Alandileni!
1. Kodi ndi nthawi iti imene imatipatsa mwai wabwino kwambili wakuti ticitile umboni? Ndipo n’cifukwa ciani?
1 Mwambo wapacaka wa Cikumbutso umatipatsa mwai waukulu wakuti ticitile umboni. Taganizani: Caka cino anthu oposa 10 miliyoni adzapezeka pa Cikumbutso kuti akamve njila zacikondi ziŵili komanso zazikulu zimene dipo la Yesu linaonetsa. (Yoh. 3:16; 15:13) Adzaphunzila za madalitso amene adzapeza cifukwa ca mphatso ya Yehova. (Yes. 65:21-23) Si mkambi yekha amene adzapeleka umboni pa mwambo umenewu. Onse opezekapo adzakhala ndi mwai wocitila umboni wamphamvu mwa kulandila mwacisangalalo anthu amene adzabwela.—Aroma 15:7.
2. Kodi tidzawalandila bwanji mwacisangalalo alendo?
2 M’malo mongokhala cete pa mpando ndi kuyembekeza kuti msonkhano uyambe, bwanji osayamba ndinu kuzidziŵikitsa kwa anthu amene ali pafupi ndi inu? Alendo angakhale omangika ndipo sangadziŵe zimene ayenela kucita. Kupeleka moni mwaubwenzi kudzathandiza kwambili kuti alendo akhale omasuka. Kuti mudziŵe ngati amene wabwela anacita kuitanidwa, mungamufunse ngati ndi koyamba kupezeka nafe pamsonkhano kapena ngati adziŵako anthu ena mumpingo. Mwina mungamupemphe kuti mukhale naye pamodzi kuti muŵelengele pamodzi Baibo ndi kuimba naye nyimbo. Ngati ena akugwilitsila nchito Nyumba ya Ufumu, mungamuonetseko malo mwacidule ngati n’kotheka. Pambuyo pa nkhani, khalani wofunitsitsa kuyankha mafunso amene angakhale nao. Ngati mpingo wanu uyenela kucoka pa Nyumba ya Ufumu mwamsanga kuti ena asonkhanilepo, mungamuuze kuti: “Ndingakonde kumva mmene mwaonela msonkhanowu. Kodi ndingakupezeni bwanji?” Kenako gwilizanani tsiku lakuti mukakumane naye. Akulu maka-maka ayenela kukhala chelu kuti akalimbikitse ofalitsa ozilala.
3. N’cifukwa ciani n’kofunika kuti tikayesetse kulandila bwino anthu pa Cikumbutso?
3 Kwa anthu ambili iyi idzakhala nthawi yoyamba kuona cimwemwe, mtendele, ndi mgwilizano umene timkhala nao m’paladaiso wauzimu monga anthu a Yehova. (Sal. 29:11; Yes. 11:6-9; 65:13, 14) Kodi alendo azikumbukila ciani pambuyo pa Cikumbutso? Zimene azikumbukila zidzadalila kwambili ndi mmene tidzaŵalandilila.