LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp19 na. 2 masa. 8-9
  • Pamene Mnzanu wa m’Cikwati Sayenda Bwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Pamene Mnzanu wa m’Cikwati Sayenda Bwino
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • MAVESI A M’BAIBO AMENE ANGAKUTHANDIZENI
  • Kupeza Citonthozo Pa Nthawi Yovuta
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2016
  • 3 Thandizo pa Kupilila Mavuto
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2018
  • Nkhawa Zokhudza Banja
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2015
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2019
wp19 na. 2 masa. 8-9
Apemphela

Pamene Mnzanu wa m’Cikwati Sayenda Bwino

Maria wa ku Spain anati: “Mwamuna wanga ataniuza kuti akunisiya cifukwa wapeza mkazi wacitsikana, cinaniŵaŵa maningi cakuti n’nali kufuna kuti nife cabe. Zonse zinali zopanda cilungamo kwa ine, makamaka pamene n’naganizila zonse zimene n’nadzimana cifukwa ca iye.”

Bill wa ku Spain anati: “Mkazi wanga atanisiya mosayembekezela, zinali monga kuti ciwalo cina m’thupi langa caleka kugwila nchito. Zolinga zathu, zinthu zimene tinali kuyembekezela kucita, komanso mapulani athu, zonse zinathela pamenepo. Masiku ena n’nali kuona kuti lelo nilibe nkhawa, koma mosayembekezela n’nali kupezeka kuti nayambanso kuvutika maganizo kwambili.”

CIMAŴAŴA kwambili ngati wina sayenda bwino m’cikwati. N’zoona kuti ena amasankha kum’khululukila mnzawo wa m’cikwati amene walapa, na kukonzanso cikwati cawo.a Koma kaya cikwati cidzapitiliza kapena ayi, mwamuna kapena mkazi amene wadziŵa kuti mnzake sanali kuyenda bwino, cimaŵaŵa kwambili. Nanga kodi n’ciani cingathandize anthu otelo?

MAVESI A M’BAIBO AMENE ANGAKUTHANDIZENI

Anthu amene anacitilidwa zosakhulupilika na mnzawo wa m’cikwati, zimawapweteka kwambili. Koma ngakhale n’conco, ambili apeza citonthozo m’Malemba. Iwo tsopano adziŵa kuti Mulungu amaona kulila kwawo ndipo amawamvela cifundo.—Malaki 2:13-16.

“Malingalilo osautsa atandiculukila mumtima mwanga, mawu anu otonthoza anayamba kusangalatsa moyo wanga.”—Salimo 94:19.

Bill anati: “Pamene n’nali kuŵelenga vesi imeneyi, n’nali kumvela monga kuti Yehova akunitonthoza mwacikondi, mmene tate wacifundo amacitila.”

“Munthu wokhulupilika, mudzamucitila mokhulupilika.”—Salimo 18:25.

Carmen amene mwamuna wake sanali kuyenda bwino kwa miyezi, anati: “Mwamuna wanga sanali wokhulupilika kwa ine. Koma n’nali na cidalilo cakuti Yehova adzakhalabe wokhulupilika kwa ine. Iye sanganisiye.”

“Musamade nkhawa ndi kanthu kalikonse, koma pa ciliconse, mwa pemphelo ndi pembedzelo . . . zopempha zanu zidziwike kwa Mulungu. Mukatelo, mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu.”—Afilipi 4:6, 7.

Sasha anati: “Lembali n’naliŵelenga mobweleza-bweleza. Ndipo pamene n’napitiliza kupemphela, Mulungu ananipatsa mtendele wa m’maganizo.”

Onse amene taŵagwila mawu pamwambapa, anafika poona kuti moyo ni wosafunika. Koma iwo anadalila Yehova Mulungu, ndipo anapeza mphamvu m’Mawu ake. Bill anakambanso kuti: “Cikhulupililo cinanithandiza kuona kuti moyo wanga ni wofunikabe, olo pamene zonse zionaoneka monga kuti zawonongeka. Ngakhale kuti kwa kanthawi ‘ninayenda m’cigwa ca mdima wandiweyani,’ Mulungu anali naine.”—Salimo 23:4.

a Kuti mudziŵe zambili pa nkhani ya kukhululukila mnzanu wa m’cikwati kapena ayi, onani nkhani zopezeka m’magazini ya Galamukani! ya May 8, 1999, za mutu wakuti, “Pamene Mwamuna Kapena Mkazi Akhala Wosakhulupilika.”

Zimene Zathandiza Ena

Kusinkha-sinkha pa malemba olimbikitsa.

Bill anafotokoza kuti: “N’nali kuŵelenga buku la Yobu komanso la Masalimo. N’nali kuconganso kamzele munsi mwa mawu okamba zofanana na zimene nikupitamo. N’nazindikila kuti anthu a m’Baibo amenewa, nawonso anamvelapo mmene ine n’nali kumvelela. Monga kukhala na nkhawa komanso kupwetekedwa mtima.”

Kupeza citonthozo m’nyimbo.

Carmen anati: “Ngati tulo twanisoŵa usiku, n’nali kumvetsela nyimbo, ndipo kucita izi kunali kunitonthoza kwambili.” Daniel anati: “N’naphunzila kuliza gita, ndipo nyimbo zake zinali kunithandiza kukhala na mtendele wa m’maganizo.”

Kuuzako ena mmene mumvelela.

Daniel anakambanso kuti: “Sin’nali kukonda kuuza ena mmene nimvelela. Koma n’nali na anzanga abwino amene n’nali kuŵafikila tsiku lililonse. N’nali kuwatulila nkhawa zanga mwa kuŵalembela makalata, komanso kukambilana nawo. Izi zinanithandiza kwambili.” Sasha anakambanso kuti: “Thandizo la acibululu linali lofunika kwambili. Amayi anga anali kunithandiza nthawi zonse. N’kafuna wokamba naye, iwo anali wokonzeka kunimvetsela. Atate anali kunipangitsa kumvela kuti ndine wotetezeka, ndiponso anali kunithandiza moleza mtima.”

Kulimbikila kupemphela.

Carmen anati: “N’nali kupemphela nthawi zonse. Ndipo n’nali kumvela monga kuti Mulungu ali pafupi naine, akunimvetsela, komanso kunithandiza. Pa nthawi yovuta imeneyo, n’nalimbitsa ubwenzi wanga na Mulungu.”

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani