Kodi Mumacita Zinthu Mogwilizana ndi Cilungamo ca Yehova?
“Ndidzalengeza dzina la Yehova . . . , Mulungu wokhulupilika, amene sacita cosalungama.”—DEUT. 32:3, 4.
1, 2. (a) Kodi Naboti ndi ana ake anacitilidwa zinthu zopanda cilungamo ziti? (b) Ni makhalidwe aŵili ati amene tidzakambilana m’nkhani ino?
GANIZILANI nkhani iyi. Munthu aimbidwa mlandu wabodza umene ciweluzo cake ndi imfa. Munthuyo akuweluzidwa kuti ni wolakwa cifukwa ca umboni wonama wopelekedwa ndi anthu odziŵika kuti ni opanda pake. Acibululu na mabwenzi ake akhumudwa ndipo asoŵa mtengo wogwila. Anthu ena okonda cilungamo nawonso akhumudwa ndipo sakumvetsa cifukwa cake munthu wosalakwayo ndi ana ake akuphedwa. Nkhaniyi si yopeka, inacitikadi. Inacitikila mtumiki wokhulupilika wa Yehova, dzina lake Naboti. Iye anakhalako pa nthawi imene Mfumu Ahabu anali kulamulila mu Isiraeli.—1 Maf. 21:11-13; 2 Maf. 9:26.
2 M’nkhani ino, tidzakambilana za Naboti, ndi za mkulu wina wokhulupilika wa mumpingo wacikhristu wa m’zaka 100 zoyambilila, amene analakwitsa zinthu zina. Pokambilana zitsanzo za m’Baibo zimenezi, tidzaona kuti kukhala odzicepetsa n’kofunika kuti ticite zinthu mogwilizana ndi cilungamo ca Yehova. Tidzaonanso mmene kukhululukila ena akatilakwila mumpingo, kumaonetsela kuti timagwilizana ndi cilungamo ca Yehova.
ANAPOTOZA CILUNGAMO
3, 4. Kodi Naboti anali munthu wotani? Nanga n’cifukwa ciani anakana kugulitsa munda wake wa mpesa kwa Mfumu Ahabu?
3 Naboti anakhalabe wokhulupilika kwa Yehova pa nthawi imene Aisiraeli ambili anali kutsatila citsanzo coipa ca Mfumu Ahabu ndi mkazi wake, Yezebeli. Iwo anali kulambila Baala, ndipo sanali kulemekeza Yehova ndi malamulo ake. Koma Naboti anali kuona kuti ubale wake na Yehova ni wa mtengo wapatali kuposa ngakhale moyo wake.
4 Ŵelengani 1 Mafumu 21:1-3. Pamene Ahabu anauza Naboti kuti am’gulitse munda wake wa mpesa, kapena kuti Ahabu atenge mundawo ndi kum’patsa munda wina wabwino kwambili, Naboti anakana. Cifukwa ciani? Mwaulemu, iye anafotokoza kuti: “Sindingacite zimenezo pamaso pa Yehova, kupeleka colowa ca makolo anga kwa inuyo.” Naboti anakana cifukwa comvela lamulo limene Yehova anapeleka kwa Aisiraeli, lakuti safunika kugulitsilatu colowa ca fuko lawo. (Lev. 25:23; Num. 36:7) Apa n’zoonekelatu kuti Naboti anali kulemekeza malamulo a Yehova.
5. N’ciani cimene Yezebeli anacita kuti Naboti aphedwe?
5 N’zomvetsa cisoni kuti Naboti atakana kugulitsa mundawo, Mfumu Ahabu ndi mkazi wake anam’konzela ziwembu zimene pambuyo pake zinawabweletsela tsoka. Pofuna kuti mwamuna wake atenge munda wa mpesawo, Yezebeli anakonza zakuti anthu ena akasemele mlandu Naboti ndi kupeleka umboni wotsutsana naye. Zimenezi zinacititsa kuti Naboti ndi ana ake aphedwe. Kodi Yehova anacita ciani ataona zinthu zopanda cilungamo zimenezi?
CIWELUZO COLUNGAMA CA MULUNGU
6, 7. Kodi Yehova anaonetsa bwanji kuti amakonda cilungamo? Nanga zimenezi ziyenela kuti zinawatonthoza bwanji acibululu a Naboti na mabwenzi ake?
6 Izi zitangocitika, Yehova anatuma Eliya kuti akakumane ndi Ahabu. Eliya atakumana ndi Ahabu anamuuza mosapita m’mbali kuti ndi wakupha ndi wakuba. Kodi Yehova anapeleka ciweluzo cotani pa nkhaniyi? Anakamba kuti Ahabu, mkazi wake, ndi ana ake adzaphedwa mmene iwo anaphela Naboti ndi ana ake.—1 Maf. 21:17-25.
7 Acibululu a Naboti na mabwenzi ake anali ndi cisoni cacikulu kaamba ka zinthu zopanda cilungamo zimene Ahabu anacita. Ndipo mosakayikila, iwo anatonthozedwa atazindikila kuti Yehova anaona zimene zinacitika ndi kucitapo kanthu mwamsanga. Komabe, zimene zinacitika pambuyo pake, ziyenela kuti zinayesa kudzicepetsa kwawo ndi kudalila kwawo Yehova.
8. Kodi Ahabu anacita ciani atamva uthenga waciweluzo wocokela kwa Yehova? Nanga panakhala zotulukapo zotani?
8 Ahabu atamva ciweluzo cimene Yehova anapeleka, “anang’amba zovala zake n’kuvala ciguduli. Iye anayamba kusala kudya, kugona paciguduli ndipo anali kuyenda mwacisoni.” Inde, Ahabu anadzicepetsa. Kodi panakhala zotulukapo zotani? Yehova anatumanso Eliya kuti akapeleke uthenga wina kwa iye. Panthawiyi, Eliya anauza Ahabu kuti popeza anadzicepetsa pamaso pa Mulungu, Yehova sadzabweletsa tsoka pa nthawi imene iye ali moyo. (1 Maf. 21:27-29) Yehova, amene “amayesa mitima,” anamucitila cifundo Ahabu.—Miy. 17:3.
KUDZICEPETSA KUMATETEZA
9. Kodi kudzicepetsa kuyenela kuti kunawateteza bwanji acibale a Naboti ndi mabwenzi ake?
9 Kodi anthu amene anadziŵa zoipa zimene Ahabu anacita, anamvela bwanji ataona kuti Mulungu wamucitila cifundo? Zimenezi ziyenela kuti zinayesa cikhulupililo ca acibale a Naboti ndi mabwenzi ake. Ngati zinali conco, ndiye kuti kudzicepetsa kunawateteza. Kunawathandiza kupitiliza kulambila Yehova mokhulupilika, ali na cidalilo cakuti Mulungu wawo sangacite zinthu zosalungama. (Ŵelengani Deuteronomo 32:3, 4.) Naboti, ana ake, ndi acibale awo, akadzaukitsidwa pa kuuka kwa olungama, adzaona kuti Yehova ndi wacilungamo. (Yobu 14:14, 15; Yoh. 5:28, 29) Kuwonjezela apo, munthu wodzicepetsa amakumbukila kuti “Mulungu woona adzaweluza nchito iliyonse ndiponso cinthu ciliconse cobisika, kuti aone ngati zili zabwino kapena zoipa.” (Mlal. 12:14) Yehova popeleka ciweluzo amapenda zinthu zina zimene ife sitingazidziŵe. Conco, kukhala odzicepetsa kudzatiteteza kuti tisawononge umoyo wathu wauzimu.
10, 11. (a) Ndi zinthu ziti zimene zingayese cikhulupililo cathu? (b) Kodi kudzicepetsa kumatiteteza bwanji?
10 Kodi mungacite bwanji ngati akulu apanga cosankha cimene inu simunacimvetsetse kapena simunagwilizane naco? Mwacitsanzo, mungamvele bwanji ngati inu kapena mnzanu wacotsedwa pa udindo kapena pa utumiki umene anali kuukonda? Nanga bwanji ngati mnzanu wa m’cikwati, mwana wanu, kapena mnzanu wacotsedwa mumpingo koma inu simukugwilizana nazo? Komanso bwanji ngati muona kuti akulu anacitila cifundo munthu wolakwa popanda zifukwa zomveka bwino? Zocitika ngati zimenezi zingayese cikhulupililo cathu mwa Yehova ndipo zingapangitse kuti tizikayikila mmene gulu lake limayendetsela zinthu. Kodi kudzicepetsa kudzatiteteza bwanji pa zocitika zaconco? Tiyeni tikambilane njila ziŵili.
Mungacite bwanji ngati akulu apeleka cilengezo cimene inu simunagwilizane naco? (Onani mapalagilafu 10, 11)
11 Yoyamba, kudzicepetsa kudzatithandiza kuzindikila kuti sitidziŵa mfundo zonse za nkhani imene yacitika. Olo kuti nkhaniyo tiidziŵa bwino, Yehova yekha ndiye amaona mmene mtima ulili. (1 Sam. 16:7) Kukumbukila mfundo yosatsutsika imeneyi kudzatithandiza kukhala odzicepetsa, kuzindikila kuti sitidziŵa zonse, ndi kusintha maganizo athu pankhaniyo. Yaciŵili, kudzicepetsa kudzatithandiza kukhala ogonjela ndi oleza mtima pamene tiyembekezela kuti Yehova adzakonze zinthu zopanda cilungamo zimene zinacitika. Baibo imati: “Anthu amene amaopa Mulungu woona zidzawayendela bwino. . . , Koma woipayo sizidzamuyendela bwino n’komwe, ndiponso sadzaculukitsa masiku ake.” (Mlal. 8:12, 13) Inde, ngati tikhalabe odzicepetsa, ife pamodzi ndi anthu ena okhudzidwa na nkhaniyo, tidzapindula kwambili.—Ŵelengani 1 Petulo 5:5.
ANACITA ZINTHU MWACIPHAMASO
12. Kodi tidzakambilana ciani tsopano? Nanga n’cifukwa ciani?
12 Akhristu a ku Antiokeya wa ku Siriya a m’zaka 100 zoyambilila, anakumana ndi zinthu zimene zinayesa kudzicepetsa kwawo ndi mtima wawo wokhululukila ena. Tiyeni tikambilane zimene zinacitikazo. Kukambilana zimenezi kudzatithandiza kudzifufuza pankhani yokhululukila ena, ndi kumvetsetsa mmene kukhululukila ena kumagwilizanilana ndi cilungamo ca Yehova.
13, 14. Ni mautumiki ati amene mtumwi Petulo anapatsidwa? Nanga anaonetsa bwanji kuti anali wolimba mtima?
13 Mtumwi Petulo anali mkulu wodziŵika ngako mumpingo wacikhristu. Iye anali mnzake wa Yesu, ndipo anapatsidwa maudindo aakulu. (Mat. 16:19) Mwacitsanzo, mu 36 C.E., Petulo anali na mwayi wolalikila uthenga wabwino kwa Koneliyo ndi a m’banja lake. Cimeneci cinali cocitika capadela cifukwa Koneliyo sanali m’Yuda komanso anali wosadulidwa. Koneliyo ndi a m’banja lake atalandila mzimu woyela, Petulo anati: “Anthu awa alandila mzimu woyela monga mmenenso ife tinalandilila. Ndani amene angaletse kuti asabatizidwe ndi madzi?”—Mac. 10:47.
14 M’caka ca 49 C.E., atumwi ndi akulu ku Yerusalemu anasonkhana kuti akambilane ngati anthu amitundu ina, amene anakhala Akhristu, anafunika kudulidwa. Pa msonkhanowo, Petulo anakamba molimba mtima. Iye anakumbutsa abale kuti m’zaka zam’mbuyo, anthu amitundu ina osadulidwa, analandilapo mphatso ya mzimu woyela. Umboni umene Petulo anapeleka, unathandiza kwambili bungwe lolamulila la m’zaka 100 zoyambilila kupanga cosankha pankhaniyi. (Mac. 15:6-11, 13, 14, 28, 29) Mwacionekele, Akhristu aciyuda ndi Akhristu amitundu ina anayamikila Petulo cifukwa cofotokoza molimba mtima zimene zinacitika. Conco, ziyenela kuti zinali zosavuta kwa iwo kukhulupilila mwamuna wokhwima mwauzimu ameneyu.—Aheb. 13:7.
15. Kodi Petulo analakwitsa ciani pamene anali ku Antiokeya wa ku Siriya? (Onani pikica kuciyambi.)
15 Patangopita nthawi yocepa kucokela pamene anacita msonkhano mu 49 C.E., Petulo anapita ku Antiokeya wa ku Siriya. Pamene anali kumeneko, anali kucita zinthu momasuka ndi abale ake amene sanali Ayuda. Mosakayikila, iwo anapindula kwambili kukhala ndi Petulo cifukwa anali munthu wodziŵa zambili ndi wodziŵa bwino Malemba. Koma iwo ayenela kuti anadabwa kwambili ataona kuti Petulo mwadzidzidzi waleka kudya nawo. Ayuda ena a mumpingo, kuphatikizapo Baranaba, nawonso anagwilizana ndi Petulo. N’ciani cinapangitsa kuti mkulu wacikhristu wokhwima mwauzimu ameneyu acite zinthu zimene zikanayambitsa magawano mumpingo? Ndipo funso lofunika kwambili n’lakuti, ni mfundo yanji imene tingatengepo pa cocitika cimeneci imene ingatithandize ngati mkulu wakamba kapena kucita zinthu zimene zatikhumudwitsa?
16. Kodi Petulo anawongoleledwa bwanji? Nanga pakubuka mafunso otani?
16 Ŵelengani Agalatiya 2:11-14. Petulo anagwela mumsampha woopa anthu. (Miy. 29:25) Iye anali kudziŵa bwino mmene Yehova anali kuonela Akhristu amitundu ina. Koma anaopa kuti Akhristu aciyuda odulidwa a mumpingo wa ku Yerusalemu adzaleka kumulemekeza akaona kuti akuyanjana ndi Akhristu amitundu ina. Mtumwi Paulo, amenenso analipo pa msonkhano umene unacitika ku Yerusalemu mu 49 C.E., anakumana ndi Petulo ku Antiokeya, ndipo anam’dzudzula cifukwa ca zaciphamaso zimene anacita. (Mac. 15:12; Agal. 2:13) Kodi Akhristu amitundu ina anacita ciani ataona zinthu zopanda cilungamo zimene Petulo anawacitila? Kodi anakhumudwa? Kodi Petulo analandidwa maudindo atacita colakwa cimeneci?
MUZIKHULULUKA
17. Kodi Petulo anapindula bwanji cifukwa cokhululukidwa na Yehova?
17 N’zoonekelatu kuti Petulo anadzicepetsa ndipo analandila uphungu wa Paulo. M’Malemba, mulibe pamene paonetsa kuti Petulo analandidwa udindo uliwonse. Ndipo pambuyo pa izi, iye anauzilidwa kulemba makalata aŵili amene anakhala mbali ya Baibo. N’zocititsa cidwi kuti m’kalata yake yaciŵili, iye anachula Paulo kuti “m’bale wathu wokondedwa.” (2 Pet. 3:15) Ngakhale kuti zinthu zopanda cilungamo zimene Petulo anacita zinawapweteka mtima Akhristu amitundu ina a mumpingowo, Yesu, mutu wa mpingo, anapitiliza kumugwilitsila nchito. (Aef. 1:22) Conco, anthu a mumpingowo anali na mwayi wotengela citsanzo ca Yesu ndi Atate wake mwa kukhululukila Petulo. Tikhulupilila kuti palibe amene anakhumudwa ndi colakwa cimene Petulo anacita.
18. Ni pa zocitika ngati ziti pamene tifunika kuonetsa kuti timagwilizana ndi cilungamo ca Yehova?
18 Monga mmene zinalili m’nthawi ya atumwi, masiku anonso mumpingo wacikhristu mulibe akulu angwilo, pakuti “tonsefe timapunthwa nthawi zambili.” (Yak. 3:2) N’zosavuta kuvomeleza mfundo imeneyi. Koma bwanji ngati m’bale watilakwila? Kodi tidzaonetsa kuti timagwilizana ndi cilungamo Yehova? Mwacitsanzo, mungacite bwanji ngati mkulu wakamba mau oonetsa tsankho? Kodi mudzakhumudwa ngati mkulu mosaganiza bwino wakamba mau amene akukhumudwitsani? M’malo moweluzilatu kuti m’baleyo sayenela kukhala mkulu, kodi mudzayembekezela moleza mtima kuti Yesu, mutu wa mpingo, adzacitapo kanthu? Kodi mudzayesetsa kuona zabwino mwa m’baleyo ndi kuganizila zaka zambili zimene iye watumikila Mulungu mokhulupilika? Komanso bwanji ngati m’bale amene anakulakwilani akupitiliza kutumikila monga mkulu kapena akulandila maudindo ena owonjezeleka, kodi mudzakondwela naye limodzi? Ngati ndinu wokonzeka kukhululukila ena, mudzaonetsa kuti mumagwilizana ndi cilungamo ca Yehova.—Ŵelengani Mateyu 6:14, 15.
19. Kodi tiyenela kuyesetsa kucita ciani?
19 Anthu okonda cilungamo amalaka-laka nthawi pamene Yehova adzathetselatu zinthu zopanda cillungamo zimene Satana ndi dongosolo lake loipa amacititsa. (Yes. 65:17) Kuyambila lelo mpaka panthawiyo, tiyeni tonse tiziyesetsa kucita zinthu mogwilizana ndi cilungamo ca Yehova. Tingacite zimenezi mwa kukhala odzicepetsa ndi kuzindikila kuti pali zinthu zina zimene sitidziŵa, ndiponso kukhala wokonzeka kukhululukila ena ndi mtima wonse.