LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp17 na. 5 masa. 7-8
  • Mmene Angelo Angakuthandizileni

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Mmene Angelo Angakuthandizileni
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ANGELO ANATHANDIZA MPINGO WACIKHRISTU WOYAMBILILA
  • MMENE ANGELO ANGAKUTHANDIZILENI
  • Tengelani Citsanzo ca Angelo Okhulupilika
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Zoona Zake Ponena za Angelo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
wp17 na. 5 masa. 7-8

NKHANI YA PACIKUTO | ANGELO KODI ALIKO ZOONA? CIFUKWA CAKE TIFUNA KUDZIŴA

Mmene Angelo Angakuthandizileni

Angelo okhulupilika amacita cidwi na umoyo wa anthu, ndipo ni odzipeleka kucita cifunilo ca Yehova. Pamene Mulungu analenga dziko lapansi, angelo ‘anafuula pamodzi mokondwela, ndipo ana onse a Mulungu anayamba kufuula ndi cisangalalo.’ (Yobu 38:4, 7) Kuyambila kale, angelo akhala akulaka-laka ‘kusuzumila’ m’maulosi okhudza zocitika za kutsogolo padziko lapansi.—1 Petulo 1:11, 12.

Baibo imaonetsa kuti panthawi ina, angelo anathandizapo alambili oona pofuna kukwanilitsa cifunilo ca Mulungu. (Salimo 34:7) Mwacitsanzo:

  • Yehova atatsala pafupi kuwononga mizinda yoipa ya Sodomu na Gomora, angelo anathandiza munthu wolungama Loti na banja lake kuthaŵa.—Genesis 19:1, 15-26.

  • Ku Babulo wakale, anyamata atatu aciheberi anaponyedwa m’ng’anjo yamoto kuti afe, koma Mulungu “anatumiza mngelo wake ndi kupulumutsa atumiki ake.”—Danieli 3:19-28.

  • Munthu wolungama Danieli atakhala m’dzenje la mikango yolusa usiku umodzi, iye anakamba kuti anapulumuka cifukwa ‘Mulungu anatumiza mngelo wake kudzatseka pakamwa pa mikango.’—Danieli 6:16, 22.

Mngelo ateteza Danieli ku mikango

Kwa zaka zambili, angelo akhala akuthandiza anthu okhulupilika

ANGELO ANATHANDIZA MPINGO WACIKHRISTU WOYAMBILILA

Nthawi zina, angelo otumidwa na Mulungu anali kuloŵelelapo pa zocitika za mpingo wacikhristu woyambilila. Anali kucita izi kukakhala kofunikila kuti akwanilitse cifunilo ca Yehova. Mwacitsanzo:

  • Pamene atumwi anali m’ndende, mngelo anatsegula zitseko za ndendeyo, na kuwauza kuti apitilize kulalikila m’kacisi.—Machitidwe 5:17-21.

  • Mngelo analamula mlaliki Filipo kupita ku msewu wa kucipululu, wocokela ku Yerusalemu kupita ku Gaza kuti akalalikile Mwiitiyopiya, amene anali kucokela ku Yerusalemu kukalambila.—Machitidwe 8:26-33.

  • Pamene Mulungu anafuna kuti anthu amene sanali Ayuda akhale Akhristu, mngelo anaonekela kwa Koneliyo mkulu wa asilikali wa Aroma m’masomphenya, na kumuuza kuti aitanile mtumwi Petulo kunyumba kwake.—Machitidwe 10:3-5.

  • Pamene mtumwi Petulo anali m’ndende, mngelo anaonekela kwa iye na kum’cotsa m’ndendemo.—Machitidwe 12:1-11.

MMENE ANGELO ANGAKUTHANDIZILENI

Palibe umboni woonetsa kuti masiku ano Mulungu amaseŵenzetsa angelo kuthandiza anthu mozizwitsa, monga mmene anacitila kwa anthu ochulidwa m’Baibo. Komabe, pokamba za masiku ano Yesu anati: “Uthenga wabwino uwu wa Ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.” (Mateyu 24:14) Kodi mudziŵa kuti ophunzila a Khristu akugwila nchitoyi motsogoleledwa na angelo?

Anthu akupitana-pitana pa kashelu ka ulaliki wapoyela

Angelo akuthandiza pa nchito yolalikila uthenga wabwino padziko lonse

Buku la Chivumbulutso limaonetsa kuti angelo adzagwila nchito mwakhama kuthandiza anthu padziko lonse kuphunzila za Yehova Mulungu na colinga cake pa anthu. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinaona mngelo winanso akuuluka capafupi m’mlengalenga. Iye anali ndi uthenga wabwino wosatha woti aulengeze monga nkhani yosangalatsa kwa anthu okhala padziko lapansi, ndi kudziko lililonse, fuko lililonse, cinenelo ciliconse, ndi mtundu uliwonse. Iye anali kunena mofuula kuti: ‘Opani Mulungu ndi kumupatsa ulemelelo, cifukwa ola lakuti apeleke ciweluzo lafika. Cotelo lambilani Iye amene anapanga kumwamba, dziko lapansi, nyanja, ndi akasupe amadzi.’” (Chivumbulutso 14:6, 7) Zocitika zambili masiku ano zimapeleka umboni wakuti angelo akucilikiza nchito yolalikila za Ufumu padziko lonse. Ndithudi, ngakhale munthu mmodzi wocimwa akalapa na kubwelela kwa Yehova, “kumakhala cisangalalo coculuka kwa angelo a Mulungu.”—Luka 15:10.

N’ciani cidzacitika nchito yolalikila ikadzatha? Magulu ankhondo a angelo kumwamba adzathandiza Yesu Khristu, Mfumu ya Mafumu, kumenya ‘nkhondo ya tsiku lalikulu la Mulungu Wamphamvuyonse’ pa Aramagedo. (Chivumbulutso 16:14-16; 19:14-16) Angelo amphamvu adzatumikila monga akupha pa ciweluzo ca Mulungu, pamene Ambuye Yesu “adzabwezela cilango kwa anthu . . . osamvela uthenga wabwino wonena za Ambuye wathu Yesu.”—2 Atesalonika 1:7, 8.

Conco, khalani otsimikiza kuti angelo onse amacita cidwi na imwe. Amadela nkhawa kwambili umoyo wa amene akufuna kutumikila Mulungu, ndipo nthawi zambili Yehova wakhala akuwaseŵenzetsa kulimbikitsa na kuteteza atumiki ake okhulupilika padziko lapansi.—Aheberi 1:14.

Aliyense wa ife afunika kupanga cosankha cacikulu. Kodi tidzamvetsela na kucitapo kanthu pa uthenga wabwino umene ukulalikidwa padziko lonse lapansi? A Mboni za Yehova a kudela lanu, adzasangalala kukuthandizani kuti mupindule na thandizo lacikondi la angelo a Mulungu amphamvu.

Kuti mudziŵe zambili zimene Baibo imakamba ponena za angelo okhulupilika ndi osakhulupilika, onani nkhani 10 m’buku la Zimene Baibulo Ingatiphunzitse lofalitsiwa na Mboni za Yehova. Lipezekanso pa webusaiti ya jw.org kapena mungaunike QR khodi iyi.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani