LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp18 na. 2 masa. 10-11
  • Malonjezo Amene Adzakwanilitsidwa

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Malonjezo Amene Adzakwanilitsidwa
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • ‘ZIDZAKWANILITSIKADI’
  • Anzake A Mulungu Adzakhala mu Paladaiso
    Na Imwe Mungakhale Mnzake wa Mulungu!
  • Ciyembekezo
    Galamuka!—2018
  • Mu Ufumu wa Mulungu, pa Dziko “Padzakhala Mtendele Woculuka”
    Galamuka!—2019
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
Onaninso Zina
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
wp18 na. 2 masa. 10-11
Mwamuna ayang’ana mapili

Malonjezo Amene Adzakwanilitsidwa

Uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ukulalikidwa padziko lonse lapansi, monga mmene Yesu anakambila. (Mateyu 24:14) Buku la m’Baibo la Danieli, limatiuza kuti Ufumu umenewu ni Boma la Mulungu. Caputa 2 ya buku imeneyi ili na ulosi wokamba za maboma kapena kuti maufumu amene adzakhalapo mokonkhana-konkhana, kuyambila na ulamulilo wa Babulo wakale mpaka masiku athu ano. Ponena zam’tsogolo vesi 44 imati:

“Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse. Ufumuwo sudzapelekedwa kwa mtundu wina uliwonse wa anthu, koma udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo, ndipo udzakhalapo mpaka kalekale.”

Ulosi wa m’Baibo umenewu komanso ena anakambilatu kuti Ufumu wa Mulungu udzaloŵa m’malo mwa maulamulilo onse a anthu na kubweletsa bata ndi mtendele padziko lapansi. Kodi umoyo udzakhala bwanji mu Ufumu umenewo? Lomba onani madalitso okondweletsa amene adzakwanilitsidwa posacedwa.

Zimenezi zidzatanthauza kukhala na moyo wamuyaya komanso wangwilo padziko lapansi la paradaiso! Izi n’zimene anatilonjeza Mlengi wathu wacikondi, Yehova Mulungu.

  • Kupatsana moni

    SIKUDZAKHALANSO NKHONDO

    Salimo 46:9: “[Mulungu] akuletsa nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi. Wathyola uta ndi kuduladula mkondo. Ndipo watentha magaleta pamoto.”

    Kupanga zida za nkhondo kumalila ndalama zambili komanso luso. Kukanakhala kuti ndalama zonsezi amaziseŵenzetsa pothandiza anthu, kodi zinthu sembe zili bwanji padziko? Lonjezo lakuti nkhondo siidzakhalakonso idzakwanilitsidwa mu Ufumu wa Mulungu.

  • Akwela

    SIKUDZAKHALANSO MATENDA

    Yesaya 33:24: “Palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”

    Ganizilani cabe, kukhala m’dziko imene palibe akudwala matenda a mtima, khansa, maleliya, kapena matenda ena alionse. Zipatala na mankhwala sizidzafunikanso. Thanzi yangwilo ndiye tsogolo la anthu okhala padziko lapansi.

  • Tiligu

    SIKUDZAKHALANSO NJALA

    Salimo 72:16: “Padziko lapansi padzakhala tiligu wambili. Pamwamba pa mapili padzakhala tiligu woculuka.”

    Dziko lapansi idzatulutsa cakudya cokwanila aliyense, ndipo cidzakhala cosavuta kucipeza. Njala na matenda obwela kaamba kopeleŵela kwa cakudya m’thupi, sizidzakhalakonso.

  • Mwamuna, mkazi, na mwana

    SIKUDZAKHALANSO ZOŴAŴA, CISONI, NA IMFA

    Chivumbulutso 21:4: “[Mulungu] adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

‘ZIDZAKWANILITSIKADI’

Kodi zonse izi ni kuwamiliza cabe nkhani, koma sizingacitike? Anthu ambili angavomeleze kuti umoyo wofotokozewa m’Baibo umene talonjezewa kutsogolo ni wabwino maningi. Koma pa zifukwa zosiyana-siyana ena ambili amaona kuti kukhala na moyo kwamuyaya n’kosamvetsetseka. Izi n’zosadabwitsa, cifukwa palibe munthu amene anakhalako na moyo umenewu kuti atifotokozele mmene ulili.

Kwa nthawi yaitali anthu akhala mu ukapolo wa ucimo na imfa, ndipo akumana na mavuto ambili-mbili, cakuti ayamba kuwaona kuti ndiye umoyo. Koma cifunilo ca Mlengi wathu Yehova Mulungu ponena za anthu, n’cosiyana kwambili na zimenezi.

Mulungu watithandiza kukhala otsimikiza kuti zimene anatilonjeza adzazikwanilitsa. Ponena za mau ake, motsimikiza iye anati: “Sadzabwelela kwa ine popanda kukwanilitsa colinga cake, koma adzacitadi zimene ine ndikufuna ndipo adzakwanilitsadi zimene ndinawatumizila.”—Yesaya 55:11.

M’Baibo, Yehova amam’kamba kuti ni Mulungu “amene sanganame.” (Tito 1:2) Popeza analonjeza zinthu zonse izi zabwino m’tsogolo, cingakhale canzelu ise kudzifunsa kuti: Kodi n’zoona kuti anthu adzakhala kwamuyaya m’Paradaiso wolonjezedwa padziko lapansi? Kodi tingacite ciani kuti tipindule na lonjezo limeneli la Mulungu? M’nkhani zotsatila za m’magazini ino, mudzapezamo mfundo zothandiza zimene ziyankha mafunso amenewa.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani