Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi
Mtumwi Paulo analemba kuti Yehova “sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile.” (1 Akor. 10:13) Kodi izi zitanthauza kuti Yehova amadziŵilatu mayeselo amene tingakwanitse kuwapilila, ndiyeno n’kusankhapo mayeselo amene tidzakumana nawo?
Ngati zimenezi zinali zoona, ganizilani mmene zikanakhudzila umoyo wathu. Mwacitsanzo, m’bale wina amene mwana wake anadzipha anafunsa kuti: ‘Kodi Yehova anadziŵilatu kuti ine na mkazi wanga tidzakwanitsa kupilila imfa ya mwana wathu? Kodi izi zinacitika cifukwa cakuti Mulungu anaona kuti tikhoza kupilila?’ Kodi pali cifukwa comveka cokhulupilila kuti Yehova amalamulila zocitika za pa umoyo wathu m’njila ya conco?
Kupendanso mau a Paulo a pa 1 Akorinto 10:13, kwatifikitsa pa mfundo iyi: Palibe cifukwa ca m’Malemba cokhulupilila kuti Yehova amadziŵilatu mayeselo amene tingakwanitse kuwapilila, ndiyeno malinga na zimene waona, n’kusankha mayeselo amene tingakumane nawo. Tiyeni tikambilane zifukwa zinayi zimene zatifikitsa pa mfundo imeneyi.
Coyamba, Yehova anapatsa anthu ufulu wodzisankhila zocita. Iye amafuna kuti tisankhe mmene tifuna kukhalila pa umoyo wathu. (Deut. 30:19, 20; Yos. 24:15) Ngati tasankha njila yabwino, tingayang’ane kwa Yehova kuti atsogolele mayendedwe athu. (Miy. 16:9) Koma tikasankha njila yolakwika tidzakumana ndi mavuto. (Agal. 6:7) Ngati kuti Yehova amasankha mayeselo amene angatigwele, kodi si ndiye kuti akupondeleza ufulu wathu wosankha?
Caciŵili, Yehova satiteteza ku “nthawi yatsoka ndi zinthu zosayembekezeleka.” (Mlal. 9:11) Munthu angapezeke m’ngozi cabe cifukwa cakuti zangocitika mwa tsoka. Yesu anakamba za anthu 18 amene anafa pangozi pamene nsanja inawagwela, ndipo anaonetsa kuti Mulungu sindiye anacititsa imfa ya anthu amenewo. (Luka 13:1-5) Kodi n’canzelu kuganiza kuti Mulungu amakonzelatu amene adzapulumuka ndi amene adzafa pa zinthu zotigwela mwadzidzidzi?
Cacitatu, aliyense wa ise amaloŵetsedwamo m’nkhani ya kukhala wokhulupilika. Kumbukilani kuti Satana anakaikila kukhulupilika kwa atumiki onse a Yehova. Iye anati sitingakhale okhulupilika kwa Yehova tikakhala pa mayeselo. (Yobu 1:9-11; 2:4; Chiv. 12:10) Ngati Yehova angatiteteze kuti tisakumane ndi mayeselo ena cifukwa coona kuti sitingawapilile, kodi sizikanaonetsa kuti zimene Satana anakamba zakuti timatumikila Mulungu cifukwa ca dyela n’zoona?
Cacinayi, Yehova safunika kudziŵilatu ciliconse cimene cidzaticitikila. Mfundo yakuti Mulungu amasankhilatu mayeselo amene tidzakumana nawo ionetsa kuti afunika kudziŵa zonse zokhudza tsogolo lathu. Koma mfundo imeneyi si ya m’Malemba. N’zoona kuti Mulungu angadziŵiletu za kutsogolo. (Yes. 46:10) Koma Baibo ionetsa kuti iye amasankha zocitika za kutsogolo zimene afuna kudziŵilatu. (Gen. 18:20, 21; 22:12) Iye amakwanitsa kudziŵa zamtsogolo, koma amaganizilanso ufulu wathu wosankha. Kodi si zimene tingayembekezele kwa Mulungu amene amalemekeza ufulu wathu, komanso amene nthawi zonse amaonetsa makhalidwe ake mwacikondi?—Deut. 32:4; 2 Akor. 3:17.
Nanga tiyenela kuwamvetsa bwanji mau a Paulo akuti: “Mulungu . . . sadzalola kuti muyesedwe kufika pamene simungapilile”? Apa Paulo anali kukamba zimene Yehova amacita pamene tikumana ndi mayeselo, osati tikalibe tikukumana nawo. Mau a mtumwiyo amatitsimikizila kuti olo tikumane na mayeselo yabwanji, Yehova adzatithandiza ngati timudalila. (Sal. 55:22) Mau otonthoza a Paulo ni ozikidwa pa mfundo ziŵili zofunika za coonadi.
Yoyamba, mayeselo amene timakumana nawo ‘amagwelanso anthu ena.’ Inde, mayeselo amene timakumana nawo ndi amenenso anthu ena amakumana nawo. Tikhoza kupilila mayeselo amenewa malinga ngati tidalila Mulungu. (1 Pet. 5:8, 9) Pokamba mau a pa 1 Akorinto 10:13, Paulo anayelekezela ndi mayeselo amene Aisiraeli anakumana nawo m’cipululu. (1 Akor. 10:6-11) Pa mayeselo amenewo, palibe ciyeso cimodzi cimene cinali cacilendo kwa anthu kapena cimene Aisiraeli okhulupilika sakanatha kupilila. Paulo anacita kukamba kanayi kuti “ena mwa iwo” sanamvele. N’zacisoni kuti Aisiraeli ena anakodwa m’zilako-lako zoipa cifukwa colephela kudalila Mulungu.
Yaciŵili, “Mulungu ndi wokhulupilika.” Mbili ya mmene Mulungu anali kucitila zinthu ndi anthu ake ionetsa kuti iye amaonetsa cikondi cake cokhulupilika kwa “anthu amene amam’konda ndi kusunga malamulo ake.” (Deut. 7:9) Mbili imeneyi ionetsanso kuti Mulungu nthawi zonse amasunga malonjezo ake. (Yos. 23:14) Mwa kupenda mbili ya kukhulupilika kwake, anthu amene amam’konda ndi kumumvela angakhale ndi cidalilo cakuti iye adzasunga lonjezo lake lozikidwa pa mfundo ziŵili ngakhale akumane ndi mayeselo: (1) Iye sadzalola mayeselo aliwonse kufika pamene sitingakwanitse kuwapilila, ndipo (2) ‘adzapeleka njila yotipulumutsila.’
Yehova “amatitonthoza m’masautso athu onse”
Kodi Yehova amapeleka bwanji njila yopulumukila kwa anthu amene amam’dalila panthawi ya mayeselo? N’zoona kuti angacotse mayeselowo ngati afuna. Koma kumbukilani Mau a Paulo akuti: “Iye [Yehova] adzapeleka njila yopulumukila kuti muthe kuwapilila.” Conco, nthawi zambili, iye ‘amapeleka njila yopulumukila’ mwa kutipatsa zimene tifunikila kuti tikwanitse kupilila mayeselowo. Onani njila zina za mmene Yehova angapelekele njila yopulumukila:
Iye “amatitonthoza m’masautso athu onse.” (2 Akor. 1:3, 4) Yehova angatsitsimule maganizo ndi mtima wathu. Angacite zimenezi kupitila m’Mau ake, mzimu wake woyela, ndi cakudya cauzimu cimene timalandila kwa kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.—Mat. 24:45; Yoh. 14:16, Aroma. 15:4.
Iye angatitsogolele pogwilitsila nchito mzimu woyela. (Yoh. 14:26) Tikakumana ndi mayeselo, mzimu ungatithandize kukumbukila nkhani za m’Baibo ndi mfundo zimene zingatithandize kusankha mwanzelu.
Angagwilitsile nchito angelo ake kuti atithandize.—Aheb. 1:14.
Angatithandize pogwilitsila nchito olambila anzathu. Mau awo ndi zocita zawo ‘zingatithandize ndi kutilimbikitsa.’—Akol. 4:11.
Conco, kodi tingati mau a Paulo a pa 1 Akorinto 10:13, atanthauza ciani? Yehova satisankhila mayeselo amene timakumana nawo. Koma tikakumana ndi mayeselo, tidzikhala otsimikiza za izi: Ngati tili ndi cidalilo conse mwa Yehova, iye sadzalola kuti mayeselo athu afike poti sitingakwanitse kuwapilila. Nthawi zonse adzapeleka njila yopulumukila kuti tikwanitse kuwapilila. Imeneyi ni mfundo yolimbikitsa kwambili.