LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 3 masa. 12-15
  • “Ndiwe Mkazi Wokongola m’Maonekedwe Ako”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Ndiwe Mkazi Wokongola m’Maonekedwe Ako”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “TULUKA M’DZIKO LAKO”
  • “ANASAMUKA M’DZIKO”
  • “KULOŴELA KU IGUPUTO”
  • Mulungu Anamucha Mfumukazi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Mpaka Anakhala na Mwana Wake!
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Abulahamu na Sara Anamvela Mulungu
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • Abulahamu—mnzake Wa Mulungu
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 3 masa. 12-15
Sara

TENGELANI CIKHULUPILILO CAWO SARA

“Ndiwe Mkazi Wokongola m’Maonekedwe Ako”

SARA anali ataimilila pakati m’cipinda akuyang’ana uku na uku. Yelekezani kuti mukuona mkazi wa ku Middle East, wa maso okongola mocititsa kaso. Kodi akuoneka ndi nkhope yacisoni? Ngati zili conco, si zovuta kumvetsa cifukwa cake. Banja limeneli linapita m’zambili. Iye na mwamuna wake wokondeka, Abulahamu, anali atakhala zaka zambili mumzinda wa Uri, ndipo anali kusangalala.a Iwo anali atapanga mzindawu kukhala mudzi wawo.

Iwo anali kukhala mumzinda wolemela wa Uri, umene unali ndi akatswili ambili a zopanga-panga ndi amalonda. Conco, ayenela kuti anali na katundu wambili. Kwa Sara, mzindawu sunali cabe malo osungilamo katundu, koma unali wokondeka kwambili. Kumeneku, iye na mwamuna wake anali kukhala na umoyo wabwino, koma nthawi zina anali kukumana ndi zokhumudwitsa. N’kumenenso anali kulambila Mulungu wawo Yehova kwa zaka zambili. Sara anali na zifukwa zambili zokondela malo amenewa.

Komabe, Sara anali wokonzeka kusiya malo amene anajaila. Ngakhale kuti mwina anali ndi zaka za m’ma 60, anakwanitsa kuyenda m’madela acilendo, na kukhala umoyo wovutitsa. Analibe ciyembekezo cakuti angabwelelenso kwawo. N’ciani cinapangitsa kuti umoyo wake usinthe kwambili conco? Nanga ife tiphunzilapo ciani pa cikhulupililo cake masiku ano?

“TULUKA M’DZIKO LAKO”

Sara ayenela kuti anakulila ku Uri. Masiku ano, mzinda umenewo ni matongwe okha-okha. Koma m’nthawi ya Sara, sitima za amalonda zinali kuyenda-yenda mumtsinje wa Firate, kubweletsa katundu wamtengo wapatali mumzinda wolemelawu kucokela m’madela akutali. Mumzinda wa Uri, anthu ambili anali kupitana-pitana m’tumiseu, sitima zinali pilingu-pilingu m’madoko, ndipo m’tumashopu munali kupezeka katundu wambili. Sara anakulila mumzindawu umene anthu ake anali otangwanika kwambili, ndipo iye anali kudziŵana ndi anthu ambili. Iwonso anali kum’dziŵa cifukwa anali mkazi wokongola maningi. Analinso na acibululu ambili mumzindawu.

Sara ni wodziŵika m’Baibo kaamba ka cikhulupililo cake colimba. Koma sikuti cikhulupililo cake cinali mwa mulungu wa mwezi amene anthu ambili anali kulambila ku Uri. Cinsanja ca mulungu ameneyu cinali kuonekela patali mumzindawu. Koma Sara anali kulambila Mulungu woona, Yehova. Malemba sakamba mmene Sara anakhalila na cikhulupililo. Poyamba, atate ŵake ayenela kuti anali kulambila mafano. Sara anakwatiwa ndi Abulahamu, amene anali kum’posa na zaka 10.b (Genesis 17:17) M’kupita kwa nthawi, Abulahamu anachedwa “tate wa onse . . . okhala ndi cikhulupililo.” (Aroma 4:11) Cikwati cawo cinali colimba, ndipo anali kulemekezana, kukambitsana bwino, ndi kukhala ofunitsitsa kuthetsa mavuto capamodzi. Koma copambana zonse n’cakuti iwo anali kudziŵika monga banja lokonda Mulungu.

Sara anali kum’konda ngako mwamuna wake. Aŵiliwa anali kukhala mumzinda wa Uri pamodzi ndi acibale awo, ndipo anali na nyumba yawo-yawo. Koma pasanapite nthawi itali, iwo anakumana ndi vuto. Baibo imakamba kuti Sara “anali wosabeleka, conco analibe mwana.” (Genesis 11:30) Malinga ndi cikhalidwe ca m’nthawi imeneyo, limeneli linali vuto lalikulu. Koma Sara anakhalabe wokhulupilika kwa Mulungu ndi kwa mwamuna wake. Loti, mwana wamasiye wa m’bale wawo, ndiye anakhala monga mwana wawo. Umoyo unali conco mpaka pamene zinthu zinasintha.

Abulahamu anapita kwa Sara ali wokondwela maningi. Cinamuvuta kukhulupilila zimene zinam’citikila. Mulungu amene anali kulambila anali ataonekela kwa iye na kukamba naye, mosakaikila kupitila mwa mngelo. Ganizilani cabe mmene Sara anayang’anitsitsila mwamuna wake ndi maso ake okongola, na kum’funsa mtima uli m’mwamba kuti: “Wakuuzani ciani? Niuzeni!” Mwina Abulahamu ayenela kuti anakhala pansi coyamba kuganizila mmene angamuuzile. Ndiyeno, anamuuza zimene Yehova anakamba kuti: “Tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako. Tiye ukaloŵe m’dziko limene ine ndidzakusonyeza.” (Machitidwe 7:2, 3) Pambuyo pakuti cisangalalo cawo catha, anayamba kuganizila za nchito imene Yehova anali atawapatsa. Anafunika kusiya umoyo wawo wabwino ndi kukakhala umoyo wosamuka-samuka. Kodi Sara adzacita ciani? Mosapeneka, Abulahamu anamuyang’ana Sara. Kodi iye adzamucilikiza pa kusintha kwakukulu kumene kudzacitika pa umoyo wawo?

Cosankha cimene Sara anafunika kupanga cingaoneke cacilendo kwa ife. Tingaganize kuti, ‘Mulungu akalibe kuniuzapo kapena kuuza mnzanga wa m’cikwati kucita ciliconse colinganako na zimenezo.’ Ngakhale n’conco, ife tonse timafunika kusankha pankhani yolinganako na imeneyi. Tikukhala m’dziko lokondetsetsa cuma, limene limatilimbikitsa kukhala ndi umoyo wa wofu-wofu na kukhala ndi katundu wambili. Koma Baibo imatiuza kusankha kuika patsogolo zinthu zauzimu, ndi kukondweletsa Mulungu m’malo modzikondweletsa tekha. (Mateyu 6:33) Pamene tiganizila zimene Sara anacita, tingadzifunse kuti, ‘Kodi n’dzasankha kucita ciani pa umoyo wanga?’

“ANASAMUKA M’DZIKO”

Pamene Sara anali kulonga katundu, iye anavutika kusankha katundu umene adzasiya ndi umene adzatenga. Sanafunike kutenga zinthu zikulu-zikulu zimene abulu na ngamila zingalephele kunyamula, komanso wosafunikila pa umoyo wosamuka-samuka. Mosakaikila, katundu wawo wambili anafunika kuugulitsa kapena kupatsa ena. Anafunikilanso kusiya mzinda umene unali ndi mamaliketi kapena tumashopu togulako zakudya monga cimanga, mpunga, nyama, zipatso, zovala, na zinthu zina.

Sara asankha katundu umene adzatenga, na umene adzasiya ku Uri

Cikhulupililo ca Sara cinam’cititsa kusiya umoyo wabwino kwawo

Mwinanso zinali zovuta kwa Sara kuti asiye nyumba yake. Ngati nyumbayo inali yolingana ndi manyumba amene ofukula zinthu zakale apeza mumzinda wa Uri, ndiye kuti Sara anasiya umoyo wabwino maningi. Zina mwa nyumbazo zinali na zipinda zopitilila 12, akasupe a madzi abwino, mabafa na zimbudzi zamkati. Ngakhale nyumba zazing’ono zinali na zitseko zokhala ndi loko. Koma kodi tenti ikanawateteza ku akawalala, mikango, anyalugwe, zimbalangondo, ndi mimbulu, zimene zinali zofala m’madela ochulidwa m’Baibo panthawiyo?

Nanga bwanji acibululu? N’ndani amene Sara anali kudzasiya? Lamulo la Mulungu lakuti, “tuluka m’dziko lako ndi pakati pa abale ako” liyenela kuti linali lovuta kwa Sara. Pokhala mkazi wacikondi, iye ayenela kuti anali ndi azilongosi ake, ana aamuna ndi aakazi a azilongosi, azakhali, ndi azimalume ake, amene anali kuwakonda kwambili, komanso amene mwina sakanawaonanso. Komabe, Sara analimba mtima, ndipo tsiku na tsiku anali kukonzekela ulendo wawo.

Mosasamala kanthu za zimenezi, tsiku laulendo litafika, Sara anali wokonzeka kunyamuka. Tera atate wawo, anapita ndi Abulahamu na Sara, olo kuti anali na zaka pafupi-fupi 200. (Genesis 11:31) N’kutheka kuti Sara anali na nchito yaikulu yosamalila kholo lokalamba limeneli. Nayenso Loti anapita nawo pomvela Yehova, ndipo iwo “anasamuka m’dziko la Akasidi.”—Machitidwe 7:4.

Coyamba iwo anayenda kudziko la Harana, pa mtunda wa makilomita 960 kumpoto ca kum’madzulo, motsatila mtsinje wa Firate. Ku Harana, banja limeneli linakhalako kwa kanthawi. Panthawiyi, Tera ayenela kuti anali wodwala ndipo sakanakwanitsa kupitiliza ulendowo. Banjali linakhala kumeneko kufikila Tera atamwalila ali na zaka 205. Panthawi ina iwo akali m’dziko la Harana, Yehova anakambanso na Abulahamu, kumuuza kuti acoke m’dzikoli na kuyenda kudziko limene Yehova anali kudzamuonetsa. Panthawi iyi, Yehova anam’lonjeza cinthu cosangalatsa kuti: “Ndidzatulutsa mtundu waukulu mwa iwe.” (Genesis 12:2-4) Pamene anali kusamuka ku Harana, Abulahamu anali na zaka 75, ndipo Sara anali na zaka 65, koma analibe mwana. Kodi mtundu waukulu ukanatuluka bwanji mwa iye? Kodi Abulahamu anafunika kukwatilanso mkazi wina? Popeza kuti nthawiyo cipali cinali cofala, mwina Sara anaganiza kuti n’zimene mwamuna wake ayenela kucita.

Mulimonse mmene zinalili, iwo anacoka ku Harana na kupitiliza ulendo. Koma onani anthu amene tsopano anali nawo paulendowu. Nkhani iyi ya m’Baibo imatiuza kuti banja la Abulahamu linasamuka ndi cuma cimene anapeza ndiponso “akapolo awo onse amene anapeza kudziko la Harana.” (Genesis 12:5) Mosakaikila, Abulahamu na Sara anali kuuzako anthu ofuna kumvetsela za cikhulupililo cawo. Mabuku ena akale aciyuda amakamba kuti akapolo ochulidwa palembali anali anthu a mitundu ina, amene anagwilizana ndi Abulahamu na Sara kulambila Yehova. Ngati zilidi conco, mosakaikila cikhulupililo colimba ca Sara cinapangitsa kuti aziuzako ena za Mulungu wake ndi ciyembekezo cake mowafika pamtima. Tifunika kutengelapo phunzilo pamenepa, cifukwa tikukhala m’nthawi imene anthu ambili alibe cikhulupililo na ciyembekezo. Mukaphunzila zinthu zabwino m’Baibo, kodi simungauzeko ena?

“KULOŴELA KU IGUPUTO”

Pambuyo pooloka mtsinje wa Firate, mwacionekele pa Nisani 14, 1943 B.C.E., iwo analoŵela ca kum’mwela kuyenda kudziko limene Yehova anawalonjeza. (Ekisodo 12:40, 41) Yelekezani kuti mukuona Sara akutembenuka kuyang’ana uku na uku, kuona kukongola kwa dzikolo komanso nyengo yake yabwino. Pafupi na mitengo ikulu-ikulu ya More imene ili pafupi na Sekemu, Yehova anaonekelanso kwa Abulahamu, na kumuuza kuti: “Ndidzapeleka dziko ili kwa mbeu yako.” Mau akuti “mbeu,” ayenela kuti anali atanthauzo kwambili kwa Abulahamu. Anam’cititsa kuganizila zimene Yehova anakamba m’munda wa Edeni kuti mbeu ya munthu idzawononga Satana. Yehova anali atauza Abulahamu kuti mtundu umene udzacokela mwa iye udzatsegula khomo la madalitso kwa anthu onse padziko lapansi.—Genesis 3:15; 12:2, 3, 6, 7.

Ngakhale n’conco, banjali linali kukumanabe na mavuto a m’dzikoli. M’dziko la Kanani munagwa njala yaikulu. Conco, Abulahamu analoŵela ca kum’mwela na banja lake kuyenda ku Iguputo. Komabe, iye anadziŵilatu zoipa zimene angadzakumane nazo m’dzikomo. Motelo, anauza Sara kuti: “Ndikudziŵa ndithu kuti ndiwe mkazi wokongola m’maonekedwe ako. Aiguputo akakuona, mosakayikila anena kuti, ‘Ameneyu ndi mkazi wake.’ Ndipo andipha ndithu, koma iweyo akusiya wamoyo. Ndiye conde, unene kuti ndiwe mlongo wanga kuti zindiyendele bwino. Ukatelo upulumutsa moyo wanga.” (Genesis 12:10-13) N’cifukwa ciani Abulahamu anapempha zimenezi?

Sikuti Abulahamu anali wabodza kapena wamantha, monga mmene otsutsa amakambila. N’zoona kuti Sara anali mlongo wake wa mimba ina. Ndipo panali zifukwa zomveka zimene Abulahamu anacitila zimenezo. Abulahamu na Sara anali kudziŵa kuti colinga ca Mulungu codzatulutsa mbeu na mtundu wapadela kupitila mwa iye, zinali zofunika maningi kuposa ciliconse. Conco, iye anaona kuti m’pofunika kuti adziteteze. Kuwonjezela apo, umboni wozikidwa pa zinthu zakale uonetsa kuti zinali zofala kwa mafumu aciiguputo kulanda mkazi wamwini mwacikakamizo na kupha mwamuna wake. Motelo, Abulahamu anacita zinthu mwanzelu, ndipo modzicepetsa Sara nayenso anagwilizana nazo.

Pasanapite nthawi itali, zimene zinacitika zionetsa kuti nkhawa ya Abulahamu inali yomveka. Akalonga a Farao anaona kuti Sara anali wokongola kwambili, ngakhale kuti panthawiyo anali wacikulile. Conco, iwo anauza Farao, ndipo iye analamula kuti mkaziyo amubweletse kwa iye. Sitingamvetse mmene Abulahamu anavutikila maganizo, kapena kumvetsa nkhawa imene Sara anali nayo. Komabe, zioneka kuti Sara anasamalidwa bwino monga mlendo wolemekezeka, osati monga kapolo. Mwina Farao anali kufuna kumukopa na cuma cake, ndiyeno n’kukambilana ndi mlongosi wake kuti am’tenge kukhala mkazi wake.—Genesis 12:14-16.

Yelekezani kuti mukuona Sara m’nyumba yacifumu akuyang’ana pawindo kuona dziko lokongola la Iguputo. Kodi iye anamvela bwanji kukhalanso m’nyumba yabwino, ndi kudya zakudya zabwino? Kodi iye anakopeka na umoyo wabwino, mwina wapamwamba kuposa umene anali nawo ku Uri? Ganizilani mmene Satana akanasangalalila sembe Sara anaganiza zosiya Abulahamu na kukhala mkazi wa Farao. Koma Sara sanacite zimenezo. Iye anali wokhulupilika kwa mwamuna wake, cikwati cake, ndi kwa Mulungu wake. M’dziko lino la ciwelewele, zingakhale bwino ngati onse a m’cikwati akanakhala okhulupilika conco. Pocita zinthu ndi anthu amene mumakonda komanso anzanu, kodi mungatengele kukhulupilika kwa Sara?

Sara ali m’nyumba yacifumu ya Farao

Sara anakhalabe wokhulupilika kwa mwamuna wake, olo kuti m’nyumba yacifumu ya Farao munali zinthu zambili zokopa

Yehova analoŵelelapo kuti ateteze mkazi wokondeka ameneyu, mwa kugwetsela Farao ndi banja lake milili. Pamene Farao anadziŵa kuti Sara anali mkazi wa Abulahamu, anam’tumiza kwa mwamuna wake, na kuuza banja lonse kuti licoke mu Iguputo. (Genesis 12:17-20) Abulahamu anakondwela kwambili kukhalanso na mkazi wake wokondeka! Kumbukilani kuti iye anali atauza mkazi wake kuti: “Ndikudziŵa ndithu kuti ndiwe mkazi wokongola m’maonekedwe ako.” Koma anayamikilanso kukongola kwina kumene Sara anali nako, kumene kunali kuposa kukongola m’maonekedwe. Sara analidi wokongola m’makhalidwe, ndipo kukongola kwaconco n’kumene Yehova amaona kuti n’kofunika. (1 Petulo 3:1-5) Kukongola kwa conco n’kumene ife tonse tifunikila kukhala nako. Tingatengele cikhulupililo ca Sara mwa kuika zinthu zauzimu patsogolo m’malo mwa zakuthupi, kuuzako ena za Mulungu, na kucilikiza mokhulupilika mfundo zake za makhalidwe abwino tikakumana ndi mayeselo.

a Poyamba, maina awo anali Abulamu ndi Sarai. Koma amadziŵika kwambili na maina amene Yehova anawapatsa.—Genesis 17:5, 15.

b Sara anali mlongosi wa Abulahamu. Atate awo anali Tera, koma amayi awo anali osiyana. (Genesis 20:12) Ngakhale kuti ukwati waconco si woyenela masiku ano, n’kofunika kuganizila mmene zinthu zinalili kalelo. Anthu anali pafupi na ungwilo umene Adamu na Hava anataya. Conco, kwa iwo kukwatilana ndi wacibululu sikunabweletse vuto lililonse kwa ana amene anali kubeleka. Koma patapita zaka 400, anthu anali atatalikilana kwambili na ungwilo. Panthawi imeneyo, Cilamulo ca Mose cinaletsa vikwati va pacibululu.—Levitiko 18:6.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani