LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • w19 July masa. 14-19
  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzila”

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzila”
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
  • Tumitu
  • Nkhani Zofanana
  • N’CIFUKWA CIANI NCHITO YOPANGA OPHUNZILA NI YOFUNIKA KWAMBILI?
  • KODI KUPANGA OPHUNZILA KUMAPHATIKIZAPO CIANI?
  • MKHRISTU ALIYENSE AMATENGAKO MBALI PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA
  • CIFUKWA CAKE NCHITO YOPANGA OPHUNZILA IMAFUNA KULEZA MTIMA
  • Kodi Mungathandize pa Nchito Yopanga Ophunzila?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2021
  • ‘Pitani Mukaphunzitse Anthu Kuti Akhale Ophunzila Anga’
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 2
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
  • Mmene Tingatsogozele Phunzilo la Baibo Lotsogolela Munthu ku Ubatizo—Gawo 1
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2020
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2019
w19 July masa. 14-19

NKHANI YOPHUNZILA 29

“Pitani Mukaphunzitse Anthu . . . Kuti Akhale Ophunzila”

“Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.”—MAT. 28:19.

NYIMBO 60 Ni Moyo Wawo

ZA M’NKHANI INOa

1-2. (a) Mogwilizana na lamulo la Yesu la pa Mateyu 28:18-20, kodi nchito yaikulu ya mpingo wacikhristu ni iti? (b) Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani ino?

YESU ataukitsidwa, anauza ophunzila ake kuti akakumane naye m’mbali mwa phili linalake ku Galileya. Atasonkhana pa malowo, ophunzilawo ayenela kuti anali kuyembekezela mwacidwi kumvetsela zimene Yesu anali kufuna kuwauza. (Mat. 28:16) Mwina iyi ndiyo nthawi imene Yesu ‘anaonekela kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi.’ (1 Akor. 15:6) N’cifukwa ciani Yesu anauza ophunzila ake kuti akasonkhane pa malowo? Anafuna kuwapatsa nchito yokondweletsa. Iye anati: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.”—Ŵelengani Mateyu 28:18-20.

2 Ophunzila a Yesu amene anamvela mawu ake amenewa ndiwo anapanga mpingo woyambilila wacikhristu. Nchito yawo yaikulu inali yophunzitsa anthu ena kuti akhale ophunzila a Khristu.b Masiku ano, pa dziko lonse lapansi pali mipingo masauzande ambili ya Akhristu oona. Ndipo nawonso nchito yawo yaikulu ni kupanga ophunzila a Khristu. M’nkhani ino, tidzakambilana mafunso anayi aya: N’cifukwa ciani nchito yopanga ophunzila ni yofunika kwambili? Kodi nchitoyi imaphatikizapo ciani? N’cifukwa ciani tinganene kuti Mkhristu aliyense amatengako mbali pa nchito yopanga ophunzila? Nanga n’cifukwa ciani tifunika kukhala oleza mtima pogwila nchitoyi?

N’CIFUKWA CIANI NCHITO YOPANGA OPHUNZILA NI YOFUNIKA KWAMBILI?

3. Mogwilizana na Yohane 14:6 ndi 17:3, n’cifukwa ciani nchito yopanga ophunzila ni yofunika kwambili?

3 N’cifukwa ciani nchito yopanga ophunzila ni yofunika kwambili? Cifukwa cakuti ni ophunzila a Khristu okha amene angakhale mabwenzi a Mulungu. Kuwonjezela apo, onse amene amatsatila Khristu amakhala na umoyo wabwino pali pano, komanso ali na ciyembekezo codzakhala na moyo wosatha kutsogolo. (Ŵelengani Yohane 14:6; 17:3.) Ndithudi, nchito imene Yesu watipatsa ni yofunika kwambili. Ndipo sitigwila tekha nchitoyi. Mtumwi Paulo pokamba za iye mwini na mabwenzi ake, analemba kuti: “Ndife anchito anzake a Mulungu.” (1 Akor. 3:9) Kukamba zoona, kukhala anchito anzake a Mulungu ni mwayi wamtengo wapatali kwambili umene Yehova na Khristu wapeleka kwa ife anthu opanda ungwilo.

4. Kodi tingaphunzilepo ciani pa citsanzo ca Ivan na Matilde?

4 Nchito yopanga ophunzila imatibweletsela cimwemwe coculuka. Ganizilani citsanzo ca m’bale Ivan na mkazi wake Matilde, amene amakhala ku Colombia. Iwo analalikila mnyamata winawake, dzina lake Davier. Mnyamatayo anawauza kuti: “Nimafuna kusintha khalidwe langa, koma zimanivuta.” Davier anali kukonda mpikisano wa nkhonya, anali kumwa moŵa kwambili, komanso kugwilitsila nchito amkolabongo. Iye analinso kukhala limodzi na cisumbali cake, dzina lake Erika. M’bale Ivan anafotokoza kuti: “Tinayamba kuphunzila naye Baibo. Pa nthawiyo, anali kukhala ku mudzi winawake wakutali. Tinali kuyenda pa njinga kwa maola ambili m’njila ya matika. Erika ataona kuti Davier wayamba kusintha khalidwe lake, nayenso anayamba kupezekapo pa phunzilo la Baibo.” M’kupita kwa nthawi, Davier analeka kuseŵenzetsa amkolabongo, kumwa moŵa, na kucita mpikisano wa nkhonya. Komanso anakwatilana mwalamulo na Erika. Mlongo Matilde anati: “Pamene Davier na Erika anali kubatizika mu 2016, tinakumbukila mawu amene Davier anali kukonda kukamba akuti, ‘Nimafuna kusintha khalidwe langa, koma zimanivuta.’ Tinakondwela ngako, moti tinagwetsa misozi yacisangalalo.” Ndithudi, tikathandiza munthu kukhala wophunzila wa Khristu, timakhala na cimwemwe cosaneneka.

KODI KUPANGA OPHUNZILA KUMAPHATIKIZAPO CIANI?

5. Kodi cinthu coyamba cimene tifunika kucita kuti tipange ophunzila n’ciani?

5 Coyamba cimene tifunika kucita kuti tipange ophunzila, ni kufuna-funa anthu amene ali na maganizo abwino. (Mat. 10:11). Timaonetsa kuti ndifedi Mboni za Yehova mwa kulalikila munthu aliyense amene tingakumane naye. Timaonetsanso kuti ndife Akhristu eni-eni mwa kutsatila lamulo la Yesu lakuti tizilalikila.

6. N’ciani cimene tingacite kuti anthu azilabadila uthenga wathu?

6 Anthu ena amene timakumana nawo amakhala ofunitsitsa kuphunzila coonadi ca m’Baibo. Koma ambili amaoneka opanda cidwi poyamba. Conco, tingafunike kuwathandiza kukulitsa cidwi. Kuti tikhale alaliki ogwila mtima, tiyenela kukonzekela bwino. Sankhani nkhani zimene muona kuti anthu ambili m’gawo lanu angacite nazo cidwi. Ndiyeno, konzekelani mawu oyamba ogwila mtima.

7. Kodi mungayambe bwanji makambilano na munthu? Nanga n’cifukwa ciani muona kuti kulemekeza anthu amene timawalalikila na kuwamvetsela mosamala n’zofunika kwambili?

7 Mwacitsanzo, mukakumana na munthu, mungayambe mwa kukamba kuti, “Ningakonde kumvako maganizo anu pa nkhani iyi. Mavuto ambili amene timakumana nawo masiku ano amacitikilanso anthu ena pa dziko lonse lapansi. Kodi inu muganiza kuti pangafunike boma lolamulila dziko lonse limene lingathetse mavuto amenewa?” Kenako, mungakambilane naye Danieli 2:44. Mwinanso mungafunse a neba anu kuti, “Kodi muganiza kuti n’ciani cingatithandize kulela bwino ana? Ningakonde kumvako maganizo anu pa nkhaniyi.” Ndiyeno, kambilanani Deuteronomo 6:6, 7. Pa nkhani iliyonse imene mwasankha kukambilana ndi anthu, muziganizila omvela. Muziganizila mapindu amene angapeze cifukwa cophunzila coonadi ca m’Baibo. Ndipo pokambilana nawo, n’kofunika kwambili kuwamvetsela mosamala komanso kulemekeza maganizo awo. Mukatelo, mudzawamvetsetsa, ndipo cidzakhala cosavuta kwa iwo kumvetsela uthenga wanu.

8. N’cifukwa ciani kupanga maulendo obwelelako kumafuna kulimbikila?

8 Munthu asanavomele kuphunzila Baibo, mungafunike kuthela nthawi yoculuka na mphamvu popanga maulendo obwelelako. Cifukwa ciani? Cifukwa cakuti nthawi zina anthu sapezeka pa nyumba pa ulendo wobwelelako. Cinanso, mungafunike kupanga maulendo obwelelako angapo mwininyumba asanavomele kuphunzila naye Baibo. Tingayelekezele zimenezi na mbewu. Kuti mbewu ikule, timafunika kuithilila mobweleza-bweleza. Mofananamo, kuti cikondi cimene munthu wacidwi ali naco pa Yehova na Yesu cikule, timafunika kukambilana naye Mawu a Mulungu mobweleza-bweleza.

MKHRISTU ALIYENSE AMATENGAKO MBALI PA NCHITO YOPANGA OPHUNZILA

9-10. N’cifukwa ciani tingakambe kuti Mkhristu aliyense amatengako mbali pa nchito yofuna-funa anthu a maganizo oyenelela?

9 Mkhristu aliyense amagwilako nchito yofuna-funa anthu oona mtima. Nchito imeneyi tingaiyelekezele na nchito yofuna-funa mwana amene wasoŵa. M’njila yotani? Ganizilani zimene zinacitika pamene mwana winawake wa zaka zitatu anasoŵa. Anthu pafupi-fupi 500 anatengako mbali pa nchito yofuna-funa mwanayo. Patapita maola 20, mmodzi mwa anthuwo anam’peza mwanayo ali m’munda winawake wacimanga. Munthuyo anakana kutamandidwa cifukwa copeza mwanayo. Iye anati: “Mwanayu wapezeka cifukwa ca khama la anthu ambili.”

Mwamuna walandila kathilakiti kwa mboni zimene zili pa ulaliki wapoyela pa eyapoti; ali ku chuti, waona abale akucita ulaliki wa poyela; atabwelela ku nyumba, mwamunayu akumvetsela kwa mboni zimene zabwela pa nyumba kudzam’lalikila

Mboni za Yehova pa dziko lonse lapansi zili pa nchito yofuna-funa anthu oyenelela (Onani ndime 9-10)c

10 Masiku ano, anthu ambili ali ngati mwana amene anasoŵa. Iwo alibe ciyembekezo ciliconse, ndipo amafuna thandizo. (Aef. 2:12) Ndiye cifukwa cake ife tonse opitilila pa 8 miliyoni, tili pa nchito yofuna-funa anthu a maganizo oyenelela. Mwina imwe simungapeze munthu amene angakonde kuphunzila Baibo. Koma ofalitsa ena amene amalalikila m’gawo limodzi-modzilo, angapeze anthu acidwi ofuna kuphunzila coonadi ca m’Baibo. Ngati m’bale kapena mlongo wapeza munthu wacidwi n’kumuthandiza kupita patsogolo mpaka kukhala wotsatila wa Khristu, ndiye kuti Mkhristu aliyense amene amatengako mbali pa nchito yofufuzayi ali na cifukwa comveka cokhalila wacimwemwe.

11. Olo kuti mulibe phunzilo la Baibo, n’ziti zina zimene mungacite kuti muthandize pa nchito yopanga ophunzila?

11 Ngakhale kuti mwina pali pano mulibe phunzilo la Baibo, mungathandize pa nchito yopanga ophunzila m’njila zina. Mwacitsanzo, acatsopano akafika pa Nyumba ya Ufumu, mungawalandile mwaubwenzi na kuwathandiza m’njila zosiyana-siyana. Kuwaonetsa cikondi mwanjila imeneyi, kudzawathandiza kuona kuti ndifedi Akhristu oona. (Yoh. 13:34, 35) Cinanso, ndemanga zimene mumapeleka pa misonkhano, olo kuti zimakhala zacidule, zingalimbikitse acatsopano kupeleka ndemanga mocokela pansi pa mtima ndi mwaulemu. Komanso, mungapite na wofalitsa watsopano mu ulaliki, ndipo pamene mulalikila, mungam’thandize kufotokoza Malemba mogwila mtima pokambilana ndi anthu. Mukatelo, ndiye kuti mukum’thandiza kutengela citsanzo ca Khristu.—Luke 10:25-28.

12. Kodi ticita kufunikila luso lapadela kuti tiphunzitse anthu kukhala ophunzila a Yesu? Fotokozani.

12 Tisaganize kuti tifunika kukhala na luso lapadela kuti tiphunzitse anthu kukhala ophunzila a Yesu. N’cifukwa ciani takamba conco? Ganizilani citsanzo ca Faustina wa ku Bolivia. Iye sanali kudziŵa kuŵelenga pamene anayamba kuphunzila na Mboni za Yehova. Lomba, iye amakwanitsako kuŵelenga, koma movutikila. Faustina tsopano anabatizika, ndipo amaikonda nchito yophunzitsa anthu coonadi. Amatsogoza maphunzilo a Baibo asanu wiki iliyonse. Ngakhale kuti Faustina sakwanitsa kuŵelenga bwino monga mmene maphunzilo ake a Baibo amaŵelengela, wathandizapo kale anthu 6 mpaka kufika pobatizika.—Luka 10:21.

13. Olo tikhale otangwanika kwambili, ni madalitso ena ati amene tingapeze ngati tigwilabe nchito yopanga ophunzila?

13 Masiku ano, Akhristu ambili amakhala otangwanika kwambili na kusamalila maudindo ofunika amene ali nawo. Ngakhale n’conco, iwo amapatula nthawi yotsogoza maphunzilo a Baibo, ndipo amakhala na cimwemwe coculuka cifukwa cocita zimenezi. Ganizilani citsanzo ca mlongo Melanie wa ku Alaska. Iye anali kulela yekha mwana wake wamkazi wa zaka 8. Mlongoyu analinso pa nchito yolembedwa, ndipo anali kusamalilanso atate ake amene anali kudwala khansa. Mlongo Melanie anali yekha Mboni mtauni yawo. Iye anali kupemphela kwa Mulungu nthawi zonse kuti am’patse mphamvu kuti apitebe kukalalikila, ngakhale m’nyengo yozizila kwambili. Mlongoyu anali kucita izi cifukwa anali wofunitsitsa kupeza munthu wophunzila naye Baibo. Patapita nthawi, anakumana na Sara, amene anakondwela kwambili kudziŵa kuti Mulungu ali na dzina. M’kupita kwa nthawi, Sara anavomela kuyamba kuphunzila Baibo. Mlongo Melanie anati: “Nthawi zambili pa Cisanu m’madzulo nimakhala wolema kwambili. Koma ine na mwana wanga wamkazi tinali kupindula tikapita kukatsogoza phunzilolo. Tinali kukondwela kufufuza mayankho a mafunso amene Sara anali kutifunsa. Ndipo tinakondwela kwambili kuona kuti wayamba kukhala bwenzi la Yehova.” Sara anapilila citsutso molimba mtima. Analeka kupita ku chechi yake, mpaka anabatizika.

CIFUKWA CAKE NCHITO YOPANGA OPHUNZILA IMAFUNA KULEZA MTIMA

14. (a) Kodi nchito yolalikila ifanana bwanji na nchito ya usodzi? (b) Kodi mawu a Paulo pa 2 Timoteyo 4:1, 2, akulimbikitsani bwanji?

14 Ngakhale ngati mukalibe kupeza munthu amene afuna kukhala wophunzila wa Khristu, musaleke kufuna-funa. Kumbukilani kuti Yesu anayelekezela nchito yopanga ophunzila na nchito ya usodzi. Asodzi angagwile nchitoyi kwa maola ambili osagwilako nsomba iliyonse. Nthawi zambili, amagwila nchitoyi usiku kapena kuseni-seni. Ndipo nthawi zina, amayenda m’nyanja mitunda itali-itali kusakila nsomba. (Luka 5:5) Mofananamo, Akhristu ena amathela maola oculuka posakila anthu m’malo osiyana-siyana, komanso pa nthawi zosiyana-siyana. Cifukwa ciani? Amafuna kupeza mipata yokambilana ndi anthu. Akhristu amene amacita khama pa nchitoyi, nthawi zambili amakhala na mwayi wopeza anthu amene ali na cidwi na uthenga wabwino. Kodi mungayeseko kulalikila pa nthawi imene muona kuti mungakumane ndi anthu, kapenanso pa malo amene muona kuti mungawapeze?—Ŵelengani 2 Timoteyo 4:1, 2.

Mwamunayo wavomela kuyamba phunzilo la Baibo; pamapeto pake akubatizika

Thandizani wophunzila wanu moleza mtima kuti apite patsogolo mwauzimu (Onani ndime 15-16)d

15. N’cifukwa ciani kutsogoza maphunzilo a Baibo kumafuna kuleza mtima?

15 N’cifukwa ciani kutsogoza maphunzilo a Baibo kumafuna kuleza mtima? Cifukwa cimodzi n’cakuti kuphunzitsa munthu kumafuna zambili, osati cabe kum’thandiza kudziŵa ziphunzitso za m’Baibo na kuzikonda. Timafunikanso kum’thandiza kudziŵa Mlembi wa Baibo, Yehova na kum’konda. Komanso, kuwonjezela pa kuphunzitsa munthu zimene Yesu anatilamula kucita, tifunika kum’thandiza kudziŵa mmene angatsatilile malamulowo mu umoyo wake. Tifunikanso kum’thandiza moleza mtima pamene ayesa-yesa kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibo mu umoyo wake. Ena amatha kusintha kaganizidwe kawo na makhalidwe awo oipa m’miyezi yoŵelengeka cabe. Koma ena amatenga nthawi yaitali.

16. Kodi mwaphunzila ciani pa citsanzo ca m’bale Raúl?

16 Ganizilani cocitika ca mmishonale wina wa ku Peru, cimene cionetsa kufunika kokhala woleza mtima. Mmishonaleyo anati: “Tinaphunzila mabuku aŵili na wophunzila Baibo, dzina lake Raúl. Koma zinali kumuvutabe kuseŵenzetsa zimene anali kuphunzila mu umoyo wake. Raúl anali na mavuto ambili m’cikwati cake, anali kukonda kutukwana, ndiponso ana ake sanali kum’lemekeza cifukwa ca khalidwe lake loipa. Ngakhale zinali conco, iye anali kupezeka pa misonkhano nthawi zonse. Cotelo, n’napitiliza kum’cezela kuti nim’thandize pamodzi na banja lake. Patapita zaka zitatu kucokela pamene n’nakumana naye, anayenelela ubatizo.”

17. Kodi tidzakambilana ciani m’nkhani yokonkhapo?

17 Yesu anatilamula kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.” Pogwila nchitoyi, nthawi zambili timakumana ndi anthu amene ali na maganizo osiyana kwambili na athu. Mwacitsanzo, timakumana ndi anthu amene sali m’cipembedzo ciliconse kapena amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu. M’nkhani yokonkhapo, tidzakambilana mmene tingalalikile uthenga wabwino kwa anthu otelo.

KODI MUNGAYANKHE BWANJI?

  • N’cifukwa ciani nchito yopanga ophunzila ni yofunika kwambili?

  • Kodi n’ndani amatengako mbali pa nchito yopanga ophunzila?

  • N’cifukwa ciani nchito yopanga ophunzila imafuna kuleza mtima?

NYIMBO 68 Fesani Mbewu za Ufumu

a Nchito yaikulu ya mpingo wacikhristu ni kuthandiza anthu kuti akhale ophunzila a Khristu. M’nkhani ino, muli malangizo amene adzatithandiza pogwila nchito imeneyi.

b KUFOTOKOZELA MAWU ENA: Ophunzila a Khristu samangophunzila zimene Yesu anakamba. Koma amayesetsa kucita zimene amaphunzila. Iwo amayesetsa mmene angathele kutsatila mapazi a Yesu, kapena kuti citsanzo cake.—1 Pet. 2:21.

c MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwamuna amene akupita ku chuti watenga kathilakiti kwa Mboni za Yehova pa eyapoti. Ali ku chutiko, waonanso Mboni zina zili pa ulaliki wa poyela. Atabwelela ku nyumba, Mboni zinanso zabwela pa nyumba kukam’lalikila.

d MAWU OFOTOKOZELA ZITHUNZI: Mwamunayo wavomela kuyamba phunzilo la Baibo. Pamapeto pake, akubatizika.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani