LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • wp20 na. 2 tsa. 3
  • “Ufumu Wanu Udze”—Pemphelo Limene Anthu Ambili Amapeleka

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • “Ufumu Wanu Udze”—Pemphelo Limene Anthu Ambili Amapeleka
  • Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Nkhani Zofanana
  • Kuyankha Mafunso a m’Baibulo
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova—2014
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?
    Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni
  • Coonadi Ponena za Ufumu wa Mulungu
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawila)—2020
wp20 na. 2 tsa. 3
Anthu amisinkhu komanso amitundu yosiyana-siyana akupemphela.

“Ufumu Wanu Udze”—Pemphelo Limene Anthu Ambili Amapeleka

Kodi munapemphelapo kuti Ufumu wa Mulungu ubwele? Kwa zaka mahandiledi ambili, anthu oculuka amachula mawu akuti “Ufumu wanu udze.” N’cifukwa ciani amapemphela mwanjila imeneyi? N’cifukwa cakuti Yesu anauza otsatila ake kupemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele.

Poyamba, otsatila a Yesu sanamvetse zonse zimene iye anakamba zokhudza Ufumu. Panthawi ina iwo anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeletsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” Koma Yesu sanaŵauze mwacindunji pamene Ufumu wa Mulungu udzabwela. Ndipo izi ziyenela kuti zinawadabwitsa. (Machitidwe 1:6, 7) Kodi zimenezi zitanthauza kuti sitingadziŵe kuti Ufumu wa Mulungu n’ciani, komanso kuti udzabwela liti? Iyai!

Magazini ino ya Nsanja ya Mlonda ikuthandizani kupeza mayankho pa mafunso aya:

  • N’cifukwa ciani tifunikila Ufumu wa Mulungu?

  • Kodi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndani?

  • Nanga Ufumu wa Mulungu udzayamba liti kulamulila dziko lapansi?

  • Kodi Ufumu wa Mulungu udzacita zotani?

  • N’cifukwa ciani tiyenela kucilikiza Ufumu wa Mulungu palipano?

  • Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani