LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w17 April masa. 28-32
  • Yehova Atamandike Cifukwa ca Kudzipeleka Kwanu!

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Yehova Atamandike Cifukwa ca Kudzipeleka Kwanu!
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • “MUMAM’PATSA CIANI?”
  • ANALI NA MANTHA, KOMA MULUNGU ANAWALIMBITSA
  • ANALI NA MAGANIZO OSIYANA KWAMBILI PANKHANI YODZIPELEKA
  • “TAMANDANI YEHOVA”
  • Mtsogoleli Watsopano na Azimayi Aŵili Olimba Mtima
    Maphunzilo Amene Tingatengemo m’Baibo
  • “Ine Ndinauka Monga Mai mu Isiraeli”
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
  • Akazi Aŵili Olimba Mtima
    Buku Langa La Nkhani Za M’baibo
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
w17 April masa. 28-32
Baraki ndi anthu ake athamangitsa Sisera ndi asilikali ake

Yehova Atamandike Cifukwa ca Kudzipeleka Kwanu!

“Cifukwa ca kudzipeleka mwaufulu kwa anthu, tamandani Yehova.”—OWER. 5:2.

NYIMBO: 150, 10

N’CIFUKWA CIANI MUKHULUPILILA KUTI YEHOVA . . .

  • sakondwela na munthu amene amanyalanyaza nchito yake?

  • amayamikila ndi kudalitsa anthu amene amam’tumikila mokhulupilika?

  • amakondwela ngati muli na mzimu wodzipeleka?

1, 2. (a) Kodi Elifazi ndi Bilidadi anakamba kuti Mulungu amauona bwanji utumiki wathu? (b) Kodi Yehova anaonetsa bwanji maganizo ake pankhaniyi?

“KODI mwamuna wamphamvu angakhale waphindu kwa Mulungu? Kodi aliyense wozindikila angakhale waphindu kwa iye? Kodi Wamphamvuyonse amasangalala kuti ndiwe wolungama? Kapena amapindula ciliconse cifukwa cakuti sucita colakwa?” (Yobu 22:1-3) Kodi mungayankhe bwanji mafunso amenewa? Pamene Elifazi wa ku Temani anafunsa Yobu mafunso amenewa, mwacionekele anali kukhulupilila kuti yankho lake n’lakuti ayi. Nayenso Bilidadi wa ku Shuwa, amene anali mnzake wa Elifazi, anakamba kuti n’zosatheka anthu kukhala olungama pamaso pa Mulungu.—Ŵelengani Yobu 25:4.

2 Anthu amenewa anabwela kudzatonthoza Yobu mwacinyengo. Iwo anakamba kuti Yehova sapindula ndi zimene timacita pom’tumikila mokhulupilika. Anakambanso kuti, kwa Mulungu, ise anthu ndise osafunika ndipo tili ngati kadziwoche, mphutsi, kapena nyongolotsi. (Yobu 4:19; 25:6) Mwina tingaganize kuti Elifazi ndi Bilidadi anali kuonetsa kudzicepetsa pokamba mau amenewa. (Yobu 22:29) Ndipo n’zoona kuti Mulungu ndi wamkulu kwambili kuposa ise anthu. Mwacitsanzo, ngati muli pamwamba pa phili lalitali kapena m’ndeke, anthu ndi zimene iwo anapanga zimaoneka ngati zacabe-cabe. Koma kodi umu ni mmene Yehova amaonela nchito imene timagwila pocilikiza Ufumu wake akamationa padziko lapansi ali kumwamba? Yehova anaonetsa maganizo ake pankhaniyi pamene anadzudzula Elifazi, Bilidadi, ndi Zofari cifukwa cokamba mabodza. Koma anakondwela ndi Yobu, ndipo anamucha “mtumiki” wake. (Yobu 42:7, 8) Conco, munthu angakhaledi “waphindu kwa Mulungu.”

“MUMAM’PATSA CIANI?”

3. Kodi Elihu anakamba ciani ponena za utumiki umene timacita kwa Yehova? Nanga anali kutanthauza ciani?

3 Yehova sanam’dzudzule Elihu pamene anafunsa kuti: “Ngati ndinudi wosalakwa, kodi mumam’patsa ciani [Mulungu]? Kodi amalandila ciani kucokela m’manja mwanu?” (Yobu 35:7) Kodi pamenepa Elihu anali kutanthauza kuti zimene timacita potumikila Mulungu n’zopanda phindu? Iyai. Anali kutanthuza kuti Yehova payekha ndi wacikwane-kwane. Pamene timulambila sitimupangitsa kukhala wolemela, kapena wamphamvu kwambili. M’malomwake, zinthu zilizonse zabwino, maluso, kapena mphamvu zimene tili nazo ni mphatso zocokela kwa Mulungu, ndipo iye amakondwela ngati tizigwilitsila nchito moyenela.

4. Kodi Yehova amaziona bwanji nchito zacifundo zimene timacitila anthu ena?

4 Yehova amaona kuti anthu akacitila zabwino atumiki ake, ndiye kuti acitila iyeyo. Lemba la Miyambo 19:17 limati: “Wokomela mtima munthu wonyozeka akukongoza Yehova, ndipo adzam’bwezela zimene anacitazo.” Kodi lembali litanthauza kuti Yehova amaona zinthu zonse zabwino zimene munthu amacitila anthu ovutika? Kodi n’zoona kuti Mlengi wacilengedwe conse amaona kuti ali na nkhongole kwa anthu amene amacitila anzawo zinthu zacifundo, ndipo adzawabwezela mwa kuwayanja ndi kuwadalitsa? Inde, n’zoona, ndipo Mwana wa Mulungu anatsimikizila mfundo imeneyi.—Ŵelengani Luka 14:13, 14.

5. Kodi tidzakambilana mafunso ati?

5 Nthawi ina, Yehova anapempha mneneli Yesaya kuti akhale wom’lankhulila wake. Zimenezi zionetsa kuti Mulungu amakonda kupatsa anthu mwayi wom’tumikila pokwanilitsa colinga cake. (Yes. 6:8-10) Yesaya anavomela udindo umene Mulungu anam’patsa. Masiku ano, anthu masauzande ambili ali na mzimu wodzipeleka monga wa Yesaya ndipo avomela kugwila nchito zovutilapo mu utumiki wa Yehova. Komabe, munthu wina angafunse kuti: ‘Kodi zimene nimacita n’zofunikadi kwa Mulungu? Nimaona kuti ni mwayi waukulu kuti Yehova wanilola kugwila nawo nchito yake. Koma kodi iye angalephele kukwanilitsa Mau ake ngati sinicita zambili pom’tumikila?’ Tiyeni tikambilane zimene zinacitika m’nthawi ya Debora ndi Baraki. Kukambilana zimenezi kudzatithandiza kuyankha mafunso amenewa.

ANALI NA MANTHA, KOMA MULUNGU ANAWALIMBITSA

6. Kodi panali kusiyana kotani pakati pa Aisiraeli ndi asilikali a Yabini?

6 Kwa zaka 20, Aisiraeli ‘anapondelezedwa kwambili’ ndi Yabini, mfumu yacikanani. Aisiraeli analibe ufulu woyenda cifukwa coopa adani awo. Analibenso zida zankhondo zomenyela adani awo kapena zodzitetezela. Koma adani awo anali ndi magaleta ankhondo 900 okhala ndi zitsulo zazitali zakuthwa m’mawilo.—Ower. 4:1-3, 13; 5:6-8.a

7, 8. (a) Kodi poyamba Yehova analamula Baraki kuti acite ciani? (b) Kodi Aisiraeli anagonjetsa bwanji asilikali a Yabini? (Onani pikica kuciyambi.)

7 Ngakhale zinali conco, Yehova kupitila mwa mneneli wamkazi Debora, analamula Baraki kuti: “Tenga amuna 10,000 pakati pa ana a Nafitali ndi ana a Zebuloni ndipo mukasonkhane paphili la Tabori. Ine ndidzakokela kwa iwe m’cigwa ca Kisoni, Sisera mkulu wa gulu lankhondo la Yabini, pamodzi ndi magaleta ake ankhondo ndi gulu lake lonse. Pamenepo ndidzam’peleka m’manja mwako.”—Ower. 4:4-7.

8 Cilengezo citapelekedwa, anthu odzipeleka anasonkhana pa Phili la Tabori. Mwamsanga, Baraki anapita kukamenyana ndi adani ake monga mmene Yehova anam’lamulila. (Ŵelengani Oweruza 4:14-16.) Nkhondo ili mkati ku Taanaki, mwadzidzidzi kunagwa cimvula coopsa cimene cinapangitsa kuti m’delalo mukhale vimadzi ndi matope okha-okha. Baraki anathamangitsa asilikali a Sisera mpaka kukafika ku Haroseti, dela limene linali pamtunda wa makilomita 24. Ali mkati mothaŵa, Sisera anasiya galeta yake podziŵa kuti siingam’pulumutse ndipo anathaŵila ku Zaananimu, dela limene mwina linali pafupi ndi Kedesi. Iye anapempha malo obisalako kwa Yaeli, mkazi wa Hiberi Mkeni, ndipo anamulandila. Kumeneko, Sisera anagona cifukwa anali atatopa kwambili kunkhondo. Popeza anali atagona, Yaeli analimba mtima n’kumupha. (Ower. 4:17-21) Apa Aisiraeli anagonjetsa adani awo kothelatu.b

ANALI NA MAGANIZO OSIYANA KWAMBILI PANKHANI YODZIPELEKA

9. Kodi pa Oweruza 5:20, 21 pamafotokoza mfundo zina ziti zokhudza nkhondo yolimbana ndi Sisera?

9 Kuti timve zambili pa zocitika zolembedwa mu Oweruza caputa 4 tifunikanso kuŵelenga caputa 5, cifukwa caputa cina cimafotokoza mfundo zimene m’caputa cinzake mulibe. Mwacitsanzo, pa Oweruza 5:20, 21 pamati: “Nyenyezi zinamenya nkhondo zili kumwamba, zinamenyana ndi Sisera zili m’njila zawo. Mtsinje wa Kisoni unawakokolola.” Kodi lembali litanthauza kuti Aisiraeli anathandizidwa ndi angelo pankhondoyo, kapena kunagwa miyala yocoka kumwamba? Baibo siifotokoza zambili pankhaniyi. Koma n’zosakayikitsa kuti Mulungu ndiye anacititsa kuti kugwe cimvula camphamvu, cimene cinapangitsa magaleta ankhondo 900 kukokoloka. Takamba conco cifukwa mvulayo inagwa pamalo eni-eni amene panali kucitikila nkhondo ndiponso panthawi yoyenela. Katatu konse, pa Oweruza 4:14, 15 pamakamba kuti Yehova ndiye anathandiza Aisiraeli kupambana nkhondoyo. Pa Aisiraeli 10,000 amene anadzipeleka kukamenya nkhondoyo, palibe amene akanakamba kuti ndiye anacititsa kuti apambane.

10, 11. Kodi “Merozi” anali ciani? Nanga n’cifukwa ciani anatembeleledwa?

10 Pali mau ena ocititsa cidwi amene Debora ndi Baraki anakamba poimba nyimbo yotamanda Yehova, atawathandiza kugonjetsa adani awo mozizwitsa. Iwo anati: “Mngelo wa Yehova anati: ‘Tembelelani Merozi, tembelelani anthu ake mosaleka, cifukwa sanathandize Yehova, sanabwele ndi anthu amphamvu kudzathandiza Yehova.’”—Ower. 5:23.

11 Merozi anatembeleledwadi, ndipo masiku ano n’zovuta kudziŵa kuti Merozi anali ciani. N’kutheka kuti Merozi unali mzinda umene nzika zake sizinafune kudzipeleka kukathandiza Aisiraeli pankhondo. Mwina Sisera anadutsa mumzinda umenewo pothawa, ndipo anthu a mumzindawo anali na mwayi womugwila koma anangomuleka. N’zodziŵikilatu kuti iwo anamva kuti Yehova anali kufuna anthu odzipeleka kuti akamenye nkhondo. Takamba zimenezi cifukwa anthu 10,000 ocokela m’madela ozungulila Merozi anasonkhana kuti akamenye nkhondoyo. Yelekezelani kuti mukuwaona anthu a ku Merozi akungomuyang’ana msilikali woopsa Sisera, pamene akuthamanga kudutsa mumzinda wao, ali yekha ndiponso ali wotopa kwambili. Panthawiyo, iwo anali na mwayi wapadela wothandiza kukwanilitsa colinga ca Yehova, ndipo akanatelo, akanadalitsidwa. Koma anangokhala cete osacitapo kanthu. Anthu amenewo analidi osiyana kwambili ndi Yaeli, amene anacita zinthu zoonetsa kulimba mtima zimene zinalembedwa pa Oweruza 5:24-27.

12. Kodi anthu ochulidwa pa Oweruza 5:9, 10 anali osiyana bwanji? Nanga ife tiphunzilapo ciani?

12 Pa Oweruza 5:9, 10, tionapo kusiyana kwina pakati pa anthu amene anadzipeleka kukamenya nkhondo na Baraki ndi amene sanadzipeleke. Debora ndi Baraki anayamikila “atsogoleli a asilikali a Isiraeli amene anadzipeleka mwaufulu pakati pa anthu awo.” Atsogoleli amenewo anali osiyana ngako ndi anthu “okwela abulu ofiilila,” amene anakana kukamenya nkhondo cifukwa conyada. Anali osiyananso ndi anthu okonda umoyo wawofu-wofu, amene anali ‘kukhala pansalu zokwela mtengo.’ Mosiyana ndi “oyenda mumsewu,” amene anali okonda umoyo wofewa, anthu amene anapita ndi Baraki anali okonzeka kukamenya nkhondo m’dela lamiyala la Tabori ndi m’cigwa cokhala na matope ca Kisoni. Anthu okonda umoyo wofewa amenewa analangizidwa kuti ‘aganizile’ za mwayi wotumikila Yehova umene anataya. N’cimodzimodzi masiku ano. Tonse tifunika kudzipenda kuti tione ngati pali zinthu zina zimene zikutilepheletsa kutumikila Mulungu mokwanila.

13. Kodi anthu a fuko la Rubeni, Dani, ndi Aseri anasiyana bwanji ndi a fuko la Zebuloni ndi la Nafitali?

13 Anthu amene anadzipeleka kukamenya nkhondo ndi Baraki anadzionela okha mmene Yehova anakwezela ulamulilo wake. Iwo anaona zinthu zolimbikitsa zimene akanauzako ena ‘posimba nchito zolungama za Yehova.’ (Ower. 5:11) Koma pa Oweruza 5:15-17, paonetsa kuti Aisiraeli a fuko la Rubeni, Dani, ndi la Aseri anaika mtima pa cuma cawo monga nkhosa, zombo, ndi madoko, osati pa nchito ya Yehova. Mosiyana ndi anthu amenewa, Aisiraeli a fuko la Zebuloni ndi la Nafitali “anatonza miyoyo yawo mpaka kuiika pangozi,” pothandiza Debora ndi Baraki. (Ower. 5:18) Magulu aŵili amenewa a anthu anali na maganizo osiyana kwambili pankhani yotumikila Mulungu. Pamenepa tingatengepo phunzilo lofunika kwambili.

“TAMANDANI YEHOVA”

14. Kodi masiku ano timaonetsa bwanji kuti timacilikiza ulamulilo wa Yehova?

14 Masiku ano, sitimenya nkhondo yeni-yeni pocilikiza ulamulilo wa Yehova, koma timaucilikiza mwa kugwila nchito yolalikila mwakhama ndi molimba mtima. Lelolino, m’gulu la Yehova mufunika anthu ambili odzipeleka kuposa kale lonse. Abale, alongo, ndi acicepele ambili-mbili adzipeleka mwa kucita mautumiki osiyana-siyana a nthawi zonse, monga upainiya, kutumikila pa Beteli, ndi kuthandiza pa nchito yomanga Nyumba za Ufumu. Ena amagwila nchito yodzipeleka pa misonkhano yadela ndi yacigawo. Komanso, ganizilani za akulu amene amagwila nchito yofunika kwambili m’Makomiti Okambilana ndi Acipatala. Kwa inu abale na alongo amene mwadzipeleka, dziŵani kuti Yehova amayamikila kwambili mzimu wanu wodzipeleka, ndipo sadzaiŵala nchito yanu.—Aheb. 6:10.

M’bale akupatsidwa mwayi wanchito, koma akuikana pambuyo poganizila mmene nchitoyo ingakhudzile umoyo wauzimu wa banja lake

Musanapange cosankha, mufunika kuganizila mmene cidzakhudzila banja lanu ndi mpingo (Onani palagilafu 15)

15. Tingadziŵe bwanji kuti sitikunyala-nyaza nchito ya Yehova?

15 Aliyense wa ife angacite bwino kudzifunsa kuti: ‘Pamene nitumikila Mulungu, kodi nimakonda kulekela ena kuti ndiwo azicita mbali yaikulu pa nchito? Kodi nikulola mtima wokonda zinthu zakuthupi kunilepheletsa kutumikila Mulungu modzipeleka? Mofanana ndi Baraki, Debora, Yaeli, ndi Aisiraeli odzipeleka 10,000, kodi nimasonyeza cikhulupililo ndi kulimba mtima mwa kuseŵenzetsa zilizonse zimene nili nazo potumikila Yehova?’ Mwina muganiza zosamukila mumzinda wina kapena m’dziko lina kumene muona kuti mukapeza ndalama zambili ndi kukhala na umoyo wabwino. Ngati n’conco, kodi munaipemphelela nkhaniyi ndi kuganizila mmene kusamukako kungakhudzile banja lanu ndi mpingo?c

16. Ngakhale kuti Yehova ali na zonse, n’ciani cimene ife tingamupatse?

16 Yehova watilemekeza kwambili mwa kutipatsa mwayi wocilikiza ulamulilo wake. Kuyambila nthawi ya Adamu ndi Hava, Mdyelekezi wakhala akukopa anthu kuti akhale kumbali ya ulamulilo wake polimbana ndi Mulungu. Koma ife tikamacilikiza ulamulilo wa Yehova, timaonetsa kuti tili kumbali ya Mulungu. Ngati tili na cikhulupililo ndipo tikutumikila Yehova modzipeleka ndi mokhulupilika, iye amakondwela ngako. (Miy. 23:15, 16) Ndipo amapeza yankho loyankha Satana, amene amamutonza. (Miy. 27:11) Conco, ngati timvela Yehova mokhulupilika, ndiye kuti tikum’patsa cinthu camtengo wapatali cimene amakondwela naco.

17. Kodi lemba la Oweruza 5:31 limafotokoza zinthu ziti zimene zidzacitika mtsogolo?

17 Posacedwa, padzikoli padzakhala anthu okhawo amene asankha kukhala kumbali ya ulamulilo wa Yehova. Tikuyembekezela mwacidwi nthawi imeneyo. Timamvela monga mmene Debora na Baraki anamvelela pamene anaimba kuti: “Inu Yehova, adani anu onse afafanizidwe cimodzimodzi, ndipo okukondani inu akhale amphamvu ngati mmene dzuŵa limakhalila.” (Ower. 5:31) Pempho limeneli lidzayankhidwa pamene Yehova adzawononga dziko loipali la Satana. Nkhondo ya Aramagedo ikadzayamba, sitidzafunika kumenya nkhondo yolimbana ndi adani athu. Imeneyo idzakhala nthawi ‘yoima cilili ndi kuona Yehova akutipulumutsa.’ (2 Mbiri 20:17) Koma pakali pano, tili na mwayi waukulu wocilikiza ulamulilo wa Yehova modzipeleka ndi molimba mtima.

18. Kodi anthu ena angapindule bwanji ngati titumikila Mulungu modzipeleka?

18 Debora na Baraki anayamba nyimbo yawo yacipambano ndi mau awa: “Cifukwa ca kudzipeleka mwaufulu kwa anthu, tamandani Yehova.” Pamenepa, iwo anali kutamanda Mulungu Wam’mwambamwamba osati anthu. (Ower. 5:1, 2) Ifenso tikamatumikila modzipeleka masiku ano, anthu ena ‘adzatamanda Yehova.’

a Nthawi zina zitsulo zimenezo zinali kukhala zokhota ngati cikwakwa. Zitsulozo ziyenela kuti zinali kukhala m’mbali mwa magaleta, ndipo mwina anali kuzimangilila ku mahabu a mawilo. Analidi magaleta a nkhondo ocititsa mantha kuwayandikila.

b Mfundo zina pa nkhani yocititsa cidwi imeneyi zinalembedwa mu Nsanja ya Mlonda ya September 1, 2015, mapeji 12-15.

c Onani nkhani yakuti “Nkhawa Zokhudza Ndalama,” mu Nsanja ya Mlonda ya September 1, 2015.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani