LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 2 masa. 3-4
  • Mphatso Yopambana Zonse

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mphatso Yopambana Zonse
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Nkhani Zofanana
  • Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse N’cifukwa Ciani ni Yamtengo Wapatali?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Ni Mphatso Iti Yoposa Zonse?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Dipo la Yesu—Mphatso ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Dipo Ni Mphatso Ya Mulungu Yopambana Zonse
    Zimene Baibulo Ingatiphunzitse
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 2 masa. 3-4
Mwamuna wacikulile apatsa kamnyamata kosongolela pensulo kooneka monga boti

NKHANI YA PACIKUTO | KODI MUDZALANDILA MPHATSO YA MULUNGU YOPAMBANA ZONSE?

Mphatso Yopambana Zonse

KOSONGOLELA pensulo kooneka monga boti m’manja mwa Jordan, kanali kuoneka kacabe-cabe. Komabe, n’kamodzi mwa zinthu za mtengo wapatali kwa iye. Jordan anakamba kuti: “A Russell, bwenzi lacikulile la banja lathu, ni amene ananipatsa pamene n’nali wamng’ono kwambili.” A Russell atamwalila, Jordan anauzidwa kuti a Russell anali kuthandiza kwambili ambuye ake aamuna ndi makolo ake. Iwo anali kuwalimbikitsa panthawi ya mavuto. Jordan anati: “Popeza tsopano nadziŵa zambili zokhudza a Russell, nimaona kuti ka mphatso kocepa kameneka ni kamtengo wapatali kwa ine kuposa kale.”

Monga mmene citsanzo ca Jordan cionetsela, anthu ena angaone kuti mphatso ina yake ni yosathandiza konse. Koma kwa munthu woyamikila, mphatsoyo ingakhale yamtengo wapatali, komanso yothandiza kwambili. Baibo imakamba za mphatso yamtengo wapatali m’mau odziŵika bwino akuti: “Mulungu anakonda kwambili dziko mwakuti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupilila iye asawonongeke, koma akhale ndi moyo wosatha.”—Yohane 3:16.

Kodi pali mphatso ina yamtengo wapatali kuposa imene ingapatse munthu moyo wosatha? Anthu ena sangaone mapindu a mphatso imeneyo, koma Akhristu oona amaiona kuti ni ‘yamtengo wapatali.’ (Salimo 49:8; 1 Petulo 1:18, 19) Nanga n’cifukwa ciani Mulungu anapeleka moyo wa Mwana wake monga mphatso ya anthu onse?

Mtumwi Paulo anafotokoza cifukwa cake m’mau awa akuti: ‘Ucimo unaloŵa m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo inafalikila kwa anthu onse.’ (Aroma 5:12) Munthu woyamba, Adamu, anacimwila dala mwa kusamvela Mulungu. Conco, iye anapatsiwa cilango ca imfa. Kupitila mwa Adamu, imfa inafikila ana ake onse, amene ni mtundu wa anthu.

“Malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.” (Aroma 6:23) Kuti Mulungu amasule mtundu wa anthu ku cilango ca imfa, anatuma Mwana wake, Yesu Khristu, kubwela pa dziko kuti adzapeleke nsembe moyo wake wangwilo cifukwa ca anthu. Onse amene akhulupilila Yesu adzakhala na moyo wamuyaya. Moyo umenewo udzatheka cifukwa ca nsembe ya Yesu, yochedwa “dipo.”—Aroma 3:24.

Pokamba za madalitso onse amene Mulungu adzapatsa alambili ake kupitila mwa Yesu Khristu, Paulo anati: “Tikuyamika Mulungu cifukwa ca mphatso yake yaulele, imene sitingathe n’komwe kuifotokoza.” (2 Akorinto 9:15) Inde, dipo ndi mphatso yapadela kwambili cakuti sitingakwanitse bwino-bwino kuifotokoza. Pa mphatso zonse zabwino zimene Mulungu anapatsa anthu, n’cifukwa ciani dipo ni yamtengo wapatali? Kodi imapambana mphatso zina za Mulungu m’njila yabwanji?a Nanga tingacitepo ciani pa mphatso imeneyi? Tikupemphani kuti muŵelenge nkhani ziŵili zotsatila kuti mudziŵe mayankho a m’Baibo pa mafunso amenewa.

a Yesu “anapeleka moyo wake [na mtima wonse] cifukwa ca ife.” (1 Yohane 3:16) Komabe, popeza nsembe imeneyo inali mbali ya colinga ca Mulungu, nkhani zino zotsatizana zidzafotokoza kwambili udindo wa Mulungu monga Wopeleka dipo.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani