Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano?
1. Kodi tidzayamba liti kuphunzila kabuku kakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? ndipo kadzatithandiza bwanji?
1 Kuyambila mlungu wa September 16, pa phunzilo la Baibo la mpingo tidzayamba kuphunzila kabuku kakuti, Ndani Amene Akucita Cifunilo ca Yehova Masiku Ano? Kabuku katsopanoka kamene kanatuluka pa Msonkhano wa Cigawo wakuti, “Tetezani Mtima Wanu,” kanakonzedwa ndi colinga cotsogolela ophunzila Baibo ku gulu. Kuphunzila kabukuka kudzatithandiza kuonjezela ciyamikilo cathu kaamba kokhala mbali ya gulu la Yehova komanso kudzatithandizanso kudziŵa kwambili cida cimeneci ca utumiki.—Sal. 48:13.
2. Kodi tiziphunzila bwanji kabuku kameneka pampingo?
2 Mmene Tiziphunzilila Kabukuka: Wocititsa adzafunika kugaŵa bwino nthaŵi kotelo kuti phunzilo lililonse likhale ndi nthaŵi yokwana bwino. Paciyambi ca phunzilo lililonse iye ndi amene aziyamba mwa kuŵelenga funso limene ndi mutu wa phunzilolo. Ndiyeno, azipempha woŵelenga kuŵelenga ndime yoyamba. Kenako, wocititsa azifunsa omvela funso limene wakonza pa ndime yoyambayo. Pambuyo pake, muyenela kuŵelenga ndi kukambitsilana ndime iliyonse payokha imene iyamba ndi mau akuda kwambili. Ndime ikaŵelengedwa, wocititsa apemphe omvela kupeleka ndemanga zofotokoza mmene ndime iyankhila funso limene ndi mutu wa phunzilolo. Kabukuka kalinso ndi zithunzi-thunzi zambili zimene abale ndi alongo angapelekepo ndemanga. Ngati nthawi ilipo, mungaŵelenge malemba amene mukuona kuti akugwilizana kwambili ndi phunzilolo. Musanayambe phunzilo lotsatila, wocititsa ayenela kubwelelamo mwa kufunsa mafunso amene ali pansi pa tsamba. Ngati m’phunzilolo muli bokosi lakuti, “Dziŵani zambili,” muyenela kuliŵelenga ndi kupempha omvela kufotokoza mmene wophunzila Baibo angapindulile ngati atsatila malangizo amene ali m’bokosi. Ngati nthawi ilipo, pamapeto paphunzilo, wocititsa angagwilitsile nchito mitu ya phunzilo monga mafunso obwelelamo. Kumbukilani kuti simuyenela kutsatila malangizo awa pocititsa phunzilo la Baibo lapanyumba.
3. Kodi tingapindule bwanji mokwanila pophunzila kabukuka?
3 Kuti tipindule mokwanila, tifunika kukonzekela bwino kwambili popita kumisonkhano. Yesetsani kuyankhapo pamsonkhano. Pokambitsilana, ganizilani mmene phunzilo lingapindulitsile ophunzila Baibo. Lolani kuti kuphunzila kabuku katsopanoka kutithandize pophunzitsa ena kuti naonso ayambe kucita cifunilo ca Mulungu ndi kukhala ndi ciyembekezo cokhala ndi moyo wosatha.—1 Yoh. 2:17.