawapatsa, wophunzitsa ana awo zinthu zauzimu.

17. Kodi ana angatonthoze bwanji ndi kulimbikitsa ena m’banja?

17 Ana amene amakonda Mulungu woona ndi kutsatila malamulo ake, amatonthoza ndi kulimbikitsa ena m’banja. Angacite zimenezi mwa kulemekeza makolo awo ndi kuwathandiza pa zinthu zakuthupi. Akhozanso kuwathandiza mwauzimu. Cigumula cisanacitike, Lameki mbadwa ya Seti, anali kulambila Yehova. Lameki anakamba zokhudza mwana wake Nowa kuti: “Uyu ndi amene adzatibweletsele mpumulo ku nchito yathu yopweteketsa manja, cifukwa colima nthaka imene Yehova anaitembelela.” Ulosi umenewu unakwanilitsidwa pamene Mulungu anacotsa tembelelo pa nthaka. (Gen. 5:29; 8:21) Masiku anonso, ana amene amalambila Mulungu angalimbikitse ena m’banja. Angawathandize kupilila ziyeso zimene akumana nazo masiku ano ndi ziyeso zina zazikulu mtsogolo.

18. N’ciani cingatithandize kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo?

18 Pemphelo, kuganizila mozama pa zitsanzo za m’Baibo, ndi kuyanjana ndi anthu a Yehova, kukuthandiza anthu mamiliyoni ambili kupeza citonthozo pa mavuto awo onse. (Ŵelengani Salimo 145:18, 19.) Kudziŵa kuti Yehova ndi Gwelo la citonthozo ceni-ceni, kudzatithandiza kupilila mavuto aliwonse amene tingakumane nawo, lomba ndiponso mtsogolo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani