Mau oyamba
MUGANIZA BWANJI?
Kodi mphatso ya Mulungu yopambana zonse imene anatipatsa ni iti?
Baibo imati: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha.”—Yohane 3:16.
Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda, ifotokoza cifukwa cake Mulungu anatuma Yesu padziko lapansi kuti adzatifele. Ifotokozanso mmene tingaonetsele ciyamikilo cathu pa mphatso imeneyo.