Nchito Yoitanila Anthu ku Cikumbutso Idzayamba pa March 1
1. Kodi nchito yoitanila anthu ku Cikumbutso idzayamba liti? Ndipo n’cifukwa ciani idzatenga nthawi yaitali caka cino?
1 Pa Lacisanu pa March 1, tidzayamba nchito yapadela ya pa caka yoitanila anthu ku Cikumbutso. Cikumbutso cidzacitika pa March 26, kutanthauza kuti nthawi yoitanila anthu idzakhala yaitali kusiyana ndi zaka zakumbuyo. Izi zidzapatsa anthu ambili mwai wakuti alandile tumapepala maka-maka amene akhala m’gawo la mpingo limene lili ndi gawo lalikulu.
2. Ndi makonzedwe ati amene apangidwa a katengedwe ka tumapepala ndi kafoledwe ka gawo?
2 Konzekelani: Akulu adzapeleka malangizo a kafoledwe ka gawo, kuphatikizapo ngati kudzakhala koyenela kusiya tumapepala pa nyumba zimene sitidzapezapo anthu. Ngati tumapepala twina tikali nato pambuyo pomaliza ulaliki wa nyumba ndi nyumba m’gawo lathu, tingatugaŵile pocita ulaliki wa poyela. Woyang’anila utumiki adzaonetsetsa kuti tumapepala tolembedwapo tumene tulipo tuziikidwa pa malo pamene pamakhala magazini ndi zofalitsa zogaŵila kuti ofalitsa atutenge, koma tumapepalato situdzaikidwa tonse pamalopo nthawi imodzi. Tidzafunika kutenga tumapepala tolinganiza mlungu umodzi cabe.
3. Kodi tifunika kukumbukila ciani pamene tiitanila anthu?
3 Tidzakamba Ciani? Tidzafunika kukamba mwacidule, n’colinga cakuti tiitanile anthu oculuka. Pa tsamba 4 pali citsanzo ca mmene tingagaŵile tumapepala mogwilizana ndi gawo lathu. Koma sitidzafunikila kupita kwina mofulumila ngati mwininyumba aoneka waubwenzi kapena ngati ali ndi mafunso. Pamene tigaŵila tumapepala pamapeto a mlungu, tingagaŵilenso magazini ngati kungakhale koyenela. Pa March 2, tidzangogaŵila tumapepala m’malo moyambitsa maphunzilo a Baibo.
4. Cifukwa ciani tiyenela kucilikiza nchito imeneyi mokangalika?
4 Tifuna kuti anthu ambili akakhale nafe pa Cikumbutso. Nkhani ya Cikumbutso idzafotokoza amene Yesu ali m’ceni-ceni. (1 Akor. 11:26) Idzafotokoza mmene imfa yake imatithandizila. (Aroma 6:23) Idzafotokozanso cifukwa cake tifunika kum’kumbukila. (Yoh. 17:3) Tiyeni tonse ticilikize nchito imeneyi mokangalika.