NKHANI YOPHUNZILA 25
Dalilani Yehova Pamene Muli na Nkhawa
“Ine ndine . . . wopsinjika maganizo.”—1 SAM. 1:15.
NYIMBO 30 Tate Wanga, Mulungu Wanga, Bwenzi Langa
ZA M’NKHANI INOa
1. N’cifukwa ciani tiyenela kulabadila cenjezo la Yesu?
MU ULOSI wake wonena za masiku otsiliza, Yesu anati: “Samalani kuti mitima yanu isalemedwe ndi . . . nkhawa za moyo” [kapena kuti nkhawa yofuna kupeza zofunikila mu umoyo; nkhawa za tsiku na tsiku]. (Luka 21:34) Tifunika kulabadila cenjezo limeneli. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti timakumana na mavuto osiyana-siyana, amene anthu onse amakumana nawo.
2. Ni mavuto anji amene abale na alongo athu akukumana nawo?
2 Nthawi zina, timakumana na mavuto angapo pa nthawi imodzi. Ganizilani zitsanzo zotsatilazi. M’bale wina dzina lake John,b amene ali na matenda owononga minyewa ya mu ubongo, anavutika maganizo kwambili pamene mkazi wake anamuthawa. Iwo anali atakhala limodzi m’cikwati kwa zaka 19. Kenako, ana ake aakazi aŵili analeka kutumikila Yehova. M’bale winanso dzina lake Bob, na mkazi wake Linda, nawonso anakumana na mavuto osiyana-siyana. Onse aŵili anacotsedwa nchito, ndipo anafunika kucoka m’nyumba imene anali kukhala. Kuwonjezela apo, mlongo Linda anam’peza na matenda oopsa a mtima, ndi ena owononga citetezo ca m’thupi.
3. Malinga na Afilipi 4:6, 7, kodi sitikayikila za ciani?
3 Sitikayikila kuti Mlengi wathu komanso Atate wathu wacikondi, Yehova, amadziŵa mmene timamvelela tikakhala na nkhawa. Ndipo amafuna kutithandiza kulimbana na mavuto amene timakumana nawo. (Ŵelengani Afilipi 4:6, 7.) Baibo ili na nkhani zambili zofotokoza mavuto amene atumiki a Mulungu anakumana nawo. Imafotokozanso mmene Yehova anawathandizila kupilila mavuto amenewo. Tiyeni tioneko zitsanzo zingapo.
“ELIYA ANALI MUNTHU MONGA IFE”
4. Ni mavuto otani amene Eliya anakumana nawo? Nanga anaona ciani ponena za Yehova?
4 Eliya anatumikila Yehova m’nthawi yovuta, ndipo anakumana na mavuto aakulu. Panthawiyo, Ahabu, Mfumu yosakhulupilika ya Isiraeli, anakwatila Yezebeli, mkazi wolambila Baala. Ahabu na mkazi wake anasonkhezela Aisiraeli ambili kuyamba kulambila Baala, ndipo anapha aneneli oculuka a Yehova. Koma Eliya anakwanitsa kuthaŵa. Iye anapulumukanso ku cilala cacikulu cimene cinagwa m’dzikolo, cifukwa anadalila Yehova. (1 Maf. 17:2-4, 14-16) Kuwonjezela apo, Eliya anadalila Yehova pamene anayang’anizana ndi aneneli a Baala komanso alambili ake. Iye analimbikitsa Aisiraeli kutumikila Yehova. (1 Maf. 18:21-24, 36-38) Inde, Eliya anali na maumboni ambili oonetsa kuti Yehova anali kum’thandiza pa nthawi zovuta zimenezo.
Yehova anatumiza mngelo kuti akalimbikitse Eliya (Onani ndime 5-6)c
5-6. Malinga n’zimene 1 Mafumu 19:1-4 imakamba, kodi Eliya anamvela bwanji? Nanga Yehova anaonetsa bwanji kuti anali kum’konda?
5 Ŵelengani 1 Mafumu 19:1-4. Eliya anacita mantha pamene Mfumukazi Yezebeli anaopseza kuti adzamupha. Conco, iye anathaŵila ku Beere-seba. Eliya anavutika maganizo kwambili, cakuti “anayamba kupempha kuti afe” cabe. N’cifukwa ciani iye anataya mtima? Cifukwa cakuti anali “munthu monga ife tomwe.” (Yak. 5:17) Mwina anali na nkhawa kwambili, komanso analema ngako. Mwinanso anaganiza kuti zonse zimene anacita polimbikitsa kulambila koona, zinangopita pacabe cifukwa anthu sanasinthe. Anaganizanso kuti anangotsala yekha-yekha mtumiki wa Yehova. (1 Maf. 18:3, 4, 13; 19:10, 14) Mwina ife sitingamvetsetse kuti n’cifukwa ciani mneneli wokhulupilika ameneyu anafika pokhala na maganizo amenewa. Koma Yehova anali kudziŵa bwino mmene Eliya anali kumvelela.
6 Yehova sanamudzudzule Eliya cifukwa cofotokoza nkhawa zake. M’malomwake, anamuthandiza kupezanso mphamvu. (1 Maf. 19:5-7) Pambuyo pake, mokoma mtima Yehova anathandiza Eliya kuwongolela maganizo ake. Anacita izi mwa kumuonetsa mphamvu zake zocititsa mantha. Ndiyeno, anamuuza kuti mu Isiraeli munali anthu 7,000, amene sanali kulambila Baala. (1 Maf. 19:11-18) Mwa kumuuza zimenezi, Yehova anathandiza Eliya kuzindikila kuti anali kum’konda.
MMENE YEHOVA AMATITHANDIZILA
7. Kodi timalimbikitsidwa bwanji tikaganizila mmene Yehova anathandizila Eliya?
7 Kodi mukukumana na mavuto othetsa nzelu? Ngati n’conco, mungalimbikitsidwe kudziŵa kuti Yehova anadziŵa mmene Eliya anali kumvelela. Izi zimatitsimikizila kuti Mulungu amamvetsetsa nkhawa zathu. Iye amadziŵa zimene tingakwanitse kucita na zimene sitingakwanitse. Amadziŵanso ngakhale maganizo athu na mmene timamvelela. (Sal. 103:14; 139:3, 4) Ngati titengela citsanzo ca Eliya mwa kudalila Yehova, iye adzatithandiza kupilila mavuto amene amaticititsa kukhala na nkhawa.—Sal. 55:22.
8. Kodi Yehova angatithandize bwanji kuthetsa nkhawa?
8 Nkhawa ingapangitse kuti titaye mtima mpaka kufooka. Cotelo, ngati tili na nkhawa, tizikumbukila kuti Yehova angatithandize kuithetsa. Kodi angatithandize bwanji? Iye amatiuza kuti tizim’fotokozela nkhawa zathu m’pemphelo. Ndipo amayankha mapemphelo athu opempha thandizo. (Sal. 5:3; 1 Pet. 5:7) Conco, nthawi zonse muzimuuza Yehova mavuto anu m’pemphelo. N’zoona kuti iye sadzakamba na imwe mofanana na mmene anakambila na Eliya. Koma adzakamba nanu kupitila m’Mawu ake Baibo, na gulu lake. Nkhani zimene mumaŵelenga m’Baibo, zingakulimbikitseni na kukupatsani ciyembekezo. Nawonso abale na alongo mu mpingo angakulimbikitseni.—Aroma 15:4; Aheb. 10:24, 25.
9. Kodi mnzathu wapamtima angatithandize bwanji?
9 Yehova anauza Eliya kuti agaŵileko Elisa nchito zina zimene anali nazo. Mwanjila imeneyi, Yehova anapatsa Eliya mnzake wabwino, amene anamulimbikitsa kwambili pa nthawi yovuta. N’cimodzi-modzinso na ife. Ngati tiuzako mnzathu wapamtima nkhawa zathu, angatilimbikitse. (2 Maf. 2:2; Miy. 17:17) Koma ngati mulibe mnzanu wapamtima amene mungamuuzeko nkhawa zanu, m’pempheni Yehova kuti akuthandizeni kupeza Mkhristu wofikapo mwauzimu, amene angakulimbikitseni mukakhala na nkhawa.
10. Kodi nkhani ya Eliya imatilimbikitsa bwanji? Nanga lonjezo la pa Yesaya 40:28, 29 lingatilimbikitse bwanji?
10 Yehova anathandiza Eliya kuthetsa nkhawa zake. Anamuthandizanso kuti am’tumikile mokhulupilika kwa zaka zambili. Nkhani ya Eliya imatilimbikitsa. Nthawi zina, tingakhale na nkhawa yaikulu imene ingatifooketse. Koma ngati tidalila Yehova, iye adzatipatsa mphamvu kuti tipitilize kum’tumikila.—Ŵelengani Yesaya 40:28, 29.
HANA, DAVIDE, NDI WAMASALIMO WINAWAKE, ANADALILA YEHOVA
11-13. Fotokozani mmene nkhawa inakhudzila atumiki atatu a Mulungu.
11 Pali anthu enanso ochulidwa m’Baibo, amene anakhalapo na nkhawa kwambili. Mwacitsanzo, Hana anavutika kwambili maganizo cifukwa sanali kubeleka, ndiponso cifukwa cotonzedwa na mkazi mnzake. (1 Sam. 1:2, 6) Iye anali kukhala na nkhawa kwambili, cakuti anali kungolila na kukana kudya.—1 Sam. 1:7, 10.
12 Nthawi zina, nayenso Mfumu Davide anali kukhala wopsinjika maganizo. Ganizilani ena mwa mavuto amene anakumana nawo. Anali kuvutika na nkhawa poganizila zolakwa zambili zimene anacita. (Sal. 40:12) Cinanso, mwana wake wokondedwa Abisalomu anam’pandukila, moti pamapeto pake Abisalomu anaphedwa. (2 Sam. 15:13, 14; 18:33) Kuwonjezela apo, mmodzi wa mabwenzi ake apamtima, anam’pandukilanso. (2 Sam. 16:23–17:2; Sal. 55:12-14) Masalimo ambili amene Davide analemba, amaonetsa nkhawa imene anali nayo cifukwa ca mavuto amene anakumana nawo. Amaonetsanso kuti iye anali kudalila kwambili Yehova.—Sal. 38:5-10; 94:17-19.
N’ciani cinathandiza wamasalimo kuyambanso kutumikila Yehova mwacimwemwe? (Onani ndime 13-15)d
13 Palinso wamasalimo winawake amene anavutika kwambili na nkhawa. Iye ayenela kuti anali mbadwa ya Asafu, Mlevi. Wamasalimo ameneyu anali kutumikila “m’malo opatulika aulemelelo a Mulungu.” Pa nthawi ina, iye anayamba kucitila nsanje anthu oipa. Izi zinapangitsa kuti azivutika maganizo kwambili na kukhala wosakondwela. Anafika poganiza kuti kutumikila Mulungu n’kungotaya nthawi.—Sal. 73:2-5, 7, 12-14, 16,17, 21.
14-15. Tiphunzilapo ciani pa zitsanzo zitatu za m’Baibo za anthu amene anadalila Yehova pamene anali na nkhawa?
14 Atumiki a Mulungu atatu amenewa, onse anadalila thandizo la Yehova. Iwo anali kupemphela kwa iye mocokela pansi pa mtima na kumuuza nkhawa zawo. Anali kum’fotokozela zonse zimene zinali kuwapangitsa kukhala na nkhawa. Ndiponso sanaleke kupita ku malo olambilila Yehova.—1 Sam. 1:9, 10; Sal. 55:22; 73:17; 122:1.
15 Yehova anawamvela cifundo na kuwathandiza. Mwacitsanzo, iye anathandiza Hana kukhala na mtendele wa mu mtima. (1 Sam. 1:18) Davide nayenso anathandizidwa, moti analemba kuti: “Masoka a munthu wolungama ndi oculuka, koma Yehova amamupulumutsa ku masoka onsewo.” (Sal. 34:19) Ndipo wamasalimo uja amene takamba, m’kupita kwa nthawi anazindikila kuti Yehova ‘anagwila dzanja lake lamanja,’ ndipo anali kum’tsogolela mwacikondi na malangizo ake. Iye anaimba kuti: “Kwa ine kuyandikila kwa Mulungu ndi cinthu cabwino. Yehova Ambuye Wamkulu Koposa ndiye pothawilapo panga.” (Sal. 73:23, 24, 28) Kodi tiphunzilapo ciani pa zitsanzo zimenezi? Tiphunzilapo kuti nthawi zina tingakhale na nkhawa kwambili cifukwa ca mavuto aakulu amene takumana nawo. Koma tingapilile ngati tiganizila mmene Yehova wakhala akuthandizila atumiki ake ena. Tiyenelanso kumumvela na kuonetsa kuti timam’dalila mwa kupemphela.—Sal. 143:1, 4-8.
DALILANI YEHOVA KUTI MUKWANITSE KUPILILA
Mlongo wina amene anali na nkhawa, poyamba anali kudzipatula. Koma atayamba kuyesetsa kuthandiza ena, nkhawa zake zinacepa (Onani ndime 16-17)
16-17. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kudzipatula? (b) Tiyenela kucita ciani kuti tipezenso mphamvu?
16 Zitsanzo zitatu zimenezi, zitiphunzitsanso mfundo ina yofunika kwambili. Mfundo yake ni yakuti, sitiyenela kutalikilana na Yehova komanso anthu ake. (Miy. 18:1) Mlongo wina, dzina lake Nancy, anapsinjika kwambili maganizo pamene mwamuna wake anamuthaŵa. Iye anati: “Nthawi zambili sin’nali kufuna kuonana na aliyense. Sin’nali kufunanso kukamba na aliyense. Koma nikakhala nekha-nekha, m’pamene n’nali kukhala wacisoni kwambili.” Zinthu zinasintha pamene Nancy anayamba kuyesetsa kuthandiza anthu ena, amenenso anali kukumana na mavuto. Iye anati: “Ena akamanifotokozela mavuto awo, n’nali kumvetsela mosamala. Ndipo n’nazindikila kuti pamene niyesetsa kuwamvela cifundo, m’pamenenso nkhawa zanga zinali kucepela-cepela.”
17 Kupezeka ku misonkhano, kungatithandize kupezanso mphamvu. Tikapezeka ku misonkhano, timapatsa Yehova mpata wakuti ‘atithandize na kutilimbikitsa.’ (Sal. 86:17) Kumeneko, iye amatilimbikitsa poseŵenzetsa mzimu wake woyela, Mawu ake, ndi anthu ake. Misonkhano imatipatsanso mwayi ‘wolimbikitsana.’ (Aroma 1:11, 12) Mlongo wina, dzina lake Sophia, anati: “Yehova komanso abale na alongo ananithandiza kupilila. N’nali kuona misonkhano kukhala yofunika kwambili. Naona kuti kugwilizana kwambili na mpingo, ndiponso kutangwanika kwambili mu nchito yolalikila, kumanithandiza kucepetsa nkhawa.”
18. Ngati tili na nkhawa, kodi Yehova amatithandiza bwanji?
18 Mukakhala na nkhawa, kumbukilani kuti Yehova walonjeza kuti posacedwa adzathetsa mavuto onse. Ndipo ngakhale pa nthawi ino, amatithandiza kulimbana na nkhawa zimene timakhala nazo. Ngati tili na nkhawa, iye amatilimbikitsa na kutipatsa mphamvu kuti tisataye mtima.—Afil. 2:13.
19. Kodi lemba la Aroma 8:37-39 limatitsimikizila mfundo yanji?
19 Ŵelengani Aroma 8:37-39. Mtumwi Paulo anatitsimikizila kuti palibe cimene cingatilekanitse na cikondi ca Mulungu. Kodi tingathandize bwanji abale na alongo athu amene ali na nkhawa? Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene tingatsatilile citsanzo ca Yehova mwa kukhala acifundo, ndiponso mwa kuthandiza abale na alongo athu amene ali na nkhawa.
NYIMBO 44 Pemphelo la Munthu Wovutika
a Nkhawa yopambanitsa kapena yokhalitsa, ingatifooketse na kutibweletsela matenda. Kodi Yehova angatithandize bwanji kuthetsa nkhawa? M’nkhani ino, tikambilana mmene Yehova anathandizila Eliya kuthetsa nkhawa zake. Tikambilananso zitsanzo zina za m’Baibo, zoonetsa zimene tingacite kuti Yehova atithandize tikakhala na nkhawa.
b Maina ena m’nkhani ino asinthidwa.
c MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Mngelo wa Yehova akudzutsa mneneli Eliya mokoma mtima na kum’patsa mkate na madzi.
d MAWU OFOTOKOZA ZITHUNZI: Wamasalimo, amene ayenela kuti anali mbadwa ya Asafu, akulemba masalimo na kuimba pamodzi na Alevi ena.