LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w25 May masa. 2-7
  • Tengelani Citsanzo ca Angelo Okhulupilika

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Tengelani Citsanzo ca Angelo Okhulupilika
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ANGELO NDI ODZICEPETSA
  • ANGELO AMAKONDA ANTHU
  • ANGELO NDI OPILILA
  • ANGELO AMATHANDIZA KUSUNGITSA CIYELO CA MPINGO
  • Mmene Angelo Angakuthandizileni
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Zoona Zake Ponena za Angelo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2017
  • Mafunso Ocokela Kwa Oŵelenga
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
w25 May masa. 2-7

NKHANI YOPHUNZILA 19

NYIMBO 6 Zakumwamba Zilengeza Ulemelelo wa Mulungu

Tengelani Citsanzo ca Angelo Okhulupilika

“Tamandani Yehova, inu angelo ake onse.”​—SAL. 103:20.

ZOFUNIKA KUMVETSETSA

Maphunzilo amene tingatengepo pa citsanzo ca angelo okhulupilika.

1-2. (a) Kodi timasiyana bwanji ndi angelo? (b) Nanga timafanana nawo pa zinthu ziti?

PAMENE Yehova anakuphunzitsani coonadi, munalowa m’banja lacikondi la alambili ake. Banja limeneli limaphatikizapo abale ndi alongo padziko lonse lapansi komanso angelo mamiliyoni ambili okhulupilika. (Dan. 7:​9, 10) Tikaganizila za angelo, nthawi zambili tingaganizile kusiyana komwe kulipo pakati pa iwo ndi ife. Mwacitsanzo, angelo analengedwa kale kwambili ife tisanalengedwe. (Yobu 38:​4, 7) Ndipo ndi amphamvu kwambili kuposa ife. Ndi oyela komanso olungama kwambili kuposa ife anthu opanda ungwilo.​—Luka 9:26.

2 Ngakhale kuti timasiyana nawo motelomo, timafanana nawo pa zinthu zambili. Mwacitsanzo, mofanana ndi angelo, nafenso tingaonetse makhalidwe okhumbilika a Yehova. Cina, monga alili angelo, nafenso tili ndi ufulu wodzisankhila zocita. Monga iwo, nafenso tili ndi maina, maumunthu osiyanasiyana, komanso maudindo osiyanasiyana. Kuwonjezela apo, monga alili angelo, nafenso tili ndi cifuno colambila Mlengi wathu.​—1 Pet. 1:12.

3. Tingaphunzile ciyani kwa angelo okhulupilika?

3 Popeza angelo timafanana nawo m’zambili, citsanzo cawo cabwino cingatilimbikitse ndipo tingaphunzile zambili kwa iwo. M’nkhani ino, tione mmene tingatengele citsanzo ca angelo okhulupilika pa kudzicepetsa kwawo, cikondi cawo pa anthu, kupilila kwawo, komanso pa khama limene amaonetsa posungitsa ciyelo mumpingo.

ANGELO NDI ODZICEPETSA

4. (a) Kodi angelo amaonetsa bwanji kuti ndi odzicepetsa? (b) N’cifukwa ciyani angelo ndi odzicepetsa? (Salimo 89:7)

4 Angelo okhulupilika ndi odzicepetsa. Iwo amadziwa zambili, ndi amphamvu, komanso ndi anzelu. Ngakhale n’telo, amamvelabe malangizo a Yehova. (Sal. 103:20) Akamacita mautumiki awo, sadzitamanda pa zimene akwanitsa kucita kapena kudzionetsela kuti ali ndi mphamvu zambili kuposa anthu. Amasangalala kucita cifunilo ca Mulungu ngakhale kuti maina awo sadziwika.a (Gen. 32:​24, 29; 2 Maf. 19:35) Iwo amakana kulandila ulemelelo woyenela kupita kwa Yehova. N’cifukwa ciyani angelo ndi odzicepetsa kwambili? N’cifukwa cakuti amam’konda Yehova ndipo amam’lemekeza kwambili.​—Welengani Salimo 89:7.

5. Kodi mngelo wina anaonetsa bwanji kudzicepetsa powongolela mtumwi Yohane? (Onaninso cithunzi.)

5 Ganizilani cocitika ici cimene cionetsa kuti angelo ndi odzicepetsadi. Ca m’ma 96 C.E., mngelo amene sanachulidwe dzina anaonetsa mtumwi Yohane zinthu zocititsa cidwi. (Chiv. 1:1) Kodi Yohane anacita ciyani ataona masomphenyawo? Anafuna kulambila mngeloyo. Koma mngelo wokhulupilikayo mwamsanga anam’letsa ndipo anauza Yohane kuti: “Samala! Usacite zimenezo! Inetu ndangokhala kapolo mnzako ndi wa abale ako . . . Lambila Mulungu.” (Chiv. 19:10) Ati kudzicepetsa kwake! Mngeloyo sanafune kutamandidwa kapena kupatsidwa ulemu. Nthawi yomweyo anauza Yohane kuti alambile Yehova Mulungu. Panthawi imodzimodzi, sanadzione kukhala wapamwamba kuposa Yohane. Mngeloyo anatumikila Yehova kwa nthawi yaitali ndipo anali wamphamvu kwambili kuposa Yohane. Koma anamuuza modzicepetsa kuti ndi kapolo mnzake. Ngakhale kuti panali pofunika kuti mngeloyo awongolele Yohane, iye sanamudzudzule mwankhanza mtumwi wokalambayo. M’malomwake, mngeloyo anakamba naye mwacikondi. Ayenela kuti anazindikila kuti Yohane anafuna kum’lambila, cabe cifukwa ca zimene anaona.

Mngelo akuletsa mtumwi Yohane kumugwadila ndi kumulambila.

Mngelo anacita zinthu modzicepetsa pokambilana ndi Yohane komanso pomuwongolela (Onani ndime 5)


6. Tingakhale bwanji odzicepetsa ngati angelo?

6 Tingatengele bwanji citsanzo ca kudzicepetsa kwa angelo? Monga zilili ndi angelo, nafenso timafuna kugwila nchito molimbika potumikila Yehova. Timafuna kucita zimenezo popanda kudzionetsela pa zimene takwanitsa kucita, kapena kufuna kuti anthu ena atitamande. (1 Akor. 4:7) Kuwonjezela apo, sitiyenela kudziona apamwamba kuposa ena ngati tatumikila Yehova kwa nthawi yaitali, kapena cifukwa ca maudindo apadela amene tili nawo. Koma pamene takhala ndi maudindo owonjezela, m’pamene tiyenelanso kukhala odzicepetsa kwambili. (Luka 9:48) Mofanana ndi angelo, nafenso timafuna kutumikila ena. Sitifuna kupangitsa ena kutiona kuti ndife apadela kuposa iwo.

7. Tingaonetse bwanji kuti ndife odzicepetsa pamene tipeleka uphungu kwa ena?

7 Tizikhalanso odzicepetsa powongolela munthu kapena pomupatsa uphungu, kaya munthuyo ndi wokhulupilila mnzathu kapena mwana wathu. Nthawi zina tingafunike kupeleka uphungu wosapita m’mbali. Koma monga mmene mngelo anapelekela uphungu kwa Yohane mokoma mtima, nafenso tingapeleke uphungu wosapita m’mbali popanda kupangitsa munthuyo kudziona kuti ndi wolephela. Ngati sitidziona kuti ndife apamwamba kuposa ena, tidzapeleka uphungu wa m’Baibo mwaulemu komanso mokoma mtima.​—Akol. 4:6.

ANGELO AMAKONDA ANTHU

8. (a) Malinga ndi Luka 15:​10, kodi angelo amaonetsa bwanji kuti amakonda anthu? (b) Kodi angelo amathandiza bwanji pa nchito yolalikila? (Onaninso cithunzi )

8 Angelo sadziona apamwamba kwambili kapena osiyana kwambili ndi anthu. Ndipo iwo amakonda anthu. Amasangalala ngati munthu amene anacita chimo lalikulu, kapena amene anasiya kutumikila Yehova wabwelela kwa iye. Amakondwelanso ngati munthu waphunzila coonadi komanso wasintha umoyo wake kuti atumikile Yehova. (Welengani Luka 15:10.) Angelo nawonso amatengako mbali mokangalika pa nchito yolalikila za Ufumu. (Chiv. 14:6) Ngakhale kuti salalikila anthu mwacindunji, iwo angatsogolele wofalitsa kwa munthu amene akufuna kuphunzila za Yehova. Koma ife sitingadziwe motsimikiza kuti pa cocitika cinacake, ndi mngelo amene anatitsogolela. Zili conco cifukwa Yehova angagwilitse nchito njila zina, monga mzimu wake woyela, pothandiza anthu kapena potsogolela atumiki ake. (Mac. 16:​6, 7) Ngakhale n’telo, iye amagwilitsa nchito angelo ake pa mlingo waukulu potithandiza pamene tikulalikila. Conco, pamene tiuzako ena uthenga wabwino, sitikaikila kuti angelo ali nafe kuti atithandize.​—Onani bokosi lakuti “Mapemphelo Awo Anayankhidwa.”b

Banja lili ndi kasitandi ka ulaliki wapoyela pomwe likuyenda mumzinda waukulu. Angelo ali capafupi ndipo akulongoza mlongo kuti aone mkazi wovutika maganizo amene wakhala pampando.

Banja lina likucoka pa ulaliki wapoyela. Pamene akubwelela kunyumba, mlongo waona mkazi amene akuoneka wovutika maganizo. Mlongoyo wakumbukila kuti angelo angatitsogolele kwa anthu amene akufuna thandizo lakuuzimu. Zimenezi zamusonkhezela kukamba ndi mkaziyo mokoma mtima (Onani ndime 8)


Mapemphelo Awo Anayankhidwa

Kodi n’kutheka kuti Yehova anagwilitsa nchito angelo kuyankha mapemphelo am’zocitika zotsatilazi?

  • Wofalitsa wina wa zaka 12 ku dziko la Peru, anali kucita ulaliki wapafoni ndi amayi ake. Anakambilana ndi mzimayi wina amene anali kupemphela kwa Mulungu kuti atumize munthu winawake kukam’thandiza kudziwa za Mulungu. Mzimayiyo anaona kuti kukambilana ndi mtsikanayo linali yankho la pemphelo lake, ndipo anayamba kuphunzila Baibo. Posapita nthawi anayamba kupezeka ku misonkhano.

  • Mzimayi wina wa ku Romania anali kuphunzila Baibo kwa kanthawi kenako analeka. Pambuyo pake, pamene anali kugwilila nchito banja lina ku Italy, anafuna kuyambanso kuphunzila. Koma iye sanali kudziwa wa Mboni aliyense kumaloko. Conco anapempha Yehova kuti am’thandize. Posapita nthawi, banjalo linamupempha kuti akawagulile zinthu ku sitolo. Anamuuza kuti asakakambilane ndi mwiniwake wa sitoloyo. Iwo anati: “Iye ndi wa Mboni za Yehova, ndipo amakamba ndi makasitomala ake zinthu zokhudza Baibo.” Zinacitikadi kuti mzimayiyu atafika ku sitolo m’bale uja anamulalikila, ndipo iye anaona kuti limeneli linali yankho la pemphelo lake. Conco anayambanso kuphunzila ndipo anapita patsogolo kuuzimu. Mwana wake ataona citsanzo cake cabwino, nayenso anayamba kuphunzila Baibo ndi kupezeka ku misonkhano.

  • Banja lina la Mboni linaganiza zogulitsa motoka yawo. Pamene banja lina linabwela kudzaona motokayo, banja la Mboni linawafotokozela cifukwa cake anali kuigulitsa. Anawafotokozela kuti anali kuigulitsa cifukwa anali kufuna kukhala ndi umoyo wosalila zambili, komanso anawafotokozela za nchito yathu yophunzitsa Baibo. Mwamuna wa banja limene linali kufuna kugula motokayo anati: “Dzulo n’napemphela kuti, ‘Conde Mulungu, ndipatseni munthu amene angan’thandize. Ndili ndi mafunso ambili ndipo nifuna kudziwa coonadi.’” Iye anaona kuti kukumana ndi banjali linali yankho la pemphelo lake. Iye ndi mkazi wake anayamba kuphunzila Baibo kuphatikizapo atsikana awo acicepele awili. Banjali tsopano limapezeka ku misonkhano ya Cikhristu.

9. Tingaonetse bwanji kuti timakonda anthu monga mmene angelo amacitila?

9 Tingaonetse bwanji kuti timakonda anthu mmene angelo amacitila? Tikamva cilengezo cakuti munthu wina wabwezeletsedwa, timakondwela monga mmene angelo amacitila. Tingacite zoposa pamenepa mwa kupita kwa munthuyo n’kumuuza kuti tamulandila, komanso kuti tikusangalala kuti wayambilanso kutumikila Yehova. (Luka 15:​4-7; 2 Akor. 2:​6-8) Tingatengelenso citsanzo ca angelo pocita zonse zimene tingathe pa nchito yolalikila. (Mlal. 11:6) Monga mmene angelo amatithandizila polalikila uthenga wabwino, nafenso tingapeze njila zothandizila abale ndi alongo athu kugwilako nchito yolalikila. Mwacitsanzo, tingapangane ndi wofalitsa watsopano kuti tikapite naye mu ulaliki. Tingathandizenso abale ndi alongo okalamba kapena amene ali ndi thanzi lofooka mwa kupita nawo mu ulaliki.

10.Tiphunzilapo ciyani pa zimene zinacitikila Sara?

10 Bwanji ngati tikulephela kucita zambili cifukwa ca mmene zinthu zilili pa umoyo wathu? Tingapezebe njila zina zogwilila nchito ndi angelo pa nchito yolalikila. Ganizilani zinacitikila Sara,c mlongo wa ku lndia. Pambuyo pocita upainiya kwa zaka 20, Sara anadwala ndipo anali kungokhala cigonele nthawi zonse. Ndipo n’zomveka kuti iye anapanikizika maganizo kaamba ka zimenezi. Koma iye anayambanso kuona zinthu moyenela. Anatelo cifukwa ca thandizo lacikondi locokela ku banja lake lauzimu, komanso cifukwa cophunzila Baibo mwakhama. Conco, anapeza njila zatsopano zocitila ulaliki. Popeza sanali kukwanitsa kukhala pansi kuti alembe makalata, anali kucita ulaliki wapafoni. Ndipo ena mwa anthu amene anali kuwalalikila pafoni, anamuuza za anthu ena amene angakonde kuphunzila Baibo. Panakhala zotulukapo zotani? M’miyezi yocepa, Sara anakhala ndi maphunzilo a Baibo 70. N’zoonekelatu kuti sakanakwanitsa kuwatsogoza maphunzilo onsewo. Conco anagawilako ena kwa abale ndi alongo mumpingo. Ambili mwa ophunzila Baibo amenewo, tsopano amapezeka pa misonkhano. N’zosacita kufunsa kuti angelo amasangalala kugwila nchito ndi abale ndi alongo monga Sara, amene amacita zimene angathe pa nchito yolalikila.

ANGELO NDI OPILILA

11. Kodi angelo okhulupilika aonetsa bwanji kupilila m’njila yapadela?

11 Angelo okhulupilika ndi citsanzo cabwino zedi pa nkhani ya kupilila. Iwo apilila kuona zinthu zopanda cilungamo komanso zoipa kwa zaka masauzande ambili. Mwacitsanzo, anaona Satana ndi angelo ena ambili, amene poyamba anali kutumikila nawo limodzi, akupandukila Yehova. (Gen. 3:1; 6:​1, 2; Yuda 6) Baibo imatiuza za mngelo mmodzi wokhulupilika amene ciwanda camphamvu cinamutsekeleza pa njila. (Dan. 10:13) Kuwonjezela apo, m’mbili yonse ya anthu, angelo aona kuti ndi anthu ocepa cabe amene asankha kulambila koona. Ngakhale n’telo, angelo okhulupilika amenewa apitiliza kutumikila Yehova mwacimwemwe komanso mokangalika. Iwo amadziwa kuti panthawi yoyenela, Mulungu adzacotsapo kupanda cilungamo konse.

12. N’ciyani cingatithandize kupilila?

12 Tingaonetse bwanji kupilila mmene angelo amacitila? Mofanana ndi angelo, ifenso timaona zopanda cilungamo ndipo timatsutsidwa. Monga iwo, nafenso tidziwa kuti panthawi yoyenela, Mulungu adzacotsapo mavuto onse. Monga angelo okhulupilika, ifenso sitileka “kucita zabwino.” (Agal. 6:9) Ndipo Mulungu analonjeza kuti adzatithandiza kupilila. (1 Akor. 10:13) Tingapemphele kwa Yehova kuti atipatse mzimu wake umene ungatithandize kukhala oleza mtima komanso acimwemwe. (Agal. 5:22; Akol. 1:11) Bwanji ngati mukutsutsidwa? Muzidalila kwambili Yehova ndipo musamacite mantha. Nthawi zonse Yehova adzakuthandizani, ndipo adzakupatsani mphamvu.​—Aheb. 13:6.

ANGELO AMATHANDIZA KUSUNGITSA CIYELO CA MPINGO

13. Kodi angelo ali ndi utumiki wapadela uti m’masiku ano otsiliza? (Mateyu 13:​47-49)

13 M’masiku ano otsiliza, Yehova wapatsa angelo utumiki winanso wapadela. (Welengani Mateyu 13:​47-49.) Anthu ocokela m’mitundu yonse ofika m’mamiliyoni amakopeka ndi uthenga wabwino. Ena mwa anthu amenewa amasintha umoyo wawo kuti aziyendela mfundo za Yehova n’colinga coti am’tumikile. Koma ena satelo. Angelo apatsidwa nchito yocotsa “oipa pakati pa olungama.” Izi zitanthauza kuti iwo apatsidwa nchito yosungitsa ciyelo ca mpingo. Izi sizitanthauza kuti aliyense amene analeka kugwilizana ndi mpingo sangabwelele ayi. Sizitanthauzanso kuti mumpingo mudzakhala mopanda mavuto ayinso. Koma sitikaikila kuti angelo akugwila nchito molimbika posungitsa ciyelo m’mipingo.

14-15. Tingatengele bwanji citsanzo ca angelo pa nkhani yosungitsa ciyelo ca mpingo? (Onaninso cithunzi.)

14 Kodi tingatengele bwanji citsanzo ca angelo posunga ciyelo ca mpingo? Mwa kucita mbali yathu poyesetsa kuti mpingo ukhale woyela m’makhalidwe komanso kuuzimu. Tingatelo mwa kusankha mabwenzi amene amakonda Mulungu, komanso kupewelatu ciliconse cimene cingawononge ubwenzi wathu ndi iye. (Sal. 101:3) Tingathandizenso alambili anzathu kukhalabe okhulupilika kwa Yehova. Mwacitsanzo, tiyenela kucita ciyani wokhulupilila mnzathu akacita chimo lalikulu? Cifukwa timam’konda, tidzamulimbikitsa kuti akauze akulu. Ngati iye sacitapo kanthu, tingapite kwa akulu kukawauza nkhaniyo. Timafuna kuti wokhulupilila mnzathu amene wawononga ubwenzi wake ndi Yehova alandile thandizo mwamsanga!​—Yak. 5:​14, 15.

15 N’zacisoni kuti ena amene amacita macimo akuluakulu amacotsedwa mumpingo. Zaconco zikacitika, ‘timasiya kugwilizana ndi anthu’ amenewo.d (1 Akor. 5:​9-13) Makonzedwe ocotsa munthu mumpingo amathandiza kusungitsa ciyelo ca mpingo. Ndipo tikamapewa kugwilizana nawo ocotsedwa, timawaonetsa kuti timawakonda. Kucita zimenezo kungawathandize kuzindikila kuti afunika kubwelela kwa Yehova. Akacita zimenezo, timakondwela pamodzi ndi Yehova ndi angelo ake.​—Luka 15:7.

Zithunzi: 1. Alongo awili ali khale m’paki ndipo akumwa khofi. Pamene mlongo mmodzi akulankhula, winayo akuyang’ana kumbali. 2. Pambuyo pake, mlongo amene anali kulankhula uja, wafikila akulu awili ku Nyumba ya Ufumu.

Tingacite ciyani ngati wokhulupilila mnzathu wacita chimo lalikulu? (Onani ndime 14)e


16. Tingatengele citsanzo ca angelo m’njila ziti?

16 Ndi mwayi waukulu kuti Yehova watilola kudziwa za angelo ndi kugwila nchito nawo limodzi. Conco, tiyeni titengele makhalidwe awo okhumbilika omwe ndi kudzicepetsa, kukonda anthu, kupilila, komanso kusunga ciyelo ca mpingo. Tikatengela citsanzo ca angelo okhulupilika, tidzakhala m’banja la alambili a Yehova kwamuyaya.

TINGATENGELE BWANJI CITSANZO CA ANGELO . . .

  • pokhala odzicepetsa?

  • pokonda anthu?

  • posungitsa ciyelo ca mpingo?

NYIMBO 123 Gonjelani Dongosolo la Mulungu

a Ngakhale kuti pali angelo mamiliyoni ambilimbili, Baibo imangochula maina a angelo awili okha, Mikayeli ndi Gabirieli.​—Dan. 12:1; Luka 1:19.

b Mungapeze zitsanzo zowonjezela m’buku la Cingelezi la Watch Tower Publications Index pa mutu waukulu wakuti “Angels” pansi pa kamutu kakuti “angelic direction (examples).”

c Maina ena asinthidwa.

d Malinga n’zimene zinafotokozedwa mu Ciunikilo Na. 2 ca Bungwe Lolamulila mu 2024, wocotsedwa akapezeka pa msonkhano wa mpingo, wofalitsa angagwilitse nchito cikumbumtima cake cophunzitsidwa Baibo kusankha kumupatsa moni wacidule ndi kumulandila.

e MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mlongo akulimbikitsa mnzake kuti akauze akulu za chimo limene anacita. Patapita nthawi, poona kuti mnzakeyo sakucita zimenezo, mlongoyo akupita kukauza akulu zomwe zinacitika.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani