LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb23 January tsa. 9
  • Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeso

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeso
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
  • Nkhani Zofanana
  • Muzikumbukila Kuti Yehova ni “Mulungu Wamoyo”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2024
  • Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Sitinakhalepo Tokha Ngakhale Pang’ono
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
  • Mmene Yehova Amatithandizira Kupirira
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2025
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano—2023
mwb23 January tsa. 9
Makolo pamodzi na ana awo aang’ono akuceza na mpingo wawo kupitila pa Zoom.

UMOYO WATHU WACIKHRISTU

Yehova Amatithandiza Kupilila Mayeso

Masiku otsiliza ano, timakumana na mayeso ambili. Nthawi zina, tingaone monga kuti mayeso athu ni aakulu kwambili moti sitingakwanitse kuwapilila. Komabe, ngati tikhalabe pa ubale wolimba na Yehova, iye adzatithandiza kupilila mayeso ngakhale ovuta kwambili. (Yes. 43:2, 4) Kodi tingalimbitse bwanji ubale wathu na Yehova pamene tikumana na mayeso?

Pemphelo. Ngati tamukhuthulila za mumtima mwathu Yehova, adzatipatsa mtendele komanso mphamvu kuti tithe kupilila.—Afil. 4:6, 7; 1 Tim. 5:17.

Misonkhano. Kuposa kale lonse, masiku ano timafunikila kwambili cakudya cauzimu komanso mayanjano amene Yehova amapeleka pa misonkhano. (Aheb. 10:24, 25) Tikamakonzekela misonkhano ya mpingo, kupezekako, na kutengako mbali, timapindula kwathunthu na thandizo la mzimu woyela wa Yehova.—Chiv. 2:29.

Ulaliki. Tikamacita zonse zotheka kuti tikhalebe okangalika mu ulaliki, cidzakhala cosavuta kuikabe maganizo athu pa zinthu zolimbikitsa. Kuwonjezela apo, tidzalimbitsa ubwenzi wathu na Yehova komanso anchito anzathu.—1 Akor. 3:5-10.

ONELELANI VIDIYO YAKUTI YEHOVA ADZAKULANDILANI, KENAKO YANKHANI MAFUNSO AWA:

  • N’ciyani cinathandiza Malu kukhalabe pa ubwenzi wolimba na Yehova pamene anali kukumana na mayeso?

  • Mofanana na Malu, kodi mawu a pa Salimo 34:18 angatilimbikitse bwanji pamene tikukumana na mayeso?

  • Kodi zimene zinacitikila Malu zionetsa bwanji kuti Yehova amapeleka “mphamvu yoposa yacibadwa” tikakumana na mayeso?—2 Akor. 4:7

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani