LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • mwb17 April tsa. 2
  • Alandileni Bwino

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Alandileni Bwino
  • Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
  • Nkhani Zofanana
  • Landilani Alendo
    Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Msonkhano (2016)
  • Alandileni!
    Utimiki Wathu wa Ufumu—2013
  • Mungacite Ciani Kuti Mujaile Mu Mpingo Wanu Watsopano?
    Nsanja ya Mlonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzila)—2017
  • Kodi Misonkhano ya Mboni za Yehova Ingakupindulileni Motani?
    Kondwelani Na Moyo Kwamuyaya!—Maphunzilo a Baibo Okambilana Komanso Zocita
Onaninso Zina
Umoyo na Utumiki Wathu Wacikhristu—Kabuku ka Misonkhano —2017
mwb17 April tsa. 2

UMOYO WACIKHRISTU

Alandileni Bwino

Kulandila ndani? Aliyense wobwela kumisonkhano yathu—kuyambila okondwelela atsopano mpaka mabwenzi athu anthawi zonse. (Aroma 15:7; Aheb. 13:2) Akhoza kukhala mboni inzathu yocokela ku dziko lina, kapena wozilala amene wabwela kumisonkhano pambuyo pa zaka. Ganizilani ngati munali imwe. Kodi simunakamva bwino kukulandilani ndi moni wotentha? (Mat. 7:12) Conco, bwanji osakhalako na cizolowezi cozungulila mu Nyumba ya Ufumu, kupatsa moni uyu na uyu misonkhano isanayambe na pambuyo pake? Izi zimapangitsa malo a msonkhano kukhala okondweletsa ndi aubwenzi, ndipo Yehova amalemekezeka. (Mat. 5:16) N’zoona kuti sizingatheke kukamba na munthu aliyense. Koma ngati tonse ticitako zimenezi, aliyense adzamva kuti walandilidwa.a

Mzimu weni-weni woceleza tiyenela kuuonetsa nthawi zonse, osati cabe pa zocitika zapadela monga pa Cikumbutso. Alendo akaona cikondi cacikhristu cimene tiwaonetsa, angayambe kutamanda Mulungu ndi kugwilizana nafe pa kulambila koyela.—Yoh. 13:35.

a Motsatila mfundo za m’Baibo, tifunika kupewa kuyanjana ndi ocotsedwa kapena ozilekanitsa amene angabwele ku misonkhano.—1 Akor. 5:11; 2 Yoh. 10.

M’bale alandila alendo mu Nyumba ya Ufumu

MMENE MUNGATHANDIZILE ALENDO

  • Apatseni moni, auzeni dzina lanu, afunseni lawo

  • Apempheni kuti akhale namwe pamodzi

  • Gaŵanani nawo Baibo na buku yanu ya nyimbo

  • Pambuyo pamsonkhano, afunseni ngati ali na mafunso kuti muwathandize

  • Ngati n’koyenela, apempheni kuti muziphunzila nawo Baibo

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani